KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi timapindula bwanji ndi imfa ya Yesu?
Mulungu atalenga anthu, anafuna kuti io akhale padziko lapansi kwamuyaya ndi kuti asamadwale kapena kufa. Koma munthu woyamba Adamu, sanamvele Mlengi ndipo anataya mwai wokhala ndi moyo wamuyaya. Popeza ndife ana a Adamu, timafa cifukwa iye anacimwa. (Aroma 5:8, 12; 6:23) Conco, Mulungu woona Yehova, anatuma Mwana wake Yesu padziko lapansi kuti adzapeleke moyo wake ndi kuombola moyo umene Adamu anataya.—Ŵelengani Yohane 3:16.
Yesu anafa kotelo kuti anthu akapeze moyo wosatha. Kodi muganiza kuti moyo wosatha padziko lapansi udzakhala wotani?
Cifukwa ca imfa ya Yesu, machimo athu amakhululukidwa ndipo timakhala ndi ciyembekezo ca moyo wamuyaya. Baibulo limatiuza mmene moyo padziko lapansi udzakhalila pamene sikudzakhala ukalamba, matenda ndi imfa.—Ŵelengani Yesaya 25:8; 33:24; Chivumbulutso 21:4, 5.
Kodi tiyenela kukumbukila bwanji imfa ya Yesu?
Usiku wakuti maŵa aphedwa, Yesu anauza otsatila ake kuti azikumbukila imfa yake mwa kucita mwambo wosavuta. Kukumbukila imfa ya Yesu caka ciliconse mwa njila imeneyi kumatipatsa mwai woyamikila cikondi cacikulu cimene Yehova ndi Yesu anationetsa.—Ŵelengani Luka 22:19, 20; 1 Yohane 4:9, 10.
Caka cino, Cikumbutso ca imfa ya Yesu cidzakhalako pa Mande, April 14 dzuŵa litaloŵa. Tikupemphani kuti mukasonkhane ndi Mboni za Yehova kumene mukhala.—Ŵelengani Aroma 1:11, 12.