UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Thandizani a m’Banja Lanu Kukumbukila Yehova
Yeremiya anapatsidwa nchito yocenjeza Ayuda za ciwonongeko cimene cinali kubwela pa iwo cifukwa anali ataiŵala Mulungu wawo, Yehova. (Yer. 13:25) Cinacitika n’ciani kuti umoyo wakuuzimu wa mtunduwu ufike poipa conco? Mabanja aciisiraeli sanalinso auzimu. N’zoonekelatu kuti mitu ya mabanja siinali kutsatila malangizo a Yehova a pa Deuteronomo 6:5-7.
Mabanja olimba kuuzimu amapangitsa mipingo kukhala yolimba. Mitu ya mabanja ingathandize mabanja awo kukumbukila Yehova mwa kumacititsa Kulambila kwa Pabanja kwa phindu nthawi zonse. (Sal. 22:27) Pambuyo potamba vidiyo yakuti “Mau Awa . . . Azikhala Pamtima Pako”—Kufunsa Mafunso Mabanja, yankhani mafunso aya:
N’ciani cathandiza mabanja ena kuthetsa zopinga zofala zimene zimalepheletsa kulambila kwa pabanja?
Kodi pali mapindu anji ngati tikhala na Kulambila kwa Pabanja kokhazikika?
Pa nkhani ya kulambila kwa pabanja, n’zovuta ziti zimene ine pacanga nimakhala nazo? Nanga nakonzekela kuzithetsa bwanji?