NKHANI YOPHUNZILA 48
Mungakhalebe na Cidalilo mu Nthawi Zovuta
“‘Limbani mtima, . . . Pakuti ine ndili ndi inu’ watelo Yehova wa makamu.”—HAG. 2:4.
NYIMBO 118 “Tiwonjezeleni Cikhulupililo”
ZIMENE TIKAMBILANEa
1-2. (a) Kodi pali kufanana kotani pakati pa mkhalidwe wathu na wa Ayuda amene anabwelela ku Yerusalemu? (b) Fotokozani mavuto amene Ayuda anakumana nawo.(Onani bokosi lakuti “Masiku a Hagai, Zekariya na Ezara.”)
KODI nthawi zina mumadela nkhawa za tsogolo lanu? Mwina munacotsedwa nchito, ndipo mumadela nkhawa mmene mudzasamalila banja lanu. N’kutheka kuti mumadela nkhawa za citetezo ca banja lanu, pa mavuto obwela cifukwa ca za ndale, cizunzo, kapena kutsutsidwa pa nchito yolalikila. Kodi mukukumana na imodzi mwa mavuto amenewa? Ngati n’telo, mungapindule kuona mmene Yehova anathandizila a Aisiraeli pamene anakumana na mavuto ofanana na amenewa.
2 Panafunika cikhulupililo kuti Ayuda acoke mu mzinda wa Babulo na kusiya umoyo wabwino, kupita kudziko limene ambili a iwo sanali kulidziŵa bwino. Atangofika, anayamba kukumana na mavuto a zacuma, a zandale, komanso citsutso. Conco, cinali covuta kwa ena kuika maganizo awo pa nchito yomanganso kacisi wa Yehova. Ndiye cifukwa cake mu 520 B.C.E., Yehova anatumiza aneneli aŵili, Hagai komanso Zekariya kuti akadzutsenso cidwi cawo. (Hag. 1:1; Zek. 1:1) Monga tionele, cilimbikitso ca aneneli aŵiliwa, cinali cothandiza kwambili. Komabe patapita zaka pafupifupi 50 Ayuda obwelela ku Yerusalemuwo, anafunikilanso cilimbikitso. Ezara, wokopela cilamulo waluso, anapita ku Yerusalemu kucokela ku Babulo, kuti akalimbikitse anthu a Mulungu kuika kulambila koona pa tsogolo.—Ezara 7:1, 6.
3. Tikambilane mafunso ati? (Miyambo 22:19)
3 Maulosi a Hagai komanso Zekariya analimbikitsa anthu a Mulungu kupitilizabe kudalila Yehova pa nthawi ya citsutso. Mofananamo, nafenso angatithandize kudalila thandizo la Yehova pa nthawi ya mavuto. (Ŵelengani Miyambo 22:19.) Pamene tikambilana uthenga wa Mulungu wopelekedwa na Hagai na Zekariya, komanso kukambilana citsanzo ca Ezara, tidzayankha mafunso otsatilawa: Kodi mavuto a pa umoyo anawakhudza bwanji Ayuda? N’cifukwa ciyani tiyenela kuika maganizo athu pa kucita cifunilo ca Mulungu pa nthawi zovuta? Nanga tingalimbitse bwanji cidalilo cathu mwa Yehova tikakhala pa mavuto?
MMENE MAVUTO ANAKHUDZILA AYUDA OBWELELA KWAWO
4-5. N’ciyani ciyenela kuti cinacepetsa cangu ca Ayuda pa nchito yomanganso kacisi?
4 Ayuda atabwelela ku Yerusalemu, anali na nchito yaikulu. Mwamsanga anamanganso guwa la Yehova, na kuyala maziko a kacisi. (Ezara 3:1-3, 10) Koma posakhalitsa cangu cawo cinatha. Cifukwa ciyani? Kuwonjezela pa nchito yomanga kacisi, iwo anafunika kumanga nyumba zawo, kulima minda, komanso kusamalila mabanja awo. (Ezara 2:68, 70) Iwo anakumananso na citsutso kucokela kwa adani awo amene anafuna kulepheletsa nchito yomanganso kacisi.—Ezara 4:1-5.
5 Ayuda ocokela ku ukapolowo, anakumananso na mavuto a zacuma komanso a zandale. Dziko lawo linakhala pansi pa ulamulilo wa Aperisiya. M’caka ca 530 B.C.E., Mfumu Koresi ya Perisiya anamwalila, ndipo analoŵedwa m’malo na Kambisesi amene anayamba kusonkhanitsa asilikali na colinga cakuti agonjetse dziko la Iguputo. Popita ku dziko la Iguputo, n’kutheka kuti asilikali ake analamula Aisiraeli kuti awapatse madzi, zakudya, komanso malo ogona, zimene zinawonjezela mavuto awo. Ulamulilo wa Daliyo Woyamba, yemwe analoŵa m’malo Kambisesi, umadziŵika kuti kuciyambi kwake kunali zipanduko, komanso mavuto ena a zandale. N’kutheka kuti zocitika zonsezi, zinapangitsa Ayuda ocoka ku ukapolo kudela nkhawa za mmene adzasamalila ma banja awo. Cifukwa ca mavuto amene anakumana nawo, Ayuda ena anaona kuti siinali nthawi yabwino yomanganso kacisi wa Yehova.—Hag. 1:2.
6. Malinga na Zekariya 4:6, 7, n’zovuta zina ziti zimene Ayuda anakumana nazo? Nanga Zekariya anawatsimikizila ciyani?
6 Ŵelengani Zekariya 4:6, 7. Kuwonjezela pa mavuto a zacuma, komanso a zandale, Ayuda anali kulimbananso na cizunzo. M’caka ca 522 B.C.E., adani awo anakwanitsa kuika ciletso pa nchito yomanganso kacisi wa Yehova. Koma Zekariya anatsimikizila Ayuda kuti Yehova adzaseŵenzetsa mzimu wake wamphamvu kucotsa zopinga zilizonse. Mu 520 B.C.E., Mfumu Daliyo anacotsa ciletsoco, ndipo anapeleka ndalama na kulamula akulu-akulu aboma ena kuti apeleke thandizo lofunikila.—Ezara 6:1, 6-10.
7. Kodi Ayuda obwelako ku ukapolo analandila madalitso otani atatsogoza kutumikila Yehova?
7 Kupitila mwa Hagai na Zekariya, Yehova analonjeza anthu ake kuti adzawathandiza ngati angaike patsogolo nchito yomanganso kacisi. (Hag. 1:8, 13, 14; Zek. 1:3, 16) Atalimbikitsidwa na aneneli, Ayuda obwelako ku ukapolo, anayambilanso kugwila nchito yomanganso kacisi mu 520 B.C.E. imene inamalizika pasanathe zaka 5. Cifukwa Ayuda anaika patsogolo kucita cifunilo ca Mulungu ngakhale pa nthawi ya mavuto, iye anawathandiza kuthupi, komanso kuuzimu. Zotsatila zake, anali kulambila Yehova mwa cimwemwe.—Ezara 6:14-16, 22.
IKANI MAGANIZO ANU PA KUCITA CIFUNILO CA MULUNGU
8. Kodi mawu a pa Hagai 2:4 angatithandize bwanji kuika maganizo athu pa kutumikila Yehova? (Onaninso mawu a m’munsi.)
8 Pamene cisautso cacikulu cikuyandikila, timaona kufunika komvela lamulo la kulalikila kuposa n’kale lonse. (Maliko 13:10) Komabe, zingakhale zovuta kuika maganizo athu pa utumiki ngati tikukumana na mavuto a zacuma, kapena ngati tikutsutsidwa pa nchito yathu yolalikila. N’ciyani cingatithandize kutsogoza za ufumu wa Mulungu? Kukhalabe na cidalilo cakuti “Yehova wa makamu”b ali kumbali yathu. Iye adzatithandiza ngati tipitilizabe kuika zinthu za ufumu patsogolo pa zofuna zathu. Conco, tilibe cifukwa coopela.—Ŵelengani Hagai 2:4.
9-10. Kodi banja lina linatsimikizila bwanji kuti mawu a Yesu a pa Mateyu 6:33 ni oona?
9 Ganizilani citsanzo ca Oleg na Irina,c banja limene likutumikila monga apainiya. Atasamukila ku dela lina, anayamba kukumana na mavuto a zacuma cifukwa ca kuipa kwa zinthu m’dziko lawo. Ngakhale kuti analibe nchito yodalilika kwa caka cimodzi, nthawi zonse anali kumva kuti Yehova ali nawo. Ndipo nthawi zina anali kulandila thandizo kucokela kwa abale na alongo awo. N’ciyani cinawathandiza kupilila zovutazi? Oleg yemwe poyamba anali wopanikizika maganizo anati, “Kukhala wotangwanika na nchito yolalikila kunanithandiza kuika maganizo pa cinthu cofunika kwambili mu umoyo.” Iye na mkazi wake anakhalabe okangalika mu utumiki pamene anali kufuna-funa nchito.
10 Tsiku lina atacoka mu utumiki, iwo anapeza kuti mnzawo wa pa mtima anayenda ulendo wa makilomita 160 kuwabweletsela matumba aŵili a zakudya. M’bale Oleg anati: “Pa tsikulo, tinaonanso kuti Yehova komanso mpingo, amasamala za ife. Ndife otsimikiza kuti Yehova sasiya atumiki ake, ngakhale atasoŵa mtengo wogwila.—Mat. 6:33.
11. Tingayembekezele ciyani ngati tiika maganizo athu pa kucita cifunilo ca Mulungu?
11 Yehova afuna kuti tiike maganizo athu pa nchito yopulumutsa miyoyo, yomwe ni nchito yopanga ophunzila. Monga taonela mu ndime 7, Hagai analimbikitsa anthu a Mulungu kuyambilanso kulambila koona, ngati kuti akuyalanso maziko a kacisi. Mwa kutelo, Yehova anawalonjeza kuti “ndikupatsani madalitso.” (Hag. 2:18, 19) Nafenso ndife otsimikiza kuti Yehova adzadalitsa khama lathu ngati tiika patsogolo nchito imene anatipatsa.
KUKULITSA CIDALILO CANU MWA YEHOVA
12. N’cifukwa ciyani Ezara na Ayuda anzake anafunikila cikhulupililo colimba?
12 M’caka ca 468 B.C.E., Ezara anapita na gulu laciŵili la Ayuda kucoka ku Babulo kupita ku Yerusalemu. Kuti ayende ulendowo, Ezara komanso Ayuda amene anali nawo anafunika cikhulupililo colimba. Anali kuzadzela msewu woopsa atanyamula golide na siliva wambili zimene zinapelekedwa kuti zithandizile pa nchito yomanganso kacisi. Izi zikanapangitsa acifwamba kuwabela. (Ezara 7:12-16; 8:31) Kuwonjezela apo, iwo anazindikila kuti ngakhale mu Yerusalemu mwenimwenimo munalibe citetezo. Mu mzindamo munali anthu ocepa, komanso mpanda na zipata zake zinafunika kukonzedwa. Kodi tingaphunzile ciyani kwa Ezara pa nkhani yokulitsa cidalilo cathu mwa Yehova?
13. Kodi Ezara anakulitsa bwanji cidalilo mwa Yehova? (Onaninso mawu a m’munsi.)
13 Ezara anali ataonapo mmene Yehova anathandizila anthu ake pa nthawi ya mavuto. Zaka zingapo m’mbuyomo, mu 484 B.C.E., mwina Ezara anali kukhala ku Babulo pamene Mfumu Ahasiwero inapeleka lamulo lakuti Ayuda onse okhala m’zigawo za Perisiya aphedwe. (Esitere 3:7, 13-15) Umoyo wa Ezara unali pa ciwopsezo! Lamulo limeneli litapelekedwa, Ayuda “m’zigawo zonse” anayamba kulila na kusala kudya, mwacionekele akupempha citsogozo ca Yehova. (Esitere 4:3) Ganizilani mmene Ezara anamvela zinthu zitasintha. M’malo moti iwo aphedwe, amene anapanga ciwembuco ndiwo anaphedwa. (Esitere 9:1, 2) Zocitika zimenezi ziyenela kuti zinakonzekeletsa Ezara ku mavuto amene anali kudzakumana nazo m’tsogolo, komanso kulimbikitsa cidalilo cake mwa Yehova cakuti ali na mphamvu zoteteza anthu Ake.d
14. Kodi mlongo wina anaphunzila ciyani Yehova atamuthandiza pa nthawi ya mavuto?
14 Yehova akatisamalila pa nthawi zovuta, cidalilo cathu mwa iye cimalimbilako. Ganizilani citsanzo ca mlongo Anastasia yemwe akhala ku m’mawa kwa Europe. Iye anasiya nchito yake n’colinga cofuna kupewa kukhalila mbali m’zandale. Iye anati: “Inali nthawi yoyamba kukhalapo wopanda ndalama mu umoyo wanga. Koma n’nasiya nkhaniyi m’manja mwa Yehova, ndipo n’naona mmene ananisamalila mwacikondi. Nchito ikadzanithelanso m’tsogolomu sinidzacita mantha. Ngati Atate wanga wakumwamba anisamalila lelo, ndiye kuti adzanisamalilanso mawa.”
15. N’ciyani cinathandiza Ezara kukhalabe na cidalilo mwa Yehova? (Ezara 7:27, 28)
15 Ezara anaona dzanja la Yehova pa umoyo wake. Mosakaikila, kuganizila nthawi zimene Yehova anamusamalila kunam’thandiza Ezara kukhalabe na cidalilo mwa Iye. Ndiye cifukwa cake anati “dzanja la Yehova Mulungu wanga linali pa ine.” (Ŵelengani Ezara 7:27, 28.) Ezara anachula mfundo imeneyi maulendo 6 m’buku lodziŵika na dzina lake.—Ezara 7:6, 9; 8:18, 22, 31.
Ni pa zocitika ziti pamene tingaone bwino kwambili dzanja la Mulungu mu umoyo wathu? (Onani ndime 16)e
16. Ni panthawi iti pamene tingaone bwino kwambili dzanja la Yehova mu umoyo wathu? (Onaninso cithunzi.)
16 Yehova angatithandize tikamakumana na zokhoma. Mwacitsanzo, pamene tipempha nthawi kwa abwana athu kuti tikapite kumsonkhano wacigawo, kapena pamene tipempha kuti tizikomboka msanga pa tsiku la msonkhano, timatsegula mpata woona dzanja la Yehova mu umoyo wathu. Ndipo tingadabwe na mmene zinthu zingayendele bwino. Zikatelo, cidalilo cathu mwa Yehova cimalimbilako.
Ezara akupemphela uku akulila ali pa kacisi cifukwa ca macimo a anthu. Khamu la anthu nalonso likulila. Ndiyeno Sekaniya akulimbikitsa Ezara pomutsimikizila kuti: “Aisiraeli ali ndi ciyembekezo pa nkhani imeneyi. . . . ndipo ife tili nawe.” (Onani ndime 17)
17. Kodi Ezara anaonetsa bwanji kudzicepetsa pa nthawi zovuta? (Onani cithunzi pa cikuto.)
17 Modzicepetsa Ezara anapempha thandizo la Yehova. Nthawi zonse akapanikizika cifukwa ca maudindo ake, modzicepetsa Ezara anali kupemphela kwa Yehova. (Ezara 8:21-23; 9:3-5) Citsanzo ca Ezara cinalimbikitsa anthu ena kum’thandiza komanso kutengela cikhulupililo cake. (Ezara 10:1-4) Conco, tikapanikizika maganizo na nkhawa zokhudza zofunikila za kuthupi, kapena citetezo ca banja lathu, tiyenela kupemphela kwa Yehova mwa cidalilo.
18. N’ciyani cingawonjezele cidalilo cathu mwa Yehova?
18 Tikamapempha thandizo kwa Yehova modzicepetsa na kulandila thandizo la okhulupilila anzathu, cidalilo cathu mwa Mulungu cimalimbilako. Mlongo Erika, mayi wa ana atatu, anasungabe cidalilo cake mwa Yehova cili colimba atakumana na mavuto aakulu. M’nthawi yocepa cabe, iye anataikilidwa mwana wake amene anapita padela, komanso mwamuna wake wokondeka. Pofotokoza zimene zinam’citikila, iye anati: “Sungadziŵiletu mmene Yehova adzakuthandizila. Thandizo lingabwele m’njila imene sunali kuliyembekezela. Naona kuti ambili mwa mapemphelo anga, ayankhidwa kupitila m’mawu na zocita za mabwenzi anga. Nikawafotokozela zimene zikunicitikila, iwo anganithandize mosavuta.”
DALILANIBE YEHOVA MPAKA MAPETO
19-20. Tiphunzila ciyani kwa Ayuda amene sanabwelele ku Yerusalemu?
19 Tingatengenso phunzilo lofunika kwa Ayuda amene sanakwanitse kubwelela ku Yerusalemu. Mwacionekele, ena a iwo sakanakwanitsa kubwelela cifukwa ca ukalamba, matenda aakulu, kapena maudindo a m’banja. Ngakhale n’telo, iwo anathandizila Ayuda anzawo amene anabwelela mwa kupanga zopeleka zocilikiza nchito yomanga kacisi. (Ezara 1:5, 6) Zioneka kuti patapita zaka 19 kucokela pamene gulu loyamba linafika ku Yerusalemu, Ayuda amene anatsala ku Babulo anapitilizabe kutumiza zopeleka ku Yerusalemu.—Zek. 6:10.
20 Ngakhale tione kuti sitikucita zambili potumikila Mulungu, tikhale otsimikiza kuti Yehova amayamikila kuyesetsa kwathu pofuna kumukondweletsa. N’cifukwa ciyani tikutelo? M’nthawi ya Zekariya Yehova anauza mneneli wake kuti apange cisoti cacifumu poseŵenzetsa golide na siliva yemwe anatumizidwa na Ayuda okhala ku Babulo. (Zek. 6:11) “Cisoti cacifumu caulemeleloco,” cinali kudzakhala cikumbutso kwa Ayuda pa zopeleka zaufulu zimene anali kupeleka. (Zek. 6:14) Ndife otsimikiza kuti Yehova sadzaiŵala kuyesetsa kwathu pom’tumikila m’nthawi zovuta.—Aheb. 6:10.
21. N’ciyani cingatithandize kuyang’ana m’tsogolo mwacidalilo?
21 Mosakaikila, tizikumanabe na zovuta m’masiku otsiliza ano, ndipo m’tsogolomu zinthu zidzafika poipa kwambili. (2 Tim. 3:1, 13) Komabe, tisade nkhawa kwenikweni. Kumbukilani mawu a Yehova kwa anthu ake m’nthawi ya Hagai. Iye anati: “Ine ndili ndi inu . . . musacite mantha.” (Hag. 2:4, 5) Ifenso tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzakhalabe nafe, malinga ngati ticita zonse zotheka kucita cifunilo cake. Tikamagwilitsa nchito zimene taphunzila m’maulosi a Hagai na Zekariya komanso ku citsanzo ca Ezara, tidzakhalabe na cidalilo mwa Yehova, mosasamala kanthu za mavuto amene tingakumane nawo m’tsogolo.
NYIMBO 122 Cilimikani, Musasunthike!
a Nkhani ino yakonzedwa kuti itithandize kulimbitsa cidalilo cathu mwa Yehova tikakumana na mavuto a zacuma, a zandale, kapena tikamatsutsidwa pa nchito yolalikila.
b Mawu akuti “Yehova wa makamu” amapezeka maulendo 14 m’buku la Hagai. Ndipo anakumbutsa Ayudawo komanso ife masiku ano kuti Yehova ali na mphamvu zopanda malile, ndipo amalamula makamu a zolengedwa zauzimu.—Sal. 103:20, 21.
c Maina ena asinthidwa.
d Monga wokopolola cilamulo ca Mulungu waluso, Ezara analimbikitsanso cidalilo cake m’mawu a ulosi a Yehova ngakhale asanapite ku Yerusalemu.— 2 Mbiri 36:22, 23; Ezara 7:6, 9, 10; Yer. 29:14.
e MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale akupempha bwana ake kuti am’patse nthawi yoti apite ku msonkhano wa cigawo. Kenako, akupempha thandizo komanso citsogozo kwa Mulungu pokonzekela kukambanso na bwana wake. Ndiyeno akuonetsa bwana wake kapepala ka ciitanilo ka msonkhanowo, na kumufotokozela kufunika kwa maphunzilo a Baibo amenewo. Bwana wake wacita cidwi ndipo wasintha maganizo.