CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | NEHEMIYA 12–13
Zimene Tikuphunzila m’Buku la Nehemiya
Nehemiya anateteza kulambila koona ndi mtima wonse
13:4-9, 15-21, 23-27
Mkulu wa ansembe Eliyasibu, analola Tobia munthu wosakhulupilila Mulungu ndi wotsutsa kumuuza zocita
Eliyasibu anakonzela Tobia malo m’cipinda codyelamo pakacisi
Nehemiya anaponya katundu yense wa Tobia kunja kwa cipinda codyelamo, anayeletsa cipindaco ndi kuyamba kucigwilitsila nchito moyenelela
Nehemiya anapitilizabe kuyeletsa mzinda wa Yerusalemu