LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp21 na. 2 tsa. 3
  • Tifunikila Dziko Labwino!

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tifunikila Dziko Labwino!
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Nkhondo Zidzatha Liti?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
    Nkhani Zina
  • Russia Athila Nkhondo Ukraine
    Nkhani Zina
  • Njala Padziko Lonse Yawonjezeka Cifukwa ca Nkhondo Komanso Kusintha kwa Nyengo—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
    Nkhani Zina
  • Kuyankha Mafunso a M’baibulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
wp21 na. 2 tsa. 3
Munthu akuyang’ana kumbali cifukwa coipidwa na nyuzi zomvetsa cisoni zimene wamvela. Iye waona zithunzi zambili za nkhondo, matenda, umphawi, ciwawa, na zinthu zina zambili zotayitsa mtima.

Tifunikila Dziko Labwino!

“Tikukhala m’dziko lodzala na mavuto,” anatelo António Guterres, kalembela wamkulu wa bungwe la United Nations. Kodi si zoona zimene anakamba?

Nthawi zambili pa nyuzi timamvela nkhani zodetsa nkhawa monga za:

  • Matenda na milili

  • Matsoka a zacilengedwe

  • Umphaŵi na njala

  • Kuwonongeka kwa cilengedwe na kutentha kwa padziko

  • Upandu, ciwawa, na katangale

  • Nkhondo

N’zosacita kufunsa kuti tifunikila dziko labwino. Dziko limene

  • Tidzakhalamo tili na thanzi labwino

  • Aliyense adzakhala wotetezeka

  • Mudzakhala cakudya coculuka

  • Lidzakhala lokongola

  • Aliyense adzacitilidwa zinthu mwacilungamo

  • Mudzakhala mtendele

Koma kodi titanthauza ciani tikanena kuti dziko labwino?

Kodi n’ciani cidzacitikila dziko limene tikukhalamoli?

Nanga tingacite ciani kuti tikakhalemo m’dziko labwino?

Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda, ifotokoza mayankho a m’Baibo okhazika mtima pansi pa mafunso amenewa na ena.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani