Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu December
“Panthawi ino ya caka, anthu ambili amaganizila za Yesu. Kodi muganiza cinthu cacikulu cimene Yesu anacita n’ciani? [Yembekezani ayankhe.] Onani mutu wa nkhani iyi patsamba 16.” M’patseni Nsanja ya Olonda ya December 1, ndi kukambilana naye mfundo zili pakamutu kalikonse kamene mungasankhe ndi lemba limodzi losagwidwa mau. Ndiyeno m’gaŵileni magaziniyo, ndi kupangana kuti mukabwelenso kudzakambilana naye funso lotsatila.
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova December 1
“Anthu ambili mwezi uno ali ndi cisangalalo ca Krisimasi. N’citi pa izi cimene muona kuti n’cofunika kwambili kucita pa nthawi ya Krisimasi? [Muonetseni zimene zadandalikidwa patsamba 3 ndipo yembekezani ayankhe. Ndiyeno pitani ku nkhaniyo ndi kuŵelenga lemba limene lili pa mutu wake.] Magazini iyi ifotokoza zimene tingacite kuti tizikumbukila Yesu caka conse, osati panthawi ya Krisimasi cabe.”
Galamukani! December
“Takucezelani cifukwa ife anthu timakumana ndi mavuto ambili. Kodi inunso mumaona kuti masiku ano anthu ambili kuleza mtima kumawavuta? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ena amadziŵa kuti tili m’masiku ovuta amene Baibo inakambilatu pa 2 Timoteyo 3:1. [Ŵelengani.] Magazini iyi ifotokoza cifukwa cake kusaleza mtima n’kopweteketsa, ndipo ionetsa zimene tingacite kuti tizikhala oleza mtima.”