Yamikani Yehova Ndipo Mudzadalitsidwa
“Yamikani Yehova, cifukwa iye ndi wabwino.”—SAL. 106:1.
1. N’cifukwa ciani Yehova ndi woyenela kumuyamikila?
YEHOVA ndi woyenela kumuyamikila, cifukwa amapeleka “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.” (Yak. 1:17) Pokhala M’busa wathu, iye mwacikondi amatisamalila mwakuthupi ndi mwa kuuzimu. (Sal. 23:1-3) Iye ndiye “pothawila pathu ndi mphamvu yathu,” makamaka panthawi ya masautso. (Sal. 46:1) Ndithudi, tili ndi zifukwa zambili zokhalila oyamikila ndi mtima wonse monga mmene wamasalimo analembela kuti: “Yamikani Yehova, cifukwa iye ndi wabwino. Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”—Sal. 106:1.
Lemba lathu la caka ca 2015: “Yamikani Yehova, cifukwa iye ndi wabwino.”—Salimo 106:1
2, 3. (a) Ndi ngozi yotani imene tingakumane nayo ngati sitiyamikila pa zinthu zabwino zimene tili nazo? (b) Ndi mafunso ati amene tikambilana m’nkhani ino?
2 N’cifukwa ciani n’kofunika kuphunzila nkhani yokhudza kukhala woyamikila? Mogwilizana ndi ulosi, anthu masiku ano acita kunyanya pa nkhani yokhala osayamikila. (2 Tim. 3:2) Anthu ambili sayamikila zinthu zabwino zimene Yehova awacitila. Dziko lokonda cumali, limalimbikitsa anthu mamiliyoni ambili kugula zinthu zambili kuposa zimene afunikila. Pa cifukwa cimeneci, anthu ambili sakhutila ndi zimene ali nazo. Mofanana ndi Aisiraeli, ifenso tingasiye kukhala oyamikila, ndipo tingayambe kuona ubwenzi wathu wamtengo wapatali ndi Yehova kukhala wosafunika. Tingasiyenso kuyamikila zinthu zabwino zimene Yehova waticitila.—Sal. 106:7, 11-13.
3 Komanso, taganizilani zimene zingacitike tikakumana ndi mavuto. Tingakhumudwe ndi kuiwala zinthu zonse zabwino zimene tingakhale nazo. (Sal. 116:3) N’ciani cingatithandize kukhalabe ndi mtima woyamikila? Nanga n’ciani cingatithandize kuonabe zinthu moyenela tikakumana ndi mavuto? Tiyeni tione.
‘INU YEHOVA MWACITA ZINTHU ZAMBILI ZODABWITSA’
4. N’ciani cingatithandize kukhalabe ndi mtima woyamikila?
4 Khama ndi lofunika kuti tikhalabe oyamikila kwa Yehova. Coyamba, tiyenela kuzindikila zinthu zabwino zimene Yehova waticitila. Ndiyeno, tiyenela kuona mmene zinthu zimenezi zimasonyezela cikondi cacikulu cimene Mulungu ali naco pa ife. Wamasalimo anadabwa kwambili atazindikila kuculuka kwa zinthu zabwino zimene Yehova anam’citila.—Ŵelengani Salimo 40:5; 107:43.
5. N’ciani cimene tikuphunzila pa citsanzo ca mtumwi Paulo pankhani yokhala oyamikila?
5 Citsanzo ca mtumwi Paulo cingatithandize kuphunzila kukhala ndi mtima woyamikila. Mwacionekele, iye anali kukonda kusinkhasinkha ndi kukamba mau oyamikila pa zinthu zabwino zimene Mulungu anam’citila. Paulo anali kukumbukila kuti kale anali “wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wacipongwe.” Motelo, iye anayamikila Mulungu ndi Kristu cifukwa comusonyeza cifundo ndi kumpatsa utumiki ngakhale kuti kale anali munthu wocimwa. (Ŵelengani 1 Timoteyo 1:12-14.) Paulo anali kuyamikilanso kwambili Akristu anzake, ndipo anali kukonda kuyamikila Yehova cifukwa ca makhalidwe abwino ndi cikhulupililo ca Akristu anzakewo. (Afil. 1:3-5, 7; 1 Ates. 1:2, 3) Iye anayamikilanso Yehova pa zonse zimene abale ake anam’citila atakumana ndi mavuto. (Mac. 28:15; 2 Akor. 7:5-7) Ndiye cifukwa cake Paulo analimbikitsa Akristu kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikila . . . , mwa masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu zogwila mtima.”—Akol. 3:15-17.
PEMPHELO NDI KUSINKHASINKHA ZIMATITHANDIZA KUKHALABE OYAMIKILA
6. Kodi mumayamikila Yehova makamaka cifukwa ca ciani?
6 Tingatengele bwanji citsanzo cabwino ca Paulo pankhani yokhala oyamikila? Mofanana ndi Paulo, aliyense ayenela kusinkhasinkha pa zinthu zimene Yehova wam’citila. (Sal. 116:12) Kodi mukanayankha bwanji ngati munthu wina akanakufunsani kuti, ‘Ndi zinthu ziti zimene Yehova anakucitilani zimene mumayamikila?’ Kodi mungacule ubwenzi wanu wamtengo wapatali ndi Yehova? Kapena kukhululukidwa macimo cifukwa ca cikhulupililo canu mu nsembe ya dipo ya Kristu? Kodi mungacule maina a abale ndi alongo amene anakuthandizani pamavuto anu? Mosakaikila, mungaculenso mkazi kapena mwamuna wanu ndiponso ana anu. Kupeza nthawi yosinkhasinkha pa zinthu zabwino zimene Yehova, Atate wathu wacikondi waticitila, kudzatithandiza kukhala ndi mtima woyamikila, ndipo tidzakhala anthu oyamikila nthawi zonse.—Ŵelengani Salimo 92:1, 2.
7. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kupeleka mapemphelo aciyamiko? (b) Ndi mapindu otani amene inuyo mudzapeza cifukwa copeleka mapemphelo aciyamiko?
7 Kusinkhasinkha pa zinthu zabwino zimene Yehova waticitila, kudzatithandiza kumuyamikila m’pemphelo. (Sal. 95:2; 100:4, 5) Anthu ambili amaganiza kuti tiyenela kupemphela cabe ngati tifuna zinthu zinazake kwa Mulungu. Komabe, ife timadziŵa kuti Yehova amakondwela ngati timuyamikila pa zinthu zimene watipatsa. M’Baibulo, muli zitsanzo zambili za mapemphelo aciyamiko monga ya Hana ndi Hezekiya. (1 Sam. 2:1-10; Yes. 38:9-20) Conco, tengelani citsanzo ca atumiki okhulupilika amene anali ndi mzimu woyamikila. Zoonadi, muyenela kuyamikila Yehova m’pemphelo cifukwa ca zinthu zabwino zimene muli nazo. (1 Ates. 5:17, 18) Mukatelo mudzapeza mapindu ambili. Mudzakhala osangalala, cikondi canu pa Yehova cidzalimba, ndipo mudzamuyandikila kwambili.—Yak. 4:8.
Ndi zinthu ziti zimene Yehova anakucitilani zimene mumayamikila? (Onani ndime 6 ndi 7)
8. N’ciani cingatipangitse kusiya kuyamikila zonse zimene Yehova waticitila?
8 Ngati sitisamala, tingasiye kuyamikila zinthu zabwino zimene Yehova amaticitila. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti ndife opanda ungwilo ndipo tinatengela mzimu wosayamikila kwa makolo athu oyamba. Yehova anaika Adamu ndi Hava m’paladaiso. Anawapatsanso zonse zimene anali kufunikila, ndipo akanakhala ndi moyo mwamtendele kosatha. (Gen. 1:28) Koma io sanayamikile zinthu zabwino zimene anapatsidwa. Mwadyela io anali kufuna zambili. Pa cifukwa cimeneci, io anataya zonse. (Gen. 3:6, 7, 17-19) Popeza tikukhala m’dziko mmene muli anthu osayamikila, ifenso tingayambe kuiwala zinthu zabwino zimene Yehova waticitila. Tingayambe kuona ubwenzi wathu ndi iye mopepuka. Ndiponso, tingalephele kuyamikila mwai umene tili nao wokhala m’gulu la abale apadziko lapansi. Tingatengeke kwambili ndi zinthu za m’dzikoli limene lidzapita posacedwapa. (1 Yoh. 2:15-17) Kuti tisakhodwe mumsampha umenewu, tiyenela kusinkhasinkha pa zinthu zabwino zimene tili nazo, ndi kuyamikila Yehova nthawi zonse kaamba ka mwai wokhala anthu ake.—Ŵelengani Salimo 27:4.
POLIMBANA NDI MAVUTO
9. N’cifukwa ciani tiyenela kuganizila zinthu zabwino zimene tili nazo tikakumana ndi mavuto?
9 Kukhala ndi mtima woyamikila kungatithandize kupilila mavuto aakulu. Timakhumudwa tikakumana ndi mavuto aakulu paumoyo, monga kusakhulupilika kwa mwamuna kapena mkazi wathu, matenda aakulu, imfa ya munthu amene timakonda, kapena mavuto ena amene tingakumane nao pambuyo pa ngozi yacilengedwe. Kukumbukila zinthu zabwino zimene tili nazo panthawiyo, kungatitonthoze ndi kutilimbikitsa. Taganizilani zitsanzo zina za amene anakumanapo ndi zimenezi.
10. Kodi Irina wapindula bwanji cifukwa coganizila zinthu zabwino zimene ali nazo?
10 Irinaa, mpainiya wanthawi zonse ku North America, anali wokwatiwa kwa mkulu mumpingo, koma mkuluyo anakhala wosakhulupilika cakuti anam’siya ndi ana. N’ciani cinathandiza Irina kupitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika? Iye anati: “Ndiyamikila Yehova cifukwa condisamalila mwacikondi. Tsiku lililonse ndikamaganizila pa zinthu zabwino zimene wandicitila, ndimaona kuti ndi mwai waukulu kudziŵika ndiponso kukondedwa ndi Atate wathu wakumwamba amene amatiteteza. Ndimadziŵa kuti sadzandisiya.” Ngakhale kuti Irina wakhala akukumana ndi mavuto ambili, kukhala wosangalala kumamuthandiza kupilila ndipo amalimbikitsa ena.
11. N’ciani cinathandiza Kyung-sook kupilila matenda oopsa?
11 Kyung-sook, amene amakhala ku Asia, anali kucita upainiya ndi mwamuna wake kwa zaka zoposa 20. Mwadzidzidzi, anam’peza ndi khansa ya m’mapapo imene inafika poipa kwambili, ndipo anauzidwa kuti adzakhala ndi moyo kwa miyezi itatu kapena 6. Ngakhale kuti iye ndi mwamuna wake anali atakumanapo ndi mavuto ambili, aakulu ndi aang’ono, io anali kuona kuti thanzi lao linali cabe bwino. Kyung-sook anati: “Nditauzidwa kuti ndili ndimatendawa, ndinakhumudwa kwambili. Ndinaona monga zonse zathela pamenepa, ndipo ndinali ndi mantha kwambili.” N’ciani cathandiza Kyung-sook kupilila? Iye akuti: “Ndisanagone usiku uliwonse, ndimapita pa denga la nyumba yathu ndi kuyamika mokweza mau pa zinthu 5 zimene zandicitikila pa tsikulo. Ndikatelo ndimamva bwino, ndipo ndimapitilizabe kukonda Yehova.” Ndi mapindu otani amene Kyung-sook wapeza cifukwa ca mapemphelo amenewo? Iye akuti: “Ndazindikila kuti Yehova amatilimbikitsa pa mavuto ndi kuti tili ndi zinthu zabwino zambili kuposa mavuto.”
Sheryl ndi mng’ono wake John (Onani ndime 13)
12. N’ciani cinatonthoza Jason mkazi wake atamwalila?
12 Jason, amene akutumikila pa ofesi ya nthambi ina mu Africa muno, wakhala muutumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 30. Iye anati: “Mkazi wanga anamwalila zaka 7 zapitazo, koma ndisaname, imfa ndi yopweteka. Mphamvu zimandithela ndikayamba kuganizila mmene mkazi wanga anavutikila ndi kansa.” N’ciani cathandiza Jason kupilila? Iye anapitiliza kuti: “Tsiku lina, ndinakumbukila mmene ine ndi mkazi wanga tinali kusangalalila monga banja. Nditakumbukila zimenezi, ndinayamikila Yehova. Mtima wanga unakhala pansi ndipo kucokela nthawiyo, ndimayamikila Yehova nthawi zonse ndikakumbukila zinthu zabwino ngati zimenezi. Kukhala oyamikila kwandithandiza kuyamba kuona zinthu moyenela. Mtima wanga umapwetekabe cifukwa ca imfa ya mkazi wanga. Koma kuyamikila Yehova kuti ndinali kusangalala ndi mkazi wanga, ndiponso kuti ndinali ndi mwai wotumikila Mulungu ndi munthu amene anali kumukonda kwambili, kwandithandiza kuona zinthu moyenela.”
“Ndikuyamikila kwambili kuti Yehova ndi Mulungu wanga.”—Sheryl
13. N’ciani cinathandiza Sheryl kupilila pamene ambili a m’banja lake anamwalila?
13 Cimphepo camphamvu cocedwa Haiyan cinasakaza cigawo capakati pa dziko la Philippines mu 2013. Panthawiyo, Sheryl, anali ndi zaka 13 zokha, ndipo zinthu zao zonse zinaonongeka. Iye anati: “Nyumba yathu inaonongeka ndipo ambili a m’banja lathu anaphedwa ndi cimpemphoco.” Makolo ake ndiponso azilongosi ake atatu, onse anafa ndi cimpempho camphamvu cimeneco. N’ciani cathandiza Sheryl kupilila mavuto amenewa popanda kukhumudwa? Iye ali ndi mtima woyamikila ndipo amakonda kuganizila zinthu zimene ali nazo. Iye anati: “Ndinaona zonse zimene abale ndi alongo anacita modzipeleka pobweletsa zinthu zosiyanasiyana pambuyo pangoziyo, komanso cilimbikitso cimene anali kupatsa anthu okhudzidwa. Ndinali kudziŵa kuti abale padziko lonse lapansi anali kundipemphelela.” Anaonjezelanso kuti: “Ndikuyamikila kwambili kuti Yehova ndi Mulungu wanga. Nthawi zonse amatipatsa zimene tifunikila.” Indedi, kukumbukila zinthu zabwino zimene tili nazo ndi mankhwala othandiza panthawi za mavuto. Kukhala ndi mtima woyamikila kumatithandiza kupilila mosasamala kanthu za zothetsa nzelu zimene tingakumane nazo.—Aef. 5:20; ŵelengani Afilipi 4:6, 7.
“INE NDIDZAKONDWELABE MWA YEHOVA”
14. Ndi ciyembekezo cosangalatsa citi cimene tili naco? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
14 M’mbili yonse, anthu a Yehova akhala akusangalala ndi zinthu zimene ali nazo. Mwacitsanzo, Aisiraeli atapulumutsidwa kwa Farao ndi magulu ake ankhondo pa Nyanja Yofiila, io anaonetsa cisangalalo cao mwa kuimba nyimbo zacitamando ndi ciyamiko zogwila mtima. (Eks. 15:1-21) Cimodzi mwa zinthu zabwino zimene tikuyembekezela ndi ciyembekezo cathu cotsimikizilika cakuti tidzapulumutsidwa ku mavuto onse amene timakumana nao. (Sal. 37:9-11; Yes. 25:8; 33:24) Ganizilani mmene tidzasangalalila pamene Yehova adzaononga adani ake onse ndi kutiloŵetsa m’dziko latsopano la mtendele ndi la cilungamo. Tsikulo lidzakhala loyamikiladi Yehova.—Chiv. 20:1-3; 21:3, 4.
15. N’ciani cimene mwatsimikiza mtima kucita m’caka conse ca 2015?
15 M’caka ca 2015 cino, tikuyembekezela kulandila madalitso osaŵelengeka akuuzimu kucokela kwa Yehova. N’zoona kuti mwina tidzakumana ndi mayeselo. Koma kaya tidzakumana ndi zotani, tili ndi cidalilo cakuti Yehova sadzatisiya. (Deut. 31:8; Sal. 9:9, 10) Iye adzapitilizabe kutipatsa zonse zofunikila kuti tipitilize kumutumikila mokhulupilika. Motelo, tiyeni tikhale otsimikiza mtima kukhalabe ndi maganizo amene mneneli Habakuku anali nao pamene anakamba kuti: “Ngakhale mkuyu usaphukile maluwa, mtengo wa mpesa usabale zipatso, mtengo wa maolivi ulephele kubala zipatso, munda wa m’mphepete mwa phili usatulutse cakudya, nkhosa ndi ng’ombe zithemo m’khola, Ine ndidzakondwelabe mwa Yehova ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wacipulumutso canga.” (Hab. 3:17, 18) Inde, kwa caka conseci, tiyeni tizikumbukila mwacisangalalo zinthu zonse zabwino ndi kutsatila malangizo amene ali m’lemba lathu la caka ca 2015, limene limati: “Yamikani Yehova, cifukwa iye ndi wabwino.”—Sal. 106:1.
a Maina ena asinthidwa.