LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 6 masa. 6-7
  • Ni Mphatso Iti Yoposa Zonse?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ni Mphatso Iti Yoposa Zonse?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Nkhani Zofanana
  • Dipo la Yesu—Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Dipo Ni Mphatso Ya Mulungu Yopambana Zonse
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse N’cifukwa Ciani ni Yamtengo Wapatali?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Pitilizani Kuyamikila Dipo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 6 masa. 6-7
Mabanja ali m’dziko latsopano

Mphatso ya dipo yocokela kwa Mulungu, imene yacititsa kuti tidzakhale na moyo wosatha, ndiye mphatso yopambana zonse

NKHANI YA PACIKUTO | NI MPHATSO ITI YOPOSA ZONSE?

Ni Mphatso Iti Yoposa Zonse?

“Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo imacokela kumwamba, pakuti imatsika kucokela kwa Atate wa zounikila zonse zakuthambo.” (Yakobo 1:17) N’zacionekele kuti lembali likamba za kuolowa manja kwa Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu. Komabe, pa mphatso zonse zimene Mulungu watipatsa pali mphatso imodzi yoposa zonse. Ni iti? Mau odziŵika bwino a Yesu apa Yohane 3:16 amatiuza kuti: “Pakuti Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”

Mulungu anatipatsa mphatso ya Mwana wake wobadwa yekha. Imeneyi ndiye mphatso yaikulu koposa zonse imene aliyense wa ife analandila, cifukwa inatimasula ku ukapolo wa ucimo, ukalamba, na imfa. (Salimo 51:5; Yohane 8:34) Olo tiyesetse bwanji, patekha sitingadzimasule ku ukapolo umenewo. Komabe, cifukwa ca cikondi cake cacikulu, Mulungu anapeleka zimene tinali kufunikila kuti timasuke. Mwa kupeleka Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Khristu monga dipo, Yehova Mulungu anapeleka ciyembekezo ca moyo wosatha kwa anthu omvela. Nanga dipo n’ciani maka-maka? N’cifukwa ciani ni yofunika maningi? Nanga ingatipindulitse bwanji?

Dipo ni malipilo a cinthu cimene cawonongeka, kapena malipilo olipilidwa kuti munthu amasuke m’ndende. Baibo imafotokoza kuti makolo athu oyambilila, Adamu na Hava, analengedwa angwilo. Iwo anali na ciyembekezo cosangalala kwamuyaya na moyo m’paradaiso padziko lapansi, pamodzi na ana awo amene anali kudzakhala nawo m’tsogolo. (Genesis 1:26-28) Koma n’zacisoni kuti anataya zonsezi mwa kusankha kusamvela Mulungu, ndipo anakhala ocimwa. Nanga zotulukapo zake zinali zabwanji? Baibo imayankha kuti: “Ndiye cifukwa cake monga mmene ucimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.” (Aroma 5:12) M’malo mopatsila moyo wangwilo kwa ana ake, Adamu anawapatsila ucimo umene unabweletsa imfa.

Pa nkhani ya dipo, malipilo ake ayenela kulingana na cinthu cimene cinawonongedwa. Pamene Adamu anasankha mwadala kusamvela Mulungu, anacimwa ndipo zotulukapo zake n’zakuti anataya moyo wangwilo—moyo wa Adamu. Malinga ndi zimene Baibo imakamba, izi zinacititsa kuti ana a Adamu akhale mu ukapolo wa ucimo na imfa. Conco, panafunika kupelekedwa moyo wina wangwilo kuti timasulidwe mu ukapolo. Moyo wa Yesu unapelekedwa monga nsembe. (Aroma 5:19; Aefeso 1:7) Cifukwa cakuti Mulungu analipila dipo limeneli, anthu ali na ciyembekezo codzasangalala na moyo wamuyaya m’paradaiso padziko lapansi. Adamu na Hava anataya moyo umenewu.—Chivumbulutso 21:3-5.

Tikaona zimene dipo yakwanilitsa, sitikaikila kuti mphatso ya dipo yocokela kwa Mulungu, imene yacititsa kuti tidzakhale na moyo wosatha, ndiye mphatso yopambana zonse. Kuti tiyamikile “mphatso yangwilo” imeneyi tiyeni tione mmene ikwanilitsila mfundo zimene tinakambilana m’nkhani yapita.

Imakhutilitsa colaka-laka cathu. Ife anthu mwacibadwa timafunitsitsa kupitiliza kukhala na moyo. (Mlaliki 3:11) Olo kuti patekha sitingakhutilitse colaka-laka cimeneci, dipo imacititsa zimenezi kukhala zotheka. Baibo imakamba kuti: “Cifukwa malipilo a ucimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 6:23.

Imakwanilitsa cosoŵa cathu. Anthu sakanakwanitsa kupeleka dipo. Baibo imafotokoza kuti: “Ndipo malipilo owombolela moyo wawo ndi amtengo wapatali, moti munthu sangathe kuwapeleka mpaka kalekale.” (Salimo 49:8) Pa cifukwa cimeneci tinali ofunikila thandizo locokela kwa Mulungu kuti timasuke mu ukapolo wa ucimo na imfa. Conco, “ndi dipo lolipilidwa ndi Khristu Yesu,” Mulungu anatipatsa cosoŵa cathu.—Aroma 3:23, 24.

Panthawi yoyenela. Baibo imatiuza kuti: “Pamene tinali ocimwa, Khristu anatifela.” (Aroma 5:8) Cifukwa cakuti mphatsoyi inapelekedwa “pamene tinali ocimwa,” dipo imationetsa mmene Mulungu amatikondela olo kuti ndife ocimwa. Ndipo imatipatsa ciyembekezo ca zinthu zina zam’tsogolo, ngakhale kuti tifunika kupilila zotulukapo za ucimo.

Na colinga cabwino copanda dyela. Baibo imafotokoza bwino cimene cinasonkhezela Mulungu kupeleka Mwana wake monga dipo. Imati: “Mulungu anatisonyeza ife cikondi cake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzela mwa iye. Cikondi cimeneci cikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda.”—1 Yohane 4:9, 10.

Mungaonetse bwanji kuti mumayamikila mphatso yopambana zonse imeneyi? Kumbukilani kuti mau a Yesu apa Yohane 3:16, amafotokoza bwino kuti “wokhulupilila” mwa iye adzapulumutsidwa. Baibo imakamba kuti cikhulupililo ni “ciyembekezo cotsimikizika ca zinthu zoyembekezeledwa.” (Aheberi 11:1) Kuti tikhale na citsimikizo cimeneci tifunika kukhala na cidziŵitso colongosoka. Conco, tikulimbikitsani kumapatula nthawi yophunzila za Yehova Mulungu amene anapeleka “mphatso yangwilo,” ndi zimene mufunika kucita kuti mukasangalale na moyo wosatha, umene udzatheka cifukwa ca dipo la Yesu.

Mungadziŵe zimenezi mwa kuphunzila mfundo za m’Baibo zili pa webusaiti ya www.jw.org. A Mboni za Yehova ni okonzeka kukuthandizani. Ndife otsimikiza kuti pamene muphunzila ndi kupindula na mphatso yopambana zonse imeneyi mudzalimbikitsidwa kufuula kuti: “Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu!”—Aroma 7:25. (Buku lopatulika)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani