Pangani Zosankha Zanu Mwanzelu
“Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu.”—MIY. 3:5.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Kodi kucita zinthu moganiza bwino popanga zosankha kumatanthauzanji?
Kodi tingakulitse bwanji luso lopanga zosankha mwanzelu?
N’ciani cingatithandize kucita zimene tasankha?
1, 2. Kodi mumamva bwanji mukafuna kupanga cosankha? Nanga mumamva bwanji mukaganizila zosankha zimene munapanga kale?
TSIKU ndi tsiku timafunikila kupanga zosankha. Kodi inu mumamva bwanji mukafuna kupanga cosankha cina cake? Anthu ena amakonda kupanga okha zosankha zilizonse. Iwo amaona kuti ndi ufulu wao kupanga zosankha ndipo amakhumudwa ngati munthu wina afuna kuwathandiza. Koma pali ena amene amaopa kupanga zosankha pa nkhani zofunika kwambili. Ndipo ena amaonononga ndalama zambili kufuna-funa malangizo m’mabuku kapena kwa aphungu.
2 Ambili a ife timadziŵa kuti sitingakwanitse kupanga zosankha zanzelu pa zinthu zina. Koma timayamikila kukhala ndi mwai wopanga zosankha zimene tifuna. (Agal. 6:5) Ngakhale zili conco, timadziŵa kuti si zosankha zonse zimene timapanga zimene ndi zanzelu kapena zothandiza.
3. Ndi malangizo ati amene angatithandize kupanga zosankha? Nanga timakumana ndi vuto lotani?
3 Pokhala atumiki a Yehova, ndife osangalala kuti iye watipatsa malangizo omveka bwino okhudza zinthu zofunika kwambili pa umoyo wathu. Timadziŵa kuti ngati titsatila malangizo amenewo, tingapange zosankha zimene zingasangalatse Yehova ndi kutipindulitsa. Komabe, nthawi zina tingakumane ndi zinthu zimene Mau a Mulungu safotokoza mwacindunji. Conco, kodi tingasankhe bwanji zinthu zoyenela kucita? Mwacitsanzo, Baibo imaletsa kuba. (Aef. 4:28) Koma kodi kuba kumaphatikizapo ciani? Kodi kumadalila mtundu wa cinthu cimene munthu watenga kapena colinga cake? Kodi timapanga bwanji zosankha pa nkhani zimene palibe malamulo acindunji? Ndipo n’ciani cingatithandize?
MUZIGANIZA BWINO POPANGA ZOSANKHA
4. Ndi malangizo otani amene tingalandile pamene tifuna kupanga cosankha?
4 Tikauza Mkristu mnzathu kuti tifuna kupanga cosankha pa nkhani inayake yaikulu, iye angatiuze kuti tifunikila kuganizila bwino tisanapange cosankhaco. Malangizo amenewa ndi abwino. Baibo imaticenjeza kuti sitiyenela kucita zinthu mosaganizila. Iyo imati: “Aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miy. 21:5) Koma kodi kucita zinthu moganizila bwino kumatanthauzanji? Kodi kumatathauza cabe kuti tipatule nthawi yoganizila bwino nkhaniyo ndi kusankha zocita mwanzelu? Kucita zimenezi n’kofunika kuti tipange cosankha cabwino, koma kucita zinthu moganizila bwino kumaphatikizapo zambili.—Aroma 12:3; 1 Pet. 4:7.
5. N’cifukwa ciani tilibe maganizo angwilo?
5 Tisaiŵale kuti palibe munthu amene ali ndi maganizo angwilo. N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa cakuti tonse tinabadwa ocimwa, ndipo matupi ndi maganizo athu ndi opanda ungwilo. (Sal. 51:5; Aroma 3:23) Kuonjezela pamenepa, kale Satana anali ‘kucitsa khungu’ maganizo athu, ndipo sitinali kudziŵa Yehova ndi miyezo yake yacilungamo. (2 Akor. 4:4; Tito 3:3) Conco, ngati tipanga zosankha motsatila maganizo athu, ndiye kuti tingasankhe molakwika kwambili ngakhale titayesetsa kuganizila nkhaniyo mozama.—Miy. 14:12.
6. N’ciani cingatithandize kukhala oganiza bwino?
6 Ngakhale kuti ife tilibe matupi ndi maganizo angwilo, Yehova, Atate wathu wakumwamba, amacita zinthu zonse mwangwilo. (Deut. 32:4) N’cosangalatsa kuti iye watithandiza kusintha maganizo athu kuti tizicita zinthu mwanzelu. (Ŵelengani 2 Timoteyo 1:7.) Ife Akristu tifunika kuganiza bwino ndi kucita zinthu mwanzelu. Timafunikila kulamulila maganizo ndi zofuna zathu kuti titengele mmene Yehova amaganizila ndi kucitila zinthu.
7, 8. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti n’zotheka kupanga cosankha canzelu mosasamala kanthu za mavuto kapena zonena za anthu ena.
7 Ganizilani citsanzo ici: Anthu ena amene anasamukila ku maiko ena amakonda kutumiza ana ao aang’ono kwa agogo ao kuti aziwasamalila. Colinga cao ndi kupitiliza kugwila nchito kuti apeze ndalama.a Mkazi wina amene anasamukila ku dziko lina anabeleka mwana wamwamuna wokongola. Nthawi imeneyo, mkaziyo anayamba kuphunzila Baibo ndipo anapita patsogolo. Anzake ndi acibale ake anayamba kumukakamiza kuti iye ndi mwamuna wake atumize mwanayo kwa agogo ake. Koma cifukwa ca kuphunzila kwake Baibo, mkaziyo anazindikila kuti iye monga kholo ali ndi udindo wocokela kwa Mulungu wolela mwanayo. (Sal. 127:3; Aef. 6:4) Kodi iye anayenela kutsatila zimene anthu ambili anali kucita? Kapena anayenela kutsatila zimene anali kuphunzila m’Baibo ndi kulola kukumana ndi mavuto a zacuma kapena kusekedwa ndi anthu? Kodi mukanakhala inu mukanacita ciani?
8 Cifukwa ca nkhawa, mkazi ameneyo anapemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima kuti am’thandize kudziŵa zoyenela kucita. Pambuyo pofunsa amene anali kuphunzila naye Baibo ndi anthu ena mumpingo, anayamba kuona mmene Yehova anali kuonela nkhaniyo. Iye anazindikila kuti mwana wake sangakule bwino ngati akhala kutali ndi makolo ake kwa nthawi yaitali. Iye atapenda nkhaniyo mwa kugwilitsila nchito Malemba, anaona kuti sanayenele kutumiza mwana wakeyo kwa agogo ake. Mwamuna wake anaona mmene mpingo unali kuthandizila banja lake ndiponso kuti mwanayo anali wosangalala ndi wathanzi. Mwamunayo analola kuphunzila Baibo ndipo anayamba kupezeka pa misonkhano ndi mkazi wake.
9, 10. Kodi kucita zinthu moganiza bwino kumatanthauzanji? Ndipo tingacite bwanji zimenezo?
9 Ici ndi citsanzo cimodzi cabe coonetsa kuti kucita zinthu moganizila bwino sikutanthauza kungotsatila maganizo a anthu ena. Maganizo athu opanda ungwilo ali ngati nkholoko yotaya. Kugwilitsila nchito kholoko yotelo kungationongetse zinthu zambili. (Yer. 17:9) Maganizo athu ndi mtima wathu ziyenela kutsogoleledwa ndi miyezo yodalilika ya Mulungu.—Ŵelengani Yesaya 55:8, 9.
10 Conco, n’zomveka kuti Baibo imatilangiza kuti: “Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukila m’njila zako zonse, ndipo iye adzawongola njila zako.” (Miyambo 3:5, 6) Onani kuti Baibo imanena kuti “usadalile luso lako lomvetsa zinthu.” Iyo imapitiliza kuti “uzim’kumbukila [Yehova].” Iye ndiye ali ndi maganizo angwilo. Conco, pamene tifuna kupanga cosankha, tiyenela kupenda zimene Baibo imanena kuti tidziŵe maganizo a Mulungu pankhaniyo. Kenako tiyenela kusankha zocita mogwilizana ndi zimene Mau a Mulungu amanena. Kucita zinthu mogwilizana ndi maganizo a Yehova ndiko kucita zinthu moganiza bwino.
PHUNZITSANI MPHAMVU ZANU ZA KULINGALILA
11. Kodi tingaphunzile bwanji kupanga zosankha zanzelu?
11 Si copepuka kupanga zosankha zanzelu ndi kucita zimene tasankhazo. Zimenezi zingakhale zovuta kwambili maka-maka kwa atsopano m’coonadi kapena amene angoyamba kupita patsogolo mwa kuuzimu. Koma anthu otelo amene Baibo imati ndi makanda a kuuzimu, angapite patsogolo mwa kuuzimu. Ganizilani mmene mwana amaphunzilila kuyenda. Iye amayamba pang’ono-pang’ono ndipo amacita zimenezo mobweleza-bweleza. Izi n’zofanana ndi zimene khanda la kuuzimu limafunikila kucita kuti lipange zosankha zanzelu. Kumbukilani zimene mtumwi Paulo anafotokoza ponena za anthu okhwima kuuzimu. Iye anakamba kuti io ‘amagwilitsila nchito mphamvu zao za kuzindikila kuti aphunzitse mphamvuzo kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.’ Mau akuti ‘amagwilitsila nchito’ ndi liu lakuti ‘kuphunzitsa,’ amaonetsa kuti pafunika khama ndi nthawi kuti munthu akhwime, ndipo zimenezi n’zofunika kwa atsopano m’coonadi.—Ŵelengani Aheberi 5:13, 14.
12. Kodi tingacite ciani kuti tikhale ndi luso lopanga zosankha zanzelu?
12 Monga mmene taonela kuciyambi kwa nkhani ino, tsiku lililonse timapanga zosankha, zazikulu ndi zazing’ono. Malinga ndi zimene anthu ena anafufuza, pafupi-fupi hafu ya zimene timasankha kucita timangozicita mwacibadwa popanda kuganizila mosamalitsa. Mwacitsanzo, mwina m’mawa uliwonse mumafunika kusankha zovala zimene muyenela kuvala. Mungaone ngati kucita zimenezi ndi nkhani yaing’ono ndipo mungasankhe zovala zimene mungafune popanda kuganizila mosamala maka-maka mukamacita zinthu mofulumila. Komabe, ndi cinthu cofunika kuganizila ngati zovala zimene mwavala ndi zoyenela mtumiki wa Yehova. (2 Akor. 6:3, 4) Mukafuna kugula zovala, mungaganizile za mafashoni ndi zinthu zina koma mufunikilanso kuganizila ngati ndi zaulemu komanso ngati muli ndi ndalama zokwanila. Tikasankha mwanzelu pankhani zimenezi, tidzaphunzitsa mphamvu zathu za kulingalila zimene zingatithandize kupanga zosankha zabwino pa nkhani zikulu-zikulu.—Luka 16:10; 1 Akor. 10:31.
KULITSANI MTIMA WOFUNA KUCITA ZABWINO
13. N’ciani cimafunikila kuti ticite zimene tasankha?
13 Tonse timadziŵa kuti kucita zinthu mogwilizana ndi zosankha zathu zanzelu zimene tapanga kungakhale kovuta. Mwacitsanzo, ena amene amafuna kusiya kusuta fodya amalephele cifukwa cakuti alibe mtima wofunitsitsa kusiya. Cimene cimafunika ndi cakuti io akhale otsimikiza mtima kucita zimene asankhazo. Ena amaona kuti tingakulitse mtima wofuna kucita zinthu zabwino monga mmene timalimbitsila minofu ya matupi athu. Ngati tigwilitsila nchito kwambili minofu imeneyi, m’pamene imakhala yamphamvu kwambili. Koma ngati sitiigwilitsila nchito kaŵili-kaŵili imakhala yofooka. Conco, kodi n’ciani cingatithandize kukulitsa mtima wofuna kucita zimene tasankha? Tiyenela kupempha Yehova kuti atithandize.—Ŵelengani Afilipi 2:13.
14. N’cifukwa ciani Paulo anakwanitsa kucita zinthu zimene anaona kuti n’zoyenela?
14 Pa umoyo wake, Paulo anaona kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Iye anadandaula kuti: “Ndimafuna kucita zabwino, koma sinditha kuzicita.” Paulo anali kudziŵa zoyenela kucita, koma zinthu zina zinali kumulepheletsa kucita zimenezo. Iye anati: “Mumtima mwanga ndimasangalala kwambili ndi cilamulo ca Mulungu, koma ndimaona cilamulo cina m’ziwalo zanga cikumenyana ndi cilamulo ca m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa cilamulo ca ucimo cimene cili m’ziwalo zanga.” Kodi iye analibe ciyembekezo ciliconse? Iyai. Iye ananena kuti: “Mulungu adzatelo kudzela mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:18, 22-25) Pa lemba lina iye analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.
15. N’ciani cimacitika kwa anthu amene amayesetsa kukwanilitsa zosankha zao kapena kwa amene amakaika-kaika?
15 Conco, n’zoonekelatu kuti tiyenela kupanga zosankha zabwino ndi kuyesetsa kuzikwanilitsa kuti tikondweletse Mulungu. Kumbukilani zimene Eliya anauza anthu olambila Baala ndi Aisiraeli opanduka pa Phili la Karimeli. Iye anati: “Kodi mukayika-kayika mpaka liti? Ngati Yehova ali Mulungu woona m’tsateni, koma ngati Baala ndiye Mulungu woona tsatilani ameneyo.” (1 Mafumu 18:21) Aisiraeli anali kudziŵa zoyenela kucita koma anali ‘kukayika-kayika.’ Mosiyana kwambili ndi zimenezi, zaka zingapo m’mbuyomo, Yoswa anapeleka citsanzo cabwino kwa Aisiraeli pamene anawauza kuti: “Ngati kutumikila Yehova kukukuipilani, sankhani lelo amene mukufuna kum’tumikila . . . Koma ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikila Yehova.” (Yoswa 24:15) Kodi iye anapeza madalitso otani cifukwa cosankha kutumikila Mulungu? Yoswa ndi ena amene anakhala kumbali yake analandila Dziko Lolonjezedwa limene linali “dziko loyenda mkaka ndi uci.”—Yoswa 5:6.
PANGANI ZOSANKHA ZANZELU KUTI MUDALITSIDWE
16, 17. Pelekani citsanzo coonetsa madalitso amene munthu amapeza cifukwa copanga zosankha mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.
16 Ganizilani citsanzo ici: Mbale wina wokwatila amene anabatizika posacedwapa ali ndi ana atatu acicepele. Tsiku lina, mnzake kunchito anamuuza kuti io aloŵe nchito ku kampani ina imene imalipila malipilo apamwamba ndi kuthandiza anchito pa zinthu zina zambili. M’baleyo anaganizila nkhaniyo ndi kuipemphelela. Iye anasankha nchito ya malipilo ocepa kuti azipezeka pamisonkhano ndi mu ulaliki pamodzi ndi banja lake kumapeto kwa mlungu. Iye anadziŵa kuti zidzakhala zovuta kucita zimenezi ngati walowa nchito yatsopanoyo. Kodi mukanakhala inu mukanacita ciani?
17 M’baleyo anakana nchitoyo poona kuti madalitso a kuuzimu amene amapeza ndi ofunika kuposa ndalama zimene angapeze ku nchito yatsopanoyo. Kodi munganiza kuti iye anadandaula cifukwa copanga cosankha cimeneci? Iyai. Iye anadziŵa kuti zinthu za kuuzimu ndi zofunika kwambili kwa iye ndi banja lake kuposa malipilo apamwamba. M’baleyo ndi mkazi wake anasangalala kwambili pamene mwana wao wamkazi wazaka 10 anawauza kuti amakonda makolo akewo, abale ndi alongo ndi Yehova. Mwanayo anakamba kuti afuna kudzipeleka kwa Yehova ndi kubatizika. Mwacionekela iye anayamikila kwambili kuti atate wake anaika zinthu za kuuzimu patsogolo.
18. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti tsiku lililonse tizipanga zosankha zanzelu?
18 Yesu Kristu amene ndi Mose Wamkulu akutsogolela olambila Yehova oona kucoka m’dziko la Satana lino limene ndi loopsa ngati cipululu. Monga Yoswa Wamkulu, Yesu watsala pang’ono kuononga dongosolo lino loipa la zinthu ndi kulowetsa otsatila ake m’dziko latsopano lacilungamo. (2 Pet. 3:13) Ino si nthawi yakuti tiyambenso kukhala ndi maganizo, zizolowezi ndi zolinga zoipa zimene tinali nazo poyamba. Koma ndi nthawi yakuti tiyesetse kuzindikila cifunilo ca Mulungu kwa ife. (Aroma 12:2; 2 Akor. 13:5) Conco, onetsetsani kuti zosankha zimene mumapanga tsiku lililonse zizionetsa kuti ndinu woyenelela kulandila madalitso osatha a Mulungu.—Ŵelengani Aheberi 10:38, 39.
[Mau apansi]
a Cifukwa cina cimene anthu amacitila zimenezo ndi cakuti agogo akaonetse adzukulu ao kwa anzao ndi acibale ao.
[Cithunzi papeji 24]
Ngati tipanga zosankha mwanzelu tsiku lililonse, timaphunzitsa mphamvu zathu za kulingalila (Onani ndime 11)
[Cithunzi papeji 26]
Muzipanga zosankha zanu mwanzelu kuti mupeze cimwemwe m’gulu la Mulungu (Onani ndime 18)