LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 August masa. 8-13
  • Yehova Amafuna Kuti Anthu Onse Alape

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Amafuna Kuti Anthu Onse Alape
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE YEHOVA ANAUZA AISIRAELI PA NKHANI YA KULAPA
  • MMENE YEHOVA AMATHANDIZILA ANTHU OCIMWA KUTI ALAPE
  • ZIMENE YESU ANAPHUNZITSA OTSATILA AKE PA NKHANI YA KULAPA
  • Zimene Yehova Anacita Kuti Apulumutse Anthu ku Ucimo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Mmene Akulu Amaonetsela Cikondi na Cifundo Kwa Munthu Wocita Chimo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Muzikhulupirira Kuti Yehova Anakukhululukirani
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Mmene Akulu Angathandizile Amene Anacotsedwa Mumpingo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 August masa. 8-13

NKHANI YOPHUNZILA 32

NYIMBO 44 Pemphelo la Munthu Wovutika

Yehova Amafuna Kuti Anthu Onse Alape

“Yehova . . . sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.”—2 PET. 3:9.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kumvetsa tanthauzo la kulapa, cifukwa cake kulapa n’kofunika, komanso mmene Yehova wathandizila anthu osiyana-siyana kulapa.

1. Kodi munthu amene walapa amacita ciyani?

TIKALAKWITSA cina cake, m’pofunika kulapa. Baibo imakamba kuti munthu akalapa, amadana na ciliconse cimene anacita, amaleka kucicita colakwaco, ndipo samafuna kucibweleza.—Onani Matanthauzo a Mawu Ena a m’Baibulo, pa mawu akuti “Kulapa.”

2. N’cifukwa ciyani tonsefe tiyenela kuphunzila za kulapa? (Nehemiya 8:​9-11)

2 Tonse tiyenela kuphunzila za kulapa. Cifukwa ciyani? Cifukwa tonsefe timacimwa tsiku lililonse. Monga mbadwa za Adamu na Hava, aliyense wa ife analandila colowa ca ucimo na imfa. (Aroma 3:23; 5:12) Conco tonsefe ndife ocimwa. Ngakhale anthu amene anali na cikhulupililo colimba monga mtumwi Paulo, anali kuvutika na zilako-lako zaucimo. (Aroma 7:​21-24) Kodi izi zitanthauza kuti tiyenela kukhalila kudziimba mlandu kaamba ka macimo athu? Ayi. Yehova ni wacifundo, ndipo amafuna kuti tikhale acimwemwe. Tiyeni tikambilane zimene zinacitikila Ayuda a m’nthawi ya Nehemiya. (Ŵelengani Nehemiya 8:​9-11.) Yehova sanafune kuti anthuwo akhale acisoni cifukwa ca macimo amene anacita kumbuyoko, koma anafuna kuti akhale acimwemwe pom’lambila. Yehova amadziŵa kuti kulapa kumabweletsa cimwemwe. Ndiye cifukwa cake iye amatiphunzitsa za kulapa. Tikalapa macimo athu, sitikaikila kuti Atate wathu wacifundo adzatikhululukila.

3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 Tiyeni tikambilane zambili pa nkhani ya kulapa. M’nkhani ino, tikambilane mfundo zitatu. Coyamba, tikambilane zimene Yehova anauza Aisiraeli pa nkhani ya kulapa. Kenako, tikambilane zimene Yehova amacita pothandiza anthu ocimwa kuti alape. Ndipo cothela, tikambilane zimene Yesu anaphunzitsa otsatila ake pa nkhani ya kulapa.

ZIMENE YEHOVA ANAUZA AISIRAELI PA NKHANI YA KULAPA

4. Kodi Yehova anawauza ciyani Aisiraeli pa nkhani ya kulapa?

4 Yehova atakhazikitsa mtundu wa Aisiraeli, anacita nawo pangano. Iwo akanasunga malamulo ake, iye akanawateteza na kuwadalitsa. Ponena za malamulowo, Yehova anatsimikizila Aisiraeli kuti: “Lamulo limene ndikukupatsani leloli si lovuta kwa inu kulitsatila, ndipo silili poti simungathe kulipeza.” (Deut. 30:​11, 16) Koma iwo akanasankha kumupandukila, monga kusankha kulambila milungu ina, iye akanacotsa madalitso ake pa iwo. Izi zikanacititsa kuti iye asiye kuwateteza, ndipo iwo akanavutika. Koma zimenezo si zikanatanthauza kuti iye akanasiyilatu kuwayanja. Zinali zotheka kwa Aisiraeli ‘kubwelela kwa Yehova Mulungu [wawo] komanso kumvela mawu ake.’ (Deut. 30:​1-3, 17-20) M’mawu ena, iwo anali na mwayi wolapa. Kucita zimenezi kukanacititsa kuti amuyandikile Yehova, ndipo kukanawacititsanso kuti alandile madalitso ake monga paciyambi.

5. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti sanawafulatile anthu ake? (2 Mafumu 17:​13, 14)

5 Anthu a Yehova osankhidwa amenewa anamupandukila Yehova mobweleza-bweleza. Kuphatikiza pa kulambila mafano, Aisiraeli anali kucita zoipa zina zambili. Ndipo zotulukapo zake n’zakuti iwo anavutika. Koma Yehova sanawafulatile anthu ake osamvela amenewa. Mobweleza-bweleza, iye anawatumizila aneneli kuti akalimbikitse anthu akewo kulapa na kubwelela kwa iye.—Ŵelengani 2 Mafumu 17:​13, 14.

6. Kodi Yehova anaseŵenzetsa bwanji aneneli ake kuphunzitsa anthu ake za kufunika kwa kulapa? (Onaninso cithunzi.)

6 Nthawi zambili, Yehova anali kuseŵenzetsa aneneli kuti akacenjeze na kuwongolela anthu ake. Mwacitsanzo, kudzela mwa mneneli wake Yeremiya, Mulungu anawauza kuti: “Bwelela Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya cifukwa ndine wokhulupilika . . . Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale. Koma vomelezani kuti ndinu olakwa cifukwa mwapandukila Yehova Mulungu wanu.” (Yer. 3:​12, 13) Kupitila mwa Yoweli, Yehova anati: “Bwelelani kwa ine ndi mtima wonse.” (Yow. 2:​12, 13) Mulungu anauzila Yesaya kuti alengeze kuti: “Dziyeletseni. Cotsani zocita zanu zoipa pamaso panga. Lekani kucita zoipa.” (Yes. 1:​16-19) Ndipo kudzela mwa Ezekieli, Yehova anafunsa kuti: “Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu wocimwa? Kodi zimene ine ndimafuna si zoti munthu wocimwayo alape nʼkupitiliza kukhala ndi moyo? Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense, . . . conco siyani kucita zoipa kuti mupitilize kukhala ndi moyo.” (Ezek. 18:​23, 32) Yehova amakondwela akaona anthu akulapa cifukwa amafuna kuti anthuwo akhale na moyo mpaka kale-kale! Koma Yehova samangokhala phee kudikhila kuti munthu wocimwa alape kenako n’kumuthandiza. Tiyeni tione zitsanzo zina pa nkhani imeneyi.

Zithunzi: Aneneli amene anatumizidwa na Yehova kukawongolela anthu ake osamvela. 1. Yoweli: cam’ma 820 B.C.E. 2. Hoseya: pambuyo pa 745 B.C.E. 3. Yesaya: pambuyo pa 732 B.C.E. 4. Ezekieli: cam’ma 591 B.C.E. 5. Yeremiya: mu 580 B.C.E.

Nthawi zambili Yehova anaseŵenzetsa aneneli ake kulimbikitsa anthu ake osamvela kuti alape (Onani ndime 6-7)


7. Poseŵenzetsa cocitika ca Hoseya na mkazi wake, kodi Yehova anawaphunzitsa ciyani anthu ake?

7 Yehova anaseŵenzetsa cocitika ceni-ceni pophunzitsa anthu ake za cikondi cake pa iwo. Iye anaseŵenzetsa cocitika ca Gomeri yemwe anali mkazi wa mneneli Hoseya. Mkaziyu anali kusiya Hoseya na kupita kukacita cigololo na amuna ena. Kodi zinali zosatheka kwa iye kulapa? Yehova amene amaona mumtima mwa munthu anauza Hoseya kuti: “Pita ukayambenso kukonda mkazi amene akukondedwa ndi mwamuna wina ndipo akucita cigololo. Ukamukonde ngati mmene Yehova amakondela Aisiraeli, ngakhale kuti iwo amalambila milungu ina.” (Hos. 3:1; Miy. 16:2) Onani kuti mkazi wa Hoseya anali kucitabe chimo lalikulu. Komabe Yehova anauza Hoseya kuti akhululukile mkaziyo na kumutengelanso kunyumba kwake kuti akapitilize kukhala mkazi wake.a Mofananamo, Yehova anali asanawasiyiletu anthu ake opandukawo ngakhale kuti anthuwo anali kucitabe macimo aakulu. Yehova anali kuwakondabe. Iye anapitiliza kuwatumizila aneneli kuti awathandize kusintha njila zawo na kulapa. Citsanzoci citiphunzitsa kuti Yehova amene amakwanitsa kuona za mumtima mwa munthu, amadziŵa bwino munthu aliyense. Iye amayesetsa kuthandiza munthu amene akali kucitabe chimo lalikulu kuti alape. (Miy. 17:3) Tiyeni tione mmene amacitila zimenezi.

MMENE YEHOVA AMATHANDIZILA ANTHU OCIMWA KUTI ALAPE

8. Kodi Yehova anacita ciyani pofuna kuthandiza Kaini kuti alape? (Genesis 4:​3-7) (Onaninso cithunzi.)

8 Kaini anali mwana woyamba wa Adamu na Hava. Monga ana ena onse a Adamu na Hava, Kaini nayenso anali na zikhotelelo zaucimo zimene analandila kwa makolo ake. Kuwonjezela apo, Baibo imakamba izi ponena za iye: “Zocita zake zinali zoipa.” (1 Yoh. 3:12) Mwina izi zifotokoza cifukwa cake Yehova “sanasangalale ndi Kaini komanso nsembe yake ngakhale pang’ono.” M’malo mosintha njila zake, “Kaini anapsa mtima kwambili ndipo nkhope yake inagwa cifukwa ca cisoni.” Kodi Yehova anacita ciyani pambuyo pake? Iye anakamba na Kaini. (Ŵelengani Genesis 4:​3-7.) Yehova anakamba naye mokoma mtima, ndipo anamuuza kuti adzamudalitsa ngati angacite zabwino. Yehova anacenjezanso Kaini za mkwiyo wake, ndipo anamuuza kuti ungamupangitse kucita coipa. N’zacisoni kuti Kaini anakana kumvela, sanalole kuti Yehova amuthandize kulapa. Pambuyo poona zimene Kaini anacita, kodi Yehova analeka kuthandiza anthu ena ocimwa kuti alape? Kutalitali!

Kaini wanyamula mtengo pomwe akupita kukapha Abele. Akuyang’ana kumbuyo kuti amve mawu a Yehova amene akucokela kumwamba.

Yehova anayesetsa kuthandiza Kaini kuti alape, ndipo anamuuza kuti adzamudalitsa akalapa (Onani ndime 8)


9. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Davide kulapa?

9 Yehova anali kukonda kwambili Mfumu Davide. Anafika pomuchula kuti “munthu wapamtima panga.” (Mac 13:22) Koma Davide anacita macimo akulu-akulu kuphatikizapo cigololo komanso kupha munthu. Malinga na Cilamulo ca Mose, Davide anayenela kuphedwa. (Lev. 20:10; Num. 35:31) Koma cifukwa ca cifundo cake, Yehova anafuna kuthandiza Davide kuti alape.b Anatuma mneneli wake Natani kupita kwa mfumuyo, ngakhale kuti panthawiyo Davide anali asanaonetse cizindikilo ciliconse ca kulapa. Natani anaseŵenzetsa fanizo lomwe linathandiza Davide kumvetsa kuti iye anali atacita chimo lalikulu. Davide anazindikila kuti wacimwila Yehova, ndipo analapa. (2 Sam. 12:​1-14) Iye analemba Salimo logwila mtima limene lionetsa kuti analapadi. (Sal. 51, tumawu twapamwamba) Anthu ambili ocimwa amalimbikitsidwa na Salimo limeneli ndipo limawasonkhezela kulapa. Kodi sindife oyamikila kuti Yehova mwacikondi anathandiza mtumiki wake wokondeka Davide kulapa?

10. Mumamva bwanji poona kuti Yehova amaleza nafe mtima komanso kuti amatikhululukila?

10 Yehova amadana na ucimo, ndipo sakondwela na chimo la mtundu uliwonse. (Sal. 5:​4, 5) Komabe, iye adziŵa kuti tonse ndife ocimwa, ndipo mwacikondi cake amasankha kutithandiza kulimbana na ucimowo. Nthawi zonse iye wakhala akuyesetsa kuthandiza anthu ngakhale ocimwa kwambili kuti alape na kumuyandikila. N’zolimbikitsa zedi kudziŵa mfundo imeneyi! Pamene tikusinkhasinkha za kuleza mtima komanso kukhululuka kwa Yehova, timalimbikitsidwa kukhalabe okhulupilika kwa iye komanso kulapa mofulumila tikacimwa. Tiyeni tsopano tikambilane zimene Yesu anaphunzitsa otsatila ake pa nkhani ya kulapa.

ZIMENE YESU ANAPHUNZITSA OTSATILA AKE PA NKHANI YA KULAPA

11-12. Kodi Yesu anawaphunzitsa ciyani amene anali kumumvetsela za kukhululuka kwa Atate wake? (Onani cikuto.)

11 Mu 29 C.E., nthawi inafika kuti Mesiya aonekele. Monga mmene tinaphunzilila m’nkhani yapita, Yehova anaseŵenzetsa Yohane M’batizi komanso Yesu Khristu kuphunzitsa anthu za kufunika kwa kulapa.—Mat. 3:​1, 2; 4:17.

12 Pamene anali kucita utumiki wake, Yesu anaphunzitsa amene anali kumumvetsela kuti Yehova ni Mulungu amene amakhululuka. Yesu anaonetsa mfundo imeneyi mwapadela pamene anafotokoza fanizo la mwana woloŵelela. Mwana wa m’fanizolo anasankha kucoka panyumba, ndipo anayamba kucita zinthu zoipa kwambili kumene anapita. Koma “nzelu zitamubwelela,” iye anasankha kubwelela kunyumba. Kodi atate ake anamulandila motani? Yesu anakamba kuti pomwe mwanayo anali “capatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa ndi cifundo. Kenako anamuthamangila n’kumukumbatila ndipo anamukisa mwacikondi.” Mwanayo sanali kuyembekezela kuti atate ake angamukhululukile. Conco anawapempha ngati angakhale wanchito wa pakhomo. Koma atate akewo anali okonzeka kumukhululukila, moti anamuitana kuti “mwana wanga.” Ndipo anamutenga monga mwana wawo mmene zinalili poyamba. Atate akewo anakamba kuti mwana wawoyo “anatayika koma wapezeka.” (Luka 15:​11-32) Pamene Yesu anali kumwamba asanabwele padziko lapansi, anaona mmene Atate wake anaonetsela cifundo coteloco kwa anthu ocimwa kwambili amene analapa. Fanizo limene Yesu anafotokoza limatikhazika mtima pansi, ndipo limaonetsa cifundo cimene Atate wathu, Yehova, ali naco!

Mwana woloŵelela amene Yesu anafotokoza m’fanizo lake akuwelamila atate ake amene akuthamanga kubwela kudzamukumbatila.

Tate wa m’fanizo la Yesu la mwana woloŵelela, akuthamanga kukakumbatila mwana wake yemwe wabwelela kunyumba. (Onani ndime 11-12)


13-14. Kodi mtumwi Petulo anaphunzila ciyani pa nkhani ya kulapa? Ndipo kodi ena anawauza ciyani za nkhaniyi? (Onaninso cithunzi.)

13 Mtumwi Petulo anaphunzila zambili kwa Yesu pa nkhani ya kulapa na kukhululuka. Petulo anali kulakwitsa zinthu kaŵilikaŵili, ndipo nthawi iliyonse Yesu anali wokonzeka kumukhululukila. Mwacitsanzo, pomwe Petulo anakana Mbuye wake katatu, iye anakhala na cisoni cofa naco. (Mat. 26:​34, 35, 69-75) Koma Yesu ataukitsidwa, anaonekela kwa Petulo. N’kutheka kuti iye anaonekela kwa Petulo pomwe Petuloyo anali kwayekha. (Luka 24:​33, 34; 1 Akor. 15:​3-5) Mosakaikila, pa cocitikaci Yesu anakhululukila mtumwi ameneyo ndipo anamutsimikizila kuti anamukhululukiladi.—Maliko 16:7.

14 Petulo anamvetsa mmene zimamvekela kulapa na kukhululukidwa. Conco iye anayamba kuphunzitsa ena za nkhani ya kulapa na kukhululuka. Patapita kanthawi pambuyo pa Cikondwelelo ca Pentekosite, Petulo anakamba nkhani kwa khamu la Ayuda osakhulupilila, ndipo anawafotokozela kuti Ayudawo anapha Mesiya. Ngakhale n’telo, iye anawalimbikitsa mwacikondi kuti: “Lapani ndi kutembenuka kuti macimo anu afafanizidwe, ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwele kucokela kwa Yehova.” (Mac 3:​14, 15, 17, 19) Motelo, Petulo anaonetsa kuti kulapa kumasonkhezela munthu wocimwa kutembenuka, kutanthauza kusintha kaganizidwe kake na kacitidwe kake ka zinthu. Ndipo munthuyo amayamba kutsatila njila yatsopano yomwe ingakondweletse Mulungu. Mtumwiyu anawaonetsanso kuti Yehova akanafafaniza macimo awo kapena kuti kuwacotselatu. Patapita zaka zambili, Petulo anatsimikizila Akhristu kuti: “Yehova . . . sakufuna kuti anthu adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) N’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova amatikhululukila na mtima wonse tikalapa macimo athu ngakhale kuti tinacita macimo aakulu!

Zithunzi: 1. Mtumwi Petulo akulila mowawidwa mtima. 2. Yesu woukitsidwayo akulankhula na Petulo momutonthoza.

Yesu anatsimikizila mtumwi Petulo mwacikondi kuti wamukhululukila (Onani ndime 13-14)


15-16. (a) Kodi Paulo anaphunzila bwanji za kukhululuka? (1 Timoteyo 1:​12-15) (b) Nanga tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

15 Saulo wa ku Tarisi anacita macimo ambili oipa. Iye anali kuzunza mwankhanza otsatila okondeka a Khristu. Koma Yesu woukitsidwayo anali kudziŵa kuti Paulo angathe kusintha na kulapa. Iye na Atate wake anaona makhalidwe abwino mwa Saulo. Yesu anakamba kuti: “Munthu ameneyu ndi ciwiya canga cosankhidwa.” (Mac. 9:15) Yesu anagwilitsa nchito cozizwitsa kuti athandize Saulo kulapa. (Mac. 7:58–8:3; 9:​1-9, 17-20) Pambuyo pokhala Mkhristu, Saulo amene pambuyo pake anadzachedwa Paulo, nthawi zambili anali kukamba za ciyamikilo cimene anali naco kwa Yehova na Yesu pomukomela mtima komanso pomucitila cifundo. (Ŵelengani 1 Timoteyo 1:​12-15.) Paulo anakamba kuti: “Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu, kusakwiya msanga komanso kuleza mtima n’colinga coti ulape.”—Aroma 2:4.

16 Paulo atamva za khalidwe locititsa manyazi la ciwelewele mumpingo wa Cikhristu wa ku Korinto, kodi anacita ciyani? Mmene iye anacitila na nkhani imeneyi, kumatiphunzitsa mmene Yehova amaonetsela cikondi mwa kupeleka cilango kwa atumiki ake, komanso kuwaonetsa cifundo akalapa. Tidzakambilana mozamilapo za nkhani imeneyo m’nkhani yotsatila.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yehova anawauza ciyani Aisiraeli za kulapa?

  • Kodi Yehova wakhala akuwathandiza bwanji anthu kulapa?

  • Kodi otsatila a Yesu anaphunzila ciyani za kulapa?

NYIMBO 33 Tulila Yehova Nkhawa Zako

a Nkhaniyi inali yapadela. Masiku ano, Yehova sakakamiza munthu wolakwilidwa kukhalabe mu ukwati na munthu amene wacita cigololo. Ndipo mwacikondi, Yehova anauza Mwana wake kufotokoza kuti, mwamuna kapena mkazi angasankhe kuthetsa ukwatiwo ngati angafune kutelo.—Mat. 5:32; 19:9.

b Onani nkhani yakuti “Yehova Ndi Wofunitsitsa Kukukhululukilani” mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2012, tsamba 21-23, ndime 3-10.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani