CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Tengelani Citsanzo ca Mmene Yehova Amalamulila
Yehova ni Wolamulila wamkulu kwambili (1 Maf. 22:19; it-2 21)
Yehova amalemekeza amene amawalamulila (1 Maf. 22:20-22; w21.02 4 ¶9)
Yehova anadalitsa zimene mngelo anacita (1 Maf. 22:23; it-2 245)
Akulu maka-maka, komanso mitu ya mabanja ayenela kutengela citsanzo ca mmene Yehova amalamulila. (Aef. 6:4; 1 Pet. 3:7; 5:2, 3) Akamacita zimenezi, anthu amene amawayang’anila amakhala acimwemwe.