LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 June masa. 20-25
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kusankha Kutumikila Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kusankha Kutumikila Yehova
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • THANDIZANI WOPHUNZILA WANU KUZINDIKILA ZIMENE ZIKUMULEPHELETSA KUPITA PATSOGOLO
  • THANDIZANI WOPHUNZILA WANU KUZAMITSA CIKONDI CAKE PA YEHOVA
  • THANDIZANI WOPHUNZILA WANU KUIKA ZOFUNIKA PATSOGOLO
  • THANDIZANI WOPHUNZILA WANU KUDZIWA ZOCITA AKAMATSUTSIDWA
  • ONETSANI KUTI MUMAM’DALILA WOPHUNZILA WANU
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuti Akakhale Ophunzila Obatizika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 2
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 1
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • ‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzila Anga’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 June masa. 20-25

NKHANI YOPHUNZILA 27

NYIMBO 79 Aphunzitseni Kucilimika

Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kusankha Kutumikila Yehova

“Khalani ndi cikhulupililo colimba . . . Khalani amphamvu.”​—1 AKOR. 16:13.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mmene tingathandizile maphunzilo athu a Baibo kukhala ndi cikhulupililo, komanso kukhala olimba mtima kuti ayambe kutumikila Yehova.

1-2. (a) N’ciyani cimadodometsa maphunzilo ena a Baibo kuti ayambe kutumikila Yehova? (b) Tikambilana ciyani m’nkhani ino?

KODI pa nthawi ina munadodomapo kukhala wa Mboni za Yehova? Mwina munali kuopa kuti anzanu a ku nchito, mabwenzi anu, kapena a m’banja lanu angakwiye nanu. Mwinanso munali kuona kuti simungakwanitse kutsatila malamulo a Yehova pa umoyo wanu. Ngati n’telo, mungawamvetse maphunzilo anu amene akuoneka ngati akudodoma kuti ayambe kutumikila Yehova.

2 Yesu anazindikila kuti mantha aconco angalepheletse munthu mosavuta kuti akule ku uzimu. (Mat. 13:​20-22) Komabe, iye sanaleke kuthandiza awo amene anali kuzengeleza kuti amutsatile. M’malomwale, kudzela m’zimene anacita, iye anationetsa mmene tingathandizile anthu otelo (1) kuzindikila zimene zikuwalepheletsa kuyamba kutumikila Yehova, (2) kuzamitsa cikondi cawo pa Yehova, (3) kuika zinthu zofunika patsogolo, ndi (4) kudziwa zimene angacite akamatsutsidwa. Tingatengele motani citsanzo ca Yesu pamene tikugwilitsa nchito buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! pothandiza wophunzila kuyamba kutumikila Yehova?

THANDIZANI WOPHUNZILA WANU KUZINDIKILA ZIMENE ZIKUMULEPHELETSA KUPITA PATSOGOLO

3. N’kutheka kuti n’ciyani cinali kulepheletsa Nikodemo kukhala wophunzila wa Yesu?

3 Nikodemo, mtsogoleli wochuka waciyuda, anali ndi copinga cimene cinali kumulepheletsa kukhala wophunzila wa Yesu. Patangodutsa miyezi 6 Yesu atayamba utumiki wake, Nikodemo anazindikila kuti Yesu anali woimilako Mulungu. (Yoh. 3:​1, 2) Komabe, Nikodemo anapita kukumana ndi Yesu mseli “cifukwa ankaopa Ayuda.” (Yoh. 7:13; 12:42) N’kutheka kuti iye anaganiza kuti adzataya zambili akakhala wophunzila wa Yesu.a

4. Kodi Yesu anam’thandiza motani Nikodemo kumvetsa zimene Mulungu anali kufuna kuti iye acite?

4 Nikodemo anali kucidziwa Cilamulo. Koma anafunika thandizo kuti amvetse zimene Yehova anali kufuna kuti iye acite. Kodi Yesu anamuthandiza motani? Yesu anali wokonzeka kukamba ndi Nikodemo nthawi iliyonse. N’cifukwa cake analola kulankhula naye usiku. Yesu anafotokozela Nikodemo momveka bwino zoyenela kucita kuti akhale wophunzila wake. Anamuuza kuti afunika kulapa macimo ake, kubatizika m’madzi, ndi kuonetsa cikhulupililo mwa Mwana wa Mulungu.​—Yoh. 3:​5, 14-21.

5. Tingam’thandize bwanji wophunzila kuzindikila zimene zikumulepheletsa kupita patsogolo?

5 Ngakhale kuti wophunzila Baibo amawadziwa bwino Malemba, angafunike thandizo kuti azindikile zimene zikumulepheletsa kupita patsogolo. N’kutheka kuti nchito kapena citsutso cocokela kwa a m’banja lake zingamulepheletse kukwanilitsa zolinga zake zauzimu. Monga anacitila Yesu, inunso muzikhala wokonzeka nthawi iliyonse kuthandiza wophunzila wanu. Mungamupemphe kuti mupite naye kokayenda. Pa nthawi ngati zimenezi pamene simukuphunzila, mungamuthandize kuti akhale womasuka kukufotokozelani zimene akukumana nazo. Mulimbikitseni kuti apange masinthidwe ofunikila, osati kuti akondweletse inu, koma kuti aonetse cikondi cake pa Yehova.

6. Mungathandize motani wophunzila kuti ayambe kugwilitsa nchito zimene amaphunzila? (1 Akorinto 16:13)

6 Ngati wophunzila ali ndi cidalilo cakuti Yehova adzamuthandiza kutsatila mfundo za m’Baibo, adzalimbikitsidwa kuyamba kugwilitsa nchito zimene amaphunzila. (Welengani 1 Akorinto 16:13.) Udindo umene tili nawo, tingauyelekezele ndi udindo wa mphunzitsi ku sukulu. Mukakumbukila nthawi imene munali pa sukulu, ndi mphunzitsi uti makamaka amene munali kukonda kwambili? Mwacidziwikile, anali mphunzitsi amene anali kukuthandizani moleza mtima kudziwa kuti mungakwanitse kucita bwino m’kalasi. Mofananamo, mphunzitsi wabwino wa Baibo samangophunzitsa wophunzila wake kudziwa zimene Mulungu afuna kuti iye azicita. Koma amatsimikizilanso wophunzila wakeyo kuti ndi thandizo la Yehova angakwanitse kupanga masinthidwe mu umoyo wake. Kodi mungatani kuti mukhale mphunzitsi wabwino?

THANDIZANI WOPHUNZILA WANU KUZAMITSA CIKONDI CAKE PA YEHOVA

7. Kodi Yesu anawathandiza bwanji amene anali kumumvetsela kuti akulitse cikondi cawo pa Yehova?

7 Yesu anali kudziwa kuti cikondi pa Mulungu n’cimene cingathandize ophunzila ake kugwilitsa nchito zimene anali kuphunzila. Nthawi zambili, iye anali kuwaphunzitsa zinthu zimene zinali kuwathandiza kukulitsa cikondi cawo pa Atate wawo wakumwamba. Mwacitsanzo, iye anayelekezela Yehova ndi munthu amene amapatsa zabwino ana ake. (Mat. 7:​9-11) N’kutheka kuti ena mwa anthu amene anali kumumvetsela Yesu sanaleledwe ndi atate amene anali kuwakonda. Ndiye ganizilani mmene iwo anamvela Yesu atafotokoza fanizo la tate wacifundo yemwe analandila mwana wake amene anacita zinthu zambili zoipa. Fanizo limenelo linathandiza anthuwo kuona kuti Yehova amawakonda kwambili komanso kuti amafuna kuwathandiza.​—Luka 15:​20-24.

8. Mungamuthandize motani wophunzila wanu kuzamitsa cikondi cake pa Yehova?

8 Inunso mungathandize wophunzila wanu kuzamitsa cikondi cake pa Yehova mwa kumuthandiza kumvetsa bwino makhalidwe a Mulungu mukamaphunzila. Nthawi zonse pophunzila naye, muzim’thandiza kuona cikondi ca Yehova m’zimene akuphunzila. Pokambilana za dipo, muunikileni mmene nkhaniyo ingamupindulile payekha. (Aroma 5:8; 1 Yoh. 4:10) Wophunzila angayambe kukonda Yehova akamaganizila mmene Yehova amamukondela payekha.​—Agal. 2:20.

9. N’ciyani cinathandiza Michael kusintha umoyo wake?

9 Michael wa ku Indonesia anaphunzila coonadi kwa a m’banja lake pomwe anali kukula, koma sanabatizike. Atafika zaka 18, iye anapita ku dziko lina kukagwila nchito yaudalaiva. Patapita nthawi, iye anabwelela ku Indonesia kukakwatila, koma anapitiliza kugwila nchito ku maiko ena. Pa nthawiyo, mkazi wake ndi mwana wake wamkazi anayamba kuphunzila Baibo ndipo anali kupita patsogolo. Koma amayi ake a Michael atamwalila, iye anabwelela ku Indonesia kukasamalila atate ake, ndipo anavomela kuyamba kuphunzila Baibo. Michael anakhudzika mtima kwambili pokambilana mbali yakuti “Kumbani Mozamilapo” m’phunzilo 27 la buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Ataganizila mmene Yehova anamvela poona Mwana wake Yesu akuzunzika, Michael anagwetsa misozi. Izi zinamulimbikitsa kuti akulitse ciyamikilo cake pa dipo, komanso kuti asinthe umoyo wake n’kubatizika.

THANDIZANI WOPHUNZILA WANU KUIKA ZOFUNIKA PATSOGOLO

10. Kodi Yesu anawathandiza motani ophunzila ake kuika zinthu zofunika patsogolo? (Luka 5:​5-11) (Onaninso cithunzi.)

10 Ena mwa ophunzila a Yesu anamuzindikila mosavuta kuti ndiye anali Mesiya wolonjezedwayo. Koma iwo anafunikilabe kuthandizidwa kuti aziika nchito yolalikila patsogolo. Pamene Yesu anauza Petulo ndi Andireya kuti amutsatile mosalekeza, iwo anali atakhala kale ophunzila ake kwa kanthawi. (Mat. 4:​18, 19) Iwo pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane, anali kugwila nchito ya usodzi ndipo inali kuyenda bwino. (Maliko 1:​16-20) Pamene Petulo ndi Andireya “anasiya maukonde awo,” n’kutheka kuti anali atapanga kale makonzedwe a mmene angasamalile mabanja awo kwinaku akutsatila Yesu. N’ciyani cinawathandiza kuika nchito yolalikila patsogolo pa bizinesi yawo? Nkhani ya m’buku la Luka imatiuza kuti Yesu anacita cozizwitsa cimene cinalimbikitsa cidalilo cawo mwa Yehova cakuti akhoza kuwasamalila.​—Welengani Luka 5:​5-11.

Petulo ndi Andireya akusiya bwato limene anali kusewenzetsa pa nchito yawo pomwe Yesu akuwauza kuti am’tsatile. Asodzi ena akhalabe m’bwato ndipo akusoka maukonde awo.

Tingaphunzile ciyani kwa Yesu tikaona mmene anathandizila ophunzila ake kuika Yehova patsogolo? (Onani ndime 10)b


11. Kodi tingagwilitse nchito motani zimene zinaticitikila polimbikitsa cikhulupililo ca wophunzila wathu?

11 N’zoona kuti sitingacite zozizwitsa monga anacitila Yesu. Koma tingafotokozele wophunzila wathu zocitika zoonetsa mmene Yehova amathandizila amene amamuika patsogolo mu umoyo wawo. Mwacitsanzo, kodi mukumbukila mmene Yehova anakuthandizilani mutayamba kupezeka ku misonkhano? N’kutheka kuti munakambilana ndi bwana wanu n’kumufotokozela kuti simudzagwilanso ovataimu ngati iwombana ndi nthawi ya misonkhano. Pouza wophunzila wanu zimene zinakucitikilani, m’fotokozeleni mmene cikhulupililo canu cinalimbila poona mmene Yehova anakuthandizilani kupanga cisankho coika patsogolo kulambila kwake.

12. (a) N’cifukwa ciyani tiyenela kutengako ofalitsa osiyanasiyana ku phunzilo lathu? (b) Mungagwilitse nchito motani mavidiyo kuti mum’fike pa mtima wophunzila wanu? Pelekani citsanzo.

12 Wophunzila wanu angapindulenso kumva mmene Akhristu ena anasinthila zinthu kuti aike Yehova patsogolo mu umoyo wawo. Conco muzipempha abale ndi alongo osiyanasiyana kukhala nanu pa phunzilo. Muziwapempha kuti afotokozeko mmene anaphunzilila coonadi, komanso zimene anacita kuti kutumikila Yehova kukhale cinthu cofunika kwambili mu umoyo wawo. Kuwonjezela apo, muzipatula nthawi yopenyelela mavidiyo ndi wophunzila wanu opezeka pa mbali yakuti “Kumbani Mozamilapo” kapena a pa mbali yakuti “Fufuzani” m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Mwacitsanzo, pokambilana phunzilo 37 mungamufotokozele mfundo za mu vidiyo yakuti Yehova Adzatisamalila.

THANDIZANI WOPHUNZILA WANU KUDZIWA ZOCITA AKAMATSUTSIDWA

13. Kodi Yesu anawathandiza motani ophunzila ake kukonzekela citsutso?

13 Yesu anauza otsatila ake mobwelezabweleza kuti padzakhala anthu owatsutsa ngakhale acibale awo. (Mat. 5:11; 10:​22, 36) Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anacenjeza ophunzila ake kuti akhoza kuphedwa cifukwa cotumikila Yehova. (Mat. 24:9; Yoh. 15:20; 16:2) Anawalimbikitsa kuti azikhala osamala mu ulaliki. Ndipo anawalangiza kuti asamakangane ndi owatsutsa, komanso kuti akhale ocenjela kotelo kuti apitilize kulalikila.

14. Tingamukonzekeletse motani wophunzila mocitila nawo anthu otsutsa? (2 Timoteyo 3:12)

14 Nafenso tingathandize wophunzila kudziwa zocita poyang’anizana ndi anthu otsutsa. Tingatelo pomuchulilako zinthu zozizilitsa m’nkhongono zomwe angamve kwa anzake akunchito, mabwenzi ake, ndi acibale ake. (Welengani 2 Timoteyo 3:12.) Anzake ena a ku nchito angayambe kumuseka cifukwa ca umoyo umene wasankha. Anthu ena, ngakhale acibale ake enieniwo, angayambe kutsutsa zimene amaphunzila m’Baibo. Tikawathandiza mwamsanga ophunzila athu mmene angacitile nawo anthu otsutsa, adzadziwa bwino zoyenela kucita akamatsutsidwa.

15. N’ciyani cingathandize wophunzila kudziwa mocitila akamatsutsidwa ndi acibale ake?

15 Ngati amene akumutsutsa wophunzila wanu ndi acibale ake, mulimbikitseni kuganizila cifukwa cake anthuwo akucita zimenezo. N’kutheka kuti iwo amaganiza kuti a Mboni akumuuza zabodza, kapena amangodana nazo Mboni za Yehova. Ngakhale acibale ena a Yesu sanali okondwela n’zimene iye anali kucita. (Maliko 3:21; Yoh. 7:5) Thandizani wophunzila wanu kukhala woleza mtima, komanso wosamala pocita zinthu ndi ena, kuphatikizapo a m’banja lake.

16. Tingam’thandize bwanji wophunzila wathu kuuzako ena mosamala zimene amaphunzila?

16 Ngati a m’banja lake aonetsa cidwi cofuna kumvetsela, wophunzila angacitebe bwino kusafotokoza zoculuka pa nthawi imodzi, kuopela kuti angawatopetse ndi kumvetsela, ndipo sangadzafunenso kukambilana naye. Conco, limbikitsani wophunzila wanu kuuzako ena zimene amakhulupilila m’njila yakuti asiyebe munthuyo ndi cidwi kaamba ka makambilano a m’tsogolo. (Akol. 4:6) Mwina mungamulimbikitse kuti apemphe a m’banja lake kupita pa jw.org. Izi zidzawathandiza kudziwa zambili zokhudza Mboni za Yehova, ndipo angacite zimenezo pa nthawi yawo komanso kusankha kuculuka kwa zimene afuna kuwelenga.

17. Tingamukonzekeletse motani wophunzila wathu kuyankha mafunso amene angafunsidwe okhudza Mboni za Yehova? (Onaninso cithunzi.)

17 Mungasewenzetsenso nkhani za pa jw.org zakuti “Mafunso Amene Amafunsidwa Kaŵilikaŵili” pothandiza wophunzila wanu kukonzekela mayankho acidule pa mafunso amene acibale ake kapena anzake a ku nchito angam’funse. (2 Tim. 2:​24, 25) Kumapeto kwa phunzilo lililonse, muzikambilana naye mbali yakuti “Anthu Ena Amakamba Kuti” m’buku la Kondwelani na Moyo kwa Muyaya! Muzilimbikitsa wophunzila wanu kuyeseza mayankho m’mawu akeake. Pakakhala pofunikila, musazengeleze kumuwongolela mmene angafotokozeleko ena zimene amakhulupilila. Makambilano otelo angamuthandize kuti azikhalila kumbuyo cikhulupililo cake molimba mtima.

Mlongo akuthandiza wophunzila wake kukonzekela ulaliki pamene akuphunzila. Wophunzilayo akulalikila kwa mlongoyo pogwilitsa nchito thilakiti yakuti “Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo?”

Limbikitsani wophunzila wanu kuuzako ena zimene amakhulupilila mwa kuyeseza naye (Onani ndime 17)c


18. Mungamulimbikitse motani wophunzila wanu kuti akhale wofalitsa? (Mateyo 10:27)

18 Yesu analimbikitsa ophunzila ake kuti aziuzako ena zimene amakhulupilila. (Welengani Mateyo 10:27.) Wophunzila amayamba kukhulupilila Yehova akayamba kuuzako ena zimene amakhulupilila. Kodi mungam’thandize motani wophunzila wanu kuziikila colinga coyamba kulalikila kwa ena? Pakalinganizidwa kampeni yolalikila ya mpingo, mulimbikitseni wophunzila wanu kuganizila zimene angacite kuti ayenelele kukhala wofalitsa. Mufotokozeleni cifukwa cake cakhala cosavuta kwa ambili kuyamba kulalikila pamakampeni aconco. Iye angapindulenso akalembetsa m’sukulu kuti azikambako nkhani pa misonkhano ya mkati mwa mlungu. Akatelo, azitha kufotokozelako ena molimba mtima zimene amakhulupilila.

ONETSANI KUTI MUMAM’DALILA WOPHUNZILA WANU

19. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuwadalila ophunzila ake? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?

19 Yesu asanabwelele kumwamba, anauza ophunzila ake kuti adzakhalanso nawo limodzi. Iwo sanamvetse kuti Yesu anali kuwauza kuti iwo adzapita kumwamba. Komabe, Yesu anaika maganizo ake pa kukhulupilika kwawo osati pa zikaiko zawo. (Yoh. 14:​1-5, 8) Iye anadziwa kuti iwo anafunikila nthawi kuti amvetse zinthu zina monga zokhudza ciyembekezo copita kumwamba. (Yoh. 16:12) Monga anacitila Yesu, nafenso tingam’dalile wophunzila wathu kuti ali ndi cikhumbo cofuna kukondweletsa Yehova.

Wophunzila amayamba kukhulupilila Yehova akayamba kuuzako ena zimene amakhulupilila

20. Kodi mlongo wina ku Malawi anaonetsa motani cidalilo mwa wophunzila wake?

20 Timakhalabe ndi ciyembekezo cakuti wophunzila wathu amafuna kucita zoyenela. Tiyeni tikambilane zimene zinacitikila mlongo wina wa ku Malawi dzina lake Chifundo. Iye anayamba kuphunzila Baibo m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! ndi mtsikana wina wa Katolika dzina lake Alinafe. Pambuyo pokambilana phunzilo 14, Chifundo anafunsa wophunzila wake mmene anali kuonela nkhani yogwilitsa nchito zifanizilo polambila. Alinafe anakwiya kwambili ndipo anayankha kuti, “Ico n’cisankho ca ine mwini!” Chifundo anada nkhawa poganiza kuti mwina Alinafe asiya kuphunzila Baibo. Koma Chifundo anakhalabe ndi ciyembekezo cakuti tsiku lina, Alinafe adzasiya kugwilitsa nchito zifanizilo. Pambuyo pa miyezi ingapo, Chifundo anafunsa Alinafe funso ya m’phunzilo 34 yakuti, “Pofika pano, kodi kuphunzila kwanu Baibo komanso za Mulungu woona Yehova, kwakupindulilani motani?” Chifundo anakamba kuti, “Alinafe anafotokoza mfundo zambili zosangalatsa. Imodzi mwa izo inali yakuti Mboni sizicita zinthu zimene Baibo imaletsa.’’ Posakhalitsa, Alinafe anasiya kugwilitsa nchito zifanizilo ndipo anayenelela ubatizo.

21. Kodi tingam’limbikitse motani wophunzila wathu kukhala ndi cifuno cotumikila Yehova?

21 Ngakhale kuti Yehova ndi “amene amakulitsa,” tili ndi udindo wothandiza wophunzila wathu kupita patsogolo. (1 Akor. 3:7) Sitimangom’phunzitsa zimene Mulungu amafuna kuti iye acite. Timam’thandiza kuzamitsa cikondi cake pa Yehova. Timam’limbikitsanso kuonetsa cikondico mwa kuika Yehova patsogolo. Ndipo timam’phunzitsanso mmene angadalilile Yehova akakumana ndi anthu otsutsa. Pomuonetsa kuti timam’dalila, timam’limbikitsa kuti nayenso angakwanitse kutsatila malamulo a Yehova ndi kuyamba kum’tumikila.

TINGAM’THANDIZE MOTANI WOPHUNZILA WATHU . . .

  • kuzindikila zimene zikumulepheletsa kupita patsogolo?

  • kukulitsa cikondi cake pa Yehova?

  • kuika Yehova patsogolo?

NYIMBO 55 Musaŵayope!

a Patapita zaka ziwili ndi hafu Nikodemo atakambilana ndi Yesu, iye anali akali membala wa khoti yaikulu ya Ayuda. (Yoh. 7:​45-52) Zolemba zina zakale zimati Nikodemo anakhala wophunzila Yesu atamwalila.​—Yoh. 19:​38-40.

b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Petulo ndi asodzi ena akusiya bizinesi yawo kuti atsatile Yesu.

c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mlongo akuthandiza wophunzila wake mmene angauzileko ena zimene amakhulupilila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani