3 Thandizo pa Kupilila Mavuto
Pali mavuto amene lomba sitingawapewe kapena kuwathetsa. Mwacitsanzo, ngati munthu amene mumam’konda anamwalila kapena ngati mudwala matenda osacilitsika, palibe mocitila koma kungopeza njila zokuthandizani kupilila. Kodi Baibo ingakuthandizeni pa mavuto aakulu ngati amenewa?
MATENDA OSACILITSIKA
Rose anakamba kuti: “N’nabadwa na matenda osacilitsika, amene amacititsa kuti nthawi zonse nizimvela kuŵaŵa maningi. Thanzi yanga siili bwino olo pang’ono.” Cimodzi mwa zinthu zimene zinali kum’detsa nkhawa kwambili, n’cakuti nthawi zina anali kulephela kuika maganizo ake pa zimene anali kuŵelenga m’Baibo na pa zinthu zina zauzimu. Koma analimbikitsidwa kwambili na mau a Yesu apa Mateyu 19:26, pamene pamati: “Zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” Rose anazindikila kuti palinso njila zina zoŵelengela Baibo. Nthawi zina anali kulephela kuŵelenga cifukwa ca matendawo, conco anayamba kumvetsela mau ojambulidwa a m’Baibo ndi a m’mabuku ophunzilila Baibo.a Iye anakamba kuti: “Ngati kuti kunalibe njila zimenezi, sinidziŵa kuti nikanacita bwanji kuti nikhalebe olimba kuuzimu.”
Rose akayamba kudzimvela cisoni cifukwa colephela kucita zimene kale anali kucita, amapeza citonthozo pa lemba la 2 Akorinto 8:12, limene limati: “Mphatso yocokela pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwela nayo, cifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apeleke zimene angathe, osati zimene sangathe.” Mau amenewa amam’kumbutsa Rose kuti ngakhale ali na matenda, Mulungu amasangalala na zimene amacita cifukwa ndiye zimene angakwanitse.
IMFA YA MUNTHU AMENE TIMAM’KONDA
Delphine amene tam’chula kuciyambi anati: “Mwana wanga wa zaka 18 atamwalila, n’nali na cisoni cacikulu cakuti siinali kukhulupilila kuti nidzapitiliza kukhala na moyo. Zinthu zinasinthilatu mu umoyo wanga.” Koma anapeza citonthozo cacikulu pa mau apa Salimo 94:19. Pa lembali wamasalimo anauza Mulungu kuti: “Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, mau anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.” Delphine anati: “N’napemphela kwa Yehova kuti anithandize kupeza zocita zimene zinganitonthoze.”
Iye anayamba kukhala bize kugwila nchito yofunika yodzipeleka. Anayambanso kudziyelekezela na coko, cimene munthu amatha kuciseŵenzetsa olo n’cophwanyika. Iye anazindikila kuti ngakhale kuti anali kudzimva monga munthu wophwanyika, akanatha kuthandiza ena. Iye anati: “N’naona kuti pamene niseŵenzetsa mfundo za m’Baibo kutonthoza anthu amene nimaphunzila nawo Baibo, imakhalanso njila imene Yehova amanitonthozela na kunilimbikitsa.” Delphine analemba maina a anthu ochulidwa m’Baibo amene panthawi inayake anavutika na cisoni cacikulu. Iye anazindikila kuti, “Onsewo anali kukonda kupemphela kwa Mulungu.” Anazindikilanso kuti munthu “sangakwanitse kupilila ngati saŵelenga Baibo.”
Kuphunzila Baibo kwam’thandizanso Delphine kusumika maganizo ake pa zam’tsogolo osati pa zakumbuyo. Kuganizila lonjezo la pa Machitidwe 24:15 kumam’tonthoza. Lembali limakamba kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” Kodi iye amakhulupililadi kuti Yehova adzaukitsa mwana wake? Delphine anati: “M’maganizo mwanga, nimayelekezela kuti nikumuona mwana wanga ataukitsidwa. Cili monga kuti Mulungu analembelatu pa kalenda tsiku limene tidzakumana na mwana wanga m’dziko latsopano. Nimayelekezela kuti nikumuona tili limodzi m’munda wathu, ndipo nikumuonetsa cikondi ngati cimene n’namuonetsa atangobadwa.”
a Zomvetsela zambili monga zimenezi zimapezeka pa webusaiti ya jw.org.
Baibo ingakuthandizeni kupeza citonthozo ngakhale pa nthawi zovuta kwambili