NKHANI YOPHUNZILA 7
Zimene Mungacite Kuti Muzipindula Kwambili Poŵelenga Baibo
“Umaŵelengamo zotani?”—LUKA 10:26.
NYIMBO 97 Moyo Umadalila Mau a Mulungu
ZIMENE TIKAMBILANEa
1. N’ciyani cionetsa kuti Yesu anali kuona Malemba kukhala ofunika kwambili?
GANIZILANI mmene zinalili kumvetsela Yesu akuphunzitsa. Nthawi zambili, iye anali kugwila mawu Malemba Oyela, ndipo malembawo anacita kuwaloŵeza pamtima. M’mawu ake oyamba pambuyo pa ubatizo wake, komanso m’mawu ake othela atatsala pang’ono kufa, Yesu anagwila mawu Malemba.b (Deut. 8:3; Sal. 31:5; Luka 4:4; 23:46) Pa utumiki wake wonse wa zaka zitatu na hafu, Yesu nthawi zambili anali kuŵelenga Malemba poyela, kuwagwila mawu, na kuwafotokozela.—Mat. 5:17, 18, 21, 22, 27, 28; Luka 4:16-20.
Pa umoyo wake wonse, Yesu anaonetsa kuti anali kuwakonda Malemba, ndipo anawalola kuti atsogolele zocita zake (Onani ndime 2)
2. Pamene Yesu anali kukula, n’ciyani cinam’thandiza kuwadziŵa bwino Malemba? (Onani cithunzi pacikuto.)
2 Kukali zaka kuti ayambe utumiki wake, Yesu nthawi zambili anali kuŵelenga na kumvetsela kuŵelengedwa kwa Mawu a Mulungu. Panyumba, mosakaika konse anali kumva Mariya na Yosefe akugwila mawu Malemba m’makambilano awo a tsiku na tsiku.c (Deut. 6:6, 7) Sitikayikila kuti Yesu anali kupita ku Sunagoge Sabata iliyonse pamodzi na banja lawo. (Luka 4:16) Kumeneko ayenela kuti anali kumvetsela mwachelu Malemba akamaŵelengedwa. M’kupita kwa nthawi, Yesu anaphunzila kudziŵelengela yekha Malemba Opatulika. Conco, iye anafika powadziŵa bwino Malembawo, komanso anawakonda kwambili. Ndipo anawalola kuti azitsogolela zocita zake. Mwacitsanzo, kumbukilani za cocitika ca m’kacisi Yesu ali na zaka 12 cabe. Aphunzitsi odziŵa bwino Cilamulo ca Mose “anadabwa kwambili ndi mayankho [a Yesu] komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambili.”—Luka 2:46, 47, 52.
3. M’nkhani ino tikambilane ciyani?
3 Nafenso tingafike pa kuwadziŵa bwino Mawu a Mulungu na kuwakonda, tikamawaŵelenga nthawi zonse. Koma n’ciyani cingatithandize kuti tizipindula kwambili na zimene timaŵelenga? Tingaphunzilepo kanthu pa zimene Yesu anauza anthu odziŵa Cilamulo, kuphatikizapo alembi, Afarisi, na Asaduki. Atsogoleli acipembedzo amenewo anali kuŵelenga Malemba kawili-kaŵili. Koma analephela kupindula na zimene anali kuŵelengazo. Yesu anaunika njila zitatu zimene zikanawathandiza amuna amenewa kupindula kwambili na Malemba. Zimene anawauza zingatithandize kuti (1) tizimvetsa zimene timaŵelenga, (2) tizipeza cuma cauzimu, komanso (3) tizilola Mawu a Mulungu kutiumba.
ŴELENGANI NA COLINGA COFUNA KUMVETSETSA
4. Kodi pa Luka 10:25-29, tiphunzilapo ciyani pa nkhani yoŵelenga Mawu a Mulungu?
4 Tiyenela kumvetsetsa tanthauzo la zimene timaŵelenga m’Mawu a Mulungu. Apo ayi, kuŵelenga kwathu sikungatipindulile kwenikweni. Mwacitsanzo, ganizilani za makambilano a Yesu na “munthu wina wodziŵa Cilamulo.” (Ŵelengani Luka 10:25-29.) Munthuyo atamufunsa zimene ayenela kucita kuti akapeze moyo wosatha, Yesu anam’tsogolela ku Mawu a Mulungu mwa kumufunsa kuti: “Kodi m’Cilamulo analembamo ciyani? Umaŵelengamo zotani?” Munthuyo anatha kuyankha pogwila mawu malemba okamba za kukonda Mulungu komanso mnzako. (Lev. 19:18; Deut. 6:5) Koma onani funso limene munthuyo anafunsa. Anati: “Nanga mnzanga amene ndikuyenela kumukonda ndani kwenikweni?” Munthuyo anaonetsa kuti sanamvetse tanthauzo lenileni la zimene anaŵelenga. Mwa ici, iye sanadziŵe mmene akanagwilitsila nchito malembawo mu umoyo wake.
Kuŵelenga na colinga cakuti timvetse ni luso limene tingalikulitse
5. N’cifukwa ciyani kupemphela komanso kusathamanga poŵelenga n’kothandiza?
5 Tingathe kuwamvetsa bwino Mawu a Mulungu, mwa kucita zinthu zina zothandiza. Nazi zina zimene zingakuthandizeni. Pemphelani musanayambe kuŵelenga. Timafunikila thandizo la Yehova kuti timvetse Malemba. Conco, muzipempha mzimu wake woyela kuti ukuthandizeni kuika maganizo pa zimene mukuŵelengazo. Cina, ŵelengani mosathamanga. Izi zidzakuthandizani kuti mumvetse zimene mukuŵelenga. Kuŵelenga Baibo motulutsa mawu kapena kutsatila kuŵelengedwa kwa Baibo kojambulidwa kungakuthandizeni kuti mumvetsetse zimene mukuŵelenga m’Mawu a Mulungu, komanso kuzikumbukila. (Yos. 1:8) Mukatsiliza kuŵelenga, pemphelaninso kwa Yehova kuti mumuyamikile kaamba ka mphatso ya Mawu ake, ndipo m’pempheni kuti akuthandizeni kugwilitsa nchito zimene mwaŵelengazo.
N’cifukwa ciyani kulemba manotsi acidule kungakuthandizeni kumvetsa na kukumbukila zimene mukuŵelenga? (Onani ndime 6)
6. Kodi kudzifunsa mafunso komanso kulemba manotsi acidule kungakuthandizeni bwanji pamene mukuŵelenga? (Onaninso cithunzi.)
6 Onaninso zinthu ziŵili izi zokuthandizani kuti mumvetsetse zimene mukuŵelenga m’Baibo. Dzifunseni mafunso pa zimene mukuŵelenga. Poŵelenga nkhani iliyonse, dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ikunena za anthu ati maka-maka? Ndani akulankhula? Kodi akulankhula kwa ndani? Ndipo n’cifukwa ciyani? Kodi nkhaniyi inacitikila kuti, komanso liti?’ Mafunso ngati amenewa angakuthandizeni kuganizila mfundo zikulu-zikulu za m’nkhaniyo, na kuzitsatila bwino. Cina, pamene mukuŵelenga lembani manotsi acidule. Kulemba manotsi kungakuthandizeni kuti zimene mwaŵelengazo zikhazikike m’maganizo mwanu, komanso kuti muzimvetse bwino. Cinanso, kulemba kungakuthandizeni kumakumbukila zimene mwaŵelenga. Mungalembe mafunso, zimene mwapeza pa kufufuza kwanu, kulemba mfundo zikulu-zikulu, mmene mungaseŵenzetsele mfundozo, kapena mungalembe mmene nkhaniyo yakukhudzilani. Kulemba mfundo zotelezi kungakuthandizeni kuona Mawu a Mulungu monga uthenga wobwela kwa inu panokha.
7. Ni khalidwe liti lofunikila poŵelenga Baibo? Nanga n’cifukwa ciyani? (Mateyu 24:15)
7 Yesu anaonetsa khalidwe lofunika kwambili limene lingatithandize kumvetsetsa zimene timaŵelenga m’Mawu a Mulungu. Khalidwelo ni kuzindikila. (Ŵelengani Mateyu 24:15.) Kodi kuzindikila n’ciyani? Ni luso lotithandiza kuona mmene mfundo imodzi imagwilizanila na mfundo ina, ndiponso mmene imasiyanilana na mfundo ina, komanso lotithandiza kudziŵa mfundo zobisika. Kuwonjezela apo, Yesu anaonetsa kuti tiyenela kukhala ozindikila kuti timvetse zocitika zimene zimakwanilitsa maulosi a m’Baibo. Timafunikilanso khalidwe la kuzindikila kuti tipindule kwenikweni na zimene timaŵelenga m’Baibo.
8. Kodi tingagwilitsile nchito bwanji luso lozindikila poŵelenga?
8 Yehova amapatsa atumiki ake luso la kuzindikila. Conco, mufikileni m’pemphelo na kum’pempha kuti akuthandizeni kukhala na khalidwe limeneli. (Miy. 2:6) Kodi mungacite bwanji zinthu mogwilizana na pemphelo lanu? Iunikeni bwino nkhani imene mukuŵelenga, ndipo onani mmene ikugwilizanila na mfundo zina zimene mumadziŵa kale. Kuti mucite zimenezi, fufuzani m’mabuku othandiza pophunzila Baibo, monga Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova. Mabukuwo adzakuthandizani kuti muzindikile tanthauzo la zimene mukuŵelenga m’Baibo, komanso kuona mmene mungaziseŵenzetsele mu umoyo wanu. (Aheb. 5:14) Mwa kugwilitsa nchito kuzindikila poŵelenga, kamvedwe kanu ka Malemba kadzakula.
ŴELENGANI NA COLINGA COFUNA KUPEZA CUMA CAUZIMU
9. Kodi Asaduki ananyalanyaza mfundo iti yofunika ya coonadi ca m’Malemba?
9 Asaduki anali kuwadziŵa bwino kwambili mabuku oyambilila asanu a Malemba Aciheberi. Koma iwo ananyalanyaza mfundo zofunika za m’mabuku ouzilidwa amenewo. Mwacitsanzo, onani mmene Yesu anawayankhila Asaduki atafuna kum’kola pa nkhani ya ciukitso. Iye anawafunsa kuti: “Kodi inu simunaŵelenge m’buku la Mose, m’nkhani ya citsamba caminga, mmene Mulungu anamuuzila kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’?” (Maliko 12:18, 26) Ngakhale kuti Asaduki anaŵelenga nkhaniyo mobweleza-bweleza, funso la Yesu linaonetsa kuti iwo ananyalanyaza mfundo yofunika ya coonadi ca m’Malemba, imene ni ciphunzitso ca kuuka kwa akufa.—Maliko 12:27; Luka 20:38.d
10. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciyani tikamaŵelenga Baibo?
10 Kodi tiphunzilapo ciyani? Tikamaŵelenga Baibo tiyenela kuyesetsa kudziŵa zonse zimene vesi kapena nkhani ya m’Baibo imeneyo itiphunzitsa. Sitiyenela kungotengapo mfundo za pamwamba zosalila kukumba. Koma timafunanso kumvetsa mfundo za coonadi zobisika ngati cuma camtengo wapatali.
11. Malinga na 2 Timoteyo 3:16, 17, kodi mungacite ciyani kuti muzipeza cuma cauzimu m’Baibo?
11 Kodi tingacite ciyani kuti tizipeza cuma cauzimu poŵelenga Baibo? Ganizilani zimene 2 Timoteyo 3:16, 17 imakamba. (Ŵelengani.) Lembali limakamba kuti “Malemba onse . . . ndi opindulitsa” pa (1) kuphunzitsa, (2) kudzudzula, (3) kuwongola zinthu, komanso (4) kulangiza. Mapindu anayi amenewa mungawapeze ngakhale m’mabuku ena a m’Baibo amene simumaŵelenga kaŵili-kaŵili. Unikani nkhani imene mukuŵelenga kuti muone zimene ikukuphunzitsani za Yehova, colinga cake, kapena zokhudza mfundo zaumulungu. Onaninso mmene nkhaniyo ilili yothandiza pa kudzudzula. Citani izi mwa kuona mmene mavesi ake akukuthandizilani kuzindikila, mwa kupewa maganizo na makhalidwe oipa kuti mukhalebe wokhulupilika kwa Yehova. Cina, onani mmene nkhani imene mukuŵelenga mungaigwilitsile nchito poongola zinthu, mwina maganizo olakwika a munthu amene munakumana naye mu ulaliki. Ndiyeno, yesani kupeza mfundo zothandiza pa kulangiza zimene zingakuphunzitseni kuti muziona zinthu mmene Yehova amazionela. Mukamakumbukila mapindu anayi amenewa poŵelenga malemba, muzipeza cuma cauzimu cimene cidzapangitsa kuti kuŵelenga Baibo kwanu kuzikhala kwaphindu.
LOLANI KUTI ZIMENE MUKUŴELENGA ZIKUUMBENI
12. N’cifukwa ciyani Yesu anafunsa Afarisi kuti “Kodi simunaŵelenge?”
12 Yesu anafunsanso Afarisi funso lakuti “Kodi simunaŵelenge?” pofuna kuonetsa kuti iwo anali na maganizo olakwika pa zimene anali kuŵelenga m’Malemba. (Mat. 12:1-7)e Yesu anawafunsa funso limeneli cifukwa Afarisi anakamba kuti ophunzila ake anaphwanya lamulo la Sabata. Yesu powayankha anachula mfundo ziŵili za m’Malemba, ndipo anagwila mawu buku la Hoseya, poonetsa kuti Afarisiwo sanamvetse colinga ca Sabata, komanso kuti analephela kuonetsa cifundo. N’cifukwa ciyani amuna amenewa sanaumbidwe na zimene anali kuŵelenga m’Mawu a Mulungu? Cifukwa poŵelenga iwo anali odzikuza, komanso anali mzimu wokonda kutsutsa. Khalidwe lawo limeneli linawalepheletsa kumvetsetsa zimene anali kuŵelenga.—Mat. 23:23; Yoh. 5:39, 40.
13. Kodi poŵelenga Baibo tiyenela kukhala na maganizo otani? Nanga n’cifukwa ciyani?
13 Pa mawu a Yesu amenewa, tiphunzilapo kuti tiyenela kuŵelenga Baibo tili na maganizo oyenela. Mosiyana na Afarisi, ife tiyenela kukhala odzicepetsa komanso ophunzitsika. ‘Tivomeleze mofatsa mawu kuti abzalidwe mwa ife.’ (Yak. 1:21) Tikakhala ofatsa, tidzalola Mawu a Mulungu kuzika mizu mumtima mwathu. Kuti zimene timaŵelenga m’Baibo zokhudza cifundo na cikondi zitiumbe, tiyenela kupewa mzimu wotsutsa komanso wodzikuza. Apo ayi sitingaumbike.
Tingadziŵe bwanji ngati tikulola Mawu a Mulungu kutiumba? (Onani ndime 14)f
14. Kodi tingadziŵe bwanji ngati tikulola Baibo kutiumba? (Onaninso zithunzi.)
14 Mmene timacitila na anthu ena zimaonetsa ngati tikulola Mawu a Mulungu kutiumba kapena ayi. Afarisi sanalole Mawu a Mulungu kuwafika pamtima. Ndipo cotulukapo cake n’cakuti iwo anali ‘kuweluza anthu osalakwa.’ (Mat. 12:7) Mofananamo, mmene timaonela ena komanso mmene timacitila nawo, zimaonetsa kaya tinalola Mawu a Mulungu kutiumba kapena ayi. Mwacitsanzo, kodi timakonda kukamba zabwino zimene timaona mwa ena, kapena timafulumila kukamba zifooko zawo? Kodi ndife acifundo komanso okonzeka kukhululukila ena? Kapena timakonda kutsutsa na kusunga cakukhosi? Kudzifufuza moona mtima mwanjilayi kungatithandize kuona ngati tikulola zimene timaŵelenga kuumba maganizo athu, mmene timamvela, na zocita zathu.—1 Tim. 4:12, 15; Aheb. 4:12.
KUŴELENGA MAWU A MULUNGU KUMATIPATSA CIMWEMWE
15. Kodi Yesu anali kuwaona bwanji Malemba Oyela?
15 Yesu anali kuwakonda Malemba Oyela. Ndipo Salimo 40:8 linalosela mmene iye anali kudzaonela Malembawo. Limati: “Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga, ndipo cilamulo canu cili mumtima mwanga.” Pa cifukwa cimeneci, iye anali wosangalala ndipo sanaleke kutumikila Yehova. Nafenso tingakhale acimwemwe, na kupitiliza kutumikila Yehova tikamalola Mawu a Mulungu kutifika pamtima.—Sal. 1:1-3.
16. Kodi muzicita zotani kuti muzipindula kwambili poŵelenga Mawu a Mulungu? (Onani bokosi lakuti “Mawu a Yesu Angakuthandizeni Kumvetsa Zimene Mukuŵelenga.”)
16 Motsatila mawu a Yesu komanso citsanzo cake, tiyeni tinole maluso athu pa nkhani yoŵelenga Baibo. Tingawonjezele kumvetsa kwathu Malemba mwa kupemphela, kuŵelenga mosathamanga, kudzifunsa mafunso, na kulemba manotsi acidule. Ndipo tingagwilitse nchito khalidwe la kuzindikila mwa kuunika bwino-bwino zimene timaŵelenga m’Baibo, poseŵenzetsa zofalitsa zozikika pa Baibo. Cina, tingaphunzile kuigwilitsa nchito bwino Baibo mwa kuyesa kupeza cuma cauzimu pa nkhani zimene tikuŵelenga m’Baibo, ngakhale m’malemba amene sitimaŵelenga kaŵili-kaŵili. Komanso, tingalole Mawu a Mulungu kutiumba pokhalabe na maganizo oyenela pamene tikuŵelenga. Tikayesetsa kucita zimenezi, tizipindula kwambili tikamaŵelenga Baibo, komanso tidzakhala pa ubale wathithithi na Yehova.—Sal. 119:17, 18; Yak. 4:8.
NYIMBO 95 Kuwala Kuwonjezeleka
a Tonsefe alambili a Yehova timayesetsa kuŵelenga Mawu ake tsiku lililonse. Anthu enanso ambili amaiŵelenga Baibo, koma zimene amaŵelengazo sazimvetsetsa. Ni mmenenso zinalili kwa anthu ena m’nthawi ya Yesu. M’nkhani ino, tikambilane zimene Yesu anauza anthu amene amaŵelenga Mawu a Mulungu, na zimene tiphunzilapo kuti tizipindula kwambili poŵelenga Baibo.
b Pa nthawi imene Yesu anabatizika na kudzozedwa na mzimu woyela, iye anayamba kukumbukila zinthu zonse zokhudza nthawi imene anali kumwamba asanabwele padziko lapansi.—Mat. 3:16.
c Mariya anali kuwadziŵa bwino Malemba, ndipo anali kuwagwila mawu. (Luka 1:46-55) Mwacionekele, Yosefe na Mariya analibe ndalama zokwanila zogulila mipukutu yawo-yawo ya Malemba. Iwo ayenela kuti anali kumvetsela mwachelu Mawu a Mulungu akamaŵelengedwa m’Sunagoge. Ndipo izi zinali kuwathandiza kuwakumbukila pambuyo pake.
d Onani nkhani yakuti “Yandikilani Mulungu—‘Iye ndi Mulungu wa Anthu a Moyo’.” Nkhaniyi ili mu Nsanja ya Olonda ya Chichewa ya February 1, 2013.
e Onaninso lemba la Mateyu 19:4-6, pomwe Yesu anafunsa Afarisi funso limodzimodzi kuti: “Kodi simunaŵelenge?” Ngakhale kuti iwo anali ataŵelenga nkhani ya kulengedwa kwa zinthu, ananyalanyaza zimene nkhaniyo inali kuwaphunzitsa za mmene Mulungu amaonela ukwati.
f MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Msonkhano uli mkati, m’bale wotumikila ku saundi walakwitsa zinthu zingapo. Ngakhale n’telo, pambuyo pa msonkhano, abale akumuyamikila pa khama lake, m’malo moika maganizo pa zimene walakwitsa