Sangalalani Ndi Nchito Yanu Yakhama
1. N’ciani cingacepetse cangu cathu ca ulaliki?
1 Munthu analengedwa kuti ‘azisangalala ndi nchito yake yakhama.’ (Mlal. 2:24) Komabe, ngati ulaliki wathu subala zipatso, timalefuka ndipo cimwemwe ndi cangu cathu zimacepa. Kodi tingacite ciani kuti tipewe zimenezi?
2. N’cifukwa ciani tiyenela kukhutilabe ndi ulaliki wathu kaya anthu alabadile kapena ai?
2 Khutilani ndi Zimene Mwacita: Kumbukilani kuti, ngakhale kuti amene analabadila Yesu anali ocepa, mosakaikila konse ulaliki wake unali wopambana. (Yoh. 17:4) M’fanizo lake la wofesa mbeu, Yesu ananenelatu kuti mitima ya anthu ambili sidzalabadila uthenga wonga mbeu za Ufumu. (Mat. 13:3-8, 18-22) Ngakhale n’conco, khama lathu limakwanilitsabe zambili.
3. Kodi ‘timabalabe’ motani “zipatso” ngakhale kuti anthu ambili salabadila ulaliki wathu?
3 Mmene Timabalila Zipatso Zoculuka: Malinga ndi fanizo la Yesu, amene alabadila uthenga ‘adzabala zipatso.’ (Mat. 13:23) Mmela wa tiligu ukakula ndi kukhwima, zipatso zimene umabala si tummela tung’ono-tung’ono, koma mbeu zatsopano. Conco, zipatso zimene Akristu amabala, kweni-kweni si ophunzila atsopano, koma ndi kufesa mbeu za Ufumu mobweleza-bweleza. Zotsatilapo zake zimakhala ‘zabwino’ ndipo zimatikhutilitsa, kaya anthu alabadile kapena ai. Timathandizila kuyeletsa dzina la Yehova. (Yes. 43:10-12; Mat. 6:9) Timasangalalanso ndi mwai wokhala anchito anzake a Mulungu. (1 Akor. 3:9) Yehova amakondwela ndi “cipatso ca milomo” cimeneci.—Aheb. 13:15, 16.
4. Kodi ulaliki wathu ungabale zipatso zina ziti zimene sitingadziŵe n’komwe?
4 Komanso, nchito yathu yakhama ingabale zipatso zina zimene sitingazione. N’kutheka kuti ena amene Yesu anawalalikila anadzakhala ophunzila ake iye atamaliza utumiki wake wa padziko lapansi. Mofananamo, mbeu ya Ufumu imene tingafese, singazike mizu ndi kumela mumtima mwa munthu panthawi imeneyo. Koma munthuyo angabwele m’coonadi pambuyo pake ife osadziŵa n’komwe. Ndithudi, ulaliki wathu umakwanilitsa zambili. Conco, tiyeni ‘tipitilize kubala zipatso zambili,’ ndi kusonyeza kuti tilidi ophunzila a Yesu.—Yoh. 15:8.