NKHANI YOPHUNZILA 43
Nzelu Yeniyeni Imafuula
“Nzelu yeniyeni imangokhalila kufuula mumsewu. Imangokhalila kutulutsa mawu ake m’mabwalo a mzinda.”—MIY. 1:20.
NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu
ZIMENE TIKAMBILANEa
1. Kodi anthu ambili amatani tikawagaŵila nzelu ya m’Baibo? (Miyambo 1:20, 21)
M’MAIKO ambili, ofalitsa Ufumu acimwemwe amaimilila m’misewu kugaŵila zofalitsa zathu kwa anthu odutsa. Kodi munayamba mwatengako m’mbali mu ulaliki wapoyela umenewu? Ngati n’conco, mosakayikila munaganizilapo mawu ofanizila opezeka m’buku la Miyambo, akuti nzelu imafuula m’mabwalo a mzinda kuti anthu amvele uphungu wake. (Ŵelengani Miyambo 1:20, 21.) M’Baibo komanso m’zofalitsa zathu, muli “nzelu yeniyeni,” imene ni nzelu ya Yehova. Anthu akufunikila nzelu imeneyo kuti akapeze moyo wosatha. N’cifukwa cake timakondwela wina wake akalandila zofalitsa zathu. Koma si onse amene amalandila. Anthu ena safuna kudziŵa zimene Baibo imanena. Ena amatiseka. Iwo amaona kuti Baibo ni buku lacikale-kale losathandiza. Enanso amatsutsa zimene Baibo imaphunzitsa pa nkhani ya makhalidwe abwino. Amaona kuti anthu amene amatsatila malangizo ake ni odzikonda komanso odzilungamitsa. Ngakhale n’conco, Yehova sanaleke kupeleka nzelu yake yeniyeni kwa anthu onse. Kodi amacita bwanji zimenezi?
2. Kodi nzelu yeniyeni imapelekedwa bwanji masiku ano? Koma kodi anthu ambili amasankha kucita ciyani?
2 Njila imodzi imene Yehova amapelekela nzelu yake, ni kupitila m’Mawu ake Baibo. Pafupifupi anthu onse akhoza kuliŵelenga buku limeneli. Nanga bwanji zofalitsa zathu zozikika pa Baibo? Cifukwa ca dalitso la Yehova, zofalitsa zimenezi zikupezeka m’zinenelo zoposa 1,000. Awo amene amaŵelenga na kugwilitsa nchito zimene aŵelengazo amapindula. Komabe, anthu ambili amasankha kunyalanyaza mawu a nzelu yeniyeni. Akafuna kupanga zisankho, amadalila nzelu zawo kapena kufunsila kwa anthu anzawo. Iwo angafike potiona kuti ndife apansi cifukwa timatsatila zimene Baibo imakamba. Nkhani ino ifotokoza cifukwa cake anthu amacita zimenezi. Koma coyamba, tiyeni tikambilane mmene tingapezele nzelu ya Yehova.
KUDZIŴA YEHOVA NDIKO CIYAMBI CA NZELU
3. Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tipeze nzelu yeniyeni?
3 Nzelu ni luso logwilitsa nchito zimene timadziŵa kuti tipange zisankho zabwino. Koma nzelu yeniyeni imaloŵetsamo zambili. Baibo imati: “Kuopa Yehova ndiko ciyambi ca nzelu. Kudziŵa Woyela Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.” (Miy. 9:10) Conco, tikafuna kupanga cisankho cacikulu, coyamba tiyenela kudziŵa maganizo a Yehova pa cisankhoco. Tingacite zimenezi mwa kufufuza m’Baibo, na m’zofalitsa zozikika pa Baibo. Tikatelo, tidzaonetsa kuti tili na nzelu yeniyeni.—Miy. 2:5-7.
4. N’cifukwa ciyani ni Yehova yekha amene angatipatse nzelu zenizeni?
4 Ni Yehova yekha amene angatipatse nzelu zenizeni. (Aroma 16:27) N’cifukwa ciyani Yehova ndiye Gwelo la nzelu? Coyamba, pokhala Mlengi wathu, iye amadziŵa zonse zokhudza cilengedwe cake. (Sal. 104:24) Caciŵili, zocita zonse za Yehova zimaonetsa nzelu. (Aroma 11:33) Cacitatu, uphungu wanzelu wa Yehova nthawi zonse umapindulila awo amene amaugwilitsa nchito. (Miy. 2:10-12) Conco, kuti tipeze nzelu zenizeni, tiyenela kuvomeleza mfundo za coonadi zimenezi, na kulola kuti zizititsogolela popanga zisankho, komanso pa zocita zathu.
5. Kodi pamakhala zotulukapo zotani anthu akakana kuvomeleza kuti Yehova ndiye Gwelo la nzelu zenizeni?
5 Anthu ambili amene timakumana nawo mu ulaliki amacita cidwi na cilengedwe cokongola. Koma amakana zakuti Mlengi aliko, ndipo amakhulupilila cisanduliko. Ena amene timakumana nawo amati Mulungu amam’khulupilila. Koma amaona kuti mfundo za m’Baibo n’zacikale-kale, ndipo amasankha kutsatila nzelu zawo. Kodi pakhala zotulukapo zotani? Kodi dziko lakhala malo abwino cifukwa cakuti anthu akudalila nzelu zawo m’malo modalila Mulungu? Kodi apeza cimwemwe ceniceni kapena ciyembekezo codalilika ca zam’tsogolo? Zimene timaona m’dzikoli zikutitsimikizila mfundo yoona yakuti: “Palibe nzelu kapena kuzindikila kulikonse, kapena malangizo alionse otsutsana ndi Yehova.” (Miy. 21:30) Izi ziyenela kutilimbikitsa kuyang’ana kwa Yehova kuti atipatse nzelu zenizeni. Koma n’zacisoni kuti anthu ambili sacita zimenezi. Cifukwa ciyani?
CIMENE ANTHU AMAKANILA NZELU ZENIZENI
6. Malinga n’kunena kwa Miyambo 1:22-25, ndani amatseka makutu nzelu yeniyeni ikamafuula?
6 Anthu ambili amatseka makutu pamene nzelu yeniyeni ‘imafuula mumsewu.’ Malinga na Baibo, pali magulu atatu a anthu amene amakana nzelu: “anthu osadziŵa” zinthu, “onyoza,” komanso “opusa.” (Ŵelengani Miyambo 1:22-25.) Tsopano tiyeni tione cifukwa cake anthu amenewa amakana nzelu yaumulungu, komanso mmene tingapewele kukhala monga iwo.
7. N’cifukwa ciyani anthu ena amasankha kukhalabe ‘osadziŵa’ zinthu?
7 “Anthu osadziŵa” zinthu ni aja amene amakhulupilila zilizonse, amatengeka mosavuta, kapena kusoceletsedwa. (Miy. 14:15) Mwacitsanzo, ganizilani za anthu mamiliyoni amene amasoceletsedwa na atsogoleli acipembedzo komanso andale. Ena amadabwa kwambili komanso kukhumudwa akatulukila kuti atsogoleli awo akhala akuwapusitsa. Koma anthu ochulidwa pa Miyambo 1:22 amasankha kukhalabe osadziŵa zinthu cifukwa n’zimene amaona kuti zili bwino. (Yer. 5:31) Iwo amakonda kucita zimene mtima wawo umafuna, ndipo safuna kuphunzila zimene Baibo imakamba kapena kumvela malamulo ake. Anthu ambili amamva mmene anamvela mayi wina wopembedza kwambili ku Quebec, ku Canada. Mayiyo anauza Mboni ina kuti, “Ngati wansembe amatisoceletsa, ilo ni vuto lake osati lathu.” Ife sitifuna olo pang’ono kutsatila anthu amene mwadala amafuna kukhala osadziŵa zinthu.—Miy. 1:32; 27:12.
8. N’ciyani cingatithandize kukhala anthu odziŵa zinthu?
8 Pa cifukwa cabwino, Baibo imatilimbikitsa kuti tisamakhale anthu osadziŵa zinthu, koma tikhale aakulu msinkhu pa luntha la kuzindikila. (1 Akor. 14:20) Timakhala anthu odziŵa zinthu tikamagwilitsa nchito mfundo za m’Baibo pa umoyo wathu. Pang’ono-m’pang’ono, timaona mmene mfundozo zimatithandizila kupewa mavuto, komanso kupanga zisankho zanzelu. Ndipo n’canzelu kudziunika kuti tione mmene tikupitila patsogolo. Ngati takhala tikuphunzila Baibo kwa nthawi yaitali na kupezeka ku misonkhano, tingadzifunse cifukwa cake pofika pano, sitinatenge sitepe lakuti tidzipatulile kwa Yehova na kubatizika. Ngati ndife obatizika, kodi tikupita patsogolo monga mlaliki na mphunzitsi wa uthenga wabwino? Kodi zisankho zathu zimaonetsa kuti timatsogoleledwa na mfundo za m’Baibo? Kodi timaonetsa makhalidwe acikhristu pocita zinthu na ena? Tikaona kuti tifunika kuwongolela, tiyenela kuganizila mozama zikumbutso za Yehova, zimene “zimapatsa nzelu munthu wosadziŵa zinthu.”—Sal. 19:7.
9. Kodi anthu “onyoza” amaonetsa bwanji kuti amakana nzelu yaumulungu?
9 Gulu laciŵili limene limakana nzelu yaumulungu, ni anthu “onyoza.” Nthawi zina, timapeza anthu otelo tikamalalikila. Iwo amakonda kunyoza ena. (Sal. 123:4) Baibo inakambilatu kuti m’masiku otsiliza, anthu adzakhala onyoza. (2 Pet. 3:3, 4) Mofanana na akamwini a Loti munthu wolungama, anthu ena masiku ano safuna kumvela macenjezo a Mulungu. (Gen. 19:14) Ambili amaseka anthu amene amatsatila mfundo za m’Baibo. Ndipo anthu onyoza amenewo amacita zimenezi cifukwa cotsatila “zilakolako zawo pa zinthu zonyoza Mulungu.” (Yuda 7, 17, 18) Mmene Baibo imafotokozela anthu onyoza amenewa, zimagwilizana na khalidwe la ampatuko, komanso anthu amene amakana Yehova.
10. Malinga na Salimo 1:1, kodi tingapewe motani kutengela khalidwe la anthu onyoza?
10 Kodi tingadziteteze motani kuti tisatengele khalidwe la anthu onyoza amenewo? Njila imodzi ni kusagwilizana nawo anthu amene amakonda kudandaula pa ciliconse. (Ŵelengani Salimo 1:1.) Izi zitanthauza kuti sitiyenela kumvetsela kapena kuŵelenga nkhani za ampatuko. Timadziŵa kuti tikapanda kusamala, tingakhale na mzimu wotsutsa, na kuyamba kukayikila Yehova komanso citsogozo cimene timalandila kupitila m’gulu lake. Kuti tipewe khalidwe limeneli, tingadzifunse kuti: ‘Kodi nthawi zambili nimakonda kudandaula tikalandila malangizo atsopano, kapena pakakhala kusintha kwa kamvedwe kathu? Kodi nimakonda kupeza zifukwa abale amene akutsogolela?’ Ngati tingathetse khalidwe limeneli mwamsanga, Yehova adzakondwela nafe.—Miy. 3:34, 35.
11. Kodi anthu “opusa” amawaona bwanji malamulo a Yehova?
11 Gulu lacitatu limene limakana nzelu ni anthu “opusa.” Iwo ni opusa cifukwa amakana kutsatila malamulo a Mulungu. Amacita zimene n’zabwino m’maso mwawo. (Miy. 12:15) Anthu otelo amakana Yehova, Gwelo la nzelu. (Sal. 53:1) Tikakumana nawo mu ulaliki, nthawi zambili iwo amatitsutsa kwambili cifukwa timalemekeza mfundo za m’Baibo. Koma zoona zake n’zakuti iwo sangatithandize kukhala na umoyo wabwino. Baibo imati: “Kwa munthu wopusa, nzelu zenizeni n’cinthu capatali. Iye satsegula pakamwa pake pacipata ca mzinda.” (Miy. 24:7) Inde, anthu opusa amenewa, m’mawu awo mulibe nzelu olo pang’ono. N’cifukwa cake Yehova amaticenjeza ‘kucoka pamaso pa munthu wopusa.—Miy. 14:7.
12. N’ciyani cingatithandize kupewa zocita za anthu opusa?
12 Mosiyana nawo anthu odana na uphungu wa Mulungu, ife timakonda kwambili njila zake, kuphatikizapo malamulo ake. Tingakulitse cikondi cimeneco poyelekezela zotulukapo zimene zimakhalapo ngati munthu amamvela, komanso ngati samvela. Ganizilani mavuto amene anthu amadzibweletsela pokana mwadala uphungu wanzelu wa Yehova. Kenako, ganizilani mmene umoyo wanu ulili wabwino cifukwa comvela Mulungu.—Sal. 32:8, 10.
13. Kodi Yehova amatikakamiza kumvela uphungu wake wanzelu?
13 Yehova amapeleka nzelu kwa aliyense, koma sakakamiza munthu kuitsatila. Komabe, iye amanena zimene zimacitika kwa anthu okana kumvetsela nzelu yake. (Miy. 1:29-32) Amene asankha kusamvela Yehova “adzadya zipatso za njila yawo.” M’kupita kwa nthawi, khalidwe lawo limawabweletsela mavuto, ndipo pamapeto pake adzawonongedwa. Koma anthu amene amamvela uphungu wanzelu wa Yehova na kuugwilitsa nchito, amawalonjeza kuti: “Munthu wondimvela adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka cifukwa coopa tsoka.”—Miy. 1:33.
NZELU YENIYENI IMATIPINDULILA
Kupelekapo ndemanga pa misonkhano kumatithandiza kukhala olimba mwauzimu (Onani ndime 15)
14-15. Kodi tiphunzilapo ciyani pa Miyambo 4:23?
14 Tikamatsatila nzelu za Mulungu, nthawi zonse timapindula. Monga takambila kale, Yehova wapangitsa nzelu zake kukhala zosavuta kupeza. Mwacitsanzo, m’buku lonse la Miyambo, muli uphungu wothandiza umene tingapindule nawo tikamaugwilitsa nchito. Tiyeni tioneko zitsanzo zinayi za uphungu wanzelu umenewo.
15 Tetezani mtima wanu wophiphilitsa. Baibo imati: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenela kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” (Miy. 4:23) Ganizilani zimene timacita kuti titeteze mtima wathu weniweni. Timadya zakudya zopatsa thanzi, kucita maseŵela olimbitsa thupi, na kupewa zizoloŵezi zoipa. Timacitanso cimodzimodzi poteteza mtima wathu wophiphilitsa. Tsiku lililonse, timadya Mawu a Mulungu. Timakonzekela misonkhano, kukapezekapo, na kupelekapo ndemanga. Cina, timakhala okangalika mwa kulalikila nthawi zonse. Ndipo timapewa kukhala na zizoloŵezi zoipa mwa kukaniza ciliconse cimene cingasokoneze maganizo athu, monga zosangulutsa zoipa komanso mayanjano oipa.
Kuona ndalama moyenela kumatithandiza kukhala okhutila na zimene tili nazo (Onani ndime 16)
16. N’cifukwa ciyani mfundo ya pa Miyambo 23:4, 5 ni yothandiza masiku ano?
16 Muzikhutila na zimene muli nazo. Baibo imapeleka langizo ili lakuti: “Usamadzitopetse ndi nchito kuti upeze cuma. . . . Kodi maso ako amayang’anitsitsa cuma, pomwe ico sicicedwa kucoka? Cifukwa ndithu cimadzipangila mapiko ngati a ciwombankhanga n’kuulukila kumwamba.” (Miy. 23:4, 5) Cuma cakuthupi cilibe maziko okhalitsa. Komabe, masiku ano anthu olemela komanso osauka amadzitopetsa kufuna-funa cuma. Kudzitangwanitsa kotelo nthawi zambili kumawapangitsa kucita zinthu zimene zimawononga mbili yawo, ubwenzi wawo na ena, komanso ngakhale thanzi lawo. (Miy. 28:20; 1 Tim. 6:9, 10) Kumbali ina, nzelu zimatithandiza kuona ndalama moyenela. Kaonedwe kameneka kamatithandiza kupewa kukhala adyela, ndipo timakhala okhutila komanso acimwemwe.—Mlal. 7:12.
Kuyamba taganiza tisanalankhule kumatithandiza kupewa kupweteka ena na mawu athu (Onani ndime 17)
17. Kodi tingakhale bwanji na “lilime la anthu anzelu” lochulidwa pa Miyambo 12:18?
17 Muziyamba mwaganiza musanalankhule. Ngati sitisamala, mawu athu akhoza kupweteka ena. Baibo imati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizila ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzelu limacilitsa.” (Miy. 12:18) Timateteza ubale wathu na anthu ena ngati timapewa kuwajeda pa zolakwa zawo. (Miy. 20:19) Kuti mawu athu akhale ocilitsa osati opweteka ena, tiyenela kudzaza mitima yathu na cidziŵitso copezeka m’Mawu a Mulungu. (Luka 6:45) Ndipo tikamasinkhasinkha zimene Baibo imakamba, mawu athu adzakhala monga “citsime ca nzelu” cimene cimatsitsimutsa ena.—Miy. 18:4.
Kutsatila malangizo a gulu kumatithandiza kunola maluso athu mu ulaliki (Onani ndime 18)
18. Kodi kuseŵenzetsa mfundo ya pa Miyambo 24:6 kungatithandize bwanji kupeza cipambano mu utumiki wathu?
18 Muzitsatila malangizo a gulu. Baibo imapeleka malangizo otsatilawa kuti zinthu zitiyendele. Imati: “Iweyo udzatha kumenya nkhondo yako potsatila malangizo anzelu, ndipo pakakhala aphungu oculuka anthu amapulumuka.” (Miy. 24:6) Ganizilani mmene kugwilitsa nchito mfundo imeneyi kumatithandizila kupeza cipambano panchito yathu yolalikila na kuphunzitsa. M’malo mocita ulaliki m’njila imene tifunila, timatsatila malangizo amene timapatsidwa. Timalandila malangizo anzelu amenewo pa misonkhano yacikhristu, kumene aphungu aciyambakale amakamba nkhani zozikika pa Baibo, komanso zitsanzo zotiphunzitsa. Kuwonjezela apo, gulu la Yehova lapeleka zida zothandiza—zofalitsa na mavidiyo—kuti anthu aimvetsetse Baibo. Kodi mukuphunzila kugwilitsa nchito zida zimenezi mogwila mtima?
19. Kodi mumaziona bwanji nzelu zimene Yehova amapeleka? (Miyambo 3:13-18)
19 Ŵelengani Miyambo 3:13-18. Timayamikila kwambili ulangizi wothandiza wopezeka m’Mawu a Mulungu. Kodi umoyo wathu ukanakhala bwanji popanda ulangizi umenewo? M’nkhani ino, taona zitsanzo za nzelu zothandiza zopezeka m’buku la Miyambo. Ndipo nzelu zothandiza zimenezo zimapezekanso m’mabuku onse a m’Baibo. Conco, tiyeni nthawi zonse tizigwilitsa nchito nzelu zimene Yehova amapeleka. Tisade nkhawa na mmene anthu m’dzikoli amaonela nzelu zaumulungu, cifukwa ndife otsimikiza kuti ‘ogwilitsitsa [nzelu] adzachedwa odala.’
NYIMBO 36 Titeteze Mitima Yathu
a Nzelu imene Yehova amapeleka, ni yofunika kuposa cinthu cina ciliconse m’dzikoli. M’nkhani ino, tikambilane mawu ofanizila ocititsa cidwi opezeka m’buku la Miyambo, akuti nzelu imakhalila kufuula mumsewu. Tikambilanenso mmene tingapezele nzelu yeniyeni, cifukwa cake anthu ena amatseka makuti kuti asamvetsele nzelu yeniyeni, komanso mmene timapindulila tikamamvetsela nzeluyo.