LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp20 na. 3 masa. 4-5
  • Mlengi Wathu Wacikondi Amasamala za Ife

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mlengi Wathu Wacikondi Amasamala za Ife
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • 1. MLENGI WATHU AMAWALITSA DZUŴA
  • 2. MLENGI WATHU AMAGWETSA MVULA
  • 3. MLENGI WATHU AMATIPATSA CAKUDYA NA ZOVALA
  • Muzifuna-funa Ufumu, Osati Zinthu Zakuthupi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Cifukwa Cake Kudziŵa Ngati Mlengi Aliko N’kofunika
    Galamuka!—2021
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
wp20 na. 3 masa. 4-5
Dzuŵa likuwala pamwamba pa mapili pamene likutuluka.

Mlengi Wathu Wacikondi Amasamala za Ife

1. MLENGI WATHU AMAWALITSA DZUŴA

Kodi muganiza umoyo padziko lapansi ukanakhala bwanji popanda dzuŵa? Dzuŵa limapeleka mphamvu ku mitengo kuti itulutse masamba, maluŵa, zipatso, njele, komanso mbewu. Limapangitsanso mitengo kukoka madzi m’nthaka kupitila m’mizu n’kuwapeleka ku masamba, mpaka kufika mu mlenga-lenga monga nthunzi.

Kuyang’ana munda wokongola wa masamba a tiyi.

2. MLENGI WATHU AMAGWETSA MVULA

Mvula ni mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa Mulungu imene imapangitsa kuti tikhale na cakudya. Mulungu amatipatsa mvula kucokela kumwamba na nyengo zimene zokolola zathu zimakhala zambili. Amatipatsa cakudya cokwanila komanso cimwemwe.

Mbalame ili panthambi ya mtengo ndipo ifuna kudya kacipatso kamene kakugwa mu mtengo.

3. MLENGI WATHU AMATIPATSA CAKUDYA NA ZOVALA

Pafupi-fupi munthu aliyense amene ni tate amayesetsa kupezela a m’banja lake cakudya cokwanila na zovala. Onani zimene Malemba amakamba: “Onetsetsani mbalame zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga cakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?”—Mateyu 6:25, 26.

“Phunzilani pa mmene maluwa akuchile amakulila. . . . Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale [Mfumu] Solomo mu ulemelelo wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. Tsopano ngati Mulungu amaveka cotelo zomela zakuchile . . . , kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo?”—Mateyu 6:28-30.

Popeza kuti Mulungu angatipatse cakudya na zovala, mosakaikila angatithandizenso kupeza zofunikila za mu umoyo wathu. Ngati tiyesetsa kucita cifunilo ca Mulungu, iye adzadalitsa zoyesa-yesa zathu pa kulima cakudya, kapena angatithandize kupeza nchito kuti tikwanitse kugula zimene tifunikila.—Mateyu 6:32, 33.

Kukamba zoona, tili na zifukwa zabwino zokondela Mulungu tikaganizila za dzuŵa, mvula, mbalame, komanso maluŵa. Nkhani yokonkhapo ifotokoza mmene Mlengi wathu amakambila na anthu.

Mlengi wathu ‘amawalitsa dzuŵa lake na kuvumbitsa mvula.’ —MATEYU 5:45

Mlengi wathu amatikonda kwambili komanso amatidela nkhawa. Monga tate wacikondi, iye amasamalila banja lake. Malemba Oyela amafotokoza kuti Mulungu ni Mpatsi wowolowa manja, amene ‘amadziŵa zimene tifuna tisanam’pemphe n’komwe.’—Mateyu 6:8.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani