UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Alongo Angakalamile Bwanji?
Alongo amacita mbali yofunika kwambili pocilikiza nchito ya Ufumu. (Sal. 68:11) Ndiwo amatsogoza maphunzilo a Baibo ambili. Ndipo apainiya oculuka a nthawi zonse ni alongo. Alongo olimbikila ofika m’masauzande amatumikila pa Beteli, ni amishonale, amadzipeleka pa nchito zamamangidwe kapena ni atumiki a nchito zamamangidwe, ndipo ena ni omasulila. Alongo ofikapo mwauzimu amalimbitsa mabanja awo na mipingo. (Miy. 14:1) Ngakhale kuti alongo sangatumikile monga akulu kapena atumiki othandiza, angadziikile zolinga mumpingo. Ngati ndimwe mlongo, kodi mungakalamile m’njila monga ziti?
Kukulitsa makhalidwe abwino acikhristu—1 Tim. 3:11; 1 Pet. 3:3-6
Kuthandiza alongo osadziŵa zambili mumpingo—Tito 2:3-5
Kuwonjezela luso na zocita mu ulaliki
Kuphunzila cinenelo cina
Kusamukila kumene kuli olengeza Ufumu ocepa
Kufunsila kuti muzithandizako pa nchito za pa Beteli kapena pa nchito yomanga malo olambilila
Kufunsila kuti mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu
ONELELANI VIDIYO YAKUTI “AKAZI OGWILA NCHITO MWAKHAMA POTUMIKILA AMBUYE”, NDIYENO YANKHANI FUNSO ILI:
Kodi zimene aliyense wa alongowa wakamba zakulimbikitsani bwanji?