LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w21 November masa. 8-13
  • Pitilizani Kuonetsana Cikondi Cosasintha

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pitilizani Kuonetsana Cikondi Cosasintha
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • NDANI AMENE TIYENELA KUONETSA CIKONDI COSASINTHA?
  • KODI TINGAPHUNZILE CIANI M’BUKU LA RUTE PA NKHANI YA CIKONDI COSASINTHA?
  • KODI TINGACIONETSE MOTANI CIKONDI COSASINTHA MASIKU ANO?
  • KODI AMENE AMONETSA CIKONDI COSASINTHA AMAPINDULA BWANJI?
  • Rute na Naomi
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Rute Ndi Naomi
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Yehova Amapulumutsa Anthu Olefuka Mtima
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
w21 November masa. 8-13

NKHANI YOPHUNZILA 45

Pitilizani Kuonetsana Cikondi Cosasintha

“Muzisonyezana kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha] ndi cifundo.”—ZEK. 7:9.

NYIMBO 107 Cikondi ca Umulungu

ZIMENE TIKAMBILANEa

1-2. Kodi pali zifukwa zabwino ziti zoonetselana cikondi cosasintha?

PALI zifukwa zabwino zoonetselana cikondi cosasintha. Kodi zina mwa zifukwazo n’ziti? Onani mmene miyambi ya m’Baibo yotsatilayi iyankhila funso limeneli: “Usasiye kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha] ndi coonadi. . . . Mulungu ndi anthu adzakukomela mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikila.” “Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha] amapindulitsa moyo wake.” “Amene akufuna-funa cilungamo ndiponso kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha] adzapeza moyo.”—Miy. 3:3, 4; 11:17; 21:21.

2 Miyambi imeneyi yachula zifukwa zimene tiyenela kuonetsela cikondi cosasintha. Coyamba, kuonetsa khalidwe limeneli kumatipangitsa kukhala a mtengo wapatali kwa Mulungu. Caciŵili, tikaonetsa cikondi cosasintha, timapindula ife eni. Mwacitsanzo, timapanga maubwenzi okhalitsa na ena. Cacitatu, kuonetsa cikondi cosasintha kudzatithandiza kukalandila madalitso kutsogolo, kuphatikizapo moyo wosatha. Kukamba zoona, tili na zifukwa zabwino zomvela mawu a Yehova akuti: “Muzisonyezana kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha] ndi cifundo.”—Zek. 7:9.

3. Kodi tikambilane mafunso ati m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tikambilane mayankho pa mafunso anayi aya: Ndani amene tiyenela kuonetsa cikondi cosasintha? Kodi tingaphunzile ciani m’buku la Rute pa nkhani yoonetsa cikondi cosasintha? Nanga tingaonetse motani cikondi cosasintha masiku ano? Kodi amene amaonetsa cikondi cosasintha amapindula bwanji?

NDANI AMENE TIYENELA KUONETSA CIKONDI COSASINTHA?

4. Tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova pa nkhani yoonetsa cikondi cosasintha?

4 Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, Yehova amaonetsa cikondi cosasintha kwa okhawo amene amam’konda na kum’tumikila. Iye amatelo mwa kumamatila kwa iwo mokhulupilika. (Dan. 9:4) Tiyenela ‘kutsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa.’ (Aef. 5:1) Conco, tiziwaonetsa cikondi cotelo abale na alongo athu auzimu, mwa kumamatila kwa iwo mokhulupilika.—Ŵelengani Maliko 10:29, 30.

5-6. Kodi kukhulupilika kungatanthauze ciani?

5 Ndithudi, inunso mungavomeleze kuti tikamvetsetsa tanthauzo la cikondi cosasintha, m’pamene tingacionetse bwino kwa alambili anzathu. Koma kuti timvetsetse tanthauzo la cikondi cosasintha, tiyeni tione kusiyana kwake na kukhulupilika cabe, kumene anthu ambili amadziŵa bwino tanthauzo lake. Ganizilani citsanzo ici.

6 Munthu amene waseŵenza pa kampani kwa zaka zambili, timanena kuti ni wanchito wokhulupilika. Zingatheke kuti pa zaka zonse zimene wagwila nchito pa kampaniyo, eni ake a kampani sanaonanepo nawo. Ndipo nthawi zina, iye sangagwilizane na malamulo a kampaniyo, ngakhale kusaikonda kumene. Koma amafunabe kugwila nchitoyo cifukwa amalandila ndalama. Iye angapitilize kugwilabe nchito pa kampaniyo mpaka pokacita lithaya, kupatula ngati angapeze nchito ina yabwino kuposa imene akugwilayo.

7-8. (a) N’ciani cimasonkhezela munthu kuonetsa ena cikondi cosasintha? (b) Kodi tikambilane macaputala ena m’buku la Rute cifukwa ciani?

7 Malinga na ndime 6, kusiyana kumene kulipo pakati pa kukhulupilika cabe na cikondi cosasintha, ni colinga cimene munthu angakhale naco pa kukhulupilika kwake. M’nthawi za m’Baibo, n’ciani cinasonkhezela anthu a Mulungu kuonetsa cikondi cosasintha? Anthu amene anaonetsa khalidwe limeneli, anacita zimenezo osati mokakamizika na mkhalidwe uliwonse, koma cifukwa cofunitsitsa kucokela pansi pa mtima. Ganizilani citsanzo ca Davide. Mtima wake unali wofunitsitsa kuonetsa cikondi cosasintha kwa bwenzi lake la pa mtima Yonatani, ngakhale kuti tate wake Yonatani anali kufuna kumupha Davide. Patapita zaka Yonatani atafa, Davide anapitilizabe kuonetsa cikondi cosasintha kwa Mefiboseti mwana wa Yonatani.—1 Sam. 20:9, 14, 15; 2 Sam. 4:4; 8:15; 9:1, 6, 7.

8 Tingaphunzile zambili pa nkhani ya cikondi cosasintha, tikaŵelenga macaputala ena a m’buku la Rute. Kodi tingaphunzile ciani zokhudza cikondi cosasintha kwa anthu ochulidwa m’bukuli? Nanga zimene tikuphunzilapo tingaziseŵenzetse bwanji mu mpingo mwathu?b

KODI TINGAPHUNZILE CIANI M’BUKU LA RUTE PA NKHANI YA CIKONDI COSASINTHA?

9. N’cifukwa ciani Naomi anaganiza kuti Yehova wamuukila?

9 M’buku la Rute, timaŵelenga za Naomi, mpongozi wake Rute, komanso munthu woopa Mulungu dzina lake Boazi, amene anali wacibale wa mwamuna wa Naomi. Cifukwa cakuti mu Isiraeli munagwa njala, Naomi, mwamuna wake, komanso ana awo aŵili, anasamukila ku Mowabu. Kumeneko, mwamuna wa Naomi anamwalila. Ana ake aŵili anakwatila, koma n’zacisoni kuti naonso anamwalila. (Rute 1:3-5; 2:1) Naomi anafika potaya mtima cifukwa ca mavuto amenewa. Iye anapsinjika maganizo kwambili cifukwa ca cisoni, moti anaganiza kuti Yehova wamuukila. Ponena za Mulungu, iye anati: “Dzanja la Yehova landiukila.” “Wamphamvuyonse wacititsa moyo wanga kukhala woŵaŵa kwambili.” Anakambanso kuti: “Ndi Yehova amene wandicititsa kukhala wonyozeka, ndipo ndi Wamphamvuyonseyo amene wandigwetsela tsokali.”—Rute 1:13, 20, 21.

10. Kodi Yehova anacitapo ciani pa zimene Naomi anakamba?

10 Kodi Yehova anacitapo ciani pa zimene Naomi anakamba? Iye sanaleke kuthandiza mtumiki wake wopsinjika maganizo ameneyu, ndipo anamuonetsa cifundo. Yehova amadziŵa kuti “kupondelezedwa kumapangitsa munthu wanzelu kucita zinthu zopanda nzelu.” (Mlal. 7:7) Ngakhale n’conco, Naomi anafunikila thandizo kuti aone kuti Yehova anali kumbali yake. Kodi Mulungu anam’thandiza motani? (1 Sam. 2:8) Iye anakhudza mtima wa Rute kuti athandize Naomi, na kumuonetsa cikondi cosasintha. Modzipeleka komanso mwacikondi, Rute anathandiza apongozi ake kupezanso mphamvu mwauzimu. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Rute?

11. N’cifukwa ciani abale na alongo okoma mtima amathandiza anthu opsinjika maganizo?

11 Cikondi cosasintha cimatilimbikitsa kuthandiza opsinjika maganizo. Mofanana na Rute amene anamamatila kwa Naomi, abale na alongo okoma mtima, modzipeleka amathandiza ena mu mpingo amene ni opsinjika maganizo. Iwo amawakonda ngako abale na alongo awo, ndipo amacita zonse zotheka kuti awathandize. (Miy. 12:25; 24:10) Izi n’zimene mtumwi Paulo anatilimbikitsa kucita pamene anati: “Lankhulani molimbikitsa kwa amtima wacisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.”—1 Ates. 5:14.

M’bale akumvetsela mwachelu pamene m’bale mnzake akufotokoza.

Mwa kumvetsela, tingathandize m’bale kapena mlongo wolefuka (Onani ndime 12)

12. Ni njila iti yabwino imene tingathandizile m’bale kapena mlongo wolefuka?

12 Nthawi zambili, njila yabwino imene tingathandizile m’bale kapena mlongo wolefuka, ni kumumvetsela mwachelu, komanso kumutsimikizila kuti timam’konda. Yehova amaona zabwino zimene tingacitile nkhosa zake za mtengo wapatali. (Sal. 41:1) Miyambo 19:17 imati: “Wokomela mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezela zimene anacitazo.”

Rute akumamatila Naomi mpongozi wake, ndipo Olipa akubwelela ku Mowabu. Rute akuuza Naomi kuti: “Kumene inu mupite inenso ndipita komweko.” (Onani ndime 13)

13. Kodi Rute anali wosiyana bwanji na Olipa? Nanga Rute anaonetsa motani cikondi cosasintha? (Onani cithunzi pacikuto.)

13 Timamvetsanso bwino zimene cikondi cosasintha cimatanthauza, tikaganizila zinacitika kwa Naomi, mwamuna wake, komanso ana ake atamwalila. Naomi atamvela kuti “Yehova wakumbukila anthu ake powapatsa cakudya,” anaganiza zobwelela kwawo. (Rute 1:6) Apongozi ake aŵili ananyamuka naye ulendo umenewo. Koma ali pa ulendowo, Naomi anacondelela apongozi akewo katatu konse kuti abwelele ku Mowabu. N’ciani cinacitika? Timaŵelenga kuti: “Olipa anapsompsona apongozi ake powatsanzika. Koma Rute anawaumililabe.” (Rute 1:7-14) Mwa kusankha kubwelela kwawo, Olipa anatsatila zimene Naomi anamuuza. Komabe, Rute anacita zoposa pamenepo. Nayenso anali na ufulu wobwelela kwawo, koma cifukwa ca cikondi cake cosasintha, anasankha kukhalabe na Naomi wamasiye. (Rute 1:16, 17) Rute anasankha kumamatila kwa Naomi, osati mokakamizika na mkhalidwewo, koma anali wofunitsitsa na mtima wonse. Zimene Rute anacitazo cinali cikondi cosasintha. Kodi tiphunzilapo ciani pa nkhani imeneyi?

14. (a) Kodi abale na alongo acikondi amatengela motani citsanzo ca Rute? (b) Malinga na Aheberi 13:16, kodi Mulungu amakondwela na nsembe zotani?

14 Kuonetsa cikondi cosasintha kumafuna kudzimana. Masiku ano, abale na alongo ambili amaonetsa cikondi cosasintha kwa alambili anzawo, ngakhale kwa anthu amene sawadziŵa n’komwe. Mwacitsanzo, akamvela kuti kwacitika ngozi yacilengedwe, mwamsanga amapeleka thandizo lofunikila. Komanso, akaona kuti wina mu mpingo wakumana na mavuto, iwo amayesetsa kupeleka thandizo lofunikila. Mofanana na Akhristu a ku Makedoniya, iwo amadzimana kwambili. Amaseŵenzetsa nthawi yawo na cuma cawo, “ngakhale zoposa pamenepo,” kuti athandize abale awo amene ali pa mavuto. (2 Akor. 8:3) Yehova amakondwela ngako akaona mzimu wacikondi umenewu!—Ŵelengani Aheberi 13:16.

KODI TINGACIONETSE MOTANI CIKONDI COSASINTHA MASIKU ANO?

15-16. Kodi Rute anaonetsa bwanji kulimbikila?

15 Tingatengepo maphunzilo angapo tikaona mmene Rute anathandizila Naomi. Tiyeni tioneko ocepa cabe.

16 Pitilizani kuwathandiza. Rute atadzipeleka kuti apita na apongozi ake ku Yuda, poyamba Naomi anayesa kum’letsa. Koma Rute sanam’siye Naomi. N’ciani cinacitika? Iye “ataona kuti walimbikila zoti apite naye limodzi, anasiya kumuuza kuti abwelele.” (Rute 1:15-18)

17. N’ciani cingatithandize kupitiliza kupeleka thandizo?

17 Zimene tiphunzilapo: Tizikhala oleza mtima pothandiza munthu wopsinjika maganizo, ndipo tisaleke kum’thandiza. Mlongo amene akufunikila thandizo, poyamba angakane thandizo lathu.c Komabe, cifukwa comuonetsa cikondi cosasintha, tidzamamatilabe kwa iye. (Agal. 6:2) Timadziŵa kuti m’kupita kwa nthawi, iye adzalola kuti tim’thandize pa vuto lakelo.

18. Kodi Rute ayenela kuti anapwetekedwa mtima na ciani?

18 Pewani kukhumudwa. Naomi na Rute atafika ku Betelehemu, Naomi anakumananso na mabwenzi ake akale. Iye anawauza kuti: “Ndinali ndi zonse pocoka kuno, koma Yehova wandibweza wopanda kanthu.” (Rute 1:21) Tangoganizilani mmene Rute anamvelela, atamvela mawu amenewa! Rute anacita zonse zotheka kuti athandize Naomi. Anali kulila naye, kumutonthoza, ndipo anakhala naye kwa nthawi yaitali. Ngakhale zinali conco, Naomi anati: “Yehova wandibweza wopanda kanthu.” Zimene Naomi anakamba zinaonetsa monga kuti sanayamikile thandizo la Rute, amene anaima pafupi naye. Mawu amenewa ayenela kuti anamupweteka mtima Rute. Ngakhale n’telo, iye anamamatilabe kwa Naomi.

19. N’ciani cingatithandize kuti tisamusiye munthu wopsinjika maganizo?

19 Zimene tiphunzilapo: Mlongo wopsinjika maganizo mwina angakambe zinthu zimene zingatikhumudwitse, ngakhale titacita zonse zotheka kuti tim’thandize. Koma ife tisakhumudwe. Tisamusiye mlongo wathuyo amene akufunikila thandizo, ndipo tipemphe Yehova kuti atithandize kupeza njila imene tingamutonthozele.—Miy. 17:17.

Zithunzi: 1. Boazi akukamba na Rute pamene akukunkha m’munda. 2. Mkulu akukambilana na mlongo pa Nyumba ya Ufumu.

Kodi akulu masiku ano angatengele bwanji citsanzo ca Boazi? (Onani ndime 20-21)

20. N’ciani cinalimbikitsa Rute kupitiliza kupeleka thandizo?

20 Pelekani cilimbikitso ca pa nthawi yake. Rute anaonetsa cikondi cosasintha kwa Naomi. Koma nayenso Rute anali kufunikila cilimbikitso. Ndipo Yehova anasonkhezela Boazi kukamulimbikitsa. Boazi anauza Rute kuti: “Yehova akudalitse cifukwa ca zimene wacita, ndipo Yehova, Mulungu wa Isiraeli akufupe mokwanila. Iye amene m’mapiko mwake wathaŵilamo ndi kupezamo citetezo.” Mawu olimbikitsa amenewa, anam’khudza mtima kwambili Rute, moti anayankha Boazi kuti: “Mwanditonthoza mtima, komanso mwalankhula mondilimbitsa mtima.” (Rute 2:12, 13) Mawu a pa nthawi yake a Boazi, analimbikitsa Rute kupitiliza kupeleka thandizo.

21. Malinga na Yesaya 32:1, 2, kodi akulu acikondi ayenela kucita ciani?

21 Zimene tiphunzilapo: Anthu amene amaonetsa cikondi cosasintha, naonso amafunikila cilimbikitso nthawi zina. Monga mmene Boazi anatsimikizila Rute kuti cikondi cake sicinapite pacabe, akulu achelu masiku ano naonso amayamikila thandizo limene abale na alongo acikondi amapeleka kwa ena. Mawu olimbikitsa komanso a pa nthawi yake amenewo, adzapatsa mphamvu abale na alongo kuti apitilize kupeleka thandizo.—Ŵelengani Yesaya 32:1, 2.

KODI AMENE AMONETSA CIKONDI COSASINTHA AMAPINDULA BWANJI?

22-23. Kodi Naomi anasintha motani maganizo ake? Nanga n’cifukwa ciani? (Salimo 136:23, 26)

22 Patapita nthawi, Boazi anapeleka mowolowa manja zakudya kwa Rute na Naomi monga mphatso. (Rute 2:14-18) Kodi Naomi anacita ciani pa kuolowa manja kwa Boazi? Iye anati: “Yehova amene sanaleke kusonyeza kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha] kwa amoyo ndi akufa, am’dalitse munthu ameneyu.” (Rute 2:20a) Apa Naomi anali atasintha mmene anali kuonela zinthu. Poyamba, kwinaku akulila, anati: “Yehova . . . wandicititsa kukhala wonyozeka.” Koma tsopano anakamba mwacisangalalo kuti: “Yehova . . . sanaleke kusonyeza kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha].” N’ciani cinathandiza Naomi kusintha maganizo ake?

23 Potsilizila pake, Naomi anayamba kuona dzanja la Yehova mu umoyo wake. Yehova anaseŵenzetsa Rute kupeleka thandizo lofunikila pa ulendo wawo wopita ku Yuda. (Rute 1:16) Naomi anaonanso dzanja la Yehova pamene Boazi, mmodzi wa ‘owaombola,’ anapeleka mphatso kwa akazi aŵili amenewo.d (Rute 2:19, 20b) Mu mtima, Naomi ayenela anati, ‘Tsopano naona kuti Yehova sananisiye. Iye wakhalabe nane kwa nthawi yonseyi.’ (Ŵelengani Salimo 136:23, 26.) Naomi anayamikila kwambili kuti Rute na Boazi anapitilizabe kum’thandiza! Tangoganizilani cimwemwe cimene onse atatu anali naco poona zotulukapo zabwino.

24. N’cifukwa ciani tiyenela kupitiliza kuonetsa cikondi cosasintha kwa anzathu?

24 Kodi taphunzila ciani m’buku la Rute ponena za cikondi cosasintha? Taphunzila kuti cikondi cosasintha cimatisonkhezela kupitiliza kuthandiza abale na alongo athu amene akumana na mavuto. Kumatisonkhezelanso kukhala odzimana kuti tiwathandize. Cina, akulu ayenela kupeleka cilimbikitso ca pa nthawi yake kwa anthu amene amaonetsa ena cikondi cosasintha. Tikaona kuti anthu amene tathandiza apezanso mphamvu mwauzimu, timakondwela kwambili. (Mac. 20:35) Komabe, n’cifukwa cacikulu citi cimene ciyenela kutipangitsa kupitiliza kuonetsa cikondi cosasintha? Cifukwa timafuna kutengela citsanzo ca Yehova, amene ni “wodzaza ndi kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha],” komanso kum’kondweletsa.—Eks. 34:6; Sal. 33:22.

KODI MUKUMBUKILA?

  • Kodi cikondi cosasintha cimasiyana bwanji na kukhulupilika cabe?

  • Tingatengele bwanji citsanzo ca Boazi komanso Rute poonetsa cikondi cosasintha?

  • Timapindula motani tikamaonetsa ena cikondi cosasintha?

NYIMBO 130 Khalani Wokhululuka

a Yehova amafuna kuti tizionetsa cikondi cosasintha kwa abale na alongo athu mu mpingo. Kuti timvetse bwino tanthauzo la cikondi cosasintha, tiyenela kuona mmene atumiki ena a Mulungu akale anaonetsela khalidwe limeneli. M’nkhani ino, tikambilane zimene tingaphunzile ku citsanzo ca Rute, Naomi, komanso Boazi.

b Kuti mupindule mokwanila na nkhani ino, tikulimbikitsani kuŵelenga pamwekha buku la Rute caputala 1 na 2.

c Cifukwa tikukambilana citsanzo ca Naomi, mfundo zake zipita kwa alongo amene afunikila thandizo. Koma zimagwilanso nchito kwa abale.

d Kuti mudziŵe zambili zokhudza udindo wa Boazi monga wowombola, onani nkhani yakuti, “Tsanzilani Cikhulupililo Cawo—‘Anali Mkazi Wabwino Kwambili,’” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2012, tsa. 19.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani