KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi Baibulo ndi Maudi a Mulungu?
Baibulo ndi buku lapadela ndipo ndi mmene Mau a Mulungu ayenela kukhalila. Mabaibulo mabiliyoni ambili asindikizidwa m’zinenelo zambili-mbili. Malangizo a m’Baibulo amathandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino.—Ŵelengani 1 Atesalonika 2:13; 2 Timoteyo 3:16.
Timadziwa kuti Baibulo ndi locokela kwa Mulungu cifukwa limanena molondola zinthu zimene zidzacitika mtsogolo. Palibe munthu amene angakwanitse kutelo pa iye yekha. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zili m’buku la Yesaya. Cigawo ca mpukutu wa Yesaya cimene cinalembedwa zaka 100 Yesu asanabadwe, cinapezeka m’phanga pafupi ndi Nyanja Yakufa. Mau a m’cigawo cimeneco amati mzinda wa Babulo udzakhala malo opanda anthu. Mau amenewa anakwanilitsidwa zaka zambili pambuyo pa utumiki wa Yesu wapadziko lapansi.—Ŵelengani Yesaya 13:19, 20; 2 Petulo 1:20, 21.
Kodi Baibulo linalembedwa bwanji?
Kulemba Baibulo kunatenga zaka zoposa 1,600. Baibulo linalembedwa ndi anthu 40. Zimene io analemba zili ndi mfundo yaikulu imodzi ndipo sizitsutsana. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Zinatheka cifukwa cakuti olembawo anauzilidwa ndi Mulungu.—Ŵelengani 2 Samueli 23:2.
Nthawi zina Mulungu anali kulankhula ndi anthu amene analemba Baibulo kupyolela mwa angelo, m’masomphenya ndi m’maloto. Nthawi zambili Mulungu anali kuika maganizo ake mwa olembawo ndi kuwalola kusankha mau oyenelela kuti afotokoze uthenga wake.—Ŵelengani Chivumbulutso 1:1; 21:3-5.