LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 11/15 masa. 8-12
  • Cifukwa Cake Tifunika Kukhala Oyela

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cifukwa Cake Tifunika Kukhala Oyela
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIYELO N’COFUNIKA
  • ONETSANI KUTI NDINU OYELA MWA KUKHALA OMVELA
  • KHALANI OYELA MWA KUMVELA LAMULO LA MULUNGU LOKHUDZA MAGAZI
  • CIFUKWA CAKE YEHOVA AMAFUNA KUTI TIKHALE OYELA
  • Muzilemekeza Mphatso Ya Moyo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Mmene Mulungu Amaonela Moyo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 11/15 masa. 8-12

Cifukwa Cake Tifunika Kukhala Oyela

“Muzikhala oyela.”—LEV. 11:45.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’cifukwa ciani kuyeletsedwa kwa Aroni ndi ana ake kuli ndi tanthauzo lalikulu kwa anthu a Yehova?

  • Kodi kumvela kugwilizana bwanji ndi kukhala oyela?

  • Tiyenela kuliona bwanji lamulo la Yehova lonena za magazi?

1. Kodi buku la Levitiko lingatithandize bwanji?

M’BUKU la Levitiko, ciyelo cimachulidwa nthawi zambili kuposa m’buku lina lililonse la m’Baibulo. Popeza limeneli ndi lamulo kwa alambili onse oona a Yehova, kumvetsetsa buku la Levitiko kudzatithandiza kukhala oyela.

2. Ndi mfundo zotani zimene zimapezeka m’buku la Levitiko?

2 Buku la Levitiko, linalembedwa ndi mneneli Mose, ndipo ndi mbali ya “Malemba onse” amene amapindulitsa pophunzitsa. (2 Tim. 3:16) M’caputala ciliconse ca buku limeneli, dzina la Yehova limachulidwa pafupifupi nthawi 10. Conco, kumvetsetsa buku la Levitiko kudzatithandiza kupewa kucita ciliconse cimene cingabweletse citonzo pa dzina la Mulungu. (Lev. 22:32) Mau akuti “Ine ndine Yehova,” amene amapezeka nthawi zambili m’buku limeneli, amatikumbutsa kuti tifunika kumvela Mulungu. M’nkhani ino ndi yotsatila, tidzakambilana mfundo zamtengo wapatali za m’buku la Levitiko, zimene zidzatithandiza kukhala oyela polambila Mulungu.

CIYELO N’COFUNIKA

3, 4. Kodi kusamba kumene Aroni ndi ana ake anali kucita kunali kuimila ciani? (Onani cithunzi cili pamwamba.)

3 Ŵelengani Levitiko 8:5, 6. Yehova anasankha Aroni kutumikila monga mkulu wa ansembe wa Isiraeli, ndipo ana ake anali kutumikila monga ansembe. Aroni amaimila Yesu Kristu, ndipo ana ake amaimila otsatila odzozedwa a Yesu. Conco, kodi kusamba kwa Aroni kumaimila kuyeletsedwa kwa Yesu? Iyai. Popeza Yesu analibe chimo, ndipo anali “wopanda cilema,” iye sanali kufunikila kuyeletsedwa. (Aheb. 7:26; 9:14) Komabe, kusamba kumene Aroni anali kucita kumaimila khalidwe loyela ndi lolungama la Yesu. Nanga kusamba kumene ana a Aroni anali kucita kumaimila ciani?

4 Kusamba kumene ana a Aroni anali kucita kumaimila kuyeletsedwa kwa aja amene anasankhidwa kukakhala ansembe a kumwamba. Kodi ubatizo wao umagwilizana ndi kuyeletsedwa kwa ana a Aroni? Iyai. Ubatizo sucotsa macimo, koma umaonetsa kuti munthu wadzipeleka kwa Yehova Mulungu ndi mtima wonse. Odzozedwa amasambitsidwa ndi “mau a Mulungu.” Ndipo amafunika kutsatila ziphunzitso za Kristu ndi mtima wonse paumoyo wao. (Aef. 5:25-27) Motelo, io amakhala oyela. Nanga bwanji za a “nkhosa zina”?—Yoh. 10:16.

5. N’cifukwa ciani tinganene kuti a nkhosa zina amayeletsedwa ndi Mau a Mulungu?

5 Ana a Aroni sanali kuimila nkhosa zina za Yesu kapena kuti a “khamu lalikulu.” (Chiv. 7:9) Komabe, a nkhosa zina naonso amayeletsedwa ndi Mau a Mulungu. Aja amene ali ndi ciyembekezo ca padziko lapansi amaphunzila zimene Baibulo limanena ponena za kufunika kwa magazi okhetsedwa a Yesu. Ndipo akakhulupilila zimenezo, amacita “utumiki wopatulika usana ndi usiku.” (Chiv. 7:13-15) Kuyeletsedwa kwa odzozedwa ndi a nkhosa zina kumacitika nthawi zonse. Ndipo zotsatilapo n’zakuti amapitilizabe kukhala ndi “khalidwe labwino.” (1 Pet. 2:12) Yehova amakondwela akaona kuti anthu ake onse ndi oyela. Amakondwelanso akaona mgwilizano umene ulipo pakati pa odzozedwa ndi a nkhosa zina, amene amamvetsela mokhulupilika ndi kutsatila M’busa wao, Yesu.

6. N’cifukwa ciani tiyenela kudzipenda nthawi zonse?

6 Lamulo lakuti akulu ansembe aciisiraeli azikhala oyela mwakuthupi, lili ndi tanthauzo lalikulu kwa anthu a Yehova masiku ano. Anthu amene timaphunzila nao Baibulo amaona kuti malo athu olambilila ndi aukhondo, ndipo timavala bwino. Conco, ciyelo ca akulu ansembe cimatithandiza kudziŵa kuti, aliyense amene akufuna kulambila Yehova ayenela kukhala “woyela mumtima mwake.” (Ŵelengani Salimo 24:3, 4; Yes. 2:2, 3.) Pocita utumiki wopatulika kwa Mulungu, tiyenela kukhala oyela m’maganizo, m’mitima, ndi matupi athu. Kucita zimenezi kumafuna kudzipenda nthawi zonse. Ena angafunike kupanga masinthidwe aakulu paumoyo wao kuti akhale oyela. (2 Akor. 13:5) Mwacitsanzo, wofalitsa wobatizika amene mwadala wakhala akupenyelela zamalisece ayenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikuyesetsa kukhala woyela?’ Iye ayenela kuyesetsa kupeza thandizo kuti aleke cizoloŵezi coipa cimeneci.—Yak. 5:14.

ONETSANI KUTI NDINU OYELA MWA KUKHALA OMVELA

7. Malinga ndi Levitiko 8:22-24, kodi Yesu anapeleka citsanzo cotani?

7 Pamene anakhazikitsa ansembe mu Isiraeli, Aroni ndi ana ake anapakidwa magazi a nkhosa yaimuna munsi mwa khutu la kulamanja, pa cala cacikulu ca kumanja, ndi ca kumwendo wa kulamanja. (Ŵelengani Levitiko 8:22-24.) Kugwilitsila nchito magazi mwanjilayi, kunali cizindikilo cakuti ansembe adzacita nchito zao mokhulupilika. Mofananamo, Yesu, Mkulu wa Ansembe, anapeleka citsanzo cabwino kwa odzozedwa ndi nkhosa zina. Iye anatsatila citsogozo ca Mulungu, anacita cifunilo ca Yehova, ndipo anatsatila njila yabwino ya moyo.—Yoh. 4:31-34.

8. N’ciani cimene alambila onse a Yehova ayenela kucita?

8 Akristu odzozedwa ndi a nkhosa zina, ayenela kutsatila citsanzo cabwino ca Yesu, Mkulu wao wa Ansembe. Alambili onse a Yehova ayenela kumvela malangizo opezeka m’Mau a Mulungu. Akatelo adzapewa ‘kumvetsa cisoni mzimu woyela.’ (Aef. 4:30) Iwo ayenela ‘kuongola njila zimene mapazi ao akuyendamo.’—Aheb. 12:13.

9. Kodi abale atatu amene akhala akugwila nchito ndi a m’Bungwe Lolamulila anakamba ciani? Ndipo zimene anakamba zingakuthandizeni bwanji kukhala oyela?

9 Ganizilani ndemanga zocokela pansi pamtima za abale atatu amene ali ndi ciyembekezo ca padziko lapansi, ndipo atumikila kwa zaka zambili ndi a m’Bungwe Lolamulila. Woyamba anati: “Ngakhale kuti kugwila nchito ndi odzozedwa ndi mwai wapadela, kugwilizana kwambili ndi io, ngakhale kuti ndi odzozedwa ndi mzimu, kwandithandiza kudziŵa kuti abale amenewa ndi opanda ungwilo. Komabe, kwa zaka zambili colinga canga cakhala kupitilizabe kumvela amene akutsogolela.” M’bale waciŵili anati: “Malemba monga 2 Akorinto 10:5, lonena za ‘kumvela Kristu,’ andithandiza kukhala womvela ndi kugwilizana ndi amene akutsogolela. Kumeneku ndi kumvela kocokela pansi pamtima.” M’bale wacitatu anati: “Kukonda zimene Yehova amakonda ndi kudana ndi zimene iye amadana nazo, ndiponso kufunafuna citsogozo cake nthawi zonse ndi kucita zimene zimam’kondweletsa, ndiko kumvela gulu la Yehova. Izi ziphatikizapo kumvela amene iye akugwilitsila nchito kuti akwanilitse colinga cake padziko lapansi.” M’bale ameneyu amakumbukila citsanzo ca m’bale Nathan Knorr, amene anali m’Bungwe Lolamulila. Iye anakamba kuti, m’bale Knorr anatsatila mosavuta mfundo zimene abale ena anazikaikila, zimene zinatuluka mu Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya mu 1925, pa mutu wakuti “Kubadwa kwa Mtundu.” Zimenezi zinacititsa cidwi m’bale ameneyu. Kuganizila kwambili mfundo za abale atatu amenewa kudzakuthandizani kumvela Mulungu ndi kukhalabe oyela.

KHALANI OYELA MWA KUMVELA LAMULO LA MULUNGU LOKHUDZA MAGAZI

10. N’cifukwa ciani kumvela lamulo la Mulungu lokhudza magazi n’kofunika kwambili?

10 Ŵelengani Levitiko 17:10. Yehova analamula Aisiraeli kuti asadye “magazi alionse.” Akristu naonso afunika kumvela lamulo lopewa magazi a nyama kapena a munthu. (Mac. 15:28, 29) Timacita mantha tikaganiza zocita zinthu zimene zingacititse kuti Mulungu atikane ndi kuticotsa mumpingo wake. Motelo, timam’konda ndipo timafunitsitsa kumvela malamulo ake. Kaya moyo wathu ukhale pangozi, sitidzagonja kwa anthu amene sadziŵa Yehova amene angatikakamize kuti tisamvele Mulungu. Tidziŵa kuti anthu ena angatinyoze cifukwa cokana kuikidwa magazi, koma timafuna kumvela Mulungu. (Yuda 17, 18) N’ciani cingatithandize kuti tikhale ‘otsimikiza mtima kwambili’ kukana kudya kapena kuikidwa magazi?—Deut. 12:23.

11. N’cifukwa ciani tinganene kuti Tsiku Lophimba Macimo silinali tsiku la mwambo cabe?

11 Kugwilitsila nchito magazi a nyama kumene mkulu wa ansembe waciisiraeli anali kucita pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo, kumatithandiza kudziŵa mmene Mulungu amaonela magazi. Magazi anali kugwilitsidwa nchito kokha pa zocitika zapadela. Anali kugwilitsidwa nchito kuphimba macimo a anthu, amene anali kufuna kuti Yehova awakhululukile. Magazi a ng’ombe ndi mbuzi anali kuwadonthetsa patsogolo pa civundikilo ca likasa la cipangano. (Lev. 16:14, 15, 19) Zocitika zimenezi zinatsegula njila yakuti Yehova akhululukile Aisiraeli macimo ao. Ndiponso, Yehova analamula kuti ngati munthu wapha nyama kuti akadye, anayenela kuthila magazi ake pansi ndi kuwafotsela. Iwo anafunikila kucita zimenezo ‘cifukwa moyo wa nyama iliyonse ndi magazi ake.’ (Lev.  17:11-14) Kodi umenewu unali mwambo cabe? Iyai. Kugwilitsila nchito magazi pa Tsiku Lophimba Macimo, ndiponso lamulo lakuti azithila pansi magazi, n’zogwilizana ndi lamulo limene Yehova anapeleka poyamba kwa Nowa ndi mbadwa zake ponena za magazi. (Gen. 9:3-6) Yehova analetsa kudya magazi monga cakudya. Nanga zimenezi zimatanthauzanji kwa Akristu?

12. Kodi Paulo anagwilizanitsa bwanji magazi ndi kukhululukidwa macimo?

12 Mtumwi Paulo anafotokoza kuti magazi ali ndi mphamvu yoyeletsa. Iye analemba kuti: “Pafupifupi zinthu zonse zimayeletsedwa ndi magazi malinga ndi Cilamulo, ndipo popanda kukhetsa magazi anthu sangakhululukidwe macimo ao.” (Aheb. 9:22) Paulo anafotokozanso kuti nsembe zanyama, ngakhale kuti zinali kugwila nchito pamlingo wocepa, zinali kungokumbutsa Aisiraeli kuti anali ocimwa, ndi kuti anafunikila nsembe yoposa yanyama kuti icotseletu macimo ao. Conco, Cilamulo cinali “mthunzi cabe wa zinthu zabwino zimene zikubwela osati zinthu zenizenizo.” (Aheb. 10:1-4) Nanga zikanatheka bwanji kuti macimo akhululukidwe?

13. Mumamva bwanji kuti Yesu anapeleka mtengo wa magazi ake kwa Yehova?

13 Ŵelengani Aefeso 1:7. Yesu Kristu anafa kuti aombole anthu onse, ndipo zimenezi zili ndi tanthauzo lalikulu kwa anthu amene amakonda iye ndi Atate wake. (Agal. 2:20) Komabe, zimene Yesu anacita pambuyo pa imfa ndi kuukitsidwa kwake, n’zimene zinacititsa kuti kukhale kotheka kuti macimo athu akhululukidwe. Yesu anakwanilitsa zimene zinali kucitilidwa cithunzi m’Cilamulo ca Mose pa Tsiku Lophimba Macimo. Patsiku limenelo, mkulu wa ansembe anali kutenga magazi ansembe zanyama, ndi kuloŵa nao m’Malo Oyela Koposa m’cihema. Kucita zimenezi kunali monga kuti wafika kwa Mulungu. (Lev. 16:11-15) Mofananamo, Yesu analoŵa kumwamba kwenikweni ndi mtengo wa magazi ake ndi kuwapeleka kwa Yehova. (Aheb. 9:6, 7, 11-14, 24-28) Ndife oyamikila kwambili kuti macimo athu amakhululukidwa, ndi kuti tili ndi cikumbumtima coyela cifukwa cokhulupilila nsembe ya Yesu.

14, 15. N’cifukwa ciani n’kofunika kumvetsetsa ndiponso kumvela lamulo la Yehova lokhudza magazi?

14 Mwina tsopano mwamvetsetsa cifukwa cake Yehova anatilamula kupewa “magazi alionse.” (Lev. 17:10) Kodi tsopano mwaona cifukwa cake magazi ndi opatulika kwa Mulungu? Iye amaona kuti magazi amaimila moyo. (Gen. 9:4) Mosakaikila, tiyenela kuona magazi monga mmene Mulungu amawaonela, ndi kumvela lamulo lake lakuti tiziwapewa. Njila imodzi imene tingakhalile pamtendele ndi Mulungu ndiyo kukhulupilila nsembe ya Yesu, ndi kumvetsetsa kuti magazi ndi amtengo wapatali kwa Mlengi wathu.—Akol. 1:19, 20.

15 Mosayembekezela, aliyense wa ife angakumane ndi nkhani yokhudza magazi. Wacibale kapena bwenzi lathu lapamtima, mosayembekezela angafunike kusankha kaya kuikidwa magazi kapena ai. Panthawi zovuta zimenezi, tingafunikile kusankha kulandila tuzigawo twa magazi ndi njila zacipatala zogwilitsila nchito magazi. Conco, n’kofunika kupemphela kwa Yehova, ndi kufufuza kuti tikhale okonzekela kaamba ka zakugwa mwadzidzidzi. Tikatelo, tidzatsimikiza mtima kupewa magazi. Sitifuna kukhumudwitsa Yehova mwa kucita zinthu zimene iye amadana nazo. Masiku ano, madokotala ndi anthu ena amalimbikitsa anthu kupeleka magazi n’colinga copulumutsa moyo. Koma anthu oyela a Yehova amadziŵa kuti Mlengi ndiye amadziŵa mmene tiyenela kugwilitsila nchito magazi. Kwa iye, “magazi alionse” ndi opatulika. Motelo, tiyenela kuyesetsa kumvela lamulo lake lopewa magazi. Ndipo khalidwe lathu loyela liyenela kuonetsa kuti timayamikila kwambili magazi a Yesu opulumutsa moyo. Ndi magazi okha a Yesu amene adzacititsa kuti macimo athu akhululukidwe, ndi kuti tikapeze moyo wosatha.—Yoh. 3:16.

CIFUKWA CAKE YEHOVA AMAFUNA KUTI TIKHALE OYELA

16. N’cifukwa ciani anthu a Yehova afunika kukhala oyela?

16 Pamene Mulungu anapulumutsa Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo, iye anawauza kuti: “Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo kuti ndikusonyezeni kuti ndine Mulungu. Muzikhala oyela, cifukwa ine ndine woyela.” (Lev. 11:45) Anthu a Yehova anayenela kukhala oyela cifukwa iye ndi woyela. Pokhala Mboni zake, nafenso tifunika kukhala oyela. Buku la Levitiko n’lothandiza kwambili pa nkhani ya ciyelo.

17. Mukumva bwanji tsopano ponena za buku la m’Baibulo la Levitiko?

17 Ndithudi, tapindula kwambili kuphunzila mfundo zina za m’buku la Levitiko. Mwacionekele, zimene taphunzila zatithandiza kuyamikila kwambili buku louzilidwa limeneli la m’Baibulo. Kuganizila kwambili mfundo zamtengo wapatali zopezeka m’buku la Levitiko, kwatithandiza kumvetsetsa cifukwa cake tiyenela kukhala oyela. Komabe, ndi mfundo zina ziti zamtengo wapatali zimene tingaphunzile m’buku la Levitiko? Nanga buku limeneli lingatithandize bwanji kulambila Mulungu m’njila yovomelezeka? Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani