LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w12 9/1 masa. 8-11
  • Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2012
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Yesu Anali Kuonela Akazi
  • Mfundo za M’Baibo Zimathandiza Akazi Kukhala Osangalala
  • Malo a Akazi m’Kakonzedwe ka Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2012
w12 9/1 masa. 8-11

Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa

ALI padziko lapansi, Yesu anasonyeza bwino makhalidwe a Atate wake komanso mmene amacitila zinthu. Iye anati: “Sindicita kanthu mongoganiza ndekha. Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsila. . . . Ndimacita zinthu zomukondweletsa nthawi zonse.” (Yohane 8:28, 29; Akolose 1:15) Conco, tingadziŵe mmene Mulungu amaonela akazi tikaphunzila na kumvetsa bwino mmene Yesu anali kacitila zinthu na akazi, komanso mmene anali kuwaonela.

Kucokela pa zimene zinalembedwa m’Mauthenga Abwino, akatswili ambili amaphunzilo amavomeleza kuti Yesu anali kuona akazi mosiyana kwambili na mmene anthu ena pa nthawiyo anali kuwaonela. Kodi n’cifukwa ciani Yesu anali kulemekeza akazi? Kodi zimene Yesu anali kuphunzitsa zimathandizanso masiku ano kuti akazi azilemekezedwa?

Mmene Yesu Anali Kuonela Akazi

Yesu saone akazi kuti anangodwela kuti azikhutulitsa cinalolako ca amuna ca kugonana. Atsogoleli ena acipembedzo Aaciyuda anali kuona kuti kucita zinthu na akazi kungapangitse kuti munthu acite ciwelewele. Cifukwa ca zimenezi akazi sanali kuloledwa kulankhula ni amuna pagulu komanso sanali kuloledwa kuyenda osaphimba kumutu. Koma Yesu analangiza amuna kuti azilemekeza akazi, ndipo asamawasale, koma kuti amunawo azidziletsa.—Mateyu 5:28.

Yesu ananenanso kuti: “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatila wina, wacita cigololo molakwila mkaziyo.” (Maliko 10:11, 12) Conco iye anatsutsa zimene Arabi anali kuphunzitsa kuti amuna azisiya akazi awo “pa cifukwa ciliconse.” (Mateyu 19:3, 9) Mfundo yoti mwamuna akacita cigololo amalakwila mkazi wake inali yacilendo kwa Ayuda ambili. Arabi anali kuwaphunzitsa kuti mwamuna akacita cigololo sanalakwile mkazi wake. Koma mkazi akacita cigololo ni amene anali kuonedwa kuti ni wosakhulupilika. Katswili wina wa Baibo ananena kuti: “Pamene Yesu ananena kuti mwamuna akacita cigololo nayenso walakwila mkazi wake, anasonyeza kuti nawonso akazi ni ofunika.”

Mmene mfundoyi imathandizila masiku ano: Mu mpingo wa Mboni za Yehova, akazi amakhala momasuka na amuna pa misonkhano. Komabe, iwo amaonetsetsa kuti pakati pawo sipakucitika zinthu zosayenela kapena kuzolowelana mopambanitsa cifukwa amuna acikhristu amaona ‘akazi acikulile ngati amayi awo, akazi acitsikana ngati alongo awo ndipo sakhala na maganizo alionse oipa.’—1 Timoteyo 5:2..

Yesu anali kuphunzitsanso akazi. Arabi anali kuona kuti akazi ni osayenela kuwaphunzitsa. Koma mosiyana na zimenezi, Yesu anali kuwaphunzitsa komanso anali kuwalimbikitsa kunena momasuka maganizo awo. Yesu sanalepheletse Mariya kukhala na mwayi womvetsela pamene iyeyo anali kuphunzitsa, ndipo pamenepa anasonyeza kuti nchito ya akazi si kuphika cabe. (Luka 10:38-42) Malita, m’bale wake wa Mariya, nayenso anapindula na zimene Yesu anali kuphunzitsa, ndipo umboni wa zimenezi ni zomwe iye anayankha Yesu, Lazaro atamwalila.—Yohane 11:21-27.

Yesu anali kucitanso cidwi na zimene akazi amaganiza pa nkhani zosiyana-siyana. Pa nthawi imeneyo, akazi ambili aciyuda anali kukhulupilila kuti munthu amakhala wosangalala akakhala na mwana wamwamuna wochuka, apo ayi mneneli. Pa nthawi ina mayi wina atafuula kuti: “Ndi wodala mayi amene mimba yake inanyamula inu,” Yesu anamuuza mfundo ina yosonyeza kuti maganizo amenewa ni olakwika. (Luka 11:27, 28) Zimene Yesu anauza mayiyu zikusonyeza kuti kumvela Mulungu ndiye kofunika kwambili kuposa kuchuka.—Yohane 8:32.

Mmene mfundoyi imathandizila masiku ano: Akulu mumpingo wacikhristu amalola kuti akazi aziyankha momasuka pamisonkhano. Iwo amayamikila akazi okonda zinthu zauzimu cifukwa cokhala “aphunzitsi a zinthu zabwino” pa zocita zawo zonse. (Tito 2:3) Akazi ni odalilikanso kwambili pa nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Salimo 68:11; onani bokosi lakuti, “Kodi Mtumwi Paulo Analetsa Akazi Kulankhula?” pa tsamba 9.

Yesu sanali kuona kuti akazi ni otsika. Kale, ana aakazi anali kuonedwa kuti ni otsika poyelekeza ni ana aamuna. Mu Talmud muli mawu awa osonyeza kuti anthu ambili analidi na maganizo amenewa: “Wodala ni munthu amene ali ni ana aamuna, koma tsoka kwa iye amene ali ni ana aakazi.” Makolo ena anali kuona kuti kukhala na mwana wamkazi ni cinchito cifukwa anali kuyenela kumupezela mwamuna, kumupelekela malowolo, komanso anali kuona kuti mwana wamkaziyo sadzawathandiza akadzakalamba.

Yesu anasonyeza kuti palibe kusiyana pakati pa mwana wamkazi ni wamwamuna. Iye anacita zimenezi poukitsa mwana wamkazi wa Yairo monganso anacitila poukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye wa ku Nayini. (Maliko 5:35, 41, 42; Luka 7:11-15) Yesu atacilitsa mayi wina “amene mzimu woipa unamudwalitsa zaka 18,” anamuchula kuti “mwana wa Abulahamu.” Zimene Yesu anacitazi, pochula mkaziyu kuti “mwana wa Abulahamu,” zinali zacilendo kwa Ayuda. (Luka 13:10-16) Pomuchula mayiyo na mawu olemekeza amenewa, Yesu anazindikila kuti mayiyu anali na cikhulupililo colimba, ndipo sanali wotsika poyelekezela na amuna.—Luka 19:9; Agalatiya 3:7.

Mmene mfundoyi imathandizila masiku ano: Ku Asia kuli mwambi wakuti: “Kulela mwana wamkazi n’kosapindulila cifukwa kuli ngati kuthilila dimba la munthu wina.” Koma makolo acikhristu sakhala na maganizo amenewa ndipo iwo amasamalila mofanana ana awo, aamuna kapena aakazi. Iwo amaonetsetsa kuti ana awo onse akusamalidwa mofanana pa nkhani ya maphunzilo na thandizo lacipatala..

Yesu analemekeza Mariya wa Magadala pomuuza kuti akadziŵitse ophunzila ake za kuuka kwake

Yesu anali kuona kuti akazi nawonso ni odalilika. M’khoti la Ayuda, umboni wa mkazi unali kuonedwa mofanana ni wa kapolo. Wolemba mbili wina wa m’nthawi ya atumwi, dzina lake Josephus, analangiza anthu kuti: “Musamagwilitse nchito umboni wa akazi cifukwa ni acibwana-bwana.”

Mosiyana na zimenezi, Yesu atangoukitsidwa anaonekela kwa akazi, ndipo anawauza kuti akauze anthu za kuuka kwake. (Mateyu 28:1, 8-10) Ngakhale kuti akazi okhulupilika amenewa anali mboni zoona na maso pamene Mbuye wawo anaphedwa na kuikidwa m’manda, atumwiwo zinawavuta kukhulupilila kuti zimene akaziwo anali kunena zinali zoona. (Mateyu 27:55, 56, 61; Luka 24:10, 11) Komabe Khristu poonekela coyamba kwa akazi, anasonyeza kuti akazi ni ofunikanso pa nkhani yocitila umboni mofanana ni amuna.—Machitidwe 1:8, 14.

Mmene mfundoyi imathandizila masiku ano: M’mipingo ya Mboni za Yehova, akulu amasonyeza kuti saona kuti akazi ni otsika. Iwo amacita zimenezi pogwilitsa nchito zimene akaziwo amanena. Komanso amuna acikhristu ‘amapatsa ulemu’ akazi awo mwa kumvetsela zimene akunena.—1 Petulo 3:7; Genesis 21:12..

Mfundo za M’Baibo Zimathandiza Akazi Kukhala Osangalala

Amuna amene amatsatila mfundo za m’Baibo amalemekeza kwambili akazi

Amuna akamatengela citsanzo ca Khristu, amalemekeza akazi awo komanso kuwapatsa ufulu ngati mmene Mulungu anafunila poyamba. (Genesis 1:27, 28) M’malo motsatila maganizo oti amuna ni apamwamba kuposa akazi, amuna acikhristu amatsatila mfundo za m’Baibo. Zimenezi zimathandiza kuti akazi awo azikhala osangalala m’banja.—Aefeso 5:28, 29.

Pa nthawi imene mayi wina, dzina lake Yelena, anali kuyamba kuphunzila Baibo n’kuti mwamuna wake akumucitila nkhanza. Komanso iye anakulila m’dela limene amuna anali kukonda kuba azimayi kuti akakhale akazi awo, ndiponso kucitila nkhanza akazi kunali kofala. Yelena ananena kuti: “Zimene n’naphunzila m’Baibo zinanithandiza kwambili. N’nayamba kuona kuti Mulungu amanikonda kwambili komanso amaniona kuti nine wofunika. Ninaonanso kuti ngati mwamuna wanga wayamba kuphunzila Baibo angayambe kunikonda.” Patapita nthawi mwamuna wake anayambadi kuphunzila Baibo, kenako anabatizika n’kukhala Mboni ya Yehova. Yelena ananenanso kuti: “Mwamuna wanga anasiya kunicitila nkhanza ndipo tinaphunzila kukhululukilana.” Pomalizila pake Yelena anati: “Mfundo za m’Baibo zanithandiza kwambili kuti niziona kuti ndine wofunika komanso wotetezeka m’banja.”—Akolose 3:13, 18, 19.

Pali mabanja ambili amene apindula cifukwa cophunzila Baibo. Akazi ambili-mbili akusangalala m’banja cifukwa coti iwo na amuna awo akuyesetsa kugwilitsa nchito mfundo za m’Baibo m’banja mwawo. Akazi otelewa amalemekezedwa, amalimbikitsidwa, komanso amakhala omasuka kuceza na Akhristu anzawo.—Yohane 13:34, 35.

Amuna na akazi acikhristu amazindikila kuti onse ni ocimwa ndipo ni opanda ungwilo. Iwo amadziŵanso kuti ali mbali ya cilengedwe cimene “cinapelekedwa ku mkhalidwe wopanda pake.” Komabe amazindikilanso kuti kukhala pa ubwenzi na Atate wawo, Yehova Mulungu, kumawathandiza kukhala na ciyembekezo coti ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala na ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.’ Cimenecitu ni ciyembekezo cosangalatsa kwambili kwa amuna na akazi omwe, amene onse Mulungu amawakonda.—Aroma 8:20, 21.

Kodi Mtumwi Paulo Analetsa Akazi Kulankhula?

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Akazi akhale cete m’mipingo.” (1 Akorinto 14:34) Kodi iye anali kutanthauza ciani ponena mawu amenewa? Kodi anali kuwadelela akazi? Ayi, cifukwatu iye anena kuti akazi amaphunzitsa zinthu zothandiza. (2 Timoteyo 1:5; Tito 2:3-5) M’kalata yake yopita kwa Akorinto, Paulo sanangolangiza akazi okha koma analangizanso amuna, omwe anali ni mphatso yolankhula malilime komanso yonenela, kuti ‘azikhala cete’ munthu wina akamalankhula.a (1 Akorinto 14:26-30, 33) Ziyenela kuti akazi ena anali kusangalala kwambili na zimene anali kuphunzila mumpingo moti munthu wina akamalankhula anali kumudula mawu n’kuyamba kumufunsa mafunso. Izi zinali zofala pa nthawiyo. Conco kuti pasakhale cisokonezo, Paulo anawauza kuti ‘azikafunsa amuna awo kunyumba.’—1 Akorinto 14:35.

a Kuti mudziŵe zambili za nchito imene akazi amagwila mumpingo, onani nkhani yakuti “Kodi Akazi a Mboni za Yehova Amaphunzitsa Mawu a Mulungu?” patsamba 23.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani