LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp20 na. 3 masa. 14-15
  • Mungapeze Madalitso Osatha kwa Mlengi Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mungapeze Madalitso Osatha kwa Mlengi Wathu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi pa Zozizwitsa Zayesu Mungaphunzilepo Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2004
  • Tiphunzilapo Ciyani pa Zozizwitsa za Yesu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Anali Kukonda Anthu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Timadziŵa za Mulungu Kucokela kwa Aneneli Ake
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
wp20 na. 3 masa. 14-15
Anthu a zikhalidwe zosiyana-siyana akusangalala na mayanjano m’paradaiso pa dziko lapansi.

““Dziko lapansi lidzapeleka zipatso zake. Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.”—SALIMO 67:6

Mungapeze Madalitso Osatha kwa Mlengi Wathu

Mulungu analonjeza mneneli Abulahamu kuti mmodzi mwa mbadwa zake adzabweletsa madalitso ku “mitundu yonse ya padziko lapansi.” (Genesis 22:18) Kodi amene anali kudzakhala mbadwayo ndani?

Zaka pafupi-pafupi 2,000 zapitazo, Mulungu anapatsa Yesu mphamvu yocita zozizwitsa zazikulu, ndipo iye ndiye anali mbadwayo ya Abulahamu. Zozizwitsazo zinaonetsa kuti lonjezo limene linapelekedwa kwa Abulahamu lidzakwanilitsidwa ku mitundu yonse ya anthu kupitila mwa Yesu.—Agalatiya 3:14.

Zozizwitsa zimene Yesu anacita, zinathandiza anthu kudziŵa kuti iye ndiye wosankhidwa na Mulungu kuti adalitse mitundu ya anthu. Ndipo zozizwitsazo, zinaonetsa mmene Mulungu adzam’seŵenzetsela podalitsa mitundu ya anthu kwamuyaya. Onani mmene zozizwitsa za Yesu zionetsela makhalidwe ake abwino.

Cikondi—Yesu anacilitsa odwala.

Panthawi ina, wakhate anacondelela Yesu kuti am’cilitse. Ndiyeno Yesu anakhudza munthuyo n’kumuuza kuti: “Ndikufuna!” Ndipo nthawi yomweyo khate lake linathelatu.—Maliko 1:40-42.

Kuwolowa manja—Yesu anadyetsa anjala.

Yesu sanali kufuna anthu kukhala na njala. Iye anadyetsa anthu masauzande mozizwitsa, mwa kuculukitsa mikate yoŵelengeka komanso tunsomba tocepa. Ndipo anacita izi osati kamodzi cabe. (Mateyu 14:17-21; 15:32-38) Atatsiliza kudya, onse anakhuta ndipo cakudya coculuka cinatsalako.

Cifundo Cacikulu—Yesu anaukitsa akufa.

‘Atagwidwa na cifundo,’ Yesu anaukitsa mwana wa mkazi wamasiye amene panthawiyo anali wacisoni kwambili, ndipo analibe aliyense wom’samalila.—Luka 7:12-15.

MADALITSO OSATHA PADZIKO LAPANSI

Yesu anaonetsa kale kuti Mulungu ali na mphamvu zobweletsa madalitso kwa anthu. Posacedwa, Yesu akadzabwelanso monga mmene analonjezela, Wamphamvuzonse adzamuseŵenzetsa kucita zozizwitsa zazikulu padziko lonse lapansi!

Kodi umoyo udzakhala bwanji padziko lapansi, Mulungu akadzakwanilitsa lonjezo limene anapanga kwa Abulahamu? Anthu amene amakonda Mulungu na kum’lemekeza “adzalandila dziko lapansi” ndipo “adzasangalala ndi mtendele woculuka.” (Salimo 37:11) “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:4.

Lidzakhala dalitso lalikulu cotani nanga, kukhala mwamtendele kwamuyaya padziko lapansi! Tikupemphani kudziŵa zambili za madalitso amene ulamulilo wa Mulungu udzabweletsa, mwa kuyenda pa www.jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani