LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsa. 13
  • Gulu Limene Limalalikila Aliyense

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Gulu Limene Limalalikila Aliyense
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Munthu Amene Amakamba Cinenelo Cina
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki —Kufikila Munthu Aliyense m’Gawo Lathu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Kugwilizana Polalikila M’gawo la Vitundu Vosiyana-siyana
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 January tsa. 13
M’bale akuseŵenzetsa ‘JW Language’ app pa cipangizo cake.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Gulu Limene Limalalikila Aliyense

Yehova analinganiza Aisiraeli mwadongosolo. Masiku anonso, iye walinganiza anthu ake mwadongosolo kuti acite cifunilo cake. Kuzungulila dziko lonse lapansi, maofesi ya nthambi, madela, mipingo, na tumagulu twa ulaliki, onse amagwilila nchito pamodzi popititsa patsogolo nchito yolengeza uthenga wabwino. Timalalikila aliyense kuphatikizapo amene amakamba citundu cina.—Chiv. 14:6, 7.

Kodi munaganizilapo zophunzila citundu cina n’colinga cakuti muthandize winawake kuphunzila coonadi? Ngakhale kuti mwina mulibe nthawi yokwanila yophunzila citundu cina, mungaseŵenzetse JW Language app kuti muphunzile ulaliki wacidule. Ndipo mukaseŵenzetsa ulaliki umenewu, mudzapeza cimwemwe cofanana na cimene abale a m’nthawi ya atumwi anapeza ataona kuti anthu ocokela ku maiko ena akhudzika pomvela “zinthu zazikulu za Mulungu” m’citundu cawo.—Mac. 2:7-11.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI KHALA BWENZI LA YEHOVA—KULALIKILA M’GAWO LA CITUNDU CINA, PAMBUYO PAKE, YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Khala Bwenzi la Yehova—Kulalikila m’Gawo la Citundu Cina.’ Kalebe akuganizila zakuti kukhala na cipangizo comasulila kungamuthandize polalikila mayi wokamba citundu cina.

    Kodi ni pa nthawi iti pamene JW Language app ingakuthandizeni?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Khala Bwenzi la Yehova—Kulalikila m’Gawo la Citundu Cina.’ Kupeleka moni na tsamba lokhala na mawu oyamba pa ‘JW Language’ app.

    Kodi zina mwa mbali za pa JW Language app n’zotani?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Khala Bwenzi la Yehova—Kulalikila m’Gawo la Citundu Cina.’ Mayi m’modzimodziyo wakondwela pambuyo pakuti Kalebe na Sofiya amupatsa moni mu ci Chinese.

    Anthu a zinenelo zonse afunika kumva uthenga wabwino

    Kodi anthu m’gawo lanu amakamba vitundu viti?

  • Kodi muyenela kucita ciani ngati munthu wina wokamba citundu cina waonetsa cidwi cofuna kumvela uthenga wa Ufumu?—od 100-101 ¶39-41

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani