LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 5/15 masa. 19-23
  • ‘Anaona’ Malonjezo a Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • ‘Anaona’ Malonjezo a Mulungu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ANALIMBIKITSIDWA ‘ATAONA’ MALONJEZO A MULUNGU
  • ‘ANAONA’ KUKWANILITSIDWA KWA MALONJEZO
  • ANAYANG’ANITSITSA PAMPHOTO
  • MUZIGANIZILA ZA MALONJEZO A UFUMU
  • TIZIKAMBILANA ZA CIYEMBEKEZO CATHU
  • Tsanzilani Cikhulupililo ca Mose
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Khalani na Cikhulupililo m’Malonjezo a Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Kodi Mukuyembekezela “Mzinda Wokhala Ndi Maziko Eni-eni”?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 5/15 masa. 19-23
Diso la munthu limene likuyang’ana moyelekezela mmene paladaiso adzakhalila

‘Anaona’ Malonjezo a Mulungu

“Sanaone kukwanilitsidwa kwa malonjezowo. Koma anawaona ali patali.”—AHEB. 11:13.

KODI MUNGAFOTOKOZE BWANJI?

  • Kodi Mulungu anatipatsa mphatso yotani imene imatithandiza kukhala ndi cikhulupililo?

  • Timadziŵa bwanji kuti amuna ndi akazi okhulupilika ochulidwa m’Baibulo anali kuganizila za mphoto yao?

  • Timapindula bwanji ngati tikambilana za ciyembekezo cathu?

1. Tingapindule bwanji ndi mphamvu yokwanitsa kuganizila zinthu zimene sitinazionepo? (Onani cithunzi pamwambapa.)

MPHAMVU imene tili nayo yokwanitsa kuganizila zinthu zimene sitinazionepo ndi mphatso yocokela kwa Mulungu. Mphamvuyi imatithandiza kupanga zosankha mwanzelu ndi kuyembekezela mwacidwi zinthu zabwino. Yehova amadziŵa zimene zidzacitika mtsogolo, ndipo amatiuzilatu zimenezo kudzela m’Malemba. Timatha kuyelekezela m’maganizo mwathu zimene zidzacitika mtsogolo. Komanso mphamvu yokwanitsa kuganizila zinthu zimene sitinazionepo imatithandiza kukhala ndi cikhulupililo.—2 Akor. 4:18.

2, 3. (a) Kodi kuganizila zinthu zimene sitinazione kungatithandize bwanji? (b) Tikambilana mafunso ati m’nkhani ino?

2 Nthawi zina, zinthu zimene timaganizila zimakhala zakuti sizingacitike. Mwacitsanzo, mwana angadziyelekezele kuti wakwela pa gulugufe. Zimenezi sizingacitike. Koma pamene Hana anali kuganizila mmene zidzakhalila akadzapeleka mwana wake Samueli ku Cihema, sanali kuganizila zinthu zosatheka. Iye anali atatsimikiza mtima kucita zimenezo, ndipo kuganizila zimenezo kunamulimbikitsa kukwanilitsa colinga cake. (1 Sam. 1:22) Tikamaganizila zimene Mulungu walonjeza, ndiye kuti tikuganizila zinthu zimene zidzacitika ndithu.—2 Pet. 1:19-21.

3 Anthu okhulupilika ochulidwa m’Baibulo anali kuganizila zinthu zimene Mulungu anawalonjeza. Kodi io anapindula bwanji cifukwa coganizila madalitso amtsogolo? Nanga tingapindule bwanji tikamaganizila zinthu zosangalatsa zimene Mulungu walonjeza anthu omvela?

ANALIMBIKITSIDWA ‘ATAONA’ MALONJEZO A MULUNGU

4. Kodi zimene Abele anali kuganiza ponena za mtsogolo zinali zozikidwa pa ciani?

4 Kodi munthu wokhulupilika woyamba, Abele, ‘anaona’ malonjezo a Yehova? Abele ayenela kuti sanali kudziŵa mmene mau amene Mulungu anauza njoka adzakwanilitsidwila. Mulungu anati: “Ndidzaika cidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake. Mbeu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza cidendene.” (Gen. 3:14, 15) Komabe, n’zoonekelatu kuti Abele anali kuganizila kwambili za lonjezolo ndipo anadziŵa kuti winawake ‘adzavulazidwa cidendene’ n’colinga cakuti anthu adzakhalenso angwilo ngati mmene Adamu ndi Hava analili asanacimwe. Sitidziŵa zonse zimene Abele anali kuganiza ponena za mtsogolo, koma tidziŵa kuti iye anali ndi cikhulupililo cozikidwa pa lonjezo la Mulungu. Ndiye cifukwa cake Yehova analandila nsembe yake.—Ŵelengani Genesis 4:3-5; Aheberi 11:4.

5. Kodi kuganizila zamtsogolo kunamulimbikitsa bwanji Enoki?

5 Enoki anali ndi cikhulupililo ngakhale kuti anali kukhala ndi anthu osaopa Mulungu amene anali kukamba zinthu zonyoza Mulungu. Mouzilidwa, Enoki ananenelatu kuti Yehova adzabwela “ndi miyandamiyanda ya oyela ake, kudzapeleka ciweluzo kwa onse, ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu cifukwa ca nchito zao zonyoza Mulungu zimene anazicita mosaopa Mulungu, komanso cifukwa ca zinthu zonse zonyoza koopsa zimene ocimwa osaopa Mulungu anamunenela.” (Yuda 14, 15) Pokhala munthu wacikhulupililo, Enoki anali kuyembekezela kuti mtsogolo padziko padzakhala anthu oopa Mulungu okhaokha.—Ŵelengani Aheberi 11:5, 6.

6. N’ciani cimene Nowa anapitiliza kuyembekezela pambuyo pa Cigumula?

6 Nowa anapulumuka Cigumula cifukwa ca cikhulupililo cake. (Aheb. 11:7) Cigumula citatha, cikhulupililo cake cinamulimbikitsa kupeleka nsembe za nyama. (Gen. 8:20) Mofanana ndi Abele, mosakaikila iye anali kukhulupilila kuti anthu adzamasulidwa ku ukapolo wa ucimo ndi imfa. Nthawi inayake pambuyo pa Cigumula, Nimurodi anayamba kucita zinthu motsutsana ndi Yehova, koma Nowa anapitilizabe kukhala ndi cikhulupililo ndiponso ciyembekezo. (Gen. 10:8-12) Iye ayenela kuti anali kulimbikitsidwa akaganizila nthawi pamene anthu onse adzamasulidwa ku ucimo, imfa ndiponso ulamulilo wopondeleza. Ifenso timayembekezela nthawi yosangalatsa imeneyo, ndipo ili pafupi kwambili.—Aroma 6:23.

‘ANAONA’ KUKWANILITSIDWA KWA MALONJEZO

7. Ndi zinthu zotani zimene Abulahamu, Isaki, ndi Yakobo ‘anaona’?

7 Abulahamu, Isaki, ndi Yakobo anali kuyembekezela tsogolo labwino cifukwa cakuti Mulungu anawalonjeza kuti kudzela mwa mbadwa zao, mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso. (Gen. 22:18; 26:4; 28:14) Mbadwa zao zinali kudzaculuka ndi kudzakhala m’dziko limene Mulungu analonjeza. (Gen. 15:5-7) Mwa cikhulupililo, anthu oopa Mulungu amenewo ‘anaona’ mbadwa zao zikukhala m’dzikolo. Ndipo kucokela pamene anthu anacimwa, Yehova wakhala akutsimikizila atumiki ake okhulupilika kuti adzalandila madalitso amene Adamu anataya.

8. N’ciani cinathandiza Abulahamu kukhala ndi cikhulupililo camphamvu?

8 N’zoonekelatu kuti kuganizila malonjezo a Mulungu n’kumene kunathandiza Abulahamu kukhala ndi cikhulupililo camphamvu. Malemba amanena kuti ngakhale kuti Abulahamu ndi atumiki ena a Mulungu “sanaone kukwanilitsidwa kwa malonjezowo” m’nthawi yao, “anawaona ali patali ndi kuwalandila.” (Ŵelengani Aheberi 11:8-13.) Abulahamu anali kukhulupilila kwambili malonjezo a Mulungu cakuti zinali ngati akuwaona akukwanilitsidwa.

9. Kodi Abulahamu anapindula bwanji cifukwa cokhulupilila Mulungu?

9 Kukhulupilila malonjezo a Mulungu kunalimbikitsa Abulahamu kucita cifunilo ca Mulungu. Cifukwa ca cikhulupililo, iye anacoka mumzinda wa Uri, ndipo anakana kukhazikika mumzinda uliwonse wa ku Kanani. Mofanana ndi mzinda wa Uri, mizindayo inalibe maziko olimba cifukwa cakuti inali kulamulidwa ndi anthu osaopa Mulungu. (Yos. 24:2) Kwa moyo wake wonse, Abulahamu “anali kuyembekezela mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.” (Aheb. 11:10) Abulahamu anali kuyembekezela nthawi imene adzakhala ndi malo okhazikika m’dziko lolamulidwa ndi Yehova. Abele, Enoki, Nowa, Abulahamu, ndi anthu ena ngati amenewa anali kukhulupilila kuti akufa adzauka. Komanso anali kuyembekezela kudzakhala ndi moyo mu “mzinda wokhala ndi maziko enieni,” umene ukutanthauza dziko lapansi lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu. Kuganizila madalitso amenewo kunalimbitsa cikhulupililo cao mwa Yehova.—Ŵelengani Aheberi 11:15, 16.

10. Kodi kuganizila zamtsogolo kunamuthandiza bwanji Sara?

10 Ganizilani za Sara, mkazi wa Abulahamu. Pamene anali ndi zaka 90 koma wopanda mwana, kuganizila zinthu zabwino zamtsogolo kunamuthandiza kukhala ndi cikhulupililo. Zinali ngati kuti iye anali kuona mbadwa zake zikusangalala ndi madalitso amene Yehova analonjeza. (Aheb. 11:11, 12) N’ciani cinamuthandiza kukhala ndi ciyembekezo cotelo? Yehova anali atauza mwamuna wake kuti: “Ndidzamudalitsa ndipo iwe ndidzakupatsa mwana wamwamuna wocokela mwa iye. Ndidzamudalitsa ndipo adzakhala mayi wa mitundu yambili ya anthu ndi wa mafumu a mitundu yambili ya anthu.” (Gen. 17:16) Sara atabeleka Isaki, cikhulupililo cake cakuti Mulungu adzakwanilitsa zonse zimene analonjeza Abulahamu cinalimba. Ifenso tili ndi mphatso yamtengo wapatali yokwanitsa kuganizila malonjezo a Mulungu omwe sangalephele.

ANAYANG’ANITSITSA PAMPHOTO

11, 12. N’ciani cinacititsa kuti Mose ayambe kukonda Yehova?

11 Mose nayenso anali kukhulupilila Yehova. Komanso anali kukonda kwambili Mulungu. Pamene Mose anali wacinyamata anali kukhala m’banja lacifumu la Aiguputo. Panthawiyo, cinali cosavuta kuti Mose ayambe kulakalaka cuma ndi ulamulilo. Koma makolo ake anamuphunzitsa za Yehova ndi colinga cake cakuti adzaombola Aheberi ku ukapolo ndi kuwapatsa Dziko Lolonjezedwa. (Gen. 13:14, 15; Eks. 2:5-10) N’zoonekelatu kuti Mose anali kuganizila kwambili za madalitso amene anthu a Mulungu adzalandile. Kucita zimenezi kunamuthandiza kuti ayambe kukonda Yehova m’malo molakalaka ulamulilo.

12 Malemba amati: “Mwa cikhulupililo, Mose atakula anakana kuchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao, ndipo anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mocita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zaucimo. Iye anacita zimenezi cifukwa anaona kutonzedwa kwake monga Wodzozedwa kukhala cuma coculuka kuposa cuma ca Iguputo, pakuti anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandile.”—Aheb. 11:24-26.

13. Kodi Mose anapindula bwanji cifukwa coganizila zimene Mulungu analonjeza?

13 Pamene Mose anali kuganizila kwambili za malonjezo a Yehova kwa Aisiraeli, cikhulupililo cake cinalimba ndipo cikondi cake pa Mulungu cinakula. Mofanana ndi atumiki ena a Mulungu, nayenso anali kuganizila nthawi pamene Yehova adzamasula anthu ku imfa. (Yobu 14:14, 15; Aheb. 11:17-19) Zimenezi zinalimbitsa Mose kukonda Mulungu amene anali kucitila cifundo Aheberi ndi anthu onse. Cikhulupililo ndi cikondi n’zimene zinalimbikitsa Mose kutumikila Mulungu mokhulupilika. (Deut. 6:4, 5) Ngakhale pamene Farao anaopseza Mose kuti adzamupha, iye sanacite mantha cifukwa anali ndi cikhulupililo, anali kukonda Mulungu, ndiponso anali kuganizila zinthu zabwino zamtsogolo.—Eks. 10:28, 29.

MUZIGANIZILA ZA MALONJEZO A UFUMU

14. Ndi maganizo olakwika ati amene anthu ambili ali nao?

14 Anthu ambili masiku ano amayembekezela zinthu zimene sizingacitike. Mwacitsanzo, anthu ena osauka amaganizila kuti adzalemela kwambili ndi kukhala opanda mavuto. Koma umoyo masiku ano ndi ‘wodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.’ (Sal. 90:10) Ena amaganiza kuti maboma a anthu adzathetsa mavuto. Koma Baibulo limaonetsa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetsa mavuto onse a anthu. (Dan. 2:44) Anthu ambili amaganiza kuti Mulungu sadzaononga dongosolo loipali, koma Baibulo limanena zosiyana kwambili ndi zimenezi. (Zef. 1:18; 1 Yoh. 2:15-17) Maganizo a anthu onyalanyaza colinga ca Yehova amenewa ndi maloto cabe.

Mwamuna wacikulile wagwila mpeni womangila ndipo akuganizila za ciyembekezo ca mtsogolo

Kodi mumayelekezela kuti muli m’dziko latsopano? (Onani ndime 15)

15. (a) Kodi Akristu amapindula bwanji akamaganizila za ciyembekezo cao? (b) Mukufunitsitsa kudzacita ciani pamene Mulungu adzakwanilitsa malonjezo ake?

15 Mosiyana ndi zimenezi, ife Akristu timalimbikitsidwa tikamaganizila za ciyembekezo cathu, kaya ndi ca kumwamba kapena ca padziko lapansi. Kodi mungayelekezele kuti mukusangalala ndi madalitso amene Mulungu walonjeza? Mwacionekele, mumasangalala kwambili mukamaganizila zimene mudzacita pamene Mulungu adzakwanilitsa colinga cake. Mwina mumayelekezela kuti muli ndi moyo wosatha padziko lapansi. Ganizilani mmene mudzasangalalila pogwila nchito yokonza dzikoli kukhala paradaiso pamodzi ndi anthu ena, ndipo anthu onse akukonda Yehova monga inuyo. Muli ndi thanzi labwino, mphamvu, ndiponso mulibe nkhawa. Mukusangalala pogwila nchitoyo cifukwa cakuti oyang’anila nchitoyo ndi acikondi. Komanso ndinu okondwa kugwilitsila nchito luso lanu cifukwa cakuti ciliconse cimene mukucita cikupindulitsa ena ndi kulemekeza Mulungu. Mwacitsanzo, mukuthandiza oukitsidwa kudziŵa Yehova. (Yoh. 17:3; Mac. 24:15) Zimenezi si maloto ai. Koma ndi zozikidwa pa Malemba, omwe ndi coonadi.—Yes. 11:9; 25:8; 33:24; 35:5-7; 65:22.

TIZIKAMBILANA ZA CIYEMBEKEZO CATHU

16, 17. Timapindula bwanji tikamakambilana za ciyembekezo cathu?

16 Tikamauza Akristu anzathu zimene timafuna kudzacita pamene Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake, ciyembekezo cathu cimakhala camphamvu kwambili. Ngakhale kuti sitidziŵa mmene zinthu zidzakhalila pa umoyo wathu m’dziko latsopano, tiyenela kuuzako ena zimene timafuna kudzacita panthawiyo. Tikamatelo, timalimbikitsana ndi kusonyeza cikhulupililo cathu m’malonjezo a Mulungu. Pamene mtumwi Paulo anapita kukacezela abale ake ku Roma, io anayamikila cifukwa ‘analimbikitsana.’ Nafenso timafuna cilimbikitso m’nthawi yovuta ino.—Aroma 1:11, 12.

Wacinyamata ali m’paladaiso ndipo akumanga nyumba pogwilitsa nchito mpeni womangila

17 Kuganizila zamtsogolo kungatithandizenso kuti tisamakhale ndi nkhawa kwambili ndi mavuto amene tikukumana nao. Mwacitsanzo, mtumwi Petulo ayenela kuti anali ndi nkhawa pamene anauza Yesu kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatilani, kodi tidzapeza ciani?” Pofuna kuthandiza Petulo ndi atumwi enawo kuganizila zamtsogolo, Yesu anayankha kuti: “Ndithu ndikukuuzani, pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pampando wacifumu waulemelelo, inu amene mwatsatila ine mudzakhalanso m’mipando yacifumu 12, kuweluza mafuko 12 a Isiraeli. Aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, abambo, amayi, ana kapena minda cifukwa ca dzina langa adzalandila zoculuka kwambili kuposa zimenezi, ndipo adzapeza moyo wosatha.” (Mat. 19:27-29) Motelo, Petulo ndi atumwi enawo anayamba kuganizila udindo umene adzakhala nao m’boma limene lidzalamulila dziko lonse ndi kubweletsa madalitso osaneneka kwa anthu omvela.

18. Timapindula bwanji tikamaganizila mmene malonjezo a Mulungu adzakwanilitsidwila?

18 Atumiki a Yehova padziko lapansi akhala akupindula akamaganizila mmene malonjezo a Mulungu adzakwanilitsidwila. Zimene Abele anali kudziŵa zokhudza colinga ca Mulungu zinamuthandiza kukhala ndi ciyembekezo ca tsogolo labwino ndiponso cikhulupililo. Abulahamu anali ndi cikhulupililo colimba cifukwa anali kuganizila za kukwanilitsidwa kwa ulosi wa Mulungu wokhudza “mbeu” yolonjezedwa. (Gen. 3:15) Komanso Mose “anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandile,” ndipo zimenezi zinamuthandiza kusonyeza cikhulupililo ndi kukulitsa cikondi cake pa Yehova. (Aheb. 11:26) Ifenso tikamaganizila mmene malonjezo a Yehova adzakwanilitsidwila, cikhulupililo ndi cikondi cathu pa Mulungu zimalimba. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene tingagwilitsile nchito bwino mphatso yathu yocokela kwa Mulungu yotha kuganizila zamtsogolo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani