LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 12/15 masa. 4-5
  • Yehova Amadalitsa Kwambili Anthu Ofunitsitsa Kupeleka

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Amadalitsa Kwambili Anthu Ofunitsitsa Kupeleka
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Nkhani Zofanana
  • “Nchitoyi Ndi Yaikulu”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • “Munthu Wopatsa Mowolowa Manja Adzalandila Mphoto”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Muziyamikila Kuolowa Manja kwa Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 12/15 masa. 4-5

Yehova Amadalitsa Kwambili Anthu Ofunitsitsa Kupeleka

MLENGI wathu anatilemekeza kwambili mwa kutipatsa mphatso yamtengo wapatali ya ufulu wodzisankhila zocita. Kuonjezela apo, iye amadalitsa kwambili anthu amene amadzipeleka ndi mtima wonse kuti apititse patsogolo kulambila koona ndiponso amene amathandiza kuti dzina lake liyeletsedwe ndi kuti colinga cake cabwino cikwanilitsidwe. Yehova safuna kuti tizimumvela mwamwambo cabe, mokakamizika kapena cifukwa coopa cilango. Koma amayamikila kwambili anthu amene amadzipeleka mofunitsitsa cifukwa comukonda ndi mtima wonse ndiponso cifukwa coyamikila kwambili zimene amawacitila.

Mwacitsanzo, pamene Aisiraeli anali m’cipululu ca Sinai, Yehova anawalamula kuti amange malo olambilila. Iye anati: “Nonse mupeleke zopeleka kwa Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa apeleke kwa Yehova.” (Eks. 35:5) Mwiisiraeli aliyense anali ndi ufulu wopeleka copeleka ciliconse caufulu cimene akanakwanitsa mosasamala kanthu za kuculuka kwake malinga ngati copelekaco cinali cakuti angathe kucigwilitsila nchito pomanga malo olambilila. Kodi Aisiraeli anacita ciani atapemphedwa kupeleka zopeleka?

“Aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa” ndi “aliyense amene anali ndi mzimu wofunitsitsa,” anapeleka copeleka caufulu “ndi mtima wofunitsitsa.” Amuna ndi akazi mofunitsitsa anapeleka zopeleka zothandiza pa nchito ya Yehova. Iwo anapeleka zinthu monga zokometsela zomanga pazovala, ndolo, mphete, golide, siliva, mkuwa, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiilila, ulusi wofiila kwambili, nsalu zabwino kwambili, ubweya wa mbuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiila, zikopa za akatumbu, matabwa a mthethe, miyala yamtengo wapatali, mafuta a basamu, ndi mafuta ena. Conco “zinthuzo zinali zokwanila pa nchito yonse yoyenela kucitika, ndipo zinaposanso zinthu zofunikila pa nchitoyo.”—Eks 35:21-24, 27-29; 36:7.

Cimene cinakondweletsa kwambili Yehova ndi mzimu wopeleka mofunitsitsa wa anthu amene anacilikiza kulambila koona osati zinthu zimene anapelekazo. Anthuwo anagwilitsilanso nchito nthawi yao ndi mphamvu zao pa nchitoyo. Nkhaniyi imanena kuti, “akazi onse aluso anawomba nsalu ndi manja ao.” Ndipo imanenanso kuti, “akazi onse aluso amene anali ndi mtima wofunitsitsa anawomba nsalu za ubweya wa mbuzi.” Komanso, Yehova anapatsa Bezaleli mtima ‘wanzelu, wozindikila, wodziŵa zinthu, kuti akhale mmisili waluso pa nchito ina iliyonse.’ Zoonadi, Mulungu anacititsa Bezaleli ndi Oholiabu kukhala ndi luso lofunika kuti akwanitse kugwila nchito yonse imene anawapatsa.—Eks. 35:25, 26, 30-35.

Pamene Yehova anapempha Aisiraeli kupeleka zopeleka, iye sanakaikile kuti “aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa” adzacilikiza kulambila koona. Iye anadalitsa kwambili Aisiraeli amene anali ndi mtima wofunitsitsa kupeleka mwa kuwatsogolela, ndipo anthuwo anali kukhala acimwemwe. Motelo Yehova anaonetsa kuti amadalitsa anthu ake amene ali ndi mtima wofunitsitsa kupanga copeleka, ndipo amaonetsetsa kuti anthu akewo sakusowa ciliconse cimene cingawathandize kukwanilitsa colinga cake. (Sal. 34:9) Mukamatumikila Yehova ndi mtima wonse, iye sadzalephela kukudalitsani.

ZIMENE ENA AMAPELEKA POCILIKIZA NCHITO YAPADZIKO LONSE

Mofanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya Paulo, Akristu ambili masiku ano amapanga bajeti kapena kuika kandalama “kenakake pambali” kuti akaponye m’mabokosi a zopeleka za “Nchito Yapadziko Lonse.” (1 Akor. 16:2) Mwezi uliwonse mipingo imatumiza zopeleka zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova m’dziko lao. N’zothekanso kutumiza nokha zopeleka zanu ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko lanu. Mungafunse ku ofesi ya nthambi m’dziko lanu kuti mudziŵe mmene mungacitile zimenezi. Adilesi ya ofesi ya nthambi iliyonse imapezeka pa webusaiti ya www.jw.org. Mungapeleke zopeleka zanu m’njila izi:

ZOPELEKA MWACINDUNJI

  • Mukhoza kupeleka ndalama, zinthu ngati ndolo (masikiyo), mphete, zibangili ndiponso zinthu zina zamtengo wapatali. Muyenela kutumiza zinthuzo limodzi ndi kalata yonena kuti ndi copeleka.

ZONGOBWELEKETSA

  • Mungapeleke ndalama n’kufotokoza kuti mudzaziitanitsa mukadzazifuna.

  • Muyenela kutumiza ndalamazo limodzi ndi kalata yonena kuti mwangowabweleka ndalamazo.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezela pa kupeleka mphatso za ndalama kapena zinthu zina zamtengo wapatali, pali njila zinanso zopelekela zinthu zothandiza pa nchito ya Ufumu padziko lonse. Njila zimenezi zili m’munsimu. Musanasankhe njila iliyonse, muyenela kufunsa ku ofesi ya nthambi kuti mudziŵe njila zimene ndi zotheka m’dziko lanu. Popeza malamulo amasiyana malinga ndi dziko, muyenela kufunsanso anthu odziŵa bwino za malamulo ndi misonkho.

Inshuwalansi: Mungakonze zoti gulu la Yehova lidzalandile ndalama za inshuwalansi kapena za penshoni.

Maakaunti Akubanki: Mukhoza kupeleka zinthu monga maakaunti anu akubanki, zikalata zosungitsila ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwilitse nchito mukadzapuma pa nchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalila, gulu la Mulungu lidzatenge zinthuzo. Pocita zimenezi, muyenela kutsatila malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendela.

Masheya: Mungapeleke ku gulu la Yehova masheya amene muli nao m’kampani kapena kukonza zoti lidzalandile masheyawo mukadzamwalila.

Malo ndi Nyumba: Mungapeleke ku gulu la Yehova malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe. Ngati nyumbayo ndi imene mukukhalamo, mukhoza kuipeleka komabe n’kupitiliza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli ndi moyo.

Cuma Camasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomelezeka ndi boma kuti gulu la Yehova lidzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, inuyo mukadzamwalila.

Ngati mufuna kudziŵa zambili, mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni zaYehova ya m’dziko lanu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani