LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 1/15 masa. 13-17
  • Cifukwa Cake Timacita Mgonelo wa Ambuye

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cifukwa Cake Timacita Mgonelo wa Ambuye
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIFUKWA CAKE TIMAKUMBUKILA IMFA YA YESU
  • KODI ZIZINDIKILO ZIMAIMILA CIANI?
  • MMENE TINGAKONZEKELELE CIKUMBUTSO
  • NDANI AYENELA KUDYA?
  • MUZIONA CIYEMBEKEZO CANU KUKHALA CAMTENGO WAPATALI
  • KODI MUDZAPEZEKAPO?
  • ‘Citani Zimenezi Pondikumbukila’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Cifukwa Cake Timapezeka pa Cikumbutso
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 1/15 masa. 13-17
Mwezi wathunthu ukuwala m’nyumba imene ili ndi cipinda capamwamba cimene Yesu ndi atumwi ake akucitilamo mwambo wa Pasika

Cifukwa Cake Timacita Mgonelo wa Ambuye

“Muzicita zimenezi pondikumbukila.”—1 AKOR. 11:24.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kucita Mgonelo wa Ambuye?

  • Kodi pa Cikumbutso amagwilitsila nchito zizindikilo ziti? Nanga zimaimila ciani?

  • Kodi Akristu ayenela kuona motani ciyembekezo cao copatsidwa ndi Mulungu?

1, 2. N’ciani cimene Yesu anacita usiku wa pa Nisani 14, mu 33 C.E.? (Onani cithunzi cili pamwamba.)

USIKU wa pa Nisani 14, mu 33 C.E., mwezi wathunthu unaonekela ku Yerusalemu. Patsikulo Yesu ndi ophunzila ake anacita Pasika, pokumbukila tsiku limene Yehova anapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo zaka 1,500 m’mbuyomo. Pamene Yesu anali ndi ophunzila ake 11 okhulupilika, iye anayambitsa mwambo wa cakudya capadela. Ophunzila ake anafunikila kucita mwambo umenewo caka ndi caka pokumbukila imfa yake.a—Mat. 26:1, 2.

2 Atapempha dalitso, Yesu anapatsila atumwi ake mkate wopanda cofufumitsa ndi kuwauza kuti: “Eni, idyani.” Anatenganso kapu ya vinyo, ndipo atapemphelanso, anawauza kuti: “Imwani nonsenu.” (Mat. 26:26, 27) Mkate ndi vinyo anali ndi tanthauzo lapadela. Ndipo Yesu anaphunzitsa atumwi ake okhulupilika zinthu zambili pausiku wosaiwalikawo.

3. Tikambilana mafunso ati m’nkhani ino?

3 Izi n’zimene Yesu anacita pamene anali kuyambitsa mwambo wa Cikumbutso ca imfa yake, cimene cimachedwanso kuti “Cakudya Camadzulo ca Ambuye.” (1 Akor. 11:20) Ponena za Cikumbutso  cimeneci, ena angafunse kuti: N’cifukwa ciani timakumbukila imfa ya Yesu? Kodi mkate ndi vinyo zimaimila ciani? Nanga tingakonzekele bwanji Cikumbutso? Ndani ayenela kudya zizindikilo? Kodi Akristu amaona bwanji zimene Malemba amanena ponena za ciyembekezo cao?

CIFUKWA CAKE TIMAKUMBUKILA IMFA YA YESU

4. N’ciani cinakhala cotheka cifukwa ca imfa ya Yesu?

4 Ife tinatengela ucimo ndi imfa kwa Adamu. (Aroma 5:12) Palibe munthu wopanda ungwilo amene angapeleke dipo kwa Mulungu kuti apulumutse moyo wake kapena wa anthu ena. (Sal. 49:6-9) Koma Yesu anapeleka moyo wake wangwilo kaamba ka ife, ndi kupeleka mtengo wa dipo lake kwa Mulungu. Mwa kucita zimenezi, Yesu anacititsa kuti zikhale zotheka kupulumutsidwa ku ucimo ndi imfa, ndiponso kudzalandila mphatso ya moyo wosatha.—Aroma 6:23; 1  Akor. 15:21, 22.

5. (a) Timadziŵa bwanji kuti Mulungu ndi Kristu amakonda anthu? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kupezeka pa mwambo wokumbukila imfa ya Yesu?

5 Dipo ndi umboni wakuti Mulungu amakonda anthu. (Yoh. 3:16) Nsembe ya Yesu ndi umboni wakuti iyenso amatikonda. Asanabwele padziko lapansi, iye anali “mmisili waluso” wa Mulungu, ndipo anali ‘kusangalala ndi zinthu zokhudzana ndi ana a anthu.’ (Miy. 8:30, 31) Kuyamikila zimene Mulungu ndi Mwana wake anaticitila kuyenela kutilimbikitsa kupezeka pa mwambo wokumbukila imfa ya Yesu. Tikatelo, ndiye kuti tikumvela lamulo lakuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.”—1 Akor. 11:23-25.

KODI ZIZINDIKILO ZIMAIMILA CIANI?

6. Kodi mkate ndi vinyo za pa Cikumbutso tiyenela kuziona motani?

6 Pamene Yesu anali kuyambitsa mwambo wa Cikumbutso, iye sanasinthe mozizwitsa mkate ndi vinyo kukhala thupi lake lenileni ndi magazi ake enieni. Ponena za mkate iye anati: “Mkate uwu ukuimila thupi langa.” Ndipo ponena za vinyo iye anati: “Vinyoyu akuimila ‘magazi anga a pangano,’ amene adzakhetsedwa cifukwa ca anthu ambili.” (Maliko 14:22-24) Conco, n’zoonekelatu kuti mkate ndi vinyo ndi ziphiphilitso kapena zizindikilo.

7. Kodi mkate umene timagwilitsila nchito pa Cikumbutso umaimila ciani?

7 Pa cocitika capadela cimeneco ca mu 33 C.E., Yesu anagwilitsila nchito mkate wopanda cofufumitsa umene unatsalako pa mwambo wa Pasika. (Eks. 12:8) Nthawi zina m’Malemba cofufumitsa cimaimila coipitsa kapena ucimo. (Mat. 16:6, 11, 12; Luka 12:1) Motelo, kunali koyenela kuti Yesu anagwilitsila nchito mkate wopanda cofufumitsa kuimila thupi lake lopanda ucimo. (Aheb. 7:26) Conco, mkate wopanda cofufumitsa ndi umene timagwilitsilanso nchito pa Cikumbutso.

8. N’ciani cimene vinyo wa pa Cikumbutso umaimila?

8 Vinyo umene Yesu anagwilitsila nchito pa Nisani 14 mu 33 C.E., unaimila magazi ake, mofanana ndi vinyo umene timagwilitsila nchito pa Cikumbutso masiku ano. Magazi a Yesu anakhetsedwa pamalo ena amene anali kunja kwa Yerusalemu ochedwa Gologota, “kuti macimo akhululukidwe.” (Mat. 26:28; 27:33) Mkate ndi vinyo za pa Cikumbutso zimaimila nsembe ya Yesu ya mtengo wapatali imene anapeleka kaamba ka anthu omvela, ndipo timayamikila mphatso yacikondi imeneyi. Conco, n’koyenela kuti aliyense akonzekele mwambo wa Mgonelo wa Ambuye umenewu.

MMENE TINGAKONZEKELELE CIKUMBUTSO

9. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kutsatila ndandanda ya kuŵelenga Baibulo pa nyengo ya Cikumbutso? (b) Mumamva bwanji mukaganizila za dipo?

9 Mu kalendala yathu ndi m’kabuku ka Kuphunzila Malemba Tsiku ndi Tsiku, mumapezeka ndandanda ya kuŵelenga Baibulo ya pa nyengo ya Cikumbutso. Kutsatila ndandanda imeneyo kungatithandize kusinkhasinkha pa zimene Yesu anacita atatsala pang’ono kuphedwa. Kucita zimenezo kungatithandize kukonzekeletsa mtima wathu kaamba ka Mgonelo wa Ambuye.b Mlongo wina analemba kuti: “Timayembekezela mwacidwi nthaŵi ya Cikumbutso. Caka ciliconse Cikumbutso cimakhala capadela kwambili kwa ife. Ndimakumbukila nditaima m’nyumba yamalilo . . . ndikuyang’ana mtembo wa atate anga okondedwa ndipo ndinayamba kuyamikila dipo ndi mtima wonse. . . . Ndinali kudziŵa malemba onse okhudza dipo ndiponso mmene ndingafotokozele malembawo. Koma pamene ndinakhudzidwa kwambili ndi imfa m’pamene mtima wanga unasangalaladi ndi zimene zidzacitika cifukwa ca dipo lamtengo wapatali limenelo.” Ndithudi, pamene tikonzekela Cikumbutso, tingacite bwino kuganizila mmene nsembe ya Yesu inatimasulila ku ucimo ndi imfa.

Wa Mboni za Yehova asinkhasinkha za umoyo wa Yesu kutatsala mlungu umodzi kuti aphedwe. Iye akugwilitsila nchito za kumapeto m’Baibulo la Cingelezi

Gwilitsilani nchito zofalitsa zathu kuti mukonzekeletse mtima wanu kaamba ka Cikumbutso (Onani ndime 9)

10. Kodi kukonzekela Cikumbutso kungakhudze bwanji utumiki wathu?

10 Kukonzekela Cikumbutso kungaphatikizepo kuganizila njila zina zoonjezela utumiki wathu. Mwina tingaciteko upainiya wothandiza pa nyengo ya Cikumbutso. Pamene tiitanila ophunzila Baibulo ndi anthu ena ku mwambo wa Mgonelo wa Ambuye, timasangalala kuuza ena za Mulungu, Mwana wake, ndiponso za madalitso amene Yehova wasungila anthu amene amam’tamanda ndi kucita zinthu zomukondweletsa.—Sal. 148:12, 13.

11. N’cifukwa ciani Akristu ena a ku Korinto anali kudya zizindikilo za pa Cikumbutso mosayenelela?

11 Pamene tikukonzekela Mgonelo wa Ambuye, tiyenela kuganizila zimene mtumwi Paulo analembela mpingo wacikristu ku Korinto. (Ŵelengani 1 Akorinto 11:27-34.) Paulo anakamba kuti aliyense wakudya mkate ndi kumwa za mkapu mosayenelela, “adzakhala ndi mlandu wokhudza thupi ndi magazi a Ambuye,” Yesu Kristu. Conco, Mkristu wodzozedwa ayenela ‘kudzifufuza’ asanadye zizindikilo zimenezo. Ngati sanadzifufuze, iye ‘angadye ndi kumwa cilango cake.’ Cifukwa ca khalidwe lao loipa, Akristu ambili a ku Korinto anali ‘ofooka ndi odwaladwala, ndipo angapo anagona mu imfa [ya kuuzimu].’ Mwacionekele, ena anali kudya ndi kumwa kwambili  asanapite ku mwambo wa Cikumbutso kapena panthawi ya mwambowo cakuti anali kulephela kukhala maso mwamaganizo ndi mwa kuuzimu. Cifukwa cakuti anali kudya zizindikilo zimenezo mosayenelela Mulungu sanawayanje.

12. (a) Kodi Paulo anayelekezela Cikumbutso ndi ciani? Nanga anapeleka cenjezo lotani kwa anthu amene amadya zizindikilo? (b) N’ciani cimene munthu amene amadya zizindikilo ayenela kucita akacimwa?

12 Paulo anayelekezela Cikumbutso ndi cakudya cimene timadya ndi ena, ndipo anacenjeza anthu amene amadya zizindikilozo kuti: “Sizingatheke kuti muzimwa za m’kapu ya Yehova komanso za m’kapu ya ziwanda. Sizingatheke kuti muzidya patebulo la Yehova komanso patebulo la ziwanda.” (1 Akor. 10:16-21) Ngati munthu amene amadya zizindikilo pa mwambo wa Mgonelo wa Ambuye wacita chimo lalikulu, ayenela kupempha akulu kuti am’thandize mwa kuuzimu. (Ŵelengani Yakobo 5:14-16.) Wodzozedwayo akaonetsa ‘zipatso zosonyeza kuti walapa,’ sangaonetse kuti akunyoza nsembe ya Yesu akadya zizindikilo za pa Cikumbutso.—Luka 3:8.

13. N’cifukwa ciani kuganizila za ciyembekezo cathu mwapemphelo n’kopindulitsa?

13 Tikamakonzekela Cikumbutso, tidzapindula kwambili kuganizila mwapemphelo za ciyembekezo cathu copatsidwa ndi Mulungu. Mtumiki wodzipeleka wa Yehova komanso wotsatila Mwana wake mokhulupilika, ayenela kulemekeza nsembe ya Yesu. Angacite zimenezi mwa kupewa kudya zizindikilo za pa Cikumbutso ngati mumtima mwake sakutsimikiza kuti ndi Mkritsu wodzozedwa. Motelo, kodi munthu angadziŵe bwanji kuti ayenela kudya zizindikilo kapena ai?

NDANI AYENELA KUDYA?

14. Kodi pangano latsopano limakhudza bwanji kudya zizindikilo za pa Cikumbutso?

14 Anthu amene amadya zizindikilo za pa Cikumbutso amatsimikiza ndi mtima wonse kuti ali m’pangano latsopano. Ponena za vinyo, Yesu anakamba kuti: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga.” (1 Akor. 11:25) Kupyolela mwa mneneli Yeremiya, Mulungu anakambilatu kuti adzacita pangano latsopano losiyana ndi pangano la Cilamulo limene anacita ndi Aisiraeli. (Ŵelengani Yeremiya 31:31-34.) Mulungu anacita pangano ndi Aisiraeli a kuuzimu. (Agal. 6:15, 16) Nsembe ya Yesu ndi imene inatheketsa zimenezi. (Luka 22:20) Yesu ndiye Mkhalapakati wa pangano limeneli, ndipo odzozedwa okhulupilika a m’pangano limeneli amapatsidwa coloŵa ca kumwamba.—Aheb. 8:6; 9:15.

15. Ndani ali m’pangano la Ufumu? Nanga adzakhala ndi mwai wotani akapitilizabe kukhala okhulupilika?

15 Anthu amene amadya zizindikilo za pa Cikumbutso amadziŵa kuti ali m’pangano la Ufumu. (Ŵelengani Luka 12:32.) Amene anali otsatila a Yesu odzozedwa ndiponso amene anakhalabe ndi iye m’masautso ake, adzalamulila pamodzi naye kumwamba. (Afil. 3:10) Odzozedwa okhulupilika adzalamulila ndi Kristu kwamuyaya monga mafumu kumwamba, cifukwa cakuti ali m’pangano la Ufumu. (Chiv. 22:5) Anthu amenewa ndi amene amadya zizindikilo pa mwambo wa Mgonelo wa Ambuye.

16. Fotokozani mwacidule zimene lemba la Aroma 8:15-17 limatanthauza.

16 Amene ayenela kudya zizindikilo za pa Cikumbutso ndi okhawo amene mzimu wawacitila umboni kuti ndi ana a Mulungu. (Ŵelengani Aroma 8:15-17.) Onani kuti Paulo anagwilitsila nchito liu la Ciaramu lakuti “Abba” limene limatanthauza “Bambo anga.” Mwana angagwilitsile nchito liu limeneli poitana atate wake mwacikondi ndi mwaulemu. Conco, anthu amene alandila ‘mzimu wakuti akhale ana,’ amachedwa ana a Mulungu a kuuzimu. Mzimu wa Mulungu umacitila umboni ndi mzimu wao kuti ndi ana odzozedwa a Yehova. Sikuti anthu amenewa angotopa ndi moyo wa padziko lapansi. Koma io akudziŵa kuti adzakhala olamulila anzake a Yesu mu Ufumu wakumwamba ngati akhalabe okhulupilika mpaka imfa. Masiku ano, pali otsalila ocepa cabe a 144,000 omwe ndi otsatila Kristu amene ndi ‘odzozedwa ndi woyelayo,’ Yehova. (1 Yoh. 2:20; Chiv. 14:1) Ndipo mzimu wa Mulungu umawacititsa kufuula kuti, “Abba, Atate!” Ndithudi, io ali paubale wamtengo wapatali ndi Mulungu.

MUZIONA CIYEMBEKEZO CANU KUKHALA CAMTENGO WAPATALI

17. Ndi ciyembekezo cotani cimene odzozedwa ali naco? Nanga ciyembekezo cao amaciona bwanji?

17 Ngati ndinu Mkristu wodzozedwa, ciyembekezo canu ca kumwamba ndi nkhani imene muyenela kuipemphelela nthawi zonse. Baibulo likamanena za “kulonjezedwa ukwati” ndi Mkwati wakumwamba, amene ndi Yesu Kristu, mumadziŵa kuti likamba za inu, ndipo mumayembekezela mwacidwi kudzakhala “mkwatibwi” wa Kristu. (2 Akor. 11:2; Yoh. 3:27-29; Chiv. 21:2, 9-14) Mulungu akamakamba kuti amakonda ana ake a kuuzimu m’Baibulo, mumtima mwanu mumati, “Akukamba za ine.” Ndiponso pamene Yehova apeleka malangizo kwa ana ake odzozedwa kupyolela m’Mau ake, mzimu woyela umakulimbikitsani kutsatila malangizowo, ndipo mumtima mwanu mumati, “Malangizo amenewa agwila nchito kwa ine.” Motelo mzimu wa Mulungu ndi mzimu wanu zimacitila umboni kuti muli ndi ciyembekezo cakumwamba.

18. Kodi a “nkhosa zina” ali ndi ciyembekezo cotani? Nanga mumamva bwanji ponena za ciyembekezo cimeneci?

18 Komabe, ngati ndinu a “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” Mulungu wakupatsani ciyembekezo ca padziko lapansi. (Chiv. 7:9; Yoh. 10:16) Mukufuna kudzakhala ndi moyo kwamuyaya m’Paladaiso, ndipo mumakhala ndi cimwemwe mukaganizila zimene Baibulo limanena ponena za mmene umoyo udzakhalila padziko lapansi. Mukuyembekezela kudzasangalala ndi mtendele woculuka pamodzi ndi banja lanu ndi anthu ena olungama. Ndipo muyembekezela mwacidwi pamene sikudzakhalanso njala, umphawi, kuvutika, matenda, ndi imfa. (Sal. 37:10, 11, 29; 67:6; 72:7, 16; Yes. 33:24) Mukulakalaka kudzaonana ndi anthu amene adzaukitsidwa ndi kuyembekezela kukhala ndi moyo kwamuyaya. (Yoh. 5:28, 29) Mukaganizila ciyembekezo cokhala ndi moyo padziko lapansi mumayamikila kwambili Yehova. Ngakhale kuti simumadya zizindikilo za pa Cikumbutso, mumapezekapo n’colinga coonetsa kuti mumayamikila nsembe ya dipo ya Yesu Kristu.

KODI MUDZAPEZEKAPO?

19, 20. (a) Kodi ciyembekezo canu cingakwanilitsidwe bwanji? (b) N’cifukwa ciani mudzapezeka pa Mgonelo wa Ambuye?

19 Kaya ciyembekezo canu ndi cakumwamba kapena ndi ca padziko lapansi, cidzakwanilitsidwa kokha ngati mumakhulupilila Yehova Mulungu, Yesu Kristu, ndi dipo. Kupezeka pa Cikumbutso kudzakuthandizani kusinkhasinkha pa ciyembekezo canu ndi kuona kuti imfa ya Yesu ndi yofunika kwambili. Conco, khalani ndi colinga cokhala mmodzi wa anthu mamiliyoni ambili amene adzapezeka pa mwambo wa Mgonelo wa Ambuye, umene udzacitika pa Cisanu April 3, 2015 dzuŵa litaloŵa. Mwambo umenewu udzacitikila m’Nyumba za Ufumu ndiponso malo ena padziko lonse.

20 Kupezeka pa Cikumbutso kudzakuthandizani kuyamikila kwambili nsembe ya dipo ya Yesu. Ndipo kumvetsela mwachelu nkhani ya Cikumbutso kudzakuthandizani kukonda anansi anu ndi kuwauzako zimene mwaphunzila ponena za cikondi ca Yehova ndi colinga cake ponena za anthu. (Mat. 22:34-40) Motelo, mudzapezekepo pa Mgonelo wa Ambuye.

a Aheberi anali kuona kuti tsiku limayamba dzuŵa likaloŵa ndi kutha tsiku lotsatila dzuŵa likaloŵa.

b Onani Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu, Cigawo 16.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani