LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 12
  • Kulimba Mtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kulimba Mtima
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli
  • Tiphunzilaponji kwa Yesu?
  • Tengelani Citsanzo ca Yesu
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuti Akakhale Ophunzila Obatizika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 2
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 1
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • ‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzila Anga’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Onaninso Zina
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 12

KUPANGA OPHUNZILA

Yesu akulankhula mwacikondi kwa munthu amene wagwada kwa iye na ophunzila ake.

Maliko 10:17-22

PHUNZILO 12

Kulimba Mtima

Mfundo Yaikulu: “Mafuta ndi zofukiza zonunkhila n’zimene zimasangalatsa mtima, cimodzimodzinso kukoma kwa mnzako cifukwa ca malangizo ake ocokela pansi pa mtima.”—Miy. 27:9.

Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli

Yesu akulankhula mwacikondi kwa munthu amene wagwada kwa iye na ophunzila ake.

VIDIYO: Yesu Apeleka Uphungu kwa Wolamulila Wacinyamata wa Cuma

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Maliko 10:17-22. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. Kodi n’kutheka Yesu anaona makhalidwe abwino ati mwa wolamulila wacinyamata ameneyu?

  2. N’cifukwa ciyani Yesu anafunikila cikondi komanso kulimba mtima kuti am’patse uphungu mnyamatayo?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Ophunzila athu tizilankhula nawo mwacikondi komanso mosapita m’mbali kuti apite bwino patsogolo kuuzimu.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Thandizani wophunzila wanu kudziikila zolinga na kuzikwanilitsa.

  1. Seŵenzetsani mbali yakuti “Colinga” m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

  2. Thandizani wophunzila wanu kudziŵa zimene ayenela kucita kuti akwanilitse zolinga zing’ono-zing’ono komanso zikulu-zikulu.

  3. Muyamikileni nthawi zonse pamene akupita patsogolo.

4. Zindikilani zopinga zimene zingam’bweze kumbuyo, ndipo m’thandizeni kuti azigonjetse.

  1. Dzifunseni kuti:

    • ‘Ngati wophunzila wanga sakupita patsogolo kuti akabatizike, cikum’pinga n’ciyani?’

    • ‘Nanga ningam’thandize bwanji?’

  2. Pemphelelani kulimba mtima kuti mukathe kukambilana naye, mwacikondi komabe mosapita m’mbali, zimene afunikila kucita.

5. Asiyeni maphunzilo amtatakuya osapita patsogolo.

  1. Kuti mudziŵe ngati wophunzila wanu akupita patsogolo kapena ayi, dzifunseni kuti:

    • ‘Kodi amagwilitsa nchito zimene akuphunzila?’

    • ‘Kodi amapezeka ku misonkhano ya mpingo, ndipo amauzako ena zimene amaphunzila?’

    • ‘Popeza waphunzila kwa nthawi ndithu, kodi lomba akufuna kukhala Mboni?’

  2. Ngati wophunzila Baibo sakufuna kupita patsogolo, citani izi:

    • M’pempheni kuti aganizilepo pa cimene cikumulepheletsa.

    • Mosamala komanso mwaubwino, m’fotokozeleni cifukwa cake simudzapitiliza kuphunzila naye.

    • Muuzeni zofunikila kugwililapo nchito ngati akufuna kuti m’tsogolo mukayambilenso kuphunzila naye.

ONANINSO MALEMBA AWA

Sal. 141:5; Miy. 25:12; 27:6; 1 Akor. 9:26; Akol. 4:5, 6

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani