LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp19 na. 2 masa. 10-11
  • Pamene Mwadwala Matenda Aakulu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pamene Mwadwala Matenda Aakulu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE ZATHANDIZA ENA
  • Yehova Mulungu Wathu Amationa Kuti Ndife Ofunika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Kodi Mapemphelo Angakuthandizeni Bwanji?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Mmene Tingathandizile Odwala Matenda a Maganizo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • Kodi Baibo Ingathandize Anthu Odwala Matenda Osathelapo?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
wp19 na. 2 masa. 10-11

Pamene Mwadwala Matenda Aakulu

Linda wa zaka 71 anati: “Nitadziŵa kuti nili na khansa m’mapapo komanso m’matumbo, n’namvela monga kuti nagamulidwa kukapika jele kwa moyo wanga wonse. Pamene n’nafika kunyumba pambuyo poonana na dokotala, n’nati, ‘Izi si zimene n’nali kuyembekezela, nifunika kupeza njila imene inganithandize kupilila.’”

Elise wa zaka 49 anati: “Nili na matenda amene amapangitsa kuti mbali ya kumanzele ya kumaso iziŵaŵa kwambili. Nthawi zina kuŵaŵa kumeneku kumanipangitsa kuvutika maganizo. Ndipo nthawi zambili n’nali kuona monga kuti palibe anganithandize, cakuti n’nafuna kudzipha cabe.”

Wacikulile wodwala ali pa njinga ya olemala, ndipo ali na anthu amene amam’konda

NGATI IMWE kapena munthu amene mumam’konda anamupeza na matenda aakulu akuti angafe nawo, mungamvetse mmene zimavutitsila maganizo. Kuwonjezela pa matendawo, pamakhalanso zina zovutitsa maganizo monga izi: Mantha komanso nkhawa pokaonana na madokotala, kusapeza msanga cithandizo kapena kusoŵa ndalama zopezela cithandizo, kapenanso mavuto ena obwela cifukwa ca kumwa mankhwala. Conco, matenda aakulu amabweletsa nkhawa zambili zosautsa.

Nanga kodi tingapeze kuti thandizo? Ambili apeza citonthozo cacikulu kwambili mwa kupemphela kwa Mulungu, komanso kuŵelenga mavesi otonthoza a m’Baibo. Tingapezenso citonthozo pamene acibululu na mabwenzi ationetsa cikondi, komanso kutithandiza.

ZIMENE ZATHANDIZA ENA

Robert wa zaka 58 anati: “Khalani na cikhulupililo mwa Mulungu pamene mulimbana na matenda, ndipo adzakuthandizani kuti mupilile. Kambani na Yehova m’pemphelo. Muuzeni mmene mumvelela. M’pempheni mzimu woyela. M’pempheni kuti akuthandizeni kukhala wolimbikitsa kwa a m’banja lanu, komanso kuti mukhale woleza mtima pamene mukupilila matenda anu.”

Robert anakambanso kuti: “Zimakhala zothandiza kwambili ngati acibululu akulimbikitsa. Tsiku lililonse abululu anga aŵili kapena mmodzi amanitumila foni ndipo amanifunsa kuti, ‘Kaya mumvelako bwanji?’ Anzanga ocokela kumadela osiyana-siyana amanilimbikitsa. Iwo amanitsitsimula ndipo zimenezi zimanithandiza kuona kuti moyo ni wofunikabe.”

Ngati mwapita kukaona mnzanu wodwala, mungacite bwino kuganizila zimene Linda anakamba. Iye anati: “Mosakaikila, munthu wodwala nayenso amafuna kukhala na umoyo wabwino-bwino, ndipo sangakonde kuti nthawi zonse muzingokhalila kukambilana za matenda ake. Conco ni bwino kukambilana nkhani zimene m’makambilana nthawi zonse.”

Mwa mphamvu za Mulungu, citonthozo ca m’Malemba, komanso thandizo la acibululu ndi anzathu amene amatikonda, tingakhalebe otsimikiza kuti moyo ni wofunika ngakhale pamene tipilila matenda aakulu.

Mavesi a m’Baibo Amene Angakuthandizeni

Dalilani Mulungu.

“Ndinafunsa kwa Yehova ndipo iye anandiyankha, Pakuthawathawa kwanga konse iye anandilanditsa. Wosautsikayu anaitana ndipo Yehova anamva.”—Salimo 34:4, 6.

Linda amene tam’gwila mawu pamwambapa, anati: “Sinimapemphela kuti, ‘Nipangitseni kumvelako bwino.’ Koma nimapemphela kuti, ‘Nithandizeni kukhala wolimba, komanso n’thandizeni kupilila matenda anga.’”

Pezani mphamvu m’Mawu a Mulungu.

“Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” —Yesaya 33:24.

Sinkha-sinkhani pa malonjezo a Mulungu a kutsogolo. Izi zidzakupatsani ciyembekezo cimene cidzakupatsani mphamvu zakuti mukwanitse kupilila.

Pemphani thandizo kwa acibululu komanso anzanu.

“Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

Elise amene tam’gwila mawu kuciyambi kwa nkhani ino, anati: “Musakhale kwa mwekha. Lolani anzanu kuti akuthandizeni. Nthawi zina ungaone monga kuti palibe angakuthandize, ndipo Mulungu nayenso samvetsela. Komabe, musakhale kwa mwekha.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani