LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 9/15 masa. 17-21
  • Makolo—Wetani Ana Anu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Makolo—Wetani Ana Anu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ADZIŴENI BWINO ANA ANU
  • PHUNZITSANI ANA ANU
  • TSOGOLELANI ANA ANU
  • Inu Makolo—Thandizani Ana Anu Kukonda Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 2
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kukonda Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 9/15 masa. 17-21

Makolo—Wetani Ana Anu

“Uyenela kudziŵa bwino maonekedwe a ziŵeto zako.”—MIY. 27:23.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi makolo ayenela kucita ciani kuti aŵete ana ao?

  • N’ciani cingathandize makolo kuphunzitsa ana ao mwa kuuzimu?

  • Kodi acicepele ambili apindula motani ndi Kulambila kwa Pabanja?

1, 2. (a) Kodi m’busa waciisiraeli anali ndi maudindo otani? (b) Nanga makolo ali ngati abusa m’njila iti?

ABUSA m’nthawi ya Isiraeli wakale anali ndi nchito yovuta kwambili. Iwo anafunikila kupilila kutentha kwa dzuŵa ndi nyengo yozizila. Ndipo anafunikilanso kuteteza nkhosa zao ku zilombo zolusa ndi akawalala. Abusawo anali kufufuza nkhosa zao nthawi zonse kuti aone ngati pali yodwala kapena yozipweteka kuti aithandize. Iwo anali kupeleka cisamalilo kwa ana a nkhosa osakhwima ndi opanda mphamvu monga mmene nkhosa zazikulu zimakhalila.—Gen. 33:13.

2 Makolo acikristu naonso ali monga abusa, ndipo ayenela kukhala ndi makhalidwe amene m’busa weniweni amakhala nao. Iwo ali ndi udindo wolela ana ao “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Kodi udindo umenewu ndi wopepuka? Iyai. Cifukwa cakuti nthawi zambili ana amavutika ndi mabodza a Satana ndi zisonkhezelo za kupanda ungwilo kwao. (2 Tim. 2:22; 1 Yoh. 2:16) Ngati muli ndi ana, kodi mungawathandize motani? Tiyeni tikambilane zinthu zitatu zimene mungacite poŵeta ana anu. Muyenela kuwadziŵa bwino, kuwaphunzitsa, ndi kuwatsogolela.

ADZIŴENI BWINO ANA ANU

3. Kodi makolo angacitenji kuti awadziŵe bwino ana ao?

3 M’busa wabwino amafufuza mosamalitsa nkhosa iliyonse kuti atsimikizile ngati ili bwino. Mofananamo, makolo angacite cimodzimodzi ndi ana anu. Baibulo limati: ‘Dziŵani bwino maonekedwe a ziŵeto zanu.’ (Miy. 27:23) Kuti mucite zimenezi, muyenela kudziŵa zocita za ana anu, zimene amaganiza, ndi zimene amafuna. Nanga mungacite bwanji zimenezi? Njila yabwino koposa ndiyo kukambilana kaŵilikaŵili ndi ana anu.

4, 5. (a) Ndi njila zothandiza ziti zimene zingathandize ana kumasuka ndi makolo ao? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Mumacita ciani kuti ana anu azimasuka kulankhula nanu?

4 Makolo ena amaona kuti ana akafika zaka za m’ma 13 mpaka 19, zimavuta kukambilana nao. Iwo akafika zaka zimenezi safuna kukambilana maganizo ao ndi zimene amafuna. Ngati zimenezi ndi zimene ana anu amacita kodi mungacitenji? M’malo mokambilana ndi ana anu kwa nthawi yaitali pamene io safuna, ndi bwino kukambilana nao monga mukuceza. (Deut. 6:6, 7) Ndipo muziyesetsa kucitila nao zinthu pamodzi. Mungawatenge kuti muyendeyendeko nao, museŵeleko nao, kapena mugwileko nao nchito za panyumba. Mipata ngati iyi ingathandize acinyamata kumasuka ndi kukamba za kukhosi kwao.

5 Nanga bwanji ngati mwana wanu safunabe kukambilana? Mungayeseko njila ina. Mwacitsanzo, m’malo mofunsa mwana wanu mmene tsiku lake layendela, zingakhale bwino kusimba mmene tsiku lanu linalili. Zimenezo zingam’thandize kuti amasuke kukamba mmene tsiku lake layendela. Ndipo ngati mufuna kudziŵa zimene mwana wanu akuganiza pa nkhani ina yake, mungam’funse maganizo ake pa nkhaniyo, osati ponena za iye. M’funseni mmene anzake amaonela nkhaniyo. Ndiyeno m’pempheni kuti achule thandizo limene angapeleke kwa anzake.

6. Ana anu angadziŵe bwanji kuti muli ndi nthawi yolankhula nao ndi kuti ndinu ofikilika?

6 Kuti ana anu azimasuka nanu, io ayenela kudziŵa kuti mudzawapatsa mpata wokamba nao ndi kuti ndinu ofikilika. Ngati nthawi zonse makolo sakhala ndi nthawi yolankhula ndi ana ao, ana m’banja angalephele kuwauza mavuto ao. Nanga mungakhale motani munthu wofikilika? Kuuza mwana wanu mau akuti, “Ungakambe nane nthawi iliyonse” si kokwanila. Ana anu amafunika kudziŵa kuti simudzakwiya ndi zimene angakuuzeni. Makolo ambili amacita bwino pa nkhani imeneyi. Kayla, mtsikana wazaka 19 anati: “Ndimakambilana ndi atate nkhani iliyonse. Iwo samandidula mau, samandiweluza, koma amangoti phee kumvetsela. Pambuyo pake, amandipatsa malangizo abwino koposa.”

7. (a) N’ciani cingathandize makolo kuona zinthu moyenela pokambilana ndi mwana nkhani yopalana cibwenzi? (b) Kodi makolo mosadziŵa angakhumudwitse motani ana ao?

7 Pamene mukambilana nao nkhani zovuta monga za cibwenzi, samalani kuti simugogomeza kwambili pa kupeleka macenjezo. Koma muziphunzitsa ana anu njila yoyenela yothetsela vutolo. Mwacitsanzo: Tinene kuti mwapita pamalo odyela, ndipo akucenjezani kuti zakudya zonse pano ndi zosasa. Mosakaikila mudzacoka pamalopo ndi kukafunafuna malo ena. Izi n’zimenenso ana anu angacite ngati mumangowapatsa macenjezo akabwela kwa inu kupempha nzelu. (Ŵelengani Akolose 3:21.) M’malo mwake, makolo adzafunikila kuona zinthu moyenela. Mlongo wacicepele dzina lake Emily anati: “Pamene ndikambilana ndi makolo anga za cibwenzi, io sakamba monga kuti ndi nkhani yoipa. Amagogomezela za kufunika kodziŵana bwino ndi munthu amene ndidzakwatilana naye. Zimenezi zandithandiza kukhala womasuka kukambilana nao nkhani imeneyi. Ndipo, ndimawauza za cibwenzi ciliconse m’malo mowabisa.”

8, 9. (a) Kodi pali mapindu otani ngati makolo amvetsela ana ao popanda kuwadula mau? (b) Kodi mwapindula motani cifukwa comvetsela ana anu?

8 Malinga ndi zimene Kayla anakamba, mungaonetse kuti ndinu ofikilika mwa kumvetsela modekha kwa mwana wanu. (Ŵelengani Yakobo 1:19.) Mai wina dzina lake Katia amene alela yekha mwana anati, “Kale ndinali wosadekha ndi mwana wanga wamkazi. Sindinali kum’patsa mpata wotsiliza kukamba zimene afuna. Mwina ndinali kukhala wolema kwambili kuti ndimvetsele kapena sindinali kufuna cabe kumvetsela. Popeza tsopano ndasintha khalidwe langa, mwana wanga nayenso wasintha. Masiku ano, iye ndi womasuka kwambili.”

9 Zimenezi zinacitikilanso tate wina dzina lake Ronald. Iye anati, “Pamene mwana wanga wamkazi anandiuza kuti anali ndi cibwenzi ku sukulu, poyamba ndinakalipa kwambili. Koma ndinaganizila mmene Yehova alili wodekha ndi wololela kwa atumiki ake. Conco, ndisanapeleke uphungu ndinaganiza zom’patsa mpata kuti akambe za kukhosi kwake. Kucita zimenezo kunathandiza kwambili. Kwa nthawi yoyamba ndinadziŵa zimene iye anali kuganiza. Atatsiliza kukamba, zinali zopepuka kukamba naye mwacikondi. Sindinayembekezele kuti adzalandila uphungu wanga. Ndipo analonjeza kuti adzasintha khalidwe lake.” Kukambilana ndi ana anu kaŵilikaŵili, kudzakuthandizani kudziŵa maganizo ao ndi zimene afuna. Mukacita zimenezi mudzawathandiza kupanga zosankha.a

PHUNZITSANI ANA ANU

10, 11. Mungacitenji kuti muthandize ana kuti asataike?

10 M’busa wabwino amadziŵa kuti nkhosa ina ingacoke pagulu ndi kusoŵa. Nthawi zina nkhosa imatengeka ndi msipu ndi kuyamba kucoka pagulu pang’onopang’ono mpaka kutaika. Mofananamo, mwana pang’onopang’ono angataike mwa kuuzimu ndi kuloŵela njila yoipa. Iye angasoceletsedwe ndi mabwenzi oipa kapena zosangulutsa zosayenela. (Miy. 13:20) Mungacitenji kuti muteteze mwana wanu kuti zimenezi zisam’citikile?

11 Pophunzitsa ana anu muyenela kucitapo kanthu mwamsanga mukaona mbali zimene sacita bwino. Limbikilani pa kuthandiza ana anu kukulitsa makhalidwe ao acikristu. (2 Pet. 1:5-8) Njila imodzi imene mungacitile zimenezo ndiyo kulambila kwa pabanja kokhazikika. Pofotokoza makonzedwe amenewa, Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2008 unati: “Mitu ya mabanja iyenela kukwanilitsa udindo umene Yehova anawapatsa poonetsetsa kuti akuphunzila Baibulo ndi banja lao nthawi zonse.” Kodi mumatengelapo mwai pa makonzedwe acikondi amenewa kuti muŵete ana anu? Khalani ndi cidalilo cakuti ana anu adzayamikila kwambili zimene mumacita powaphunzitsa.—Mat. 5:3; Afil. 1:10.

12. (a) Kodi acicepele apindula motani ndi Kulambila kwa Pabanja kokhazikika? (Onani bokosi lakuti, “Amayamikila.”) (b) Nanga inu panokha mwapindula motani ndi Kulambila kwa Pabanja?

12 Onani zimene wacicepele wina dzina lake Carissa anakamba ponena za mmene Kulambila kwa Pabanja kwapindulitsila banja lao. Iye anati, “Ndimakondwela kuti tonse timakhala pamodzi ndi kukambilana. Kucita zimenezi kumatigwilizanitsa ndipo timakhala ndi zambili zodzasimba mtsogolo. Atate amacititsa Kulambila kwa Pabanja mlungu uliwonse. N’zolimbikitsa kuona kuti io amakuona kukhala kofunika kwambili. Zimenezi zandithandiza kuti ndiziona Kulambila kwa Pabanja kukhala kofunika. Ndipo zandithandizanso kuti ndiziwalemekeza monga atate ndi mutu wa banja wa kuuzimu.” Mlongo wacicepele dzina lake Brittney anafotokoza kuti: “Kulambila kwa pabanja kwandithandiza kuyandikila kwambili makolo anga. Ndimaona kuti io amafuna kudziŵa mavuto anga ndi kuti amandiganizila. Zimenezi zathandiza banja lathu kukhala lolimba ndi logwilizana.” Ndithudi, kuphunzitsa ana anu mwa kuuzimu pa Kulambila kwa Pabanja ndi njila imodzi yofunika imene mungakhalile m’busa wabwino.b

TSOGOLELANI ANA ANU

13. N’ciani cingathandize mwana wanu kuyamba kutumikila Yehova?

13 M’busa wabwino amagwilitsila nchito ndodo potsogolela ndi poteteza nkhosa zake. Colinga cake cacikulu ndi kutsogolela nkhosa ku “msipu wabwino.” (Ezek. 34:13, 14) Monga kholo, kodi cimeneci ndiye colinga canu ca kuuzimu? Mumafuna kutsogolela ana anu kuti atumikile Yehova. Ndipo mumafunanso ana anu kuti azidzimva monga wamasalimo amene anati: “Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga, ndipo cilamulo canu cili mumtima mwanga.” (Sal. 40:8) Ana anu akayamba kudzimva motelo, adzadzipeleka kwa Yehova ndi kubatizika. Kuti apange cosankha cimeneci, io ayenela kumvetsetsa zinthu ndi kukhala ofunitsitsa kutumikila Yehova.

14, 15. (a) Kodi makolo acikristu ayenela kukhala ndi colinga cotani? (b) N’cifukwa ciani acicepele angayambe kukaikila kulambila koona?

14 Bwanji ngati ana anu sapita patsogolo? Nanga bwanji ngati amakaikila ubale wao ndi Yehova? Kodi mungacitenji? Yesetsani kukambilana ndi ana anu ndi kuwaphunzitsa kukonda Yehova kucokela pansi pamtima. Aphunzitseni kuyamikila zonse zimene Mulungu awacitila. (Chiv. 4:11) Ndiyeno, akadzakonzeka adzapanga cosankha cotumikila Mulungu.

15 Koma bwanji ngati pali pano io ayamba kukaikila coonadi? Athandizeni kumvetsetsa kuti kutumikila Yehova ndi njila yabwino koposa, ndipo kumabweletsa mapindu osatha. Muyenelanso kudziŵa zimene zimawacititsa kukaikila. Mwacitsanzo, kodi mwana wanu amatsutsa ziphunzitso za m’Baibulo? Kapena amangocita mantha kulalikila anzake? Kodi amakaikila ngati malamulo a Mulungu ndi othandiza? Kapena amangomangika ndi kuti anzake safuna kuceza naye?

16, 17. Kodi makolo angathandize bwanji ana ao kuti akhale paubale ndi Mulungu?

16 Mungacitenji kuti muthandize ana anu kuti aleke kukaikila coonadi? Zimene makolo ambili aona kuti n’zothandiza ndi kufunsa ana ao mafunso monga akuti: “Umadzimva bwanji kukhala Mkristu? Ndi mapindu otani amene wapezeka cifukwa cokhala Mkristu? Nanga kukhala Mkristu kungabweletse mavuto otani? Kodi umaona kuti madalitso amene umapeza tsopano, ndi amene udzapeza mtsogolo ndi ambili kuposa mavuto amene ungakumane nao?” Tsimikizani kuti mukufunsa mafunso amenewa m’mau anuanu, mokoma mtima, ndi mokopa. Koma musacite zimenezo monga wapolisi. Pokambilana zingakhale bwino kupenda lemba la Maliko 10:29, 30. Acicepele ena angafune kulemba zimene mwakambilana. Iwo angacite zimenezo mwa kulemba mizela iŵili, umodzi angalembe mavuto amene amapeza, ndipo wina angalembe madalitso amene amapeza. Kuona zimene zili papepala kungawathandize kudziŵa mavuto ao ndi kuwathandiza kudziŵa zimene angacite ndi mavutowo. Ngati timaphunzila ndi anthu ena buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa ndi buku la Cikondi ca Mulungu, nanga kuli bwanji kuphunzila ndi ana athu? Kodi ndi zimene mumacita?

17 Ana anu akakula zidzawathandiza kusankha amene adzatumikila. Iwo sadzasankha kutumikila Mulungu cabe cifukwa cakuti inu mumam’tumikila. Ana anu ayenela kusankha okha kukhala paubale ndi Yehova. (Miy. 3:1, 2) Nanga bwanji ngati mwana wanu zim’vuta kukhala paubale ndi Mulungu? Mulimbikitseni kuti alingalile pa zimene amakhulupilila mwa kudzifunsa kuti: “Ndimadziŵa bwanji kuti Mulungu aliko? Ndingatsimikize bwanji kuti Yehova Mulungu amandiŵelengela? N’cifukwa ciani ndimakhulupilila kuti miyezo ya Yehova ingandipindulitse?” Makolo khalani abusa abwino ndipo tsogolelani ana anu modekha. Athandizeni kudziŵa kuti kutumikila Yehova ndi kopindulitsa kwambili.c—Aroma 12:2.

18. Kodi makolo angatsatile motani citsanzo ca Yehova, M’busa Wamkulu?

18 Akristu onse oona amafuna kutsatila citsanzo ca M’busa Wamkulu. (Aef. 5:1; 1 Pet. 2:25) Makamaka makolo ayenela kudziŵa maonekedwe a nkhosa zao, amene ndi ana ao okondedwa. Ndipo ayenela kuyesetsa kuwatsogolela kuti akalandile madalitso a Yehova a mtsogolo. Conco, makolo citani zimene mungathe kuti muŵete ana anu ndi kuwathandiza kukonda Mulungu.

a Kuti mudziŵe zambili, onani Nsanja ya Olonda ya August 1, 2008, masamba 10-12.

b Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani yakuti, “Kulambila kwa Pabanja N’kofunika Kwambili Kuti Tidzapulumuke” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2009, masamba 29-31.

c Nkhani imeneyi ipezekanso mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2012, masamba 18-21.

AMAYAMIKILA

Onani ndemanga zocokela pansi pamtima za atsikana aŵili amene amakondwela ndi kulambila kwa pabanja.

“Kulambila kwa Pabanja kumathandiza munthu kuyandikilana ndi banja lake ndi Yehova. Kumam’cititsa kuzidziŵa bwino ndi kudziŵa mmene apitila patsogolo. Ndipo kumam’thandiza kuzindikila zimene afunika kuongolela.”

“Kulambila kwa pabanja kumatipatsa mpata wolankhula maganizo athu momasuka. Ndi nthawi pamene timaika pambali nkhawa za tsiku ndi tsiku ndi kuika maganizo athu pa za kuuzimu. Kale sitinali kucita kulambila kwa pabanja. Koma tsopano timacita ndipo ndi dalitso.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani