NKHANI YOPHUNZIRA 33
NYIMBO 4 ‘Yehova ni M’busa Wanga’
Muzikhulupirira Kuti Yehova Amakukondani
“Ndakukokera kwa ine ndi cikondi cokhulupirika.”—YER. 31:3.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Cifukwa cake tiyenera kukhulupirira kuti Yehova amatikonda komanso zimene tingacite kuti titsimikize kuti amatikondadi.
1. Kodi n’cifukwa ciani munadzipatulira kwa Yehova? (Onaninso cithunzi.)
KODI mukumbukira zimene munamuuza Yehova m’pemphero podzipatulira kwa iye? Munapanga cisankho cimeneco mutafika pom’dziwa bwino komanso pom’konda. Munamulonjeza kuti kum’tumikira kudzakhala cinthu cofunika koposa mu umoyo wanu ndi kuti mudzapitiriza kumukonda ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu wonse, ndi mphamvu zanu zonse. (Maliko 12:30) Kucokera tsikulo, cikondi canu pa iye cakhala cikukulira-kulira. Ndiye mungayankhe bwanji wina atakufunsani kuti, “Kodi mumamukondadi Yehova?” Mosapeneka konse, mungamuyankhe kuti, “Inde, ndimamukonda kwambiri kuposa mmene ndimakondera munthu wina aliyense kapena cinthu cina ciliconse!”
Kodi mukukumbukira mmene cikondi canu pa Yehova cinalili pamene munadzipatulira kwa Iye ndi kubatizika? (Onani ndime 1)
2-3. Kodi Yehova akufuna kuti tikhale otsimikiza za ciani? Nanga tikambirana ciani m’nkhani ino? (Yeremiya 31:3)
2 Nanga mungayankhe bwanji wina atakufunsani kuti, “Kodi ndinu wotsimikiza kuti Yehova amakukondani pacanu?” Kodi mungazengereze kupereka yankho, mwina poganiza kuti ndinu wosayenerera cikondi ca Yehova? Mlongo wina amene anakula mobvutikira anati: “Ndidziwa kuti Yehova ndimamukonda. Izo n’zosacita kufunsa. Cimene ndimadzifunsa nthawi zambiri n’coti, Kodi Yehova amandikonda?” Nanga kodi Yehova amamva bwanji ponena za inu?
3 Yehova amafuna kuti mukhale wotsimikizadi kuti amakukondani. (Werengani Yeremiya 31:3.) Zoona n’zakuti Yehova anakukokerani kwa iye. Ndipo pamene munadzipereka kwa iye n’kubatizika, munalandira cinacake camtengo wapatali kucokera kwa iye, cikondi cake cokhulupirika. Cikondi cimeneci ndi cozama ndipo sadzakutayani konse. Cimamupangitsa kuona alambiri ake okhulupirika kuphatikizapo inu ngati “cuma capadera.” (Mal. 3:17) Yehova amafuna kuti mukhale wotsimikiza kuti amakukondani, ngati mmene mtumwi Paulo anacitira. Mwacidaliro, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera, mphamvu, msinkhu, kuzama kapena colengedwa ciliconse, sizidzatha kutisiyanitsa ndi cikondi ca Mulungu.” (Aroma 8:38, 39) Mu nkhani ino, tikambirana cifukwa cake tiyenera kulimbitsa citsimikizo cakuti Yehova amatikonda komanso zimene zingatithandize kucita zimenezo.
CIFUKWA CAKE TIYENERA KUKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA AMATIKONDA
4. Kodi ndi bodza liti limene Satana amafuna kuti tikhulupirire? Nanga tingalikanize motani?
4 Kukhulupirira kuti Yehova amatikonda kumatithandiza kuti ‘tilimbane ndi zocita zacinyengo’ za Satana. (Aef. 6:11) Satana adzacita ciliconse cotheka kuti atilepheretse kutumikira Yehova. Imodzi mwa njira zacinyengo zimene Satana amagwiritsa nchito ndi bodza lakuti Yehova satikonda. Musaiwale kuti Satana ndi munthu amene amafuna kupezerapo mpata pa zinthu zimene zikuticitikira. Nthawi zambiri amatiukira pamene tafooka. Izi zingacitike pamene tikuganizira za zoipa zimene zinaticitikira kale, mabvuto amene tikukumana nao palipano, kapena nkhawa yokhudza tsogolo lathu. (Miy. 24:10) Satana ali ngati mkango umene ukufuna-funa mpata woti ugwire nyama yosatetezeka. Satana amatengerapo mwai pamene tili ofooka kuti atipangitse kufuna kuleka kutumikira Yehova. Tikapitiriza kulimbitsa citsimikizo cathu cakuti Yehova amatikonda, tidzatha ‘kulimbana’ ndi macenjera a Satana.—1 Pet. 5:8, 9; Yak. 4:7.
5. N’cifukwa ciani muyenera kumva kuti Yehova amakukondani komanso kuti ndinu amtengo wapatali?
5 Kukhulupirira kuti Yehova amatikonda kumatithandiza kuti tiyandikirane naye kwambiri. N’cifukwa ciani tikutero? Yehova anatilenga kuti tizikondana wina ndi mnzake. Ena akationetsa cikondi, ifenso timalimbikitsidwa kuwakonda. Conco tikamva kuti Yehova amatikonda kwambiri ndi kutiona kuti ndife amtengo wapatali, ifenso tidzalimbikitsidwa kumukonda kwambiri. (1 Yoh. 4:19) Ndipo tikakulitsa cikondi cathu pa iye, iyenso adzakulitsa cikondi cake pa ife. Baibo imatiuza mosapita m’mbali kuti: “Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yak. 4:8) Nanga tingatani kuti tilimbitse citsimikizo cathu cakuti Yehova amatikonda?
N’CIANI CINGATITHANDIZE KUKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA AMATIKONDA?
6. Ngati sindife otsimikiza kuti Yehova amatikonda, kodi tingapempherere ciani?
6 Muzipemphera mwacindunji komanso mosalekeza. (Luka 18:1; Aroma 12:12) Nthawi zina mungafunike kupempha Yehova kangapo pa tsiku kuti akuthandizeni kuona mmene iye amakuonerani. Komabe, nthawi zina zingakhale zobvuta kutsimikizira mtima wathu kuona kuti Yehova amatikonda. Koma kumbukirani kuti Yehova ndi wamkulu kuposa mtima wanu. (1 Yoh. 3:19, 20) Iye amakudziwani bwino kuposa mmene inu mumazidziwira, ndipo amatha kuona zimene inu simungathe kuziona. (1 Sam. 16:7; 2 Mbiri 6:30) Conco, musazengereze ‘kumukhuthulira’ za mu mtima mwanu pomupempha kuti akuthandizeni kukhala wotsimikiza kuti amakukondani. (Sal. 62:8) Kenako citani mogwirizana ndi mapemphero anu posewenzetsa njira zotsatirazi.
7-8. Kodi Masalimo amanena ciani cimene cimatitsimikizira kuti Yehova amatikonda?
7 Muzikhulupirira zimene Yehova amakamba. Iye anauzira olemba Baibo kuti amufotokoze mmene alilidi. Davide, mmodzi mwa anthu olemba Baibo, anafotokoza kuti Yehova amasamala za ife. Iye analemba kuti, “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Iye amapulumutsa anthu amene akhumudwa.” (Sal. 34:18, mau a m’munsi.) Mukakhala wokhumudwa, mungamamve ngati muli nokha-nokha. Koma Yehova amalonjeza kuti pa nthawi ngati zimenezo amakhala pafupi ndi inu cifukwa m’pamene mukufunikira kwambiri thandizo lake. Davide analembanso kuti: “Sungani misozi yanga mʼthumba lanu lacikopa.” (Sal. 56:8) Yehova amaona mukamabvutika. Amasamala kwambiri za inu ndipo zimamukhudza akamaona zimene mukupitamo. Zili ngati kuti iye amasunga misozi yanu m’thumba lacikopa komanso kuiona kuti ndi yofunika kwambiri monga mmene munthu amene akuyenda m’cipululu angaonere madzi amene ali m’thumba lacikopa kukhala amtengo wapatali. Pa Salimo 139:3, Davide anauza Yehova kuti: “Mumadziwa ciliconse cimene ndikucita.” Yehova amaona zilizonse zimene mumacita, koma amaona kwambiri zabwino zimene mumacita. (Aheb. 6:10) Cifukwa ciani? Cifukwa n’cakuti Yehova amayamikira zilizonse zimene mumacita pofuna kumusangalatsa.a
8 Kudzera m’Mau ake olimbikitsa omwe ndi ouziridwa, zili ngati Yehova akunena kuti: “Ndikufuna udziwe kuti ndimakukonda kwambiri komanso ndimasamala za iwe.” Koma monga taonera kumbuyoku, Satana amalimbikitsa bodza lakuti Yehova sakukondani. Conco ngati nthawi zina mumakaikira zakuti Yehova amakukondani, mungacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzakhulupirira ndani, “tate wake wa bodza” kapena “Mulungu wa coonadi”?’—Yoh. 8:44; Sal. 31:5.
9. Kodi Yehova akuwatsimikizira ciani anthu amene amamukonda? (Ekisodo 20:5, 6)
9 Ganizirani mmene Yehova amamvera ponena za anthu amene amam’konda. Ganizirani zimene Yehova anauza Mose ndi Aisiraeli. (Werengani Ekisodo 20:5, 6.) Yehova analonjeza kuti adzapitiriza kuonetsa cikondi cokhulupirika kwa anthu amene amam’konda. Mau amenewa amatitsimizira kuti n’zosatheka kuti alambiri a Yehova amukonde koma iye osawakonda. (Neh. 1:5) Conco ngati nthawi zina mungafunikire citsimikizo cakuti Yehova amakukondani, imani pang’ono n’kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimam’konda Yehova?’ Kenako ganizirani izi: Ngati mumam’konda Yehova ndipo mumayesetsa kucita zimene zimamusangalatsa, khalani wotsimikiza kuti iye amakukondani kwambiri. (Dan. 9:4; 1 Akor. 8:3) M’mau ena, ngati simukaikira kuti mumam’konda Yehova, n’kukaikiriranji kuti amakukondani? Khalani wotsimikiza kuti Yehova amakukondani ndi kuti sadzakusiyani.
10-11. Kodi Yehova amafuna kuti muziiona bwanji dipo? (Agalatiya 2:20)
10 Muziganizira za dipo. Nsembe ya dipo la Yesu Khristu ndiyo mphatso yabwino koposa imene Yehova anapatsa mtundu wa anthu. (Yoh. 3:16) Koma kodi mphatsoyo inaperekedwanso kwa inu panokha? Inde. Ganizirani zinacitika kwa mtumwi Paulo. Iye asanakhale Mkhristu, anacitapo macimo akulu-akulu. Ndipo atakhala Mkhristu, anafunika kupitiriza kulimbana ndi kupanda ungwiro kwake. (Aroma 7:24, 25; 1 Tim. 1:12-14) Komabe iye anafika poyamba kuona dipo monga mphatso imene Yehova anapereka kwa iye pacake. (Werengani Agalatiya 2:20.) Kumbukirani kuti Yehova ndiye anauzira Paulo kulemba mau amenewa. Ndipo zonse zimene zinalembedwa m’Baibo zinalembedwa kuti zitilangize. (Aroma 15:4) Mau a Paulo aonetsa mmene Yehova amafunira kuti inu muzionera dipo. Amafuna kuti muziiona kuti ndi mphatso yocokera kwa iye kupita kwa inu pacanu. Mukayamba kuona dipo mwanjira imeneyi, mudzalimbitsa cidaliro canu cakuti Yehova amakukondani inuyo panokha.
11 Timayamikira Yehova cifukwa cotuma Yesu padziko lapansi kuti adzatifere. Koma cifukwa cina cimene Yesu anabwerera padziko lapansi ndi kudzauza anthu coonadi ponena za Mulungu. (Yoh. 18:37) Coonadi cimeneci cimaphatikizapo mmene Yehova amamvera ponena za ana ake.
MMENE YESU AMATITHANDIZIRA KUKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA AMATIKONDA
12. N’cifukwa ciani tiyenera kukhulupirira zimene Yesu anafotokoza ponena za Yehova?
12 Yesu ali padziko lapansi, anali kukonda kuuza anthu mmene Yehova alili. (Luka 10:22) Sitiyenera kukaikira zimene Yesu anafotokoza zokhudza Yehova cifukwa iye anali atakhala ndi Yehova kumwamba kwa zaka mabiliyoni asanabwere pa dziko lapansi. (Akol. 1:15) Yesu anadzionera yekha mmene Yehova amakondera ana ake okhulupirika. Kodi Yesu amawathandiza bwanji anthu kukhulupirira kuti Mulungu amawakonda?
13. Kodi Yesu amafuna kuti Yehova tizimuona motani?
13 Yesu amafuna kuti tiziona Yehova mmene iye amamuonera. M’mabuku a Uthenga Wabwino, Yesu anachula Yehova kuti “Atate” kwa nthawi zoposa 160. Polankhula ndi ophunzira ake, Yesu anali kuchula Yehova ndi mau akuti “Atate wanu” ndi akuti “Atate wanu wakumwamba.” (Mat. 5:16; 6:26) Yesu asanabwere padziko lapansi, atumiki okhulupirika a Yehova anali kuchula Yehova ndi maina ena audindo monga ‘Wamphamvuzonse,’ ‘Wapamwambamwamba,’ komanso ‘Mlengi Wamkulu.’ Koma kawiri-kawiri, Yesu anali kuchula Yehova kuti ‘Atate’ wathu. Izi zionetsa kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake azim’konda ngati mmene mwana amakondera atate ake amene amam’samalira. N’zoonekeratu kuti Yesu amafuna kuti tiziona Yehova mmene iye amamuonera, kuti ndi Tate wacikondi amene amakonda kwambiri ana Ake. Tiyeni tikambirane zitsanzo ziwiri pomwe Yesu anachula Yehova kuti “Atate.”
14. Kodi Yesu anaonetsa motani kuti aliyense wa ife ndi wofunika kwa Atate wathu wakumwamba? (Mateyu 10:29-31) (Onaninso cithunzi.)
14 Coyamba, onani mau a Yesu a pa Mateyu 10:29-31. (Werengani.) Mpheta ndi timbalame tocepetsetsa timene sitingathe kusonyeza cikondi kwa Yehova kapena kum’lambira. Ngakhale n’tero, Atate wathuyo amasamala kwambiri za mpheta iliyonse moti amadziwa ngakhale itagwera pansi. Ngati mbalame amaziona motero, ndiye kuli bwanji za aliyense wa atumiki ake okhulupirika amene amam’tumikira cifukwa comukonda! Amamuona kukhala wofunika kopambana. Yesu anatinso Atate wathu amadziwa kuculuka kwa tsitsi la m’mutu mwathu. Popeza kuti Yehova amadziwa ngakhale zinthu zing’ono-zingo’no zokhudza ife, sitikaikira kuti amasamaladi za ife. Ndithudi, Yesu amafuna kuti tizikhulupirira kuti aliyense wa ife ndi wamtengo wapatali kwa Atate wathu wakumwamba.
Yehova amasamala kwambiri za mpheta iliyonse, moti amadziwa ngakhale itagwera pansi. Ndiye kuli bwanji za aliyense wa atumiki ake okhulupirika amene amamutumikira cifukwa comukonda! (Onani ndime 14)
15. Kodi mau a Yesu a pa Yohane 6:44 amakuuzani ciani ponena za Atate wanu wakumwamba?
15 Onani citsanzo caciwiri pomwe Yesu anachula Yehova kuti “Atate.” (Werengani Yohane 6:44.) Atate wanu wakumwamba anakukokani inuyo panokha kapena kuti kukukopani mwacikondi kuti mubwere m’coonadi. N’ciani cinam’pangitsa kuti akukopeni? Cifukwa cakuti anaonamo mtima wabwino mwa inu. (Mac. 13:48) Pamene Yesu anakamba mau a pa Yohane 6:44, n’kutheka kuti anali kuloza ku mau a Yehova opezeka pa Yeremiya 31:3. Pa lembali, Yehova anauza anthu ake kuti: “Ndakukokera kwa ine ndi cikondi cokhulupirika [kapena kuti, nʼcifukwa cake ndapitiriza kukusonyeza cikondi cokhulupirika.]” (Yer. 31:3; mawu a m’munsi; yerekezerani ndi Hoseya 11:4.) Ganizirani tanthauzo la mau amenewa. Atate wathu wakumwamba amenenso ndi wacikondi amapitiriza kuonamo zabwino mwa inu, ngakhale zimene inuyo simungathe kuziona.
16. (a) Kodi Yesu akutiuza ciani kwenikweni? Ndipo n’cifukwa ciani tiyenera kum’khulupirira? (b) Kodi n’ciani cingakuthandizeni kukhala otsimikiza kuti Yehova ndi Atate wanu wabwino koposa? (Onaninso danga lakuti “Atate Amene Tonsefe Timafunikira.”)
16 Yesu pochula Yehova kuti Atate wathu, m’ceniceni akutiuza kuti: “Yehova si Atate wanga ndekha koma ndi Atate wanunso. Ndipo ndikukutsimikizirani kuti amakukondani ndi kuti amasamaladi za inu panokha.” Conco ngati nthawi zina mumakaikira zakuti Yehova amakukondani, yambani mwaima n’kudzifunsa kuti, ‘Kodi sindiyeneradi kukhulupirira mau a Mwana wake amene amawadziwa bwino Atate wathu, amenenso amalankhula zoona nthawi zonse?’—1 Pet. 2:22.
PITIRIZANI KULIMBIKITSA CIKHULUPIRIRO CANU CAKUTI YEHOVA AMAKUKONDANI
17. N’cifukwa ciani tiyenera kupitiriza kulimbitsa cikhulupiriro cathu cakuti Yehova amatikonda?
17 Tifunika kupitiriza kulimbitsa cikhulupiriro cathu cakuti Yehova amatikonda. Monga taonera kale, mdani wathu wamacenjera acinyengo, Satana, sagona tulo pofuna kutilepheretsa kutumikira Yehova. Satana amafuna kutifooketsa. Iye adzacita zilizonse zotheka kuti atipangitse kuona ngati Yehova satikonda. Koma tiyeni tim’cititse manyazi Satana posakhulupirira bodza lake lamkunkhuniza!—Yobu 27:5.
18. Kodi mungalimbitse bwanji cikhulupiriro canu cakuti Yehova amakukondani?
18 Kuti mulimbitse cikhulupiriro cakuti Yehova amakukondani, muyenera kupemphera kwa iye kuti akuthandizeni kuona makhalidwe abwino amene iye amaona mwa inu. Muziganizira mmene olemba Baibo ouziridwa anafotokozera za cikondi cake cacikulu. Cina, muzikumbukira kuti Yehova adzapitiriza kuonetsa cikondi kwa anthu amene amamukonda. Musamaiwale kuti Yehova anapereka dipo ngati mphatso kwa inu pacanu. Komanso muzikhulupirira mau acitsimikizo omwe Yesu ananena kuti Yehova ndi Atate wanu wakumwamba. Ndiyeno ngati wina wakufunsani kuti: “Kodi ndinudi wotsimikiza kuti Yehova amakukondani?” mudzatha kumuyankha motsimikiza kuti: “Inde amandikondadi! Ndipo tsiku lililonse ndimacita zonse zotheka poonetsa kuti inenso ndimam’konda!”
NYIMBO 154 “Cikondi Sicitha”
a Kuti mupeze Malemba otsimikizira kuti Yehova amatikonda, onani mutu wakuti “Kudzikayikira” m’buku la Chichewa lakuti Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu.