LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w23 January masa. 14-19
  • Yehova Akukuthandizani Kupambana Mayeso

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Akukuthandizani Kupambana Mayeso
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZINTHU ZIKASINTHA MOSAYEMBEKEZELA
  • ZINTHU ZIKAFIKA PA MWANA WAKANA PHALA
  • MMENE YEHOVA AMAKUTHANDIZILANI KUPAMBANA MAYESO
  • YAMIKILANI MADALITSO AMENE MWALANDILA
  • Kapolo Amene Anamvela Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Yosefe Aponyedwa M’ndende
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Yehova Sanamuiŵale Yosefe
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • “Kodi Mulungu Sindiye Amamasulila Maloto?”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
w23 January masa. 14-19

NKHANI YOPHUNZILA 3

Yehova Akukuthandizani Kupambana Mayeso

“Yehova anakhalabe ndi Yosefe . . . , ndi kuti ciliconse cimene anali kucita, Yehova anali kucidalitsa.”—GEN. 39:2, 3.

NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa

ZIMENE TIKAMBILANEa

1-2. (a) N’cifukwa ciyani sitidabwa kukumana na mayeso? (b) Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

IFE ANTHU a Yehova sitidabwa tikamakumana na mayeso. Timadziŵa kuti “tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikaloŵe mu ufumu wa Mulungu.” (Mac. 14:22) Tidziŵanso kuti ena mwa mavuto athu sadzathelatu, kufikila titaloŵa m’dziko latsopano la Mulungu mmene simudzakhalanso ‘imfa, kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.’—Chiv. 21:4.

2 Yehova saticinjiliza ku mayeso. Komabe, iye amatithandiza kuti tiwapilile. Onani zimene mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Roma. Coyamba anachula mayeso amene iye na Akhristu anzake anali kukumana nawo. Kenako, iye anawauza kuti: “Tikugonjetsa zinthu zonsezi kudzela mwa iye amene anatikonda.” (Aroma 8:35-37) Izi zionetsa kuti Yehova angakuthandizeni kupambana ngakhale pamene muli mkati moyesedwa. Tiyeni tione mmene Yehova anathandizila Yosefe kupambana mayeso, komanso mmene angakuthandizileni inuyo.

ZINTHU ZIKASINTHA MOSAYEMBEKEZELA

3. Kodi zinthu zinasintha bwanji mwadzidzidzi mu umoyo wa Yosefe?

3 Yakobo anali kuonetsa poyela kuti mwana wake Yosefe amam’konda kwambili. (Gen. 37:3, 4) Izi zinapangitsa kuti ana ena a Yakobo ayambe kum’citila nsanje mng’ono wawo. Mpata utapezeka, iwo anam’gulitsa Yosefe kwa amalonda acimidiyani. Amalondawo anatenga Yosefe kupita naye ku dziko lakutali ku Iguputo, kumene anagulitsidwanso. Kumeneko anagulitsidwa kwa Potifara, mkulu wa asilikali olondela Farao. Umoyo wa Yosefe unasintha mosayembekezela. Anacoka pa kukhala mwana wokondeka, n’kukhala kapolo wacabe-cabe wa Mwiguputo!—Gen. 39:1.

4. Ni mavuto ati amene tingakumane nawo ofanana ndi amene Yosefe anakumana nawo?

4 Baibo imakamba kuti “zinthu zosayembekezeleka zimagwela onse.” (Mlal. 9:11) Nthawi zina timakumana na mavuto “amene amagwela anthu”—kutanthauza mavuto amene anthu onse amakumana nawo. (1 Akor. 10:13) Kapena tingakumane na mavuto cabe cifukwa ndife ophunzila a Yesu. Mwacitsanzo, tinganyozedwe, kutsutsidwa, ngakhale kumangidwa kumene cifukwa ca cikhulupililo cathu. (2 Tim. 3:12) Kaya mukumane na mavuto otani, Yehova angakuthandizeni kuti mupambane. Nanga Yosefe anam’thandiza bwanji?

Potifara akugula Yosefe kuti akhale kapolo wake.

Yehova anathandiza Yosefe kupambana mayeso ngakhale pamene anagulitsidwa kukhala kapolo wa Potifara ku Iguputo (Onani ndime 5)

5. Kodi Potifara anazindikila ciyani cokhudza Yosefe? (Genesis 39:2-6)

5 Ŵelengani Genesis 39:2-6. Potifara anazindikila kuti Yosefe anali mnyamata waluso kwambili, komanso wolimbikila nchito. Anadziŵanso cifukwa cake. Potifara anaona kuti “ciliconse cimene [Yosefe] anali kucita, Yehova anali kucidalitsa.”b M’kupita kwa nthawi, Mwiguputoyo anaika Yosefe kukhala mtumiki wake. Anamuikanso kukhala woyang’anila nyumba yake. Cotulukapo n’cakuti Potifara anadalitsidwa.

6. Kodi Yosefe ayenela kuti anamva bwanji poona mmene zinthu zinalili mu umoyo wake?

6 Ganizilani mmene Yosefe anali kumvela. Kodi anali kufunitsitsa ciyani? Kodi anali kufuna kukopa cidwi Potifara kuti am’patse mphoto? Yosefe ayenela kuti anali kufunitsitsa kumasulidwa kuti abwelele kwa atate wake. Ngakhale kuti iye anali na maudindo ambili m’nyumba ya Potifara, anali akali kapolo wa mbuye wosalambila Yehova. Yehova sanacititse Potifara kumasula Yosefe. Ndipo zinthu mu umoyo wa Yosefe zinaipilaipila.

ZINTHU ZIKAFIKA PA MWANA WAKANA PHALA

7. Kodi zinthu zinaipilaipila motani mu umoyo wa Yosefe? (Genesis 39:14, 15)

7 Monga mmene Genesis caputala 39 ifotokozela, mkazi wa Potifara anakopeka naye Yosefe, moti mobweleza-bweleza anali kum’nyengelela kuti agone naye. Koma nthawi zonse Yosefe anali kukana. Pothela pake, iye anamukwiyila kwambili Yosefe, moti anam’namizila kuti anafuna kumugwilila. (Ŵelengani Genesis 39:14, 15.) Potifara ataimva nkhaniyi, anaponya Yosefe m’ndende, ndipo anakhala mmenemo kwa zaka ndithu. (Gen. 39:19, 20) Kodi ndendeyo inali yotani? Liwu la Ciheberi limene Yosefe anagwilitsa nchito lakuti “ndende” lingatanthauze “citsime,” kapena “dzenje.” Izi zionetsa kuti m’ndendemo munali mdima, ndipo anaona monga alibiletu mtengo wogwila. (Gen. 40:15) Cina, Baibo imaonetsa kuti kwa nthawi ndithu, mapazi a Yosefe anamangidwa m’matangadza, ndipo khosi lake linali mu unyolo. (Sal. 105:17, 18) Zinthu zinali kuipilaipila mu umoyo wa Yosefe. Anacoka pa kukhala kapolo wodalilika n’kukhala mkaidi wamba.

8. Tingakhale otsimikiza za ciyani ngakhale zinthu zitafika pothina?

8 Kodi munakhalapo mu mkhalidwe wovuta, moti zinthu zinali kungoipilaipila, ngakhale kuti munali kupemphela mocokela pansi pa mtima? Zotelezi zimacitika. Yehova saticinjiliza ku mavuto a m’dziko lolamulidwa na Satanali. (1 Yoh. 5:19) Ngakhale n’telo, mungakhale otsimikiza za mfundo iyi: Yehova amadziŵa bwino zimene mupitamo, ndipo amasamala za inu. (Mat. 10:29-31; 1 Pet. 5:6, 7) Kuwonjezela apo, iye analonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb. 13:5) Yehova angakuthandizeni kupilila olo zinthu zitaoneka kuti zafika pothina. Tiyeni tione mmene anacitila zimenezi kwa Yosefe.

Yosefe akupeleka malangizo kwa akaidi anzake.

Yehova sanamusiye Yosefe ngakhale pamene anali m’ndende, ndipo anaikidwa kukhala woyang’anila akaidi anzake (Onani ndime 9)

9. N’ciyani cionetsa kuti Yehova sanamusiye Yosefe pamene anali m’ndende? (Genesis 39:21-23)

9 Ŵelengani Genesis 39:21-23. Ngakhale panthawi yovuta imene Yosefe anali m’ndende, Yehova anam’thandiza kupambana pa mayeso. Motani? M’kupita kwa nthawi, mkulu woyang’anila ndende anayamba kum’dalila kwambili Yosefe na kum’lemekeza, monga anacitila Potifara poyamba. Posakhalitsa, mkulu woyang’anila ndendeyo anaika Yosefe kukhala woyang’anila akaidi anzake. Ndipo Baibo imati “mkulu wa ndendeyo sanali kuyang’anilanso ciliconse cimene cinali m’manja [mwa Yosefe].” Yosefe tsopano anakhala na nchito yopindulitsa imene akanaikapo maganizo ake. Mwadzidzidzi, zinthu zinasinthila kwabwino! Zinatheka bwanji kuti mkaidi woganizilidwa kuti anali kufuna kugwilila mkazi wa nduna ya mfumu, apatsidwe udindo wofuna munthu wodalilika? Genesis 39:23 iyankha funsoli kuti, “cifukwa Yehova anali ndi Yosefe, ndipo ciliconse cimene iye anali kucita Yehova anali kucidalitsa.”

10. Fotokozani cimene mwina cinapangitsa Yosefe kuona kuti Mulungu sanali kum’dalitsa.

10 Yesaninso kuganizila mmene Yosefe anamvela. Pambuyo posemeledwa mlandu na kuponyedwa m’ndende, kodi iye anali kuonabe kuti ciliconse cimene anali kucita Mulungu anali kucidalitsa? N’ciyani cimene Yosefe anali kulakalaka? Kodi anali kufuna kukopa cidwi ca mkulu woyang’anila ndendeyo kuti azimukonda? Yosefe ayenela kuti anali kufunitsitsa kumasulidwa basi. Ndipo anacita kupempha mkaidi mnzake amene anali atatsala pang’ono kumasulidwa, kuti akamulankhulileko kwa Farao kuti atulutse Yosefe m’ndende yoipa imeneyo. (Gen. 40:14) Koma mkaidiyo sanauze Farao zimenezo mwamsanga. Cotulukapo cake n’cakuti Yosefe anakhalabe m’ndendeyo kwa zaka zina ziŵili. (Gen. 40:23; 41:1, 14) Ngakhale n’conco, Yehova anapitiliza kum’thandiza Yosefe. Motani?

11. Kodi Yehova anapatsa Yosefe luso lotani lapadela? Nanga zimenezi zinathandiza bwanji kukwanilitsa colinga ca Mulungu?

11 Yosefe ali m’ndende, Yehova anapangitsa mfumu ya Iguputo kulota maloto aŵili ovutitsa maganizo. Farao anafunitsitsa kudziŵa tanthauzo la malotowo. Mfumuyo itadziŵa kuti Yosefe amakwanitsa kumasulila maloto, inamuitana. Mwa thandizo la Yehova, Yosefe anamasulila malotowo. Ndipo Farao anakondwela na ulangizi wabwino umene Yosefe anam’patsa. Farao ataona kuti Yehova anali na Yosefe, anaika mnyamatayo kukhala woyang’anila cakudya ca dziko lonse la Iguputo. (Gen. 41:38, 41-44) Patapita nthawi, kunagwa njala yaikulu imene inakhudza dziko la Iguputo, ngakhalenso dziko la Kanani, kumene kunali banja la Yosefe. Apa Yosefe anatha kupulumutsa banja lake ku njalayo, n’kuteteza mzele wobadwila Mesiya.

12. Kodi Yehova anam’thandiza motani Yosefe kuti apambane pa mayeso?

12 Ganizilani zocitika izi zocititsa cidwi mu umoyo wa Yosefe. N’ciyani cinapangitsa Potifara kucita cidwi na Yosefe kapolo wamba? Ndani anapangitsa mkulu woyang’anila ndende uja kukonda Yosefe, mkaidi wosanunkha kanthu? Ndani anapangitsa Farao kulota maloto ovutitsa maganizo na kupatsa Yosefe luso lomasulila malotowo? Ndani anapangitsa Farao kuika Yosefe kukhala woyang’anila cakudya m’dziko lonse la Iguputo? (Gen. 45:5) Mosakaika konse, Yehova ndiye anali kudalitsa zonse zimene Yosefe anali kucita. Ngakhale kuti abale a Yosefe anafuna kumupha, Yehova anasintha zinthu kuti colinga cake cikwanilitsidwe.

MMENE YEHOVA AMAKUTHANDIZILANI KUPAMBANA MAYESO

13. Kodi Yehova amaloŵelelapo pa zocitika zonse mu umoyo wathu? Fotokozani.

13 Kodi tiphunzilapo ciyani pa nkhani ya Yosefe? Kodi Yehova amaloŵelelapo kuti atithandize pa vuto lililonse tingakumane nalo? Kodi Mulungu ndiye amacititsa zoipa zonse mu umoyo wathu, ndipo zoipa zonsezo zimacitika pa zifukwa zabwino? Ayi, Baibo siiphunzitsa zimenezo. (Mlal. 8:9; 9:11) Koma mfundo imene timadziŵa ni yakuti: Tikakumana na mayeso, Yehova amadziŵa zimenezo, ndipo amamvela mapemphelo athu opempha thandizo. (Sal. 34:15; 55:22; Yes. 59:1) Koposa zonse, Yehova angatithandize kupilila mavuto athu kuti tipambane. Motani?

14. Kodi Yehova amatithandiza bwanji pa nthawi zovuta?

14 Imodzi mwa njila zimene Yehova amatithandiza nazo, ni kutipatsa citonthozo na cilimbikitso pa nthawi imene tifunikila kwambili zimenezi. (2 Akor. 1:3, 4) Izi n’zimene zinacitika kwa m’bale Eziz, wa ku Turkmenistan. M’baleyu anagamulidwa kukapika ndende kwa zaka ziŵili kaamba ka cikhulupililo cake. Iye anati, “Pa tsiku loweluza mlandu wanga m’maŵa, m’bale wina ananiŵelengela Yesaya 30:15 imene imati: ‘Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi acikhulupililo.’ Nthawi zonse vesili linali kunithandiza kukhala wodekha komanso kudalila Yehova pa zonse. Kusinkhasinkha lembali kunanithandiza pa nthawi yonse imene n’nali m’ndende.” Kodi mungakumbukile nthawi imene Yehova anakuthandizani, pokutonthozani na kukupatsani cilimbikitso panthawi imene munafunikila kwambili zimenezi?

15-16. Kodi mwaphunzilapo ciyani pa cokumana naco ca mlongo Tori?

15 Kambili, mayeso akatha m’pamene timazindikila kuti Yehova anali kutithandiza pa nthawi yonseyo. Mlongo Tori anazindikila kuti mfundoyi ni yoona. Mwana wake Mason, anavutika na matenda a khansa kwa zaka 6 mpaka kumwalila. Imfa yake inamupweteka kwambili mlongo Tori. Mlongoyu anati, “Iyi inali nthawi yovuta kwambili kwa ine monga nakubala. Ndipo nikhulupilila kuti makolo ena angavomeleze kuti kuona mwana wako akuthatha na moyo cifukwa codwala, n’koŵaŵa kwambili kuposa iwe kholo kudwala.”

16 Ngakhale kuti mayesowo anali aakulu zedi, pambuyo pake mlongo Tori anaganizila mmene Yehova anali kum’thandizila kuti apilile pa nthawi yonseyo. Iye anafotokoza kuti, “Nikayang’ana kumbuyo, nimaona kuti Yehova ananithandiza pa nthawi yonse imene mwana wanga anali kudwala. Mwacitsanzo, matenda a Mason atafika pa kaya-kaya, moti sakanathanso kukambilana na obwela kudzamuona, abale na alongo anali kuyendabe kwa maola aŵili na motoka kubwela kucipatala. Nthawi zonse m’cipinda coyembekezela, munali kukhala wina wake woticilikiza. Kuwonjezela apo, abale na alongo anatisamalila mwa kuthupi. Ngakhale pa nthawi yovuta kwambili imeneyo, sitinasoŵe kanthu.” Yehova anapatsa mlongo Tori zofunikila kuti apilile, ndipo anacitanso cimodzimodzi kwa Mason.—Onani kabokosi kakuti “Yehova Anatipatsa Zimene Tinali Kufunikiladi.”

“Yehova Anatipatsa Zimene Tinali Kufunikiladi”

Mason anamupeza na matenda a khansa ali na zaka 7, ndipo analimbana nawo matendawa kwa zaka 6. Pa nthawi imene anali kudwala, Mason anagonekedwa ku cipatala maulendo ambili. Ngakhale n’telo, abale mu mpingo wa Mason anali kuona kuti nthawi zonse iye akatuluka m’cipatala, mwamsanga anali kuyamba kulalikila. Thanzi lake likamulola, M’bale Mason anali kukonda kulalikila mmene angathele.

Mason atamwalila, anthu opitilila 700 anabwela ku malilo ake, kuphatikizapo anzake ambili a kusukulu komanso aziphunzitsi. Mphunzitsi wina amene anaonana naye asanamwalile, anakamba kuti afuna ana ake nawonso atengeleko cikhulupililo cimene Mason anali naco. Iye anati kwa zaka zisanu zimene anakhala m’delalo, Mboni za Yehova sizisanamufikilepo. Tsiku lotsatila, Mboni ziŵili zinamufikila ku nyumba kwake. Mphunzitsiyo anavomela kupita ku msonkhano wa mpingo.

Mlongo Tori, mayi wake wa Mason anati: “Yehova sanacilitse Mason mozizwitsa, ndipo nthawi zina malingalilo amenewa anali kunilepheletsa kuona mmene Yehova anali kutithandizila. Koma anali kutithandiza. Yehova anatipatsa zimene tinali kufunikiladi pa nthawi yake.”

YAMIKILANI MADALITSO AMENE MWALANDILA

17-18. N’ciyani cidzatithandiza kuzindikila thandizo la Yehova pa nthawi zovuta, na kuyamikila? (Salimo 40:5)

17 Ŵelengani Salimo 40:5. Munthu akamamanga nyumba, colinga cake cimakhala kuitsiliza na kusamukilamo. Koma nchito yomanga nyumbayo ili mkati, nthawi na nthawi munthuyo angamaime na kuganizila mmene nchitoyo ikupitila patsogolo. Mofananamo, nthawi na nthawi muziima na kuganizila mmene Yehova akukuthandizilani, ngakhale pamene muli mkati mopilila vutolo. Kumapeto kwa tsiku lililonse muzidzifunsa kuti: ‘Kodi Yehova wanidalitsa motani lelo? Ngakhale kuti vutoli likalipo, kodi Yehova akunithandiza bwanji kulipilila?’ Muziyesa kupeza ngakhale cinthu cimodzi cimene Yehova wakucitilani pokuthandizani kupilila.

18 N’zoona kuti mungamapemphele kuti vuto lanu lithe. Izi n’zomveka ndipo n’zoyenela. (Afil. 4:6) Koma tiyenelanso kuzindikila madalitso amene tili nawo kale pali pano. Ndipo Yehova anatilonjeza kuti adzatilimbitsa na kutithandiza kupilila. Conco, muziyamikila nthawi zonse kuti Yehova akukuthandizani. Mukatelo, muziona mmene Yehova akukuthandizilani kupambana mayeso, ngakhale mkati mwa mayeso, monga anacitila kwa Yosefe.—Gen. 41:51, 52.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Yosefe pamene anali mtumiki wa Potifara?

  • Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Yosefe kupambana mayeso pamene anali m’ndende?

  • Kodi Yehova angakuthandizeni bwanji kupambana mayeso?

NYIMBO 32 Ima ku Mbali ya Yehova

a Pamene tili mkati mwa mayeso, tingaone monga kuti Yehova sakutithandiza. Koma mayesowo akatha m’pamene timaona kuti Yehova anatithandiza. Komabe, zocitika pa umoyo wa Yosefe zitiphunzitsa mfundo yofunika kwambili yakuti, Yehova angatithandize kupambana ngakhale pamene tili pa mayeso. Nkhani ino ifotokoze mmene amacitila zimenezi.

b Baibo imafotokoza masinthidwe a umoyo wa Yosefe monga kapolo m’mavesi ocepa cabe. Koma masinthidwe amenewa anacitika pa zaka zambili.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani