MBILI YANGA
“Tsopano Nimaukonda Ulaliki!”
N’NAKULILA m’tauni ya Balclutha ku South Island m’dziko la New Zealand. Nili mwana, n’nali kuona kuti nili pafupi na Yehova, ndipo coonadi n’nali kucikonda. Misonkhano siinali yotopetsa kwa ine, ndipo mpingo unali malo anga acitetezo komanso acimwemwe. Ngakhale kuti n’nali wamanyazi, n’nali kukondwela kutengako mbali mu ulaliki wiki iliyonse. Sin’nali kuopa kulalikila anzanga a kusukulu na ena. N’nali kunyadila kuchedwa Mboni ya Yehova, ndipo n’tafika zaka 11, n’napatulila moyo wanga kwa Mulungu.
N’NATAYA CIMWEMWE CANGA
Zacisoni n’zakuti n’tafika zaka zaunyamata, ubwenzi wanga na Yehova unayamba kuzilala. N’nali kuona kuti anzanga a kusukulu ali na ufulu woculuka, ndipo n’nayamba kuganiza kuti nikumanidwa. N’nali kuona kuti kutsatila malamulo a makolo na mfundo zacikhristu n’kolemetsa, ndipo kucita zinthu zauzimu n’nali kukuona kukhala cinchito ngako. Ngakhale kuti sin’nakayikilepo zakuti Yehova aliko, umoyo wauzimu unayamba kumveka wosanunkha kanthu kwa ine.
Komabe, sin’nali kufuna kukhala wozilala. Conco n’nali kulalikila mwa apa na apo. Popita mu ulaliki sin’nali kukonzekela, moti zinayamba kunivuta kuyambitsa makambilano na kuwapitiliza. Mwa ici, ulaliki wanga unakhala wosabala zipatso ndiponso wosasangalatsa. Izi zinangowonjezela kaonedwe kanga ka zinthu kolakwika. Poona izi, n’nayamba kudzifunsa kuti, ‘Na mmene ulaliki ukuvutilamu, kodi munthu angakwanitse kulalikila mlungu na mlungu, mwezi na mwezi?’
N’tafika zaka 17, n’natengekelatu na maganizo ofuna kudziimila panekha. Conco, n’nalonga zinthu zanga muvyola, kucoka panyumba, na kupita ku Australia. Cinali covuta kwa makolo anga kuniona nikucoka panyumba. Iwo anada nkhawa, koma anali kuganiza kuti nidzapitiliza kucita zinthu zauzimu.
Ku Australia, umoyo wanga wauzimu unaloŵelatu pansi. N’nayamba kupita ku misonkhano mwa apa na apo. N’nagwilizana na acicepele anzanga amene amati akapezeka ku misonkhano wiki ino, wiki yamaŵa n’kupita kukamwa na kuvina m’manaitikalabu. Nikayang’ana kumbuyo, nimaona kuti panthawiyo mwendo wanga wina unali m’coonadi, pamene wina unali kudziko. Sin’nali kudziŵa kuti n’nali mbali iti kweni-kweni.
MOSAYEMBEKEZELA N’NAPHUNZILA KENA KAKE
Patapita zaka monga ziŵili, n’nakumana na mlongo wina amene mosadziŵa ananipangitsa kuyambanso kuganizila za umoyo wanga. N’nali kukhala m’nyumba imodzi na alongo asanu osakwatiwa. Ndipo tinaitanila woyang’anila dela na mkazi wake Tamara, kuti adzakhale kunyumba kwathu kwa mlungu umodzi. Pamene woyang’anila delayo anali kusamalila zampingo, mkazi wake Tamara anali kuceza nafe tikumaseka momasukilana ndithu. Ndipo zinanikondweletsa kwambili zimenezi. Anali wosadzikonda, ndipo anali womasuka. N’nadabwa kuona kuti munthu wokhwima bwino mwauzimu, n’kukhalanso wocezeka conco.
Mlongo Tamara anali kukamba mwaumoyo. Kukonda kwake coonadi na ulaliki zinali kukhudzanso anthu ena. Iye anali kukondwela kupatsa Yehova zonse zimene angathe, pamene ine amene sin’nali kucita zambili mu utumiki n’nalibe cimwemwe. Kapenyedwe kake koyenela ka zinthu, komanso cimwemwe ceni-ceni cimene anali naco, zinanithandiza kuti nisinthe umoyo wanga. Citsanzo cake cinanilimbikitsa kuganizila mfundo ya m’Malemba iyi: Yehova amafuna kuti tonsefe tizim’tumikila “mokondwela” komanso ‘kufuula mosangalala.’—Sal. 100:2.
KUYATSANSO CIKONDI CANGA PA ULALIKI
N’nafuna kukhala na cimwemwe cimene mlongo Tamara anali naco. Koma kuti zimenezo zitheke, n’nafunika kupanga masinthidwe aakulu. Panapita nthawi, koma n’nayamba masitepu a pang’ono pang’ono. N’nayamba kukonzekela ulaliki, ndipo n’nali kucitako upainiya wothandiza nthawi na nthawi. Izi zinanithandiza kuthetsa mantha anga, ndipo n’nayamba kukhala na cidalilo. Pamene n’nali kuseŵenzetsa kwambili Baibo mu ulaliki, n’nali kusangalala kwambili na ulaliki. Posapita nthawi, n’nayamba kucita upainiya wothandiza mwezi uliwonse.
Apa lomba n’nayamba kuyanjana na mabwenzi a misinkhu yonse, ocita bwino m’coonadi, komanso osangalala na utumiki wawo kwa Yehova. Citsanzo cawo cabwino cinanithandiza kupendanso zinthu zimene nimaika patsogolo mu umoyo wanga, na kukhala na pulogilamu yabwino yocita zinthu zauzimu. N’nayamba kukonda kwambili ulaliki, ndipo m’kupita kwa nthawi, n’nakhala mpainiya wanthawi zonse. Kwanthawi yoyamba m’zaka zambili, n’namva kuti ndine wokhazikika mumpingo, komanso wacimwemwe.
N’NAPEZA MPAINIYA MNZANGA WACIKHALILE
Patapita caka cimodzi, n’nakumana na Alex, munthu wokoma mtima komanso wokhulupilika, amenenso anali kukonda Yehova na ulaliki. Iye anali mtumiki wothandiza, ndipo anali atacita upainiya kwa zaka 6. Cina, m’bale Alex anatumikilapo kumalo osoŵa ku Malawi kwa kanthawi. Kumeneko, anali kuyanjana na amishonale amene anali citsanzo cabwino kwa iye, ndipo anamulimbikitsa kupitiliza kuika zinthu za Ufumu patsogolo.
Mu 2003, ine na Alex tinakwatilana ndipo tikupitiliza kucita utumiki wanthawi zonse. Taphunzila zoculuka, ndipo Yehova watidalitsa m’njila zambili.
KHOMO LA MADALITSO OWONJEZELEKA LINATITSEGUKILA
Tili mu ulaliki m’tauni ya Gleno, ku Timor-Leste
Mu 2009, tinatumizidwa kukatumikila monga amishonale ku Timor-Leste, dziko laling’ono ku cimodzi mwa zisumbu zing’ono-zing’ono ku Indonesia. Tinadabwa, tinakondwela, komanso panthawi imodzimodzi tinacita mantha. Pambuyo pa miyezi isanu, tinafika mu mzinda wa Dili, likulu la dziko la Timor-Leste.
Kusamuka kunafuna kuti tisinthe zinthu zambili mu umoyo wathu. Tinafunika kuzoloŵela cikhalidwe catsopano, kuphunzila citundu, kuzoloŵela zakudya zatsopano, na umoyo wa kumeneko. Kambili mu ulaliki, tinali kukumana na anthu osauka, osaphunzila, komanso opondelezedwa. Ndipo tinali kuona anthu ambili amene anavulazidwa pankhondo, ndiponso opsinjika maganizo.a
Utumiki unali wosangalatsa kwambili! Mwacitsanzo, n’nakumana na mtsikana wina wa zaka 13 dzina lake Maria,b amene anali kuoneka wacisoni. Amayi ake anali atamwalila zaka zingapo kumbuyoko, ndipo atate ake sanali kuwaona kaŵili-kaŵili. Mofanana na ana ambili a msinkhu wake, Maria sanali kudziŵa kuti umoyo wake ukuloŵela kuti. Nikumbuka nthawi ina analila pamene anali kufotokoza mmene anali kumvelela. Komabe, sin’nali kumvetsa zimene anali kukamba cifukwa pa nthawiyo, n’nali nisanadziŵe kukamba bwino citundu cake. N’napemphela kwa Yehova, kum’pempha kuti anithandize kumulimbikitsa. Kenako n’nayamba kumuŵelengela malemba olimbikitsa. Patapita zaka zingapo, n’naona mmene coonadi cinasinthila kaonedwe ka zinthu ka Maria, maonekedwe ake, na umoyo wake. Iye anabatizika, ndipo tsopano amatsogoza maphunzilo ake a Baibo. Tsopano, Maria ali na banja lalikulu lauzimu, ndipo amaona kuti amakondedwa.
Yehova akudalitsa nchito yolalikila ku Timor-Leste. Ngakhale kuti ofalitsa ambili anabatizika m’zaka 10 zapitazi, ambili akutumikila monga apainiya, atumiki othandiza, kapena akulu. Ena akutumikila m’maofesi omasulila mabuku, ndipo akuthandiza kupeleka cakudya cauzimu m’zinenelo za m’dzikolo. Zinanikondweletsa kwambili kuwaona akuimba pamisonkhano, kuona nkhope zawo zili zacimwemwe, ndiponso kuona kuti akupita patsogolo mwauzimu.
Nili na Alex, pa ulendo wopita ku gawo losafoledwa kaŵili-kaŵili kukagaŵila tumapepala toitanila anthu ku Cikumbutso.
UMOYO UNALI WOSANGALATSA KWAMBILI KUPOSA MMENE N’NALI KUGANIZILA
Umoyo ku Timor-Leste unali wosiyana kwambili na ku Australia, koma unali wokondweletsa ngako. Nthawi zina, tinali kukwela basi yaing’ono yodzala na anthu, komanso nsomba zouma, na ndiyo zamasamba kucokela ku msika. Nthawi zina, tinali kutsogoza phunzilo la Baibo m’kanyumba kakang’ono kotentha komanso kadothi, ndipo nkhuku zinali kungothamanga-thamanga. Ngakhale kuti panali zopinga zimenezi, mu mtima n’nali kukamba kuti, ‘Izi n’zocitsa cidwi!’
Tili pa ulendo wopita ku gawo
Nikayang’ana kumbuyo, nimawayamikila zedi makolo anga pocita zonse zotheka kuti aniphunzitse njila za Yehova, na kunicilikiza ngakhale m’zaka zovuta zacitsikana canga. Miyambo 22:6 yakwanilitsidwa pa ine. Amayi na atate, amatinyadila ine na Alex, ndipo amakondwela kuona kuti Yehova akutiseŵenzetsa. Kucokela mu 2016 takhala tikutumikila mu nchito ya m’dela m’gawo la nthambi ya Australasia.
Nikuonetsa vidiyo ya Kalebe na Sofiya kwa ana ena acimwemwe a ku Timor-Leste
Sinikhulupilila kuti poyamba ulaliki n’nali kuuona kukhala cinchito colemetsa. Koma lomba nimaukonda ngako! Nafika pozindikila kuti mosasamala kanthu za mavuto a paumoyo, cimwemwe ceni-ceni cimabwela cifukwa cotumikila Mulungu na mtima wonse. Kukamba zoona, zaka 18 zimene takhala tikutumikila Yehova pamodzi na Alex, zakhala zosangalatsa kwambili mu umoyo wanga. Tsopano naona kuti mawu amene wamasalimo Davide anakamba kwa Yehova ni oona. Iye anati: “Onse othaŵila kwa inu adzakondwa. Adzafuula mokondwela mpaka kalekale. . . . Okonda dzina lanu adzakondwa cifukwa ca inu.”—Sal. 5:11.
N’zosangalatsa kuphunzila Baibo na anthu odzicepetsa ngati amenewa!
a Kuyambila mu 1975, dziko la Timor-Leste linali pa nkhondo yomenyela ufulu wodziimila palokha kwa zaka makumi aŵili.
b Maina ena asinthidwa.