Colinga ca Webu Saiti Yathu Ndi Kuthandiza Ife ndi Anthu Ena
Yesu analamula kuti tilalikile uthenga wabwino wa Ufumu “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Kuti ‘tikwanilitse mbali zonse za utumiki wathu,’ ma Webu saiti a watchtower.org, jw-media.org, ndi jw.org awapatikiza ndi kupanga Webu saiti imodzi ya jw.org.—2 Tim. 4:5.
“Padziko Lonse Lapansi”: Pafupi-pafupi munthu mmodzi mwa anthu atatu alionse padziko lapansi amagwilitsila nchito Intaneti. Iyo yakhala mbali yaikulu imene anthu ambili, maka-maka acinyamata, amapezako cidziŵitso. Webu saiti yathu imapatsa anthu mayankho oona pa mafunso a m’Baibo. Imawathandiza kudziŵa gulu la Yehova ndipo zimakhala zosavuta kuti apemphe phunzilo la Baibo laulele la panyumba. Zimenezi zimapangitsa kuti uthenga wabwino ufike m’madela ena amene anthu alibe mpata womvela uthenga wa Ufumu.
“Mitundu Yonse”: Kuti tipeleke umboni ku “mitundu yonse,” tifunika kufalitsa coonadi ca m’Baibo m’zinenelo zambili. Anthu amene amapita pa Webu saiti yathu ya jw.org, angapeze nkhani mosavuta m’zinenelo pafupi-fupi 400 kuposa pa Webu saiti ina iliyonse.
Igwilitsileni Nchito Bwino: Webu saiti yathu yokonzedwanso ya jw.org, colinga cake sikungolalikila anthu osakhulupilila. Koma yakonzedwanso kaamba ka Mboni za Yehova. Ngati muli ndi Intaneti, tikulimbikitsani kuti muidziŵe bwino Webu saiti yathu. Malangizo otsatilawa afotokoza mmene mungaigwilitsilile nchito.
[Cithunzi papeji 3]
(Kuti muone mau onse, pitani ku cofalitsa)
Iyeseni
1 Lembani www.jw.org pa malo olembapo adilesi pa kompyuta yanu.
2 Pezani nkhani imene mufuna mwa kudiniza pa tumitu, menyu, ndi malinki.
3 Yesani kugwilitsila nchito jw.org pafoni yanu ngati ili ndi Intaneti. Nkhani zake anazikonza kuti zizikwana pafoni yanu, koma n’zofanana ndi za pa kompyuta.