LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 September tsa. 8
  • Zimene Tiyenela Kupewa Pocititsa Phunzilo la Baibulo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Tiyenela Kupewa Pocititsa Phunzilo la Baibulo
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nkhani Zofanana
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuti Akakhale Ophunzila Obatizika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Kuphunzitsa M’njila Yosavuta Kumva
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 2
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Motsogozela Phunzilo la Baibo Poseŵenzetsa Buku la “Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!”
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 September tsa. 8

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Zimene Tiyenela Kupewa Pocititsa Phunzilo la Baibulo

Yopulinta
M’bale akamba kwambili pophunzitsa wophunzila Baibulo

Kukamba Kwambili: Musaganize kuti mufunika kufotokoza zonse. Yesu anaseŵenzetsa mafunso kuti athandize anthu kuganiza ndi kuona zimene afunika kucita. (Mat. 17:24-27) Mafunso amacititsa phunzilo kukhala logwila mtima. Angakuthandizeni kudziŵa ngati wophunzila akumvetsetsa zimene akuphunzila ndi kuzikhulupilila. (be-CN, tsa. 253 ndime 3-4) Mukafunsa funso, muzileza mtima n’kuyembekezela yankho. Ngati wophunzila wapeleka yankho lolakwika, musamuyankhile. M’malomwake, m’thandizeni kupeza yankho mwa kumufunsa mafunso ena owonjezela. (be tsa. 238 ndime 1-2) Musafotokoze mothamanga mfundo zatsopano kuti wophunzila amvetsetse.—be-CN, tsa. 230 ndime 4.

Mfundo zambili zovuta kumva zokhudza cifukwa cake timakalamba

Kufotokoza Zambili: Pewani kukamba zonse zimene mudziŵa pa nkhani imene muphunzila. (Yoh. 16:12) Kambani cabe mfundo yaikulu m’ndime. (be-CN, tsa. 226 ndime 4-5) Zinthu zina, ngakhale n’zocititsa cidwi zingangophimba mfundo yaikulu. (be-CN, tsa. 235 ndime 3) Ngati wophunzila wamvetsetsa mfundo yaikulu, pitani m’ndime yotsatila.

M’bale aphunzitsa wophunzila Baibulo zinthu zambili cakuti zikumusokoneza

Kufuna Kutsiliza Buku: Colinga cathu si kutsiliza buku, koma kufika pamtima pa wophunzila. (Luka 24:32) Lolani mphamvu ya Mau a Mulungu kugwila nchito mwa munthuyo mwa kufotokoza malemba a mfundo zazikulu za m’nkhaniyo. (2 Akor. 10:4; Aheb. 4:12; be-CN, tsa. 144 ndime 1-3) Seŵenzetsani mafanizo osavuta kumva. (be-CN, tsa. 245 ndime 2-4) Dziŵani mavuto ndi zikhulupililo za wophunzila, ndipo fotokozani mfundo zogwilizana ndi umoyo wake. M’funseni mafunso monga akuti: “Mumvela bwanji ndi zimene muphunzila?” “Kodi zimenezi zitiphunzitsa ciani za Yehova?” “Muona kuti mungapindule bwanji ngati museŵenzetsa mfundo izi?”—be-CN, tsa. 238 ndime 3-5; tsa. 259 ndime 1.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani