LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w16 December masa. 8-12
  • Tinamasulidwa mwa Cisomo ca Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tinamasulidwa mwa Cisomo ca Mulungu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • TINAKHULULUKIDWA MWA CISOMO CAKE
  • KUYAMIKILA CISOMO CA MULUNGU
  • MUKHOZA KUPAMBANA NKHONDOYO
  • Tiziyamikila Kukoma Mtima Kwakukulu Kumene Tinalandila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Lalikilani Uthenga Wabwino Wokamba za Kukoma Mtima
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Lolani Kuti “Lamulo la Kukoma Mtima Kosatha” Lizikutsogolelani
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
w16 December masa. 8-12
Mtumwi Paulo alalikila ku Roma

Tinamasulidwa mwa Cisomo ca Mulungu

‘Ucimo usakhale mbuye kwa inu, cifukwa muli . . . pansi pa kukoma mtima kwakukulu.’—AROMA 6:14.

NYIMBO: 46, 127

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’cifukwa ciani dipo limene Mulungu anapeleka limaonetsa cisomo cake?

  • Kodi tingakhale bwanji “ngati akufa ku ucimo”?

  • N’cifukwa ciani kuyamikila cisomo ca Mulungu kumatilimbikitsa kupewa macimo alionse?

1, 2. N’cifukwa ciani lemba la Aroma 5:12 n’lofunika kwa Mboni za Yehova?

YELEKEZANI kuti mufuna kundandalika malemba amene Mboni za Yehova zimakonda kuwaseŵenzetsa. Kodi lemba la Aroma 5:12 mungaliike cakumwamba kwa mndandanda wanu? Kodi mau ake mwaaŵelengapo kangati, akuti: “Monga mmene ucimo unaloŵela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa”?

2 Lembali limapezeka kangapo konse m’buku yakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse. Mwacionekele, pamene muphunzila Baibo ndi ana anu kapena anthu ena, mumaŵelenga Aroma 5:12 pokambilana za colinga ca Mulungu cokhudza dziko lapansi, dipo, na mkhalidwe wa akufa, m’nkhani 3, 5, na 6. Koma kodi mumaganizilapo za mmene lemba la Aroma 5:12 limakhudzila kaimidwe kanu pamaso pa Yehova, zocita zanu, ndi tsogolo lanu?

3. Tifunika kukumbukila ciani pankhani yaucimo?

3 Tonse tifunika kukumbukila kuti ndife ocimwa. Timalakwa tsiku lililonse. Komabe, timatsimikiza kuti Mulungu amadziŵa kuti ndife fumbi, ndi kuti ni wofunitsitsa kuticitila cifundo. (Sal. 103:13, 14) Yesu m’pemphelo lake lacitsanzo anapempha Mulungu kuti: “Mutikhululukile macimo athu.” (Luka 11:2-4) Conco, palibe cifukwa congokhalila kuganizila macimo amene Mulungu anatikhululukila kale. Koma tingapindule ngati timaganizila zimene iye anacita kuti atikhululukile.

TINAKHULULUKIDWA MWA CISOMO CAKE

4, 5. (a) N’ciani cimatithandiza kumvetsa bwino lemba la Aroma 5:12? (b) Kodi “kukoma mtima kwakukulu” kochulidwa pa Aroma 3:24 n’ciani?

4 M’macaputa ofotokoza mau a mtumwi Paulo a pa Aroma 5:12, monga m’caputa 6, timapezamo mfundo zolimbikitsa. Macaputa amenewo amatithandiza kudziŵa mmene Yehova angatikhululukile. M’caputa 3 timaŵelenga kuti: “Onse ndi ocimwa ndipo . . .  kuyesedwa olungama cifukwa ca kukoma mtima kwake kwakukulu kumene wakusonyeza, powamasula ndi dipo lolipilidwa ndi Khiristu Yesu, kuli ngati mphatso yaulele.” (Aroma 3:23, 24) Kodi Paulo anatanthauza ciani pamene anakamba kuti “kukoma mtima kwakukulu”? Malinga n’kunena kwa buku ina, iye anaseŵenzetsa liu la Cigiriki limene limatanthauza “kucitila wina zabwino mwa cisomo cako, mosayembekezela cobwezela ciliconse.” Ndiko kukoma mtima kosayang’ana nkhope.

5 Katswili wina, John Parkhurst, anati: “Pokamba za Mulungu kapena Khiristu, liulo [la Cigirikilo] nthawi zambili limatanthauza kukoma mtima kwa m’cisomo cawo kowombola na kupulumutsa anthu.” Conco, cimasulilo ca liulo cakuti “kukoma mtima kwakukulu,” mu Baibulo la Dziko Latsopano n’coyenelela. Koma kodi Mulungu anaonetsa bwanji cisomo cimeneci? Ndipo cimakhudza bwanji ciyembekezo canu na ubale wanu ndi iye? Tiyeni tione.

6. Kodi anthu angapindule bwanji na cisomo ca Mulungu?

6 Adamu ndiye “munthu mmodzi” amene kupitila mwa iye, ucimo na imfa ‘zinaloŵa m’dziko.’ Conco, “cifukwa ca ucimo wa munthu mmodziyo imfa inalamulila monga mfumu.” Paulo anawonjezela kuti “kukoma mtima kwakukulu koculuka [kwa Mulungu]” kunaonetsedwa “kudzela mwa munthu mmodziyu, Yesu Khiristu.” (Aroma 5:12, 15, 17) Cisomo cimeneci cinabweletsa madalitso ku mtundu wa anthu. “Kudzela mwa kumvela kwa munthu mmodziyu [Yesu], ambili adzakhala olungama.” Zoonadi, cisomo ca Mulungu cimatsogolela ku ‘moyo wosatha kupitila mwa Yesu Khiristu.’—Aroma 5:19, 21.

7. N’cifukwa ciani dipo imene Mulungu anapeleka imaonetsa cisomo cake? Nanga n’cifukwa ciani inali yosatiyenelela?

7 Yehova sakanakhala ndi mlandu akanapanda kutumiza Mwana wake pa dziko lapansi kuti adzapeleke dipo. Ndi iko komwe, anthu ocimwa sanali oyenelela dipo limene Mulungu na Yesu anapeleka kuti awakhululukile macimo. Conco, kukhululukidwa kwathu macimo na kupatsidwa ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya, cilidi cisomo cabe ca Mulungu. N’cifukwa cake tifunikiladi kuyamikila cisomo cimeneci monga mphatso yapadela m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku.

KUYAMIKILA CISOMO CA MULUNGU

8. Ni maganizo olakwika ati amene anthu ena angakhale nawo pa macimo awo?

8 Pokhala mbadwa za Adamu zopanda ungwilo, cibadwa cathu cimakhotelela pa kulakwitsa zinthu, kucita zoipa, na kucimwa. Ngakhale n’conco, kungakhale kulakwa kutenga cisomo ca Mulungu kukhala cifukwa cocitila zoipa. Mwacitsanzo, tingakhale na maganizo monga akuti: ‘Ngakhale nicimwile Mulungu, siniyenela kuda nkhawa kweni-kweni. Yehova adzanikhululukila.’ Ndi mmene Akhiristu ena anali kuganizila ngakhale panthawi imene atumwi ena anali moyo. (Ŵelengani Yuda 4.) N’zoona kuti ise sitingacite kukamba zimenezo. Koma maganizo olakwika amenewa angabyalidwe mumtima mwathu na kuyamba kukula.

9, 10. Kodi Paulo na anthu ena anamasulidwa bwanji ku ucimo ndi imfa?

9 Paulo anagogomeza kuti tifunika kupewelatu maganizo monga akuti: ‘Mulungu amamvetsetsa. Adzangoiŵalako zolakwa zanga.’ Cifukwa? Paulo analemba kuti Akhiristu ali “ngati akufa ku ucimo.” Ndiye cifukwa cake. (Ŵelengani Aroma 6:1, 2.) Popeza Akhiristuwo anali akali na moyo padziko lapansi, kodi anali “ngati akufa ku ucimo” m’lingalilo liti?

10 Mulungu, kupilitila mwa dipo, anakhululukila Paulo macimo ake ndi anthu ena a m’nthawi yake. Anawadzoza na mzimu woyela ndi kuwapatsa mwayi wokhala ana ake auzimu. Ndiyeno, anakhala na ciyembekezo ca kumwamba. Anafunikila kukhalabe okhulupilika kuti akapite kumwamba kukalamulila pamodzi na Khiristu. Koma pamene Paulo ananena kuti iwo anali “ngati akufa ku ucimo,” anali akali na moyo, ndipo anali kutumikilabe Mulungu padziko lapansi.” Iye anagwilitsila nchito citsanzo ca Yesu, amene anafa monga munthu, koma anaukitsidwa monga munthu wamzimu ndi kupita kumwamba. Yesu anagonjetsa imfa. N’cimodzi-modzi na Akhiristu odzozedwa. Iwo anali kudziona “ngati akufa ku ucimo koma amoyo kwa Mulungu mwa Khiristu Yesu.” (Aroma 6:9, 11) Umoyo wawo sunali monga mmene unalili kale. Sanalinso kugonjelanso ku zilako-lako zawo zaucimo. Anali atafa ku umoyo wawo wakale.

11. Kodi ise amene tidzakhala m’Paradaiso kwamuyaya tili “ngati akufa ku ucimo” m’lingalilo lanji?

11 Nanga bwanji ise Akhiristu masiku ano? Tisanakhale Akhiristu, tinali kucita macimo, ndipo mwina sitinali kudziŵa mmene Mulungu anali kukhumudwila na zocita zathu zoipa. Tinali monga “akapolo a zonyansa ndiponso akapolo a kusamvela malamulo.” (Aroma 6:19, 20) Ndiyeno tinaphunzila coonadi ca m’Baibo, tinasintha umoyo wathu, tinadzipeleka kwa Mulungu, na kubatizika. Kucokela panthawiyo, cakhala colinga cathu ‘kulabadila mocokela pansi pa mtima’ ziphunzitso ndi miyezo ya Mulungu. ‘Tinamasulidwa ku ucimo’ ndi ‘kukhala akapolo a cilungamo.’ (Aroma 6:17, 18) Conco, ifenso tili “ngati akufa ku ucimo.”

12. N’cosankha canji cimene aliyense wa ife afunika kupanga?

12 Tsopano ganizilani umoyo wanu malinga na mau a Paulo akuti: “Musalole kuti ucimo uzilamulilabe monga mfumu m’matupi anu okhoza kufawo kuti muzitsatila zilakolako zawo.” (Aroma 6:12) ‘Tingalole kuti ucimo uzilamulilabe’ ngati timangocita zinthu malinga ndi zilako-lako za thupi lathu locimwa. Popeza n’zotheka ‘kulola’ kapena kuletsa ucimo kutilamulila, funso n’lakuti, Kodi mtima wanga udzasankha citi maka-maka? Dzifunseni kuti: ‘Kodi nthawi zina nimalola thupi langa kapena maganizo anga kunitsogolela ku zinthu zosayenela? Kapena kodi ndine wakufa ku ucimo? Kodi nimakhala umoyo wocita cifunilo ca Mulungu mwa Khiristu Yesu?’ Kweni-kweni, zimadalila ngati timayamikiladi cisomo ca Mulungu cotikhululukila zocimwa zathu.

MUKHOZA KUPAMBANA NKHONDOYO

13. Ni umboni wanji umene umatipatsa cidalilo cakuti n’zotheka kufulatila macimo?

13 Cifukwa cokonda Mulungu ndi kum’tumikila, anthu a Yehova anafulatila nchito zawo zakale asanadziŵe Mulungu. Mwina kale ena anali kucita ‘zinthu zimene tsopano amacita nazo manyazi,’ zimenenso zikanawacititsa kuyenelela imfa. (Aroma 6:21) Koma lomba anasintha, mofanana ndi Akorinto amene Paulo anawalembela kalata. Ena anali opembedza mafano, acigololo, amuna ogonana ndi amuna anzawo, akuba, zidakwa, ndi ena aconco. Komabe, ‘anasambitsidwa kukhala oyela’ ndi ‘kupatulidwa.’ (1 Akor. 6:9-11) Ndi mmenenso Akhiristu a ku Roma nawonso anasinthila. Mouzilidwa, Paulo anawalembela kuti: “Musapeleke ziwalo zanu ku ucimo kuti zikhale zida zocitila zinthu zosalungama, koma dzipelekeni kwa Mulungu monga anthu amene auka kwa akufa. Ziwalo zanunso muzipeleke kwa Mulungu monga zida zocitila cilungamo.” (Aroma 6:13) Paulo anali wotsimikiza kuti anthuwo akhoza kukhalabe oyela mwauzimu, ndi kupitiliza kupindula na cisomo ca Mulungu.

14, 15. Tiyenela kudzifunsa mafunso ati pankhani ‘yomvela mocokela pansi pa mtima’?

14 N’cimodzi-modzinso masiku ano. N’kutheka kuti abale ndi alongo ena panthawi ina anali monga anthu a ku Korinto. Koma nawonso anasintha. Analeka macita-cita awo akale, ndipo ‘anasambitsidwa kukhala oyela.’ Nanga inu zinthu zili bwanji pamaso pa Mulungu? Popeza lomba tili na cisomo ca Mulungu ndipo timakhululukidwa macimo, kodi ndimwe ofunitsitsa kupewa ‘kupelekanso ziwalo zanu ku ucimo’? Kodi ‘mudzadzipeleka kwa Mulungu monga anthu amene wouka kwa akufa?’

15 Kuti ticite zimenezo, tifunika kupewelatu macimo akulu-akulu amene anthu ena a ku Korinto anali kucita. Zimenezi n’zofunika ngati tinalandiladi cisomo ca Mulungu, ndiponso ngati ‘ucimo suli mbuye kwa ife.’ Komanso, kodi ndife otsimikiza mtima kupewanso macimo amene anthu ena angawaone ngati ni aang’ono?—Aroma 6:14, 17.

16. Tidziŵa bwanji kuti kukhala Mkhiristu kumafuna zambili kuposa kuleka cabe kucita macimo aakulu?

16 Ganizilani za mtumwi Paulo. Iye sanali kucitako macimo aakulu ochulidwa pa 1 Akorinto 6:9-11. Ngakhale n’conco, anavomeleza kuti anali wocimwa. Analemba kuti: “Ndine wakuthupi, wogulitsidwa ku ucimo. Sindimvetsetsa kuti n’cifukwa ciani ndimacita zinthu motele. Cifukwa zimene ndimafuna kucita, sindizicita. Koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimacita.” (Aroma 7:14, 15) Izi zionetsa kuti panali zinthu zina zimene Paulo anaona kuti anali macimo zimene anali kulimbana nazo. (Ŵelengani Aroma 7:21-23.) Ifenso ticite cimodzimodzi poyesetsa kukhala ‘omvela mocokela pansi pa mtima.’

17. N’cifukwa ninji mumafuna kukhalabe munthu woona mtima?

17 Mwacitsanzo, ganizilani nkhani yokhala woona mtima. Mkhiristu aliyense afunika kukhala woona mtima. (Ŵelengani Miyambo 14:5; Aefeso 4:25.) Satana ndiye “tate wake wa bodza.” Ndipo Hananiya na mkazi wake Safira anafa cifukwa conama. Ise sitifuna kutengela anthu amenewa. Conco, timapewa kunama. (Yoh. 8:44; Mac. 5:1-11) Koma kuona mtima kumaloŵetsamo zambili. Kuyenela kuonetsanso kuti timayamikila kwambili cisomo ca Mulungu.

18, 19. N’cifukwa ciani kukhala woona mtima kumafuna kupewa cinyengo ciliconse?

18 Kunama ni kukamba cinthu cimene si coona. Koma Yehova amafuna kuti anthu ake asamangopewa kunama cabe. Iye anauza Aisiraeli akale kuti: “Mukhale oyela, cifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyela.” Ndiyeno, anafotokoza mmene tingakhalile oyela. Mulungu anati: “Musabe, musanamizane ndipo aliyense asacitile mnzake cinyengo.” (Lev. 19:2, 11) Komabe, munthu angamapewe mabodza apoyela, koma n’kumagwila ena m’maso, kumawapita pansi.

M’bale akamba na a bwana ake ndipo anzake amvetsela

Kodi tidzapewelatu kunama na cinyengo ciliconse? (Onani palagilafu 19)

19 Mwacitsanzo, munthu angalaile kunchito kuti mailo sadzabwela ku nchito, kapena kuti adzakomboka msanga, cifukwa akukaonana ndi dokota. Koma zoona n’zakuti akungokatenga cabe mankhwala kapena kukalipila ndalama cabe kwa dokota. Colinga cake ceni-ceni cingakhale kupita paulendo na banja lake kupikiniki. N’zoona kuti polaila anachulako zopita kucipatala, koma kodi tinganene kuti munthuyo anali woona mtima, kapena cinali cinyengo? Mwina mudziŵako njila zinanso zimene anthu ena amacitila zacinyengo. Ena amacita zimenezi kuti apewe cilango, kapena pofuna kudyela ena masuku pamutu. Ngakhale ngati angaone kuti bodza lake n’laling’ono, nanga bwanji za lamulo la Mulungu lakuti: “Musanamizane”? Ganizilaninso Aroma 6:19 imene imati: “Pelekaninso ziwalo zanu kuti zikhale akapolo a cilungamo kuti muzicita nchito za ciyelo.”

20, 21. Kodi kuyamikila cisomo ca Mulungu kuyenela kutithandiza kucita ciani?

20 Apa mfundo ni yakuti kuyamikila cisomo ca Mulungu kumafuna zambili kuposa kupewa cabe cigololo, kukolewa, kapena macimo ena amene anthu a ku Korinto anali kucita. Kulandila cisomo ca Mulungu sikutanthauza cabe kupewa zaciwelewele. Kumaphatikizaponso kupewelatu zosangulutsa zolaula zilizonse. Kupeleka ziwalo zathu mu ukapolo ku cilungamo sikutanthauza kungopewa cabe kukolewa, koma ngakhale kupewa kumwa moŵa motsala pang’ono kukolewa. Kulimbana ndi makhalidwe oipa amenewa kumafuna kulimbikila. Koma n’zotheka kupambana pankhondoyi.

21 Colinga cathu cizikhala kupewa macimo akulu-akulu, pamodzi na zolakwa zing’ono-zing’ono. N’zoona kuti sitingapeweletu kulakwa kulikonse. Koma tiyenela kuyesa-yesa mofanana ndi Paulo. Iye analimbikitsa abale ake kuti: “Musalole kuti ucimo uzilamulilabe monga mfumu m’matupi anu okhoza kufawo kuti muzitsatila zilakolako zawo.” (Aroma 6:12; 7:18-20) Ngati tilimbana na ucimo uliwonse, timaonetsa kuti timayamikiladi cisomo ca Mulungu mwa Khiristu.

22. Ni mphoto yanji imene anthu amene amayamikila cisomo ca Mulungu adzalandila?

22 Mwa cisomo ca Mulungu, macimo athu anakhululukidwa, ndipo angapitilizebe kukhululukidwa. Poonetsa kuyamikila, tiyeni tiziyesa-yesa kupewelatu macimo alionse amene anthu ena angawaone ngati ni aang’ono. Paulo anagogomeza mphoto imene tidzalandila pamene anati: “Tsopano cifukwa munamasulidwa ku ucimo ndipo munakhala akapolo a Mulungu, mukukhala ndi zipatso za ciyelo, ndipo pa mapeto pake mudzakhala ndi moyo wosatha.”—Aroma 6:22.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani