LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w23 November masa. 8-13
  • Mmene Tingalimbikitsile Cikondi Cathu pa Ena

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Tingalimbikitsile Cikondi Cathu pa Ena
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’CIFUKWA CIYANI TIYENELA KUKONDANA WINA NA MNZAKE?
  • TINGAONETSE BWANJI KUTI TIMAKONDANA?
  • MMENE TINGALIMBITSILE CIKONDI CATHU PA ENA
  • CIFUKWA CAKE CIKONDI N’COFUNIKA KWAMBILI MASIKU ANO
  • Musalole Kuti Cikondi Canu Cizilale
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Cikondi Khalidwe Lamtengo Wapatali
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Muzikulabe m’Cikondi Canu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
w23 November masa. 8-13

NKHANI YOPHUNZILA 47

Mmene Tingalimbikitsile Cikondi Cathu pa Ena

“Tiyeni tipitilize kukondana, cifukwa cikondi cimacokela kwa Mulungu.”—1 YOH. 4:7.

NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse

ZIMENE TIKAMBILANEa

1-2. (a) N’cifukwa ciyani Paulo anati cikondi ndiye “cacikulu”? (b) Tikambilane mafunso ati m’nkhani ino?

PAMENE mtumwi Paulo anali kufotokoza za cikhulupililo, ciyembekezo, na cikondi, anamaliza na mawu akuti “koma cacikulu pa zonsezi ndi cikondi.” (1 Akor. 13:13) N’cifukwa ciyani Paulo ananena zimenezi? M’tsogolo, sitidzafunikanso kuonetsa khalidwe la cikhulupililo pa malonjezo a Mulungu onena za dziko latsopano kapena kukhala na ciyembezo cakuti malonjezowo adzakwanilitsidwa cifukwa adzakhala atakwanilitsidwa kale. Koma nthawi zonse tidzafunika kukonda Yehova na anthu ena. Ndipo cikondi cathu pa iwo cizapitiliza kukula mpaka kale-kale.

2 Popeza tidzafunika kupilitiza kuonetsa cikondi, tiyeni tikambilane mafunso atatu. Loyamba, n’cifukwa ciyani tiyenela kukondana wina na mnzake? Laciŵili, tingaonetse bwanji cikondi kwa ena? Lacitatu, tingatani kuti cikondi cathu pa ena cikhalebe colimba?

N’CIFUKWA CIYANI TIYENELA KUKONDANA WINA NA MNZAKE?

3. N’cifukwa ciyani tiyenela kukondana?

3 N’cifukwa ciyani tiyenela kukondana? Cifukwa cimodzi n’cakuti cikondi cimatiziŵikitsa monga Akhristu oona. Yesu anauza atumwi ake kuti: “Mwakutelo, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Komanso, kukondana kumatithandiza kukhala ogwilizana. Paulo anati cikondi “cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.” (Akol. 3:14) Palinso cifukwa cina cofunika coyenela kukondelana wina na mnzake. Mtumwi Yohane analembela okhulupilila anzake kuti: “Munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.” (1 Yoh. 4:21) Tikamaonetsana cikondi pa wina na mnzake, timaonetsa kuti Mulungu tikamakonda.

4-5. Pelekani citsanzo coonetsa kugwilizana pakati pa kukonda Mulungu na kukonda anzathu.

4 Kodi kukonda abale na alongo athu kugwilizana bwanji na kukonda Mulungu? Tiyeni tiyelekeze kugwilizana komwe kulipo pakati pa mtima wathu na mbali zina za thupi lathu. Ngati dokotala wagwila pa dzanja lathu kuti adziŵe kuthamanga kwa mtima wathu, iye angadziŵenso mfundo zina zokhudza mmene mtima wathu ulili. Kodi mfundo ya m’citsanzoci igwilizana bwanji na nkhani yoonetsana cikondi?

5 Monga mmene dokotala amadziŵila thanzi la mtima wathu akatigwila pa dzanja kuti adziŵe mmene ukuthamangila, nafenso tingadziŵe kukula kwa cikondi cathu pa Mulungu tikaona mmene timakondela ena. Tikaona kuti cikondi cathu pa okhulupilila anzathu cikucepa, cingakhale cizindikilo cakuti cikondi cathu pa Mulungu naconso cikucepa. Koma ngati timaonetsa cikondi kwa okhulupilila anzathu, cingakhale cizindikilo cabwino cakuti cikondi cathu pa Mulungu n’colimba. 

6. N’cifukwa ciyani tiyenela kuda nkhawa ngati cikondi cathu pa abale na alongo cayamba kucepa? (1 Yohane 4:​7-9, 11)

6 Tiyenela kuda nkhaŵa ngati cikondi cathu pa abale na alongo cikucepa. Cifukwa ciyani? Cifukwa izi zingatanthauze kuti uzimu wathu uli pa ciopsezo. Mtumwi Yohane anamveketsa bwino mfundoyi pamene anatikumbutsa kuti: “Pakuti amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:20) Tiphunzilapo ciyani? Yehova amasangalala nafe ngati ‘timakondana.’—Ŵelengani 1 Yohane 4:​7-9, 11.

TINGAONETSE BWANJI KUTI TIMAKONDANA?

7-8. Ni njila zina ziti zimene tingaonetsele cikondi kwa ena?

7 Nthawi zambili m’mawu a Mulungu timapezamo lamulo lakuti, “muzikondana.” (Yoh. 15:​12, 17; Aroma 13:8; 1 Ates. 4:9; 1 Pet. 1:22; 1 Yoh. 4:11) Komabe, cikondi ni khalidwe la mu mtima, kapena kuti umunthu wamkati, ndipo palibe munthu amene angaone mu mtima mwa mnzake. Conco kodi tingacite ciyani kuti cikondi cathu pa wina na nzake cionekele? Tingatelo mu zokamba na zocita zathu.

8 Pali njila zambili zimene tingaonetsele cikondi cathu kwa abale na alongo. Mwacitsanzo: “Muzilankhulana zoona zokhazokha.” (Zek. 8:16) “Sungani mtendele pakati panu.” (Maliko 9:50) “Posonyezana ulemu khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) “Landilanani.” (Aroma 15:7) “Pitilizani. . .kukhululukilana” (Akol. 3:13) “Musaleke kunyamulilana zolemetsa.” (Agal. 6:2) “Muzilimbikitsana.” (1 Ates. 4:18) “Pitilizani kutonthozana.” (1 Ates. 5:11) ‘Muzipemphelelana.’—Yak. 5:16.

Zithunzi: 1. Mlongo akupemphela. 2. Akumvetsela pomwe mlongo wina akum’fotokozela za mumtima mwake. 3. Waimbila foni mlongo amene akudwala kupitila pa vidiyo komfalensi. 4. Akutumiza mawu olimbikitsa amene akulemba pamodzi na mphatso. 5. Akugaŵana cakudya na mlongo amene anapwetekeka dzanja.

Kodi tingam’thandize bwanji wokhulupilila mnzathu amene akukumana na mavuto? (Onani ndime 7-9)

9. N’cifukwa ciyani kutonthoza ena ni njila yabwino kwambili yoonetsela cikondi? (Onaninso cithunzi.)

9 Tiyeni tikambilane njila imodzi yoonetselana cikondi imene taichula m’ndime ili pamwambapa. Tidzakambilana mawu a Paulo akuti: “Pitilizani kutonthozana.” N’cifukwa ciyani kutonthoza ena ili njila yabwino yowaonetsela cikondi? Buku lina lofotokoza Baibo linakamba kuti mawu amene mtumwi Paulo anaseŵenzetsa akuti “kutonthoza” amatanthuza “kukhala pafupi na munthu kuti timutonthoze pamene akumana na zovuta zazikulu.” Motelo, tikatonthoza wolambila mnzathu, timam’thandiza kuti apeze mphamvu, ndiponso kuti apitilizebe kuyenda pa njila ya ku moyo. Conco, nthawi iliyonse tikatonthoza abale na alongo athu, timaonetsa kuti timawakonda.—2 Akor. 7:​6, 7, 13.

10. Pali kugwilizana kotani pakati pa cifundo na kutonthoza ena?

10 Pali kugwilizana pakati pa kumvela ena cifundo komanso kuwatonthoza. Motani? Munthu amene wagwidwa cifundo, amayesetsa kutonthoza ena komanso kuwathandiza pa mavuto awo. Coyamba, timagwidwa na cisoni, kenako timapeleka nthandizo. Onani mmene mtumwi Paulo akugwilizanitsila cifundo ca Yehova na citonthozo cimene amapeleka. Paulo akufotokoza kuti Yehova ni “Atate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse.” (2 Akor. 1:3) Paulo anaseŵenzetsa mawu akuti “cifundo cacikulu” pofotokoza cifundo cimene timakhala naco pa ena. Conco, “Mulungu amachedwa Tate kapena kuti gwelo la cifundo cacikulu cifukwa cifundo cimacokela kwa iye.” Ndipo cifundoci n’cimene cimamusonkhezela kuti atitonthoze “m’masautso athu onse.” (2 Akor. 1:4) Monga mmene madzi abwino a pa kasupe amatsitsimulila munthu waludzu, Yehova amatsitsimula komanso kutonthoza opsinjika maganizo. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova ca kumvela ena cifundo komanso kuwatonthoza? Njila imodzi imene tingacitile zimenezi ni kukulitsa makhalidwe abwino mu mtima mwathu amene angatithandize kutonthoza ena. Kodi ena mwa makhalidwe amenewa ni ati?

11. Malinga na Akolose 3:12 komanso 1 Petulo 3:​8, ni makhalidwe ena ati amene tiyenela kukulitsa kuti tisonyeze cikondi cotilimbikitsa kutonthoza ena?

11 N’ciyani cingatithandize kukhalabe na cikondi kuti “tipitilize kutonthozana” tsiku na tsiku. Tiyenela kukhala na makhalidwe monga kumvela ena cisoni, kukonda abale, komanso kukhala okoma mtima. (Ŵelengani Akolose 3:12; 1 Petulo 3:8.) Kodi makhalidwewa adzatithandiza bwanji? Ngati tipanga cifundo na makhalidwe ena otelo kukhala mbali ya umunthu wathu, sicidzakhala covuta kutonthoza amene akuvutika. Yesu anakamba kuti, “pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’cuma cake cabwino.” (Mat. 12:​34, 35) Kutonthoza abale na alongo amene akukumana na zovuta ni njila yaikulu imene timaonetsela kuti timawakonda.

MMENE TINGALIMBITSILE CIKONDI CATHU PA ENA

12. (a) Kodi tiyenela kusamala na ciyani? (b) Tikambilane funso iti tsopano?

12 Tonse timafuna kuti “tipitilize kukondana.” (1 Yoh. 4:7) Komabe, n’pofunika kwambili kukukumbukila cenjezo la Yesu lakuti “cikondi ca anthu ambili cidzazilala.” (Mat. 24:12) Yesu sanatanthauze kuti izi zidzacitika pa mlingo waukulu pakati pa ophunzila ake. Ngakhale n’telo, tiyenela kukhala osamala kuti tisasoceletsedwe na kupanda cikondi kwa m’dzikoli. Tili na mfundo imeneyi m’maganizo, tiyeni tikambilane funso lofunika kwambili ili: Kodi pali njila imene tingadziŵile ngati cikondi cathu pa abale cikali colimba?

13. N’ciyani cingayese cikondi cathu?

13 Njila imodzi imene tingadziŵile ngati cikondi cathu cikali colimba, ni kuona mmene timasamalila zocitika zina mu umoyo wathu. (2 Akor. 8:8) Cocitika cimodzi cinachulidwa na mtumwi Petulo. Iye anati: “Koposa zonse, khalani okondana kwambili, pakuti cikondi cimakwilila macimo oculuka.” (1 Pet. 4:8) Conco, zifooko komanso kupanda ugwilo kwa ena zingatithandize kudziŵa ngati cikondi cathu pa iwo cikali colimba.

14. Malinga na 1 Petulo 4:​8, tiyenela kukhala na cikondi cotani? Fotokozani.

14 Tiyeni tikambilane mwacifatse mawu a Petulo amenewa. Mbali yoyamba ya vesi 8 ionetsa mtundu wa cikondi umene tiyenela kukhala nawo—“kukondana kwambili.” Mawu amene Petulo anaseŵenzetsa akuti “kwambili” amatanthauza “kufutukula.” Mbali yaciŵili ya vesiyi ionetsa zimene zingacitike ngati timakondana kwambili. Timatha kukwilila macimo a abale. Tiyelekeze motele: Timagwila cikondi na manja aŵili monga nsalu imene ingatambasuke. Timaitambasula mpaka itaphimba, osati imodzi kapena aŵili, koma “macimo oculuka.” “Kuphimba” kutanthauza kukhululuka. Monga momwe nsalu ingaphimbile kusaoneka bwino kwa zinthu, cikondi naconso cimaphimba zifooko komanso kupanda ungwilo kwa ena.

15. Ngati cikondi cathu pa abale na alongo n’cacikulu, kodi tidzakwanitsa kucita ciyani? (Akolose 3:13)

15 Cikondi cathu pa ena ciyenela kukhala cacikulu kuti tikwanitse kukhululukila zophophonya za okhulupilila anzathu, ngakhale kuti nthawi zina sicopepuka kutelo. (Ŵelengani Akolose 3:13.) Tikakwanitsa kukhululukila ena timaonetsa kuti cikondi cathu pa iwo n’colimba, ndiponso kuti tifuna kukondweletsa Yehova. N’ciyaninso cina cingatithandize kunyalanyaza zophophonya za ena komanso kuti tisamakhumudwe na zocita zawo?

Kacithunzi kamkati kaonetsa m’bale akufafaniza cimodzi mwa zithunzi zimene wajambula pa maceza pa foni yake. Cithunzi cina anaciika pa shelefu.

Monga mmene timasungila zithunzi zabwino na kufafaniza zimene sizinaoneke bwino, timaganizila zocitika zabwino za alambili anzathu m’malo moganizila zoipa (Onani ndime 16-17)

16-17. N’ciyaninso cina cingatithandize kunyalanyaza zophophonya zing’ono- zing’ono za ena? Fotokozani. (Onaninso cithunzi.)

16 Muziika maganizo anu pa zabwino zimene abale na alongo anu amacita, osati pa zolakwa zawo. Ganizilani cocitika ici. Yelekezani kuti muli pa maceza na kagulu ka abale na alongo. Mukusangalala na maceza, ndiyeno kumapeto kwa macezawo, mukujambula cithunzi ca gulu lonse. Mukujambulanso zithunzi zina ziŵili kucitila kuti mwina coyambaco sicinaoneke bwino. Tsopano muli na zithunzi zitatu. Koma mwazindikila kuti pa cimodzi mwa zithunzizo, m’bale wina sanamwetulile. Kodi mungatani na cithunzico? Mungacifafanize cifukwa muli na zithunzi zina ziŵili pamene aliyense pa gulupo akumwetulila kuphatikizapo m’baleyo.

17 Tingayelekeze zithunzi zimene timasunga na zinthu zimene timakumbukila zokhudza ena. Nthawi zambili timakumbukila zinthu zabwino zimene tinacita pamodzi na abale na alongo. Koma bwanji ngati pa cocika cina m’bale kapena mlongo anakamba kapena kucita cinthu cimene cinakukhumudwitsani? Kodi mungatani na cocitika cimeneco? Kodi simungacifafanize m’maganizo mwanu monga mmene mungafafanizile cithunzi cija? (Miy. 19:11; Aef. 4:32) Tingakwanitse kufafaniza cocitikaco m’maganizo mwathu cifukwa tili na zocitika zambili zabwino zokhudza m’baleyo. Izi ndiye zocitika zimene tiyenela kusunga m’maganizo mwathu na kuzinyadila.

CIFUKWA CAKE CIKONDI N’COFUNIKA KWAMBILI MASIKU ANO

18. Kodi takambilana mfundo zikulu-zikulu ziti zokhudza cikondi?

18 N’cifukwa ciyani tiyenela kusunga cikondi cathu pa wina na mnzake cili colimba? Monga taonela, timaonetsa kuti timakonda Yehova tikamakonda abale na alongo athu. Kodi timaonetsa bwanji cikondi kwa okhulupilila anzathu? Njila imodzi ni mwa kuwatonthoza. “Tingapitilize kutonthoza ena” ngati timawamvela cifundo. Kodi tingasunge bwanji cikondi cathu pa ena cili colimba? Mwakucita zonse zotheka kuti tizikhululukila ena.

19. N’cifukwa ciyani kuonetsana cikondi n’kofunika kwambili maka-maka masiku ano?

19 N’cifukwa ciyani kuonetsana cikondi n’kofunika kwambili maka-maka masiku ano? Onani cifukwa cimene Petulo anapeleka: “Mapeto a zinthu zonse ayandikila. Conco, . . . khalani okondana kwambili.” (1 Pet. 4:​7, 8) Pamene mapeto a dzikoli akuyandikila, kodi tingayembekezele ciyani? Ponena za otsatila ake, Yesu ananena kuti: “Mitundu yonse idzadana nanu cifukwa ca dzina langa.” (Mat. 24:9) Kuti tikwanitse kupilila cidanici, tiyenela kukhalabe ogwilizana. Tikatelo, zoyesa-yesa za Satani kuti atigaŵanitse zidzalephela cifukwa ndife ogwilizana m’cikondi, cimene “cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.”—Akol. 3:14; Afil. 2:​1, 2.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kukonda abale na alongo athu?

  • Timaonetsa bwanji kuti timawakonda okhulupilila anzathu?

  • Kodi kufunitsitsa kwathu kukhululukila ena kumaonetsa bwanji kuti timawakonda?

NYIMBO 130 Khalani Wokhululuka

a Koposa n’kale lonse, masiku ano tiyenela kuwakonda abale na alongo athu. N’cifukwa ciyani? Nanga tingaonetse bwanji cikondi kwa ena pa mlingo wokulilapo?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani