LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w17 February masa. 8-12
  • Dipo—‘Mphatso Yangwilo’ Yocokela kwa Atate

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Dipo—‘Mphatso Yangwilo’ Yocokela kwa Atate
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “DZINA LANU LIYELETSEDWE”
  • “UFUMU WANU UBWELE”
  • “CIFUNILO CANU CICITIKE”
  • ONETSANI KUTI MUMAYAMIKILA DIPO
  • DIPO INABWELETSA “NYENGO ZOTSITSIMUTSA” KUCOKELA KWA YEHOVA
  • Dipo Ni Mphatso Ya Mulungu Yopambana Zonse
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Pitilizani Kuyamikila Dipo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Dipo la Yesu—Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • “Mulungu Akuonetsa Cikondi Cake Kwa Ife”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
w17 February masa. 8-12
Yesu aphunzitsa khamu la anthu

Dipo—‘Mphatso Yangwilo’ Yocokela kwa Atate

“Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo imacokela . . . kwa Atate.”—YAK. 1:17.

NYIMBO: 148, 109

KODI DIPO . . . . . .

  • imathandiza bwanji kuyeletsa dzina la Yehova?

  • idzabweletsa bwanji madalitso mu ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu?

  • idzathandiza bwanji kuti colinga ca Mulungu cikwanilitsike?

1. Tidzapeza madalitso anji cifukwa ca dipo?

TIMAPEZA madalitso ambili cifukwa ca nsembe ya dipo la Yesu Khiristu. Dipo linatsegula khomo kwa ana onse a Adamu okonda cilungamo kuti adzakhale mbali ya banja la Mulungu. Ndiponso, dipo linapangitsa kuti zikhale zotheka kudzakhala kwamuyaya mwacimwemwe. Koma dipo la Khiristu sikuti idzangobweletsa cabe madalitso amtsogolo ku mtundu wa anthu ayi. Kudzipeleka kwa Yesu kuti afe ali wokhulupilika kwaYehova, kumakhudza nkhani zofunika kwambili kwa zolengedwa za kumwamba ndi padziko lapansi.—Aheb. 1:8, 9.

2. (a) Ni nkhani ziti zokhudza cilengedwe conse zimene zipezeka m’pemphelo la Yesu? (Onani pikica pamwambapa.) (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

2 Zaka ziŵili Yesu asanafe ndi kupeleka nsembe ya dipo, anaphunzitsa ophunzila ake kupemphela kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzi-modzinso pansi pano.” (Mat. 6:9, 10) Kuti tikulitse ciyamikilo cathu kaamba ka dipo, tiyeni tikambilane mmene dipolo limagwilizanilana ndi kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu, ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu, ndi kukwanilitsika kwa colinga ca Mulungu.

“DZINA LANU LIYELETSEDWE”

3. Kodi dzina la Yehova limaonetsa ciani? Nanga Satana ananyozela bwanji dzina lopatulika la Mulungu?

3 M’pemphelo lake la citsanzo, cinthu coyamba cimene Yesu anachula ni kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu. Dzina la Yehova limaonetsa bwino-bwino ukulu wake, mphamvu, ndi ciyelo. M’pemphelo lina, Yesu anachula Yehova kuti “Atate Woyela.” (Yoh. 17:11) Popeza Yehova ni woyela, mfundo zonse na malamulo ake onse ndi zoyela. Mosasamala kanthu za zimenezi, mwamacenjela Satana anatsutsa zakuti Mulungu ni woyenela kukhazikitsila anthu malamulo m’munda wa Edeni. Mwa kukamba zabodza zokhudza Yehova, Satana ananyozela dzina lopatulika la Mulungu.—Gen. 3:1-5.

4. Kodi Yesu anathandiza bwanji kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe?

4 Yesu anali kulikonda dzina la Yehova. (Yoh. 17:25, 26) Iye anathandiza kuti dzinalo liyeletsedwe. (Ŵelengani Salimo 40:8-10.) Motani? Mwa zocita zake ndi zimene anali kuphunzitsa, Yesu anathandiza anthu kuzindikila kuti miyezo ya Yehova ni yoyenela, ndi kuti zonse zimene amatipempha kucita zili kaamba ka ubwino wathu. Ngakhale kuti Satana anacititsa Yesu kufa imfa yoŵaŵa, Yesu anakhalabe wokhulupilika kwa Atate wake wakumwamba. Mwa kukhala wokhulupilika, Yesu anaonetsa kuti n’zotheka munthu wangwilo kusungabe miyezo yolungama ya Mulungu.

5. Kodi tingathandize bwanji kuyeletsa dzina la Mulungu?

5 Nanga ise tingaonetse bwanji kuti timaikonda dzina la Yehova? Tingaonetse mwa zocita zathu. Yehova afuna kuti tizikhala oyela. (Ŵelengani 1 Petulo 1:15, 16.) Izi zitanthauza kuti tiyenela kulambila Yehova yekha cabe, ndi kumumvela na mtima wathu wonse. Ngakhale pamene tizunzidwa, timayesetsa mmene tingakwanitsile kukhala moyo mogwilizana ndi mfundo ndi malamulo ake olungama. Mwa zocita zathu zabwino, timaonetsa kuwala kwathu ndi kucititsa kuti dzina la Yehova lilemekezeke. (Mat. 5:14-16) Pokhala anthu oyela, timaonetsa mwa zocita zathu kuti malamulo a Yehova ni abwino, ndi kuti zokamba za Satana n’zabodza. Tikalakwa, timalapa moona mtima ndi kuleka kucita zinthu zosalemekeza Yehova.—Sal. 79:9.

6. N’cifukwa ciani Yehova angatione olungama ngakhale kuti ndise ocimwa?

6 Yehova amaseŵenzetsa nsembe ya Khiristu kuti akhululukile macimo a anthu amene amaonetsa cikhulupililo. Iye amalandila anthu amene adzipeleka kwa iye kukhala alambili ake. Yehova amachula Akhiristu odzozedwa olungama kuti ana ake, ndipo a “nkhosa zina” olungama kuti mabwenzi ake. (Yoh. 10:16; Aroma 5:1, 2; Yak. 2:21-25) Ngakhale masiku ano, dipo limatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wathu, ndi kutengako mbali pa kuyeletsa dzina lake.

“UFUMU WANU UBWELE”

7. Ni madalitso ati amene adzatheka mu ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu cifukwa ca dipo?

7 M’pemphelo la citsanzo, Yesu anapempha Mulungu cinthu caciŵili. Anati: “Ufumu wanu ubwele.” Kodi dipo imagwilizana bwanji ndi Ufumu wa Mulungu? Dipo inacititsa kuti zikhale zotheka kusonkhanitsa a 144,000 kuti akatumikile monga mafumu ndi ansembe pamodzi na Khiristu kumwamba. (Chiv. 5:9, 10; 14:1) Yesu ndi olamulila anzake, amene onse amapanga Ufumu wa Mulungu, adzathandiza mtundu wa anthu kupindula ndi dipo kwa zaka zoposa cikwi. Dziko lapansi lidzasanduka paradaiso, ndipo anthu onse okhulupilika adzakhala angwilo. Adzagwilizanitsa pamodzi mbali ya banja la Mulungu ya kumwamba ndi ya padziko lapansi. (Chiv. 5:13; 20:6) Yesu adzaphwanya mutu wa njoka ndi kuthetselatu mavuto onse obwela cifukwa ca kupanduka kwa Satana.—Gen. 3:15.

8. (a) Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzila ake kuona kufunika kwa Ufumu wa Mulungu? (b) Timaonetsa bwanji kuti tikucilikiza Ufumu wa Mulungu masiku ano?

8 Pamene Yesu anali padziko lapansi, anathandiza ophunzila ake kuona kufunika kwa Ufumu wa Mulungu. Pambuyo pa ubatizo wake, mwamsanga Yesu anayamba kulengeza “uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu” kulikonse. (Luka 4:43) M’mau ake otsiliza asanabwelele kumwamba, Yesu analangiza ophunzila ake kukhala mboni zake mpaka “kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:6-8) Kupitila m’nchito yolalikila Ufumu, anthu zungulile dziko lapansi ali ndi mwayi wophunzila za dipo ndi kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu. Masiku ano, timaonetsa kuti tikucilikiza Ufumu wa Mulungu mwa kuthandiza abale a Yesu ali padziko lapansi pa nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse.—Mat. 24:14; 25:40.

“CIFUNILO CANU CICITIKE”

9. N’cifukwa ciani tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzakwanilitsa colinga cake cokhudza mtundu wa anthu?

9 Kodi Yesu anatanthauza ciani pamene anapempha kuti: “Cifunilo canu cicitike”? Yehova ni Mlengi. Akakamba kuti adzacita cina cake, cili monga kuti wacita kale cinthuco. (Yes. 55:11) Iye sadzalola kuti kupanduka kwa Satana kusokoneze colinga cake pa mtundu wa anthu. Kucokela paciyambi, Yehova anali kufuna kuti padziko lapansi padzaze ana angwilo a Adamu na Hava. (Gen. 1:28) Zikanakhala kuti Adamu na Hava anafa opanda ana, sembe colinga ca Mulungu cakuti padziko padzaze ana awo sicikanakwanilitsika. N’cifukwa cake, Adamu ndi Hava atacimwa, Yehova anawalola kubala ana. Kupitila m’dipo, Mulungu anapeleka mwayi kwa onse amene amaonetsa cikhulupililo wakuti akhalenso angwilo, ndi kukhala ndi moyo kwamuyaya. Yehova amakonda anthu, ndipo afuna kuti anthu omvela akakhale mmene iye anali kufunila.

10. Kodi dipo limapindulitsa bwanji anthu amene anafa?

10 Nanga bwanji za anthu mabiliyoni ambili amene anafa asanadziŵe Yehova ndi kum’tumikila? Dipo inacititsa kuti pakhale ciyembekezo ca kuuka kwa akufa. Atate wathu wacikondi wakumwamba adzawaukitsa na kuwapatsa mwayi wophunzila colinga cake, ndi kukhala ndi moyo wamuyaya. (Mac. 24:15) Yehova afuna kuti anthu akhale ndi moyo, osati kufa. Popeza iye ni Gwelo la moyo, amakhala Tate wa aliyense woukitsidwa. (Sal. 36:9) Conco, mpake kuti Yesu anatiphunzitsa kupemphela kuti: “Atate wathu wakumwamba.” (Mat. 6:9) Yehova anapatsa Yesu udindo woukitsa akufa. (Yoh. 6:40, 44) M’paradaiso, Yesu adzakwanilitsa udindo wake monga “kuuka ndi moyo.”—Yoh. 11:25.

11. Kodi Mulungu ali nalo colinga canji “khamu lalikulu”?

11 Sikuti ni anthu ocepa cabe amene adzapindula ndi madalitso a Yehova iyayi. Yesu anati: “Aliyense wocita cifunilo ca Mulungu, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga ndi mayi anga.” (Maliko 3:35) Colinga ca Mulungu n’cakuti “khamu lalikulu” limene silidziŵika ciŵelengelo, locokela m’dziko lililonse, fuko lililonse, ndi cinenelo ciliconse, likhale olambila ake. Amene amakhulupilila dipo ya Khiristu, komanso amene amacita cifunilo ca Mulungu angakhale pakati pa anthu amene akufuula kuti: “Cipulumutso cathu cacokela kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.”—Chiv. 7:9, 10.

12. Kodi colinga ca Yehova cokhudza anthu omvela cimaonekela bwanji m’pemphelo la citsanzo?

12 Colinga ca Yehova cokhudza mtundu wa anthu omvela cikuonekela bwino m’pemphelo la citsanzo la Yesu. Mogwilizana ndi pemphelo limeneli, tifunika kuyesetsa kuyeletsa dzina la Yehova. (Yes. 8:13) Dzina leni-leni la Yesu limatanthauza kuti “Yehova Ni Cipulumutso.” Ndipo cipulumutso cathu kupitila m’dipo, cimapeleka ulemu ndi ulemelelo ku dzina la Yehova. Mulungu adzagwilitsila nchito Ufumu wake kubweletsa madalitso a dipo kwa anthu omvela. Inde, pemphelo la citsanzo limatitsimikizila kuti palibiletu cingalepheletse cifunilo ca Mulungu kucitika.—Sal. 135:6; Yes. 46:9, 10.

ONETSANI KUTI MUMAYAMIKILA DIPO

13. Kodi ubatizo wathu umaonetsa ciani?

13 Njila yaikulu imene timaonetsela kuti timayamikila dipo, ni mwa kudzipeleka kwa Yehova cifukwa cokhulupilila dipo na kubatizika. Ubatizo wathu umaonetsa kuti “ndife a Yehova.” (Aroma 14:8) Umaonetsa kuti tinapempha Mulungu kutipatsa cikumbumtima cabwino. (1 Pet. 3:21) Yehova amayankha pempho lathu limeneli mwa kutiyeletsa na magazi a nsembe ya Khiristu. Tili ndi cidalilo conse kuti iye adzatipatsa zonse zimene anatilonjeza.—Aroma 8:32.

Munthu abatizika kukhala wa Mboni za Yehova, ndipo atengako mbali mu ulaliki

Kodi timaonetsa bwanji kuti timayamikila dipo? (Onani palagilafu 13, 14)

14. N’cifukwa ciani tinalamulidwa kukonda mnansi wathu?

14 Ni njila ina iti imene timaonetsela kuti timayamikila dipo? Zonse zimene Yehova amacita, amazicita cifukwa ca cikondi. Conco, iye afuna kuti olambila ake onse azionetsa cikondi, limene ni khalidwe lawo lalikulu. (1 Yoh. 4:8-11) Timaonetsa kuti timafuna kukhala “ana a Atate [wathu] wakumwamba” mwa kukonda mnansi wathu. (Mat. 5:43-48) Lamulo lakuti tizikonda mnansi wathu ni laciŵili pa lamulo lakuti tizikonda Yehova. (Mat. 22:37-40) Njila yaikulu imene timaonetsela kuti timakonda mnansi wathu, ni mwa kumvela lamulo lakuti tizilalikila uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu. Tikamaonetsa cikondi kwa anzathu, timaonetsa ulemelelo wa Mulungu. Ndipo cikondi cathu pa Mulungu ‘cimakhala cokwanila’ pamene timvela lamulo lakuti tizikonda ena, maka-maka Akhiristu anzathu.—1 Yoh. 4:12, 20.

DIPO INABWELETSA “NYENGO ZOTSITSIMUTSA” KUCOKELA KWA YEHOVA

15. (a) Ni madalitso anji amene timalandila kwa Yehova? (b) Nanga ni madalitso anji amene tiyembekezela?

15 Tikakhulupilila dipo, timakhala ndi mwayi wokhululukidwa macimo. Mau a Mulungu amatitsimikizila kuti macimo athu ‘angafafanizidwe.’ (Ŵelengani Machitidwe 3:19-21.) Monga mmene takambilana kale, kupitila m’dipo Yehova amatenga Akhiristu odzozedwa kukhala ana ake. (Aroma 8:15-17) Kwa ife a “nkhosa zina,” zili monga kuti Yehova walemba dzina lathu pa satifiketi yotivomeleza kukhala ana ake. Pambuyo pakuti takhala angwilo ndi kupyola pa ciyeso cotsiliza, Yehova adzasaina satifiketi imeneyo, titelo kukamba kwake, na kutitenga kukhala ana ake okondeka a padziko lapansi. (Aroma 8:20, 21; Chiv. 20:7-9) Cikondi ca Yehova pa ana ake a mtengo wapatali n’cosatha. Nawonso madalitso a dipo ni a muyaya. (Aheb. 9:12) Mphatso imeneyi siizatha nchito olo pang’ono, ndipo palibe angatilande.

16. Kodi dipo imatimasula bwanji?

16 Palibe cimene Mdyelekezi angacite kuti alepheletse anthu onse olapa moona mtima kudzakhala m’banja la Yehova. Yesu anabwela padziko lapansi na kufa “kamodzi kokha.” Mwa ici, dipo inalipilidwa kwamuyaya. (Aheb. 9:24-26) Idzacotselatu ucimo umene tinatengela kwa Adamu. Tiyamikila kwambili nsembe ya Khiristu, cifukwa imatimasula mu ukapolo wa dzikoli lolamulidwa ndi Satana, ndipo sitiopanso imfa.—Aheb. 2:14, 15.

17. Kodi cikondi ca Yehova cimatanthauzanji kwa imwe?

17 Malonjezo a Mulungu ni odalilika kwambili. Monga mmene malamulo a zacilengedwe sasinthila, Yehova nayenso sasintha. Sangatigwilitse mwala. (Mal. 3:6) Yehova anatipatsa zinthu zambili osati cabe mphatso ya moyo. Amatipatsa cikondi cake. Baibo imati: “Tikudziŵa ndipo tikukhulupilila za cikondi cimene Mulungu ali naco kwa ife.” (1 Yoh. 4:16) Dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso wosangalatsa kwambili, ndipo aliyense padziko adzaonetsa cikondi ca Mulungu. Conco, tiyeni tigwilizane ndi zolengedwa zokhulupilika za kumwamba pokamba kuti: “Mulungu wathu wanzelu, wamphamvu ndi wa nyonga, atamandidwe, apatsidwe ulemelelo ndi ulemu, ndipo ayamikilidwe kwamuyaya. Ame.”—Chiv. 7:12.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani