UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Paulo Anayamika Mulungu Ndipo Analimba Mtima”
Mpingo wa ku Roma utamva zakuti Paulo akubwela, abale osankhidwa anayenda mtunda wa makilomita 64 kuti akakumane naye. Kodi cikondi cimene iwo anaonetsa cinamukhudza bwanji Paulo? “Paulo atawaona, anayamika Mulungu, ndipo analimba mtima.” (Mac. 28:15) N’zoona kuti Paulo anali kudziŵika kuti anali kulimbikitsa mipingo imene anali kucezetsa. Koma apa, pamene anali mkaidi, ndiye analimbikitsidwa.—2 Akor. 13:10.
Masiku ano, oyang’anila madela amayendela mipingo kuti azilimbikitsa abale na alongo. Mofanana na anthu ena onse a Mulungu, nawonso nthawi zina amamvela kulema, amakhala na nkhawa, ndiponso zinthu zolefula. Conco, woyang’anila dela na mkazi wake akadzabwela kudzacezetsa mpingo wanu, mudzacitapo ciani kuti muwathandize kukhala olimba mtima, na kuti pakakhale ‘kulimbikitsana’?—Aroma 1:11, 12.
Muzipezeka pa kukumana kokonzekela ulaliki. Woyang’anila dela amalimbikitsidwa ngati ofalitsa amadzimana zina kuti acilikize mokwanila wiki yapadela. (1 Ates. 1:2, 3; 2:20) Mungaciteko upainiya wothandiza m’mwezi wa kucezetsa kwake. Kodi simungalembetseko kuti mukapite naye mu ulaliki pamodzi na mkazi wake, kapena kutengako mmodzi wa iwo na kupita naye ku phunzilo la Baibo? Iwo amakondwela kuseŵenza na ofalitsa osiyana-siyana, ngakhale acatsopano kapena amene alibe luso lolalikila.
Khalani oceleza. Kodi mungapelekeko malo ogona kwa woyang’anila dela kapena kumuitanila ku cakudya? Kucita izi, kudzaonetsa kuti muma’mkonda pamodzi na mkazi wake. Iwo sayembekezela zinthu zapamwamba.—Luka 10:38-42.
Muzimvela na kuseŵenzetsa malangizo na uphungu wake. Mwacikondi, woyang’anila dela amatithandiza kuona mbali zimene tifunika kuwongolela pocita utumiki wathu kwa Yehova. Nthawi zina, angafunike kupeleka uphungu wamphamvu. (1 Akor. 5:1-5) Ndipo akaona kuti ndise omvela komanso ogonjela, amakondwela kwambili.—Aheb. 13:17.
Onetsani kuyamikila. Uzani woyang’anila dela na mkazi wake mmene mumapindulila cifukwa ca khama lawo. Mungacite zimenezi mwa kuwauza mwacindunji kapena mwa kuwapatsa khadi olo kuwalembela kakalata.—Akol. 3:15.