Kodi Mudzatengako Mbali?
Cikumbutso Cimene Cikubwela Cidzatipatsa Mwai Woyamikila
1. Kodi Cikumbutso cidzatipatsa mwai wapadela wotani?
1 Cikumbutso cimene cidzacitika pa April 14 cidzatipatsa mwai wapadela wosonyeza kuyamikila ubwino wa Yehova. Nkhani ya pa Luka 17:11-18 imafotokoza mmene Yehova ndi Yesu amaonela kuyamikila. N’zomvetsa cisoni kuti pa anthu 10 akhate amene anacilitsidwa, mmodzi cabe ndi amene anasonyeza kuyamikila. M’tsogolomu, mphatso ya dipo idzacititsa matenda onse kutha, ndipo idzacititsanso moyo wosatha kukhala weni-weni. Mosakaikila, tidzayamikila Yehova tsiku lililonse cifukwa ca madalitso amenewa. Komabe tingaonetse bwanji kuyamikila milungu ikubwelayi?
2. Tingacite ciani kuti tiziyamikila dipo?
2 Khalani Woyamikila: Kuyamikila kumayambila m’maganizo. Potithandiza kuyamikila makonzedwe a dipo, ndandanda yapadela ya Cikumbutso yoŵelenga Malemba ingapezeke mu Kalendala ndi m’kabuku ka Kuphunzila Malemba Tsiku ndi Tsiku. Mungacite bwino kuŵelenga Malemba amenewo monga banja. Kucita zimenezo kudzaonjezela ciyamikilo cathu kaamba ka dipo. Zimenezi zimaticititsa kukhala ndi makhalidwe abwino.—2 Akor. 5:14, 15; 1 Yoh. 4:11.
3. Ndi njila ziti zimene tingaonetsele kuyamikila pa nyengo ya Cikumbutso?
3 Sonyezani Kuyamikila: Nchito n’zimene zimasonyeza kuyamikila. (Akol. 3:15) Munthu wakhate woyamikila anayesetsa kufuna-funa Yesu kuti amuyamikile. N’zosakaikitsa kuti mosangalala anali kuuza ena za kucilitsidwa kwake mozizwitsa. (Luka 6:45) Kodi kuyamikila dipo kudzaticititsa kutengako mbali mwacangu poitanila anthu ku Cikumbutso? Kucita upainiya wothandiza kapena kuonjezela utumiki wathu panyengo ya Cikumbutso ndi njila ina yabwino yosonyeza kuyamikila. Patsiku la Cikumbutso, mtima woyamikila udzatilimbikitsa kulandila alendo momasuka ndi kuyankha mafunso amene angakhale nao.
4. Tingacite ciani kuti tisadzadziimbe mlandu panthawi ya Cikumbutso imene ikubwela?
4 Kodi ici cidzakhala Cikumbutso comaliza? (1 Akor. 11:26) Sitidziŵa, koma zimene tidziŵa n’zakuti ngati cingakhale comaliza, ndiye sitidzakhalanso ndi mwai wapadela wosonyeza kuyamikila. Kodi mudzatengako mbali? Conco, tiyeni tilole mau a pakamwa pathu ndi kusinkha-sinkha kwa mtima wathu, zikondweletse Yehova amene moolowa manja watipatsa dipo.—Sal. 19:14.