LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 February tsa. 3
  • Kodi Mumawaona Makhalidwe Osaoneka a Mulungu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mumawaona Makhalidwe Osaoneka a Mulungu?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Nkhani Zofanana
  • Phunzilani Zambili za Yehova Poyang’ana Cilengedwe Cake
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Gwilitsani Nchito Zacilengedwe Pophunzitsa Ana Anu za Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Mmene Cilengedwe Cimaonetsela Cikondi ca Mulungu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Kodi Mulungu Wosaonekayo Mungamuone?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 February tsa. 3

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mumawaona Makhalidwe Osaoneka a Mulungu?

Mukayang’ana duŵa lokongola, nyenyezi, kapena mathithi a madzi, kodi mumaiona nchito ya Mlengi? Cilengedwe cimene timaona cimaonetsa poyela makhalidwe osaoneka a Yehova. (Aroma 1:20) Tikayang’ana zinthu zimene Mulungu analenga, timakwanitsa kuona mphamvu zake, cikondi, nzelu, na cilungamo, komanso kuwolowa manja kwake.—Sal. 104:24.

Ni zinthu zina ziti zimene Yehova analenga zimene mumaona tsiku lililonse? Olo kuti mukhala mu mzinda waukulu, mungathe kuona mitengo na mbalame. Kuyang’anitsitsa cilengedwe ca Yehova kungatithandize kucepetsako nkhaŵa, kuika maganizo athu pa zinthu zofunika, ndiponso kukulitsa cidalilo cakuti Yehova adzatisamalila kwa moyo wathu wonse. (Mat. 6:25-32) Ngati muli ndi ana, athandizeni kuona makhalidwe osaoneka a Yehova. Kuyamikila cilengedwe cimene timaona, kudzatithandiza kumuyandikila kwambili Mlengi wathu.—Sal 8:3, 4.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI ZODABWITSA ZA CILENGEDWE ZIMAONETSA ULEMELELO WA MULUNGU—KUWALA NA MITUNDU, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILA:

  • N’ciani cimatithandiza kuona mitundu ya zinthu?

  • N’ciani cimapangitsa kuti tiziona mitundu yosiyana-siyana pa cinthu cimodzi?

  • N’cifukwa ciani timaona mitundu yosiyana-siyana m’mitambo?

  • Kodi imwe kwanu mumaona mitundu iti yocititsa cidwi m’cilengedwe?

  • N’cifukwa ciani tifunika kuyang’anitsitsa zinthu za m’cilengedwe?

Duŵa pinki, gulugufe wa buluu, cipatso ca mitundu yosiyana-siyana, ndipo dzuŵa likuloŵa

Kodi kuwala na mitundu zimaonetsa ciani cokhudza makhalidwe a Yehova?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani