LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 10/15 masa. 23-27
  • Muziyamikila Mwai Wanu Wogwila Nchito ndi Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muziyamikila Mwai Wanu Wogwila Nchito ndi Yehova
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • NANGA BWANJI ZA NCHITO YA ANTHU?
  • MUZIONA NCHITO YANU MOYENELA
  • PITILIZANI KUKONDWELA NDI MWAI WANU WOGWILA NCHITO NDI YEHOVA
  • Kugwila Nchito ndi Mulungu Kumabweletsa Cimwemwe
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Njila Zowonjezela Utumiki Wanu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Muzikondwela Nayo Nchito Yanu
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Muzikumbukila Amene Ali mu Utumiki Wanthawi Zonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 10/15 masa. 23-27

Muziyamikila Mwai Wanu Wogwila Nchito ndi Yehova

“Ndife anchito anzake a Mulungu.”—1 AKOR. 3:9.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Ndi mwai wotani umene atumiki a Yehova akhala nao nthawi zonse?

  • N’ciani makamaka cimene tiyenela kuyamikila masiku ano?

  • Tili ndi ciyembekezo cokondweletsa cotani ca mtsogolo?

1. Kodi Yehova amaiona bwanji nchito? Ndipo amacita ciani?

YEHOVA amakondwela kugwila nchito. (Sal. 135:6; Yoh. 5:17) Kuti athandize zolengedwa zake zanzelu kukhutila ndi kukhala ndi cimwemwe cimene iye ali naco, Yehova amagaŵila zolengedwa zake nchito yabwino ndi yokondweletsa. Mwacitsanzo, polenga zinthu iye anagwila nchito ndi Mwana wake woyamba kubadwa. (Ŵelengani Akolose 1:15, 16.) Baibulo limatiuza kuti Yesu asanakhale munthu, anali pambali pa Mulungu kumwamba “monga mmisili waluso.”—Miy. 8:30.

2. N’ciani cionetsa kuti zolengedwa zauzimu nthawi zonse zimagwila nchito yokondweletsa ndi yokhutilitsa?

2 Kuyambila m’buku la Genesis mpaka Chivumbulutso, Baibulo lili ndi zitsanzo zoonetsa kuti Yehova nthawi zonse amagaŵila nchito ana ake auzimu. Adamu ndi Hava atacimwa ndi kucotsedwa m’Paladaiso, Mulungu “anaika akerubi kum’maŵa kwa munda wa Edeniwo. Anaikanso lupanga loyaka moto, limene linali kuzungulila mosalekeza, kuchinga njila yopita ku mtengo wa moyo.” (Gen. 3:24) Ndipo buku la Chivumbulutso 22:6, limaonetsa kuti Yehova “anatumiza mngelo wake kudzaonetsa akapolo ake zinthu zimene ziyenela kucitika posacedwa.”

NANGA BWANJI ZA NCHITO YA ANTHU?

3. Yesu ali padziko lapansi, kodi anatsatila motani citsanzo ca Atate wake?

3 Yesu mokondwela anagwila nchito imene Yehova anam’patsa pamene anali padziko lapansi monga munthu wangwilo. Potsatila citsanzo ca Atate wake, Yesu anagaŵila nchito yofunika kwa ophunzila ake. Ndipo kuti awathandizile kuona kufunika kwa nchito imeneyi, iye anati: “Ndithudi ndikukuuzani, wokhulupilila ine, nayenso adzacita nchito zimene ine ndimacita, ndipo adzacita nchito zazikulu kuposa zimenezi, cifukwa ine ndikupita kwa Atate.” (Yoh. 14:12) Pogogomezela kufulumila kwa nchito imeneyi, Yesu anati: “Tiyenela kugwila nchito za iye amene anandituma ine kudakali masana. Usiku ukubwela pamene munthu sangathe kugwila nchito.”—Yoh. 9:4.

4-6. (a) N’cifukwa ciani timayamikila kuti Nowa ndi Mose anagwila nchito yao imene Yehova anawapatsa? (b) Kodi nchito zimene Mulungu amapatsa atumiki ake zili ndi zotsatilapo zotani?

4 Yesu asanabwele padziko lapansi, Yehova anagaŵila anthu nchito yokhutilitsa. Ngakhale kuti Adamu ndi Hava analephela kugwila nchito imene anapatsidwa, anthu ambili anagwila nchito imene Mulungu anawapatsa. (Gen. 1:28) Nowa anapatsidwa malangizo osapita m’mbali opangila cingalawa kuti anthu akapulumukilemo pa Cigumula. Iye anacita ndendende zimene Yehova anamuuza. Tili ndi moyo cifukwa cakuti Nowa anatsatila malangizowo mosamalitsa.—Gen. 6:14-16, 22; 2 Pet. 2:5.

5 Mose anapatsidwa malangizo osapita m’mbali omangila cihema, ndi kusankha ansembe. Ndipo anatsatila malangizo amenewo mosamalitsa. (Eks. 39:32; 40:12-16) Ngakhale masiku ano, timapindula cifukwa cakuti iye anagwila nchito imeneyo mokhulupilika. Nanga timapindula motani? Mtumwi Paulo anafotokoza kuti mbali za Cilamulo zinali m’thunzi wa ‘zinthu zabwino zimene zinali kubwela.’—Aheb. 9:1-5, 9; 10:1.

6 Nchito imene Mulungu amapatsa atumiki ake imasiyanasiyana malinga ndi mmene cifunilo cake cikukwanilitsidwila. Ngakhale n’conco, nchito imene io amapatsidwa nthawi zonse imalemekeza Yehova, ndi kupindulitsa anthu okhulupilika. Nchito imeneyi imaphatikizapo nchito imene Yesu anagwila ali kumwamba ndi pamene anali padziko lapansi. (Yoh. 4:34; 17:4) Mofananamo, nchito imene tapatsidwa masiku ano imalemekeza Yehova. (Mat. 5:16; ŵelengani 1 Akorinto 15:58.) N’cifukwa ciani zili conco?

MUZIONA NCHITO YANU MOYENELA

7, 8. (a) Kodi Akristu masiku ano ali ndi mwai wogwila nchito yotani? (b) Nanga malangizo a Yehova tiyenela kuwaona bwanji?

7 Ndi mwai wapadela kuti Yehova wapempha anthu opanda ungwilo kukhala anchito anzake. (1 Akor. 3:9) Akristu ena ali ndi mwai wogwila nchito yomanga Nyumba za Misonkhano, Nyumba za Ufumu, ndi maofesi a nthambi. Nchito imeneyi ifanana ndi imene Nowa ndi Mose anagwila. Kaya tigwila nchito yokonza Nyumba za Ufumu kapena yomanga likulu lathu ku Warwick, New York, tiyenela kuyamikila mwai wotumikila mwanjila imeneyi. (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino cojambulidwa pa manja.) Umenewu ndi utumiki wopatulika. Komabe, nchito yaikulu imene Akristu akupemphedwa kucita ndi nchito yolalikila. Nchito imeneyi imalemekeza Yehova ndipo imapindulitsa anthu omvela. (Mac. 13:47-49) Gulu la Mulungu limapeleka malangizo oyenela ogwilila nchito imeneyi. Nthawi zina zimenezi zingatanthauze kupatsidwa nchito zatsopano.

8 Nthawi zonse atumiki a Yehova okhulupilika amatsatila mofunitsitsa malangizo a gulu la Mulungu. (Ŵelengani Aheberi 13:7, 17.) Nthawi zina sitingamvetsetse cifukwa cake tapatsidwa nchito zatsopano. Komabe, timalandila nchitozo cifukwa timadziŵa kuti kusintha kumacokela kwa Yehova ndipo kumatipindulitsa.

9. Ndi citsanzo cotani cimene akulu amapeleka mumpingo ponena za kugwila nchito?

9 Akulu ndi ofunitsitsa kugwila nchito ya Yehova, ndipo zimenezi zimaonekela ndi mmene amatsogolela mpingo. (2 Akor. 1:24; 1 Ates. 5:12, 13) Iwo amafunitsitsa kugwila nchito mwakhama ndi kutsatila malangizo. Ndipo sazengeleza kuphunzila njila zatsopano zolalikilila. Ena akhala ndi zotsatilapo zabwino mwa kugwilitsila nchito ulaliki wa pafoni, ulaliki wa ku dooko, kapena ulaliki wa poyela, ngakhale kuti sanadziŵe mmene njila zatsopano zimenezi zidzathandizila. Mwacitsanzo, apainiya anai ku Germany, anaganiza zolalikila m’gawo la malonda limene silinalalikidwe kwa zaka. Michael mmodzi wa io anati: “Papita zaka zambili pamene tinacitapo ulaliki umenewu, conco tinali ndi mantha kwambili. Mwacionekele, Yehova anaona zimenezi, ndipo anatithandiza cakuti tsikulo ndi losaiŵalika kwa ife. Tiyamikila kuti tinatsatila malangizo a mu Utumiki Wathu wa Ufumu ndi kudalila Yehova.” Kodi ndinu okonzeka kugwilitsila nchito njila zatsopano zolalikilila m’gawo lanu?

10. Gulu la Yehova lapanga masinthidwe otani m’zaka zaposacedwapa?

10 Nthawi zina gulu limapanga masinthidwe. Posacedwapa maofesi a nthambi angapo anawaphatikiza pamodzi. Ngakhale kuti kusintha kumeneku kungacititse abale ndi alongo amene akutumikila panthambi zimenezo kupanga masinthidwe paumoyo wao, m’kupita kwa nthawi io amaona ubwino wake. (Mlal. 7:8) Anchito odzipeleka amenewa ndi okondwa kutengako mbali pa nchito ya anthu a Yehova masiku ano.

11-13. Ena apanga masinthidwe otani cifukwa ca kusintha kumene gulu lapanga?

11 Tingaphunzile zambili kwa aja amene anali kutumikila panthambi zimene anaphatikiza pamodzi. Ena atumikila panthambi za kumaiko akwao kwa zaka zambili. Banja lina limene linali kutumikila panthambi yaing’ono ku Central America, linapemphedwa kukakatumikila ku nthambi yaikulu kwambili ku Mexico. Rogelio anati: “Zinali zovuta kwambili kusiya mabanja ndi mabwenzi athu.” M’bale wina dzina lake Juan, amene anapita kukatumikila ku Mexico, anati: “Zimakhala monga kuti wabadwanso, ndipo umafunikila kupanga mabwenzi atsopano. Umafunikilanso kuphunzila zikhalidwe ndi zinthu zatsopano.”

12 Mofananamo, atumiki a pa Beteli a kumaiko a ku Europe, amene anapemphedwa kukatumikila ku ofesi ya nthambi ku Germany, naonso anamva cimodzimodzi. Aliyense amene amakonda kukhala kudela la mapili angamvetsetse kuti zinali zovuta kwa abale kucoka ku nthambi ya ku Switzerland, imene inali m’dela la mapili okongola. Ndipo abale amene anacoka ku Austria, poyamba anali kuyewa umoyo wa kwao.

13 Kwa abale amene anasamukila ku maiko ena, zinawavuta kuzoloŵela nyumba zatsopano, kuseŵenza ndi abale ndi alongo acilendo, ndipo mwina kuphunzila nchito zatsopano. Anafunikilanso kuzoloŵela mipingo yatsopano, kulalikila m’magawo atsopano, mwina ngakhale kulalikila m’cinenelo cina. Kusintha kumeneku kungakhale kovuta. Komabe, atumiki ambili a pa Beteli anapanga masinthidwe amenewa. N’cifukwa ciani anacita zimenezo?

14, 15. (a) Ena aonetsa motani kuti amayamikila mwai wao wogwila nchito ndi Yehova mosasamala kanthu ndi nchito imene apatsidwa? (b) Nanga io amapeleka citsanzo cotani kwa ife?

14 Mlongo wina dzina lake Grethel anati: “Ndinavomela kukatumikila kudziko lina cifukwa ndi njila imodzi yoonetsa kuti ndimakonda Yehova, osati kukonda kwambili dziko, nyumba, kapena udindo winawake.” Dayska anati: “Kukumbukila kuti Yehova ndiye anandipempha kuti ndikatumikile kwina kunandithandiza kuvomela mosavuta.” André ndi Gabriela anavomeleza kuti: “Zimenezi zinatipatsa mwai wina wotumikila Yehova, ndi kuika pambali zofuna zathu. ‘Iwo anaona kuti ngati gulu la Yehova lapanga masinthidwe, ndi bwino kuvomela mosavuta m’malo motsutsa.’”

15 Nthambi zikaphatikizidwa, atumiki ena a panthambi angawatumize kukatumikila monga apainiya. Izi n’zimene zinacitika kwa atumiki a pa Beteli ambili, pamene anaphatikiza pamodzi nthambi za ku Denmark, Norway, ndi Sweden ndi kupanga ofesi ya nthambi ya Scandinavia kumpoto kwa Europe. Florian ndi Anja ndi amodzi mwa amene anatumizidwa kukacita upainiya. Iwo anati: “Timaona utumiki wathu watsopano kukhala wokondweletsa koma umafuna kulimbikila. Timakondwela kugwilitsidwa nchito ndi Yehova mosasamala kanthu kumene tikutumikila. Kukamba zoona timaona kuti ndife odalitsika kwambili.” Ngakhale kuti nthawi zina zimenezi sizingacitike kwa ife, tiyenela kutsatila citsanzo ca abale ndi alongo odzipeleka amenewa ndi kuika zinthu za Ufumu patsogolo. (Yes. 6:8) Nthawi zonse, Yehova amadalitsa anthu amene amayamikila mwai wogwila nchito ndi iye, mosasamala kanthu kumene akutumikila.

PITILIZANI KUKONDWELA NDI MWAI WANU WOGWILA NCHITO NDI YEHOVA

16. (a) Kodi lemba la Agalatiya 6:4 limatiuza kucita ciani? (b) Ndi mwai waukulu uti umene tonse tili nao?

16 Nthawi zambili anthu opanda ungwilo amakonda kuyelekezela zinthu. Koma mau a Mulungu amatiuza kuti tiyenela kuika maganizo athu pa zimene timakwanitsa kucita. (Ŵelengani Agalatiya 6:4.) N’zosatheka kuti tonse tikhale akulu, apainiya, amishonale, kapena atumiki a pa Beteli. N’zoona kuti mautumiki amenewa ndi okondweletsa. Koma tisaiŵale kuti mwai waukulu umene ife tonse tili nao ndiwo kukhala ofalitsa a uthenga wabwino monga anchito anzake a Yehova. Umenewu ndi mwai umene tiyenela kuyamikila.

17. Malinga ngati dziko la Satana lilipo, sitingakwanitse kucitanji? Koma n’cifukwa ciani zimenezi siziyenela kutibweza m’mbuyo?

17 Malinga ngati dziko la Satana lilipo, sitingatumikile Yehova mmene tingafunile. Pali zinthu zina zimene zingatilepheletse kutumikila bwino, zinthu monga maudindo a m’banja, kudwala, kapena mavuto ena. Komabe, zinthu zimenezi siziyenela kutibweza m’mbuyo. Tisadelele zimene tingakwanitse kucita pogwila nchito ndi Mulungu mwa kucitila umboni za dzina lake ndi kulengeza za Ufumu wake. Cofunika kwambili n’cakuti timagwila naye nchito mmene tingathele. Ndipo timapemphela kuti adalitse abale athu amene amacita zambili kuposa ife. Tizikumbukila kuti aliyense amene amatamanda dzina la Yehova ndi wamtengo wapatali kwa iye.

18. N’ciani cimene tiyenela kuika pambali? Nanga n’cifukwa ciani?

18 Yehova amatigwilitsila nchito monga anchito anzake, mosasamala kanthu ndi zofooka zathu ndi kupanda ungwilo kwathu. Timayamikila kwambili mwai wathu wogwila nchito ndi Mulungu m’masiku ano otsiliza. Conco, tiyenela kukhala ofunitsitsa kuika pambali zokonda zathu podziŵa kuti m’dziko latsopano, Yehova adzatidalitsa ndi ‘moyo weniweni,’ moyo wosatha, m’mikhalidwe yacimwemwe ndi yamtendele.—1 Tim. 6:18, 19.

19. Kodi Yehova watisungila ciani mtsogolo?

19 Pamene tili pafupi kuloŵa m’dziko latsopano, tiyenela kuganizila zimene Mose anauza Aisiraeli, io atatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wako adzakucititsa kukhala ndi zinthu zosefukila pa nchito iliyonse ya manja ako.” (Deut. 30:9) Pambuyo pa Armagedo, Mulungu adzapeleka dziko latsopano kwa anthu amene anali kugwila nchito ndi iye monga mmene anawalonjezela. Panthawiyo, nchito yathu yatsopano idzakhala yokonza dziko lapansi kuti likhale paladaiso.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani