CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YOBU 38-42
Yehova Amakondwela Tikamapemphelela Ena
Yehova anafuna kuti Yobu apemphelele Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari
42:7-10
Yehova anauza Elifazi, Bilidadi ndi Zofari kuti apeleke nsembe yopseleza
Yobu anali kufunika kupemphelela anzake atatu
Yobu anadalitsidwa atapemphelela anzakewo
Yehova anadalitsa Yobu kwambili cifukwa ca cikhulupilililo cake ndi kupilila
42:10-17
Yehova anathetsa mavuto a Yobu, ndipo anamucilitsa matenda ake
Yobu anatonthozedwa ndi anzake komanso acibale ake pa mavuto amene anakumana nao
Yehova anabwezeletsa cuma cimene Yobu anali naco kuwilikiza kaŵili
Yobu ndi mkazi wake anakhalanso ndi ana ena 10
Yobu anakhala ndi moyo zaka zina 140, ndipo anali ndi mwai woona mbadwo wacinai wa mzele wake wobadwila