LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w19 July masa. 1-32
  • Kulalikila Anthu Osapembedza Mowafika pa Mtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kulalikila Anthu Osapembedza Mowafika pa Mtima
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUZIWAONA MOYENELA ANTHU
  • MUZIWAFIKA PA MTIMA ANTHU
  • KULALIKILA COONADI KWA ANTHU OCOKELA KU ASIA
  • Thandizani Anthu Osapembedza Kudziŵa Mlengi Wawo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Pitilizani Kukhala na Maganizo Oyenela pa Ulaliki Wanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Wacicepele, Limbitsa Cikhulupililo Cako
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Kodi Mumawaona Bwanji Anthu a mu Gawo Lanu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
w19 July masa. 1-32

NKHANI YOPHUNZILA 30

Kulalikila Anthu Osapembedza Mowafika pa Mtima

“Ndakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana, kuti mulimonse mmene zingakhalile ndipulumutseko ena.”—1 AKOR. 9:22.

NYIMBO 82 “Onetsani Kuwala Kwanu”

ZA M’NKHANI INOa

1. Ni kusintha kotani kumene kwakhalapo m’maiko ena m’zaka zaposacedwa?

KWA zaka masauzande, anthu ambili pa dziko anali okonda zacipembedzo. Koma m’zaka zaposacedwa, zinthu zasintha ngako. Anthu osapembedza akuculuka kwambili. Ndipo m’maiko ena, ciŵelengelo ca anthu amene amakamba kuti sapemphela n’cacikulu kuposa ca anthu amene amakamba kuti ni opembedza.b—Mat. 24:12.

2. N’zifukwa zina ziti zimene zapangitsa kuti ciŵelengelo ca anthu osapembedza cikule?

2 N’cifukwa ciani ciŵelengelo ca anthu osapembedza cikukula?c Cifukwa cakuti ena amatengeka na zosangalatsa kapena nkhawa za moyo uno. (Luka 8:14) Ndipo ena analeka kukhulupilila kuti kuli Mulungu. Pali enanso amene amakhulupilila ndithu kuti kuli Mulungu, koma amaganiza kuti cipembedzo n’cosathandiza masiku ano. Amaganizanso kuti n’cosagwilizana na sayansi kapena nzelu yeni-yeni. Nthawi zambili, iwo amamvela anzawo, kapena aphunzitsi awo akukamba kuti moyo unakhalapo cifukwa ca cisanduliko. Nthawi zina, amamvela zimenezi pa wailesi kapena pa TV. Koma samvela kaŵili-kaŵili umboni wokhutilitsa woonetsa kuti kuli Mulungu. Ena analeka kupemphela cifukwa coipidwa na atsogoleli acipembedzo, amene ni adyela pa ndalama na udindo. Cinanso, m’maiko ena, boma linaika malamulo oletsa anthu kulambila mwaufulu.

3. Kodi colinga ca nkhani ino n’ciani?

3 Yesu anatilamula kuti ‘tiphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila’ ake. (Mat. 28:19) Kodi tingawathandize bwanji anthu osapembedza kuyamba kukonda Mulungu mpaka kukhala ophunzila a Khristu? Tifunika kukumbukila kuti zimene munthu angacite akamvetsela uthenga wathu, zingadalile kumene anakulila. Mwacitsanzo, mmene anthu okulila ku Europe angalabadilile uthenga wathu zingasiyane na mmene anthu a ku Asia angacitile. Cifukwa ciani? Ku Europe, anthu ambili amaidziŵako ndithu Baibo, ndiponso anamvapo kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse. Koma ku Asia, anthu ambili sadziŵa ciliconse za Baibo, kapena amangodziŵa zocepa cabe, ndipo ena sakhulupilila kuti kuli Mlengi. Colinga ca nkhani ino ni kutithandiza kulalikila anthu onse mowafika pa mtima, mosasamala kanthu kuti acokela kuti kapena amakhulupilila ciani.

MUZIWAONA MOYENELA ANTHU

4. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala na cikhulupililo cakuti anthu osapembedza angasinthe?

4 Khalani na Cikhulupililo Cakuti Angasinthe. Caka ciliconse, anthu amene anali osapembedza amabatizika n’kukhala Mboni za Yehova. Ambili mwa anthu amenewa anali kale na makhalidwe abwino, ndipo anali kunyansidwa na cinyengo ca m’zipembedzo. Koma ena anali na makhalidwe oipa amene anafunika kuleka. Conco, mwa thandizo la Yehova, tingathe kupeza anthu amene ali na ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’—Mac. 13:48; 1 Tim. 2:3, 4.

M’bale akulalikila mnzake wogwila naye nchito ku cipatala; pambuyo pake, mnzakeyo wapita pa webusaiti yathu ya jw.org

Muzisintha mocitila ulaliki wanu pamene mulalikila anthu amene sakhulupilila Baibo (Onani ndime 5-6)d

5. N’ciani kaŵili-kaŵili cimapangitsa anthu kulabadila uthenga wathu?

5 Khalani Okoma Mtima Komanso Osamala. Kambili, anthu amalabadila uthenga wathu, osati cifukwa ca zimene timakamba powalalikila, koma cifukwa ca mmene timakambila nawo. Iwo amayamikila ngati tikamba nawo mokoma mtima, mosamala, ndiponso moonetsa kuti tili nawo cidwi ceni-ceni. Sitiwakakamiza kumvetsela uthenga wathu. M’malomwake, timayesetsa kuzindikila cifukwa cake sacita cidwi ndi zacipembedzo. Mwacitsanzo, anthu ena sakonda kukambilana nkhani za cipembedzo ndi anthu amene sawadziŵa. Ena amaona kuti n’kusoŵa ulemu kufunsa munthu kuti afotokoze maganizo ake ponena za Mulungu. Ndipo enanso amamvela manyazi ngati anthu awaona akuŵelenga Baibo, maka-maka ngati acita izi na Mboni za Yehova. Mulimonsemo, ife timayesetsa kucita zinthu mowaganizila anthu otelo.—2 Tim. 2:24.

6. Kodi mtumwi Paulo anali kusintha bwanji kalalikidwe kake? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?

6 Nanga tingacite ciani ngati munthu aoneka womangika pamene tichula mawu monga akuti “Baibo,” “cilengedwe,” “Mulungu,” kapena “cipembedzo” pom’lalikila? Tingatengele citsanzo ca mtumwi Paulo mwa kusintha kalalikidwe kathu. Pamene iye anali kulalikila kwa Ayuda, anali kuseŵenzetsa Malemba. Koma pamene anali kulalikila kwa akatswili acigiriki a nzelu zawo ku Areopagi, iye sanachuleko Malemba. (Mac. 17:2, 3, 22-31) Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo? Ngati mwakumana na munthu amene sakhulupilila Baibo, ni bwino kupewa kumaichula pokamba naye. Ngati mwaona kuti munthu ni womangika kuŵelenga naye Baibo, yesani kuŵelenga naye m’njila yakuti anthu ena asaone zimenezi. Mungaŵelenge naye Baibo pa tabuleti kapena pafoni.

7. Malinga n’zimene zinalembedwa pa 1 Akorinto 9:20-23, kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo?

7 Yesetsani Kuwamvetsetsa. Tifunika kuyesetsa kudziŵa maganizo amene anthu ali nawo pa nkhani zosiyana-siyana, ndiponso kudziŵa zimene zimawapangitsa kukhala na maganizo otelo. (Miy. 20:5) Ganizilaninso citsanzo ca Paulo. Iye anakulila pakati pa Ayuda. Podziŵa izi, anali kusintha ulaliki wake polalikila anthu a mitundu ina, amene anali kudziŵa zocepa cabe za Yehova na Malemba kapena amene sanali kudziŵa ciliconse. Nafenso tingafunike kufufuza kapena kufunsako ofalitsa amene atumikila kwa nthawi yaitali mu mpingo mwathu, kuti atithandize kudziŵa bwino anthu a m’gawo lathu, n’colinga cakuti tizicita zinthu mowaganizila.—Ŵelengani 1 Akorinto 9:20-23.

8. Kodi ni njila imodzi iti imene tingayambitsile makambilano a ulaliki?

8 Colinga cathu pa nchito yolalikila ni kupeza anthu ‘oyenelela.’ (Mat. 10:11) Kuti tidziŵe anthu oyenelela, tifunika kuwalimbikitsa kufotokoza maganizo awo na kuwamvetsela mwachelu. M’bale wina ku England amapempha anthu kuti afotokoze zimene aona kuti zingawathandize kukhala na banja lacimwemwe, kulela bwino ana, kapena kupilila zinthu zopanda cilungamo. Pambuyo pomvetsela mayankho awo, m’baleyo amawafunsa kuti: “Muona bwanji malangizo awa amene analembedwa zaka pafupi-fupi 2,000 zapitazo?” Ndiyeno, popanda kuchula mawu akuti “Baibo,” amawaŵelengela mavesi osankhidwa bwino pa foni yake.

MUZIWAFIKA PA MTIMA ANTHU

9. Kodi tingathandize bwanji anthu amene amakonda kukana kukambilana nawo za Mulungu?

9 N’zotheka kuwafika pa mtima anthu amene amakonda kukana kukambilana nawo za Mulungu. Tingacite izi mwa kukambilana nawo zinthu zimene amacita nazo cidwi. Mwacitsanzo, anthu ambili amacita cidwi na zacilengedwe. Conco, mwina tingakambe kuti: “Nikhulupilila kuti imwe mudziŵa kuti zipangizo zambili zimene zilipo, asayansi pozipanga, anacita kukopela zinthu zimene zilipo kale. Mwacitsanzo, akatswili opanga mamaikolofoni anaphunzila za matu, ndipo akatswili opanga makamela anaphunzila za maso. Kodi muganiza kuti zinthu zimene akatswiliwa anakopela zinacokela kuti? Kodi zinakhalako zokha kapena zinacita kulengedwa na winawake?” Pambuyo pomvetsela yankho, mungawonjezele kuti: “Akatswili a zopanga-panga akamaphunzila za mmene matu na maso anapangidwila, m’ceni-ceni amakhala akutengela luso la winawake. N’nacita cidwi na zimene wolemba ndakatulo wina wakale analemba. Iye anati: ‘Kodi amene anakupatsani makutu, sangamve? Kapena amene anapanga maso, sangaone?’ Iye ndiye ‘amaphunzitsa anthu kuti akhale ozindikila.’ Asayansi ena afika povomeleza mfundo imeneyi, ndipo amakhulupilila kuti zinthu zinacita kulengedwa.” (Sal. 94:9, 10) Kenako, tingawatambitse vidiyo ya pa jw.org®, pa mbali yakuti “Zocitika pa Moyo wa Anthu Ena,” pa cigawo cakuti “Mmene Moyo Unayambila.” (Pitani ku Chichewa, pa MABUKU > MAVIDIYO.) Kapena mungawagaŵile kabulosha kakuti Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa?, kapena kakuti Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri.

10. Kodi tingayambe bwanji kulalikila munthu amene safuna kukambilana naye za Mulungu?

10 Anthu ambili amafuna kukhala na tsogolo labwino. Koma ena amakhala na mantha cifukwa coganiza kuti dziko lapansi lidzawonogedwa, kapena kuti lidzaipitsidwa kothelatu, cakuti anthu sadzakhalaponso. Woyang’anila woyendela wina ku Norway anakamba kuti anthu amene safuna kukamba nawo za Mulungu, kambili amacita cidwi ngati akambilana nawo za mmene zinthu zilili pa dzikoli. M’baleyo akapeleka moni kwa anthu, amawafunsa kuti: “Kodi muganiza bwanji za tsogolo lathu? Kodi tiyenela kudalila andale, asayansi kapena winawake?” Pambuyo pomvetsela mosamala, m’baleyo amaŵelenga kapena kugwila mawu lemba linalake lokamba za tsogolo labwino. Ena amacita cidwi na lonjezo la m’Baibo lakuti dziko lapansi lidzakhalapo mpaka kalekale, na kuti anthu abwino adzakhala mmenemo kwamuyaya.—Sal. 37:29; Mlal. 1:4.

11. N’cifukwa ciani tifunika kuseŵenzetsa njila zosiyana-siyana zoyambila makambilano? Nanga tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo pa Aroma 1:14-16?

11 Tiyenela kuseŵenzetsa njila zosiyana-siyana zoyambila makambilano polalikila. Cifukwa ciani? Cifukwa anthu amasiyana-siyana. Nkhani imene wina angacite nayo cidwi, wina sangakondwele nayo. Ena amaona kuti palibe vuto kukambilana nawo za Mulungu kapena Baibo, pamene ena amamvetsela uthenga wathu ngati coyamba tikamba nawo zinthu zina. Mulimonsemo, tiyenela kucita zonse zotheka kuti tilalikile anthu a mitundu yonse. (Ŵelengani Aroma 1:14-16.) Koma tifunikanso kukumbukila kuti Yehova ndiye amacititsa kuti coonadi cikule m’mitima ya anthu okonda cilungamo.—1 Akor. 3:6, 7.

KULALIKILA COONADI KWA ANTHU OCOKELA KU ASIA

Wa Mboni za Yehova akukambilana mfundo yothandiza ya m’Baibo na mzimayi wocokela ku dziko losapembedza

Ofalitsa Ufumu ambili amaonetsa cidwi kwa anthu ocokela ku maiko amene si acikhristu, ndipo amakambilana nawo mfundo zothandi za za m’Baibo (Onani ndime 12-13)

12. Kodi tingawathandize bwanji anthu a ku Asia amene sanaganizilepo zakuti kuli Mlengi?

12 Pa dziko lonse, ofalitsa ambili amakumana ndi anthu ocokela ku maiko a ku Asia, kuphatikizapo ena ocokela ku maiko amene boma linaika ciletso pa nkhani ya kulambila. M’maiko ena a ku Asia, anthu ambili sanaganizilepo mozama nkhani yakuti kuli Mlengi. Conco, ena amacita cidwi na uthenga wathu, ndipo amavomela mwamsanga kuphunzila Baibo. Koma ena poyamba sakhala na cidwi cophunzila Baibo. Kodi tingawathandize bwanji? Ofalitsa ena amene ni aciyambakale aona kuti ulaliki umawayendela bwino ngati ayamba mwa kuceza nawo anthu otelo, komanso kuwaonetsa cidwi. Ndiyeno, pakakhala poyenela, amawafotokozela mmene umoyo wawo unasinthila cifukwa coseŵenzetsa mfundo za m’Baibo.

13. N’ciani cingakope anthu kuti ayambe kuphunzila Baibo? (Onani cithunzi pa cikuto.)

13 Anthu ambili amakopeka na mfundo zothandiza za m’Baibo. (Mlal. 7:12) Mlongo wina ku America, amene amalalikila anthu okamba Cimandarini, anati: “Nimayesetsa kuonetsa cidwi kwa anthu na kuwamvetsela mwachelu. Nikadziŵa kuti ni alendo obwela kumene, nimawafunsa kuti: ‘Kaya umoyo uyenda bwanji kuno kwathu? Kodi nchito munaipeza? Kodi anthu kuno mukhala nawo bwanji?’” Nthawi zina, kufunsa mafunso otelo kumathandiza mlongoyo kuyamba kukambilana ndi anthu mfundo za m’Baibo. Akaona kuti m’poyenela, mlongoyo amafunsanso kuti: “Kodi muganiza kuti n’ciani cingatithandize kuti tizikhala bwino ndi anthu? Kodi mungakonde kuti nikuonetsenkoni mwambi wina wa m’Baibo? Mwambiwu umati: “Ciyambi ca mkangano cili ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo. Conco mkangano usanabuke, cokapo.’ Kodi muganiza kuti malangizo amenewa angatithandize kuti tizikhala bwino ndi anthu ena?” (Miy. 17:14) Kukambilana ndi anthu mwanjila imeneyi, kungatithandize kuzindikila anthu amene angafune kuphunzila zambili.

14. Kodi m’bale wina wa kum’maŵa kwa Asia amawalalikila bwanji anthu amene amakamba kuti sakhulupilila Mulungu?

14 Nanga bwanji za anthu amene amakamba kuti sakhulupilila Mulungu? Kodi tingawalalikile bwanji? M’bale amene wakhala akulalikila anthu osapembedza kwa nthawi yaitali kum’maŵa kwa Asia, anati: “Nthawi zambili, munthu kuno akakamba kuti sakhulupilila Mulungu, amatanthauza kuti salambila milungu ya makolo. Conco, nimavomeleza kuti milungu yambili ni yopangidwa ndi anthu, komanso si milungu yeni-yeni. Ndiyeno, nimaŵelenga Yeremiya 16:20, imene imati: ‘Kodi munthu wocokela kufumbi angapange milungu? Zimene munthu amapangazo si milungu yeni-yeni.’ Kenako, nimafunsa kuti: ‘Kodi tingasiyanitse bwanji pakati pa Mulungu weni-weni na milungu yopangidwa ndi anthu?’ Pamene akuyankha, nimamvetsela mosamala, ndiyeno nimaŵelenga Yesaya 41:23, imene imati: ‘Nenani zinthu zimene zikubwela m’tsogolo, kuti tidziŵe kuti inu ndinu milungu.’ Ndiyeno, nimam’fotokozela umodzi mwa maulosi a Yehova amene anakwanilitsika.”

15. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca m’bale wa kum’maŵa kwa Asia?

15 M’bale winanso wa kum’maŵa kwa Asia anafotokoza zimene amakamba pamene apanga maulendo obwelelako. Iye anati: “Nimafotokozela mwininyumba zitsanzo zoonetsa kuti kutsatila mfundo za m’Baibo n’cinthu canzelu. Nimam’fotokozelanso zitsanzo za maulosi a m’Baibo amene anakwanilitsika, komanso za malamulo a m’cilengedwe. Ndiyeno, nimamuuza kuti zonsezo ni umboni wakuti kuli Mlengi wamoyo ndi wanzelu. Ngati iye wayamba kukhulupilila kuti Mulungu alikodi, nimakambilana naye zimene Baibo imakamba ponena za Yehova.”

16. Malinga na Aheberi 11:6, n’cifukwa ciani ophunzila Baibo afunika kukhala na cikhulupililo mwa Mulungu na Baibo? Nanga tingawathandize bwanji kukhala na cikhulupililo cimeneco?

16 Pamene tiphunzila Baibo ndi anthu osapembedza, tifunika kupitiliza kuwathandiza kulimbitsa cikhulupililo cawo cakuti Mulungu aliko. (Ŵelengani Aheberi 11:6.) Tifunikanso kuwathandiza kukhulupilila kwambili Baibo. Kuti zimenezi zitheke, tingafunike kuwafotokozela mobweleza-bweleza mfundo zina za coonadi. Pa phunzilo lililonse, tingakambilane nawo umboni woonetsa kuti Baibo ni Mawu a Mulungu. Izi zingaphatikizepo kukambilana nawo mwacidule za maulosi a m’Baibo amene anakwanilitsika, umboni wakuti imakamba zolondola pa nkhani za sayansi na mbili yakale, komanso kuti ili na mfundo zothandiza mu umoyo wathu.

17. Kodi kukonda anthu kungawathandize kucita ciani?

17 Timathandiza anthu kukhala ophunzila a Khristu mwa kuwaonetsa cikondi, kaya akhale opembedza kapena ayi. (1 Akor. 13:1) Pamene tiphunzila nawo, tifunika kuwathandiza kuona kuti Mulungu amatikonda, ndipo amafuna kuti nafenso tizim’konda. Caka ciliconse, anthu masauzande amene poyamba anali na cidwi cocepa pa za cipembedzo, kapena amene analibiletu cidwi, amabatizika cifukwa amaphunzila za Mulungu na kuyamba kum’konda. Conco, muziwaona moyenela anthu. Muzikonda anthu a mitundu yonse na kuwaonetsa cidwi. Komanso muziwamvetsela mosamala. Yesetsani kumvetsetsa mmene amaonela zinthu. Ndipo mwa citsanzo canu, aphunzitseni kukhala ophunzila a Khristu.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Tingacite ciani kuti tiziwaona moyenela anthu mu ulaliki?

  • Tingawalalikile bwanji mofika pa mtima anthu osapembedza?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kulalikila coonadi kwa munthu aliyense amene takumana naye?

NYIMBO 76 Kodi Mumamvela Bwanji?

a Masiku ano, pa dzikoli pali anthu ambili osapembedza kuposa kale lonse. Ena timakumana nawo m’gawo lathu pamene tili mu ulaliki. Nkhani ino, idzafotokoza mmene tingalalikile coonadi ca m’Baibo kwa anthu otelo. Idzafotokozanso mmene tingawathandizile kuti ayambe kukhulupilila Yehova Mulungu na mawu ake, Baibo.

b Malinga na kufufuza kumene kunacitika, ena mwa maiko amenewa ni Albania, Australia, Austria, Azerbaijan, Canada, China, Czech Republic, Denmark, France, Germany, Hong Kong, Ireland, Israel, Japan, Netherlands, Norway, South Korea, Spain, Sweden, Switzerland, United Kingdom, na Vietnam.

c KUFOTOKOZELA MAWU ENA: M’nkhani ino, liwu lakuti osapembedza litanthauza anthu amene sali m’cipembedzo ciliconse, kapena amene sakhulupilila kuti kuli Mulungu.

d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale akulalikila mnzake wogwila naye nchito ku cipatala. Pambuyo pake, mnzakeyo wapita pa webusaiti yathu ya jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani