LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 October masa. 2-5
  • 1925—Zaka 100 Zapitazo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 1925—Zaka 100 Zapitazo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE ANALI KUYEMBEKEZELA SIZINACITIKE
  • NCHITO YOFALITSA COONADI PAWAILESI IKULA
  • CLARIFYING OUR BELIEFS
  • KUCITILA UMBONI YEHOVA
  • KUBWELELAKO KWA ANTHU ACIDWI
  • KUYANG’ANA M’TSOGOLO
  • 1924—Zaka 100 Zapitazo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • 1922—Zaka 100 Zapitazo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Njila Zolalikilila—Kugwilitsila Nchito Njila Zosiyanasiyana Polalikila Anthu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 October masa. 2-5
Khamu la abale ndi alongo pamsonkhano wa cigao mu 1925 aimilila panja kujambulitsa cithunzi, mumzinda wa Indianapolis, ku Indiana.

Msonkhano wacigao mumzinda wa Indianapolis, ku Indiana, mu 1925

1925​—Zaka 100 Zapitazo

“AKHRISTU akhala akuyembekezela caka cino mwacidwi kwambili,” inatelo Nsanja ya Mlonda ya January 1, 1925. Komabe, Nsanja imeneyi inaonjezela kuti: “Akhristu asade nkhawa kwambili ndi zimene zingacitike caka cino moti n’kulephela kugwila nchito mwacimwemwe imene Ambuye wawapatsa.” Kodi Ophunzila Baibo anali kuyembekezela ciani mu 1925? Kodi anakwanitsa kucita zinthu zotani m’nchito ya Ambuye ngakhale kuti zimene anali kuyembekezela sizinacitike?

ZIMENE ANALI KUYEMBEKEZELA SIZINACITIKE

Ophunzila Baibo ambili anali kuyembekezela kuti Paradaiso adzabwezeletsedwa padziko lapansi mu 1925. Cifukwa ciani? M’bale Albert Schroeder, amene anadzatumikilapo m’Bungwe Lolamulila, anafotokoza cifukwa cake motele: “Tinali kukhulupilila kuti mu 1925 odzodzedwa adzapita kumwamba, ndipo anthu okhulupilika monga Abulahamu, Davide, ndi ena adzaukitsidwa kuti akhale akalonga padziko lapansi.” Pamene cakaci cimadutsa, zimene anali kuyembekezela sizinacitike. Conco, m’pomveka kuti ena anakhumudwa.​—Miy. 13:⁠12.

Ngakhale kuti zimene Ophunzila Baibo ambili anali kuyembekezela sizinacitike, iwo anakhalabe okangalika pa nchito yolalikila, ndipo anayamba kuzindikila kuti nchitoyi ndiyo yofunika koposa. Mwacitsanzo, onani mmene anagwilitsila nchito wailesi pofalitsa coonadi kwa anthu ambili.

NCHITO YOFALITSA COONADI PAWAILESI IKULA

Ophunzila Baibo ataona kuti nyumba ya wailesi ya WBBR inagwila bwino nchito mu 1924, mu 1925 anamanga nyumba ina ya wailesi pafupi ndi mzinda wa Chicago, ku Illinois. Wailesiyo anaicha WORD. Ralph Leffler, mmodzi wa anthu amene anathandizila kumanga nyumba ya wailesi yatsopanoyi, anati: “Anthu ambili anali kumvetsela wailesi imeneyi maka-maka madzulo kuli kozizila.” Mwacitsanzo, banja lina limene linali kukhala mumzinda wa Pilot Station, ku Alaska, pamtunda wa makilomita oposa 5,000 kucokela panyumba ya wailesi imeneyi, anamvetselako imodzi mwa mapulogilamu oyambilila amene anaulutsidwa pawailesiyo. Banjalo litamvetsela pulogilamuyo, linalembela kalata amene anali kugwilila nchito panyumba ya wailesiyo. Kalatayo inali yowayamikila cifukwa ca pulogilamu yauzimu imene anamvetsela.

Kumanzele: Milongoti youlutsila ya nyumba ya mphempo yochedwa WORD ku Batavia, Illinois

Kulamanja: Ralph Leffler akugwila nchito m’nyumba youlutsila

Nsanja ya Mlonda ya December 1, 1925 pofotokoza kumadela kumene uthenga woulutsidwa ndi wailesiyi unali kufika, inati: “Wailesiyi ndi imodzi mwa mawailesi omwe amamveka kutali kwambili mu America monse. Anthu akutha kumvetsela wailesi imeneyi mu America monse, ku Cuba, ngakhale kumadela a kumpoto kwambili m’dziko la Alaska. Ambili omwe anali asanamvepo coonadi akhala ndi cidwi cifukwa comvetsela mapulogilamu a pawailesiyi.”

George Naish

Pa nthawi imodzi-modziyo, Ophunzila Baibo anafuna kuyamba kugwilitsa nchito wailesi polalikila uthenga wabwino ku Canada. Mu 1924, Ophunzila Baibo anamanga nyumba ya wailesi yochedwa CHUC mu mzinda wa Saskatoon, ku Saskatchewan. Inali imodzi mwa mawailesi acipembedzo oyambilila ku Canada. Pofika mu 1925, anafunika kupeza malo ena oti amangepo nyumba ya wailesi yaikulu. Conco, gulu lathu linasamutsila nyumba zao zoulutsila mau ku nyumba ina yakale ku Saskatoon, yomwe anagula n’kuikonza kuti aziulutsilamo mau.

Cifukwa ca nyumba youlutsila mauyi, anthu ambili okhala m’matauni ang’ono-ang’ono komanso m’midzi m’Pulovinsi ya Saskatchewan anamva uthenga wabwino kwa nthawi yoyamba. Mwacitsanzo, Amai Graham, omwe anali kukhala m’tauni ina yakutali atamvetsela wailesiyi, analemba kalata yopempha mabuku ophunzilila Baibo. M’bale George Naish anakamba kuti m’kalata imene maiyu analemba, anaonetsa kuti anali ndi cidwi cacikulu kwambili moti anam’tumizila mpambo wonse wa mabuku akuti Studies in the Scriptures. Posakhalitsa, Amai Graham anayamba kufalitsa uthenga wa Ufumu mpaka kumadela akutali.

CLARIFYING OUR BELIEFS

Nsanja ya Mlonda ya March 1, 1925, inali ndi nkhani yofunika kwambili yakuti “Kubadwa kwa Mtundu.” N’ciani cinapangitsa nkhaniyo kukhala yofunika kwambili? Kwa nthawi ndithu, Ophunzila Baibo anali kudziwa kuti Satana ali ndi gulu limene muli ziwanda, zipembedzo zonyenga, maboma, ndi a zamalonda. Pogwilitsa nchito nkhaniyi, “kapolo wokhulupilika ndiponso wanzelu” anathandiza abale kudziwa kuti Yehova nayenso ali ndi gulu, limene ndi losiyana kwambili ndi gulu la Satana. Ndipo magulu awiliwa amatsutsana. (Mat. 24:45) Kuonjezela apo, kapolo anafotokoza kuti Ufumu wa Mulungu unali utakhazikitsidwa mu 1914, ndipo m’caka cimeneci Satana ndi ziwanda zake anaponyedwa padziko lapansi pa nkhondo imene inacitika kumwamba.​—Chiv. 12:​7-9.

Ophunzila Baibo ena cinawabvuta kubvomeleza kamvedwe katsopanoka. Kapolo poonelatu zimenezi, ananena izi mu Nsanja ija: “Ngati pali ena omwe awelenga nkhaniyi koma sakugwilizana nayo, tikuwalimbikitsa kuti akhale oleza mtima ndi kukhulupilila Ambuye, akum’tumikila ndi mtima woyela.”

M’bale Tom Eyre, kopotala (masiku ano timati mpainiya) wa ku Britain, anafotokoza mmene Ophunzila Baibo ambili anamvela. Anati: “Abale anasangalala kwabasi atamva kufotokozedwa kwa Chivumbulutso 12. Titangozindikila kuti Ufumu wa Mulungu unali utakhazikitsidwa kumwamba, tinagwila nchito yolengeza uthenga wabwinowu ndi cimwemwe cacikulu. Mfundoyi inasonkhezela cangu cathu pa nchito yolalikila. Inatithandizanso kuona kuti Yehova adzacita zinthu zazikulu m’tsogolo.”

KUCITILA UMBONI YEHOVA

Masiku ano, a Mboni za Yehova amawadziwa bwino mau a pa Yesaya 43:10 akuti: “ ‘Inu ndinu Mboni zanga,’ akutelo Yehova, ‘Inde, mtumiki wanga amene ndamusankha.’ ” Komabe, cisanafike caka ca 1925, lembali silinali kugwilitsidwa nchito kawili-kawili m’zofalitsa zathu. Koma izi zinali zitatsala pang’ono kusintha. M’caka ca 1925 cokha, Yesaya 43:10 ndi 12 inafotokozedwa m’magazini a Nsanja ya Mlonda okwana 11!

Kumapeto kwa August 1925, Ophunzila Baibo anacita msonkhano wacigao mumzinda wa Indianapolis, ku Indiana. Pa uthenga wolonjela omvela womwe unapulintidwa pa kapulogilamu, M’bale Joseph F. Rutherford anati: “Tabwela pamsonkhano uno kuti tipeze . . . mphamvu mwa Ambuye kuti pomwe tikubwelela m’munda tikhale titakulitsa cikhumbo cathu cofuna kukhala Mboni zake.” Pa masiku onse 8 a msonkhano umenewo, opezekapo analimbikitsidwa kucitila umboni Yehova pa mpata ulionse.

Pa Ciwelu, pa August 29, M’bale Rutherford anakamba nkhani yakuti “Tigwile Nchito Mwakhama.” M’nkhani yake, anagogomeza kufunika kocitila umboni pomwe anati: “Yehova akuti kwa anthu ake . . . : ‘Inu ndinu Mboni zanga . . . ndipo ine ndine Mulungu.’ Kenako akuwalamula mwamphamvu ndi momveka bwino kuti: ‘Anthu a mitundu yosiyana-siyana muwakwezele cizindikilo.’ Palibenso anthu ena padziko lapansi amene angakwezele anthu cizindikilo kupatulapo [anthu ake], anthu amene ali ndi mzimu wa Ambuye, amenenso ndi Mboni zake.”​—Yes. 43:12; 62:⁠10.

Thilakiti yokhala ndi uthenga wa pacikalata cochedwa “Uthenga Wopatsa Ciyembekezo.

Thilakiti yakuti Uthenga Wopatsa Ciyembekezo

M’bale  Rutherford atamaliza nkhani yake anawelenga cikalata cochedwa “Uthenga Wopatsa Ciyembekezo.” Omvetsela onse anagwilizana ndi uthenga wa m’cikalataci womwe unanena kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo udzabweletsa “mtendele, citukuko, thanzi labwino, moyo wosatha, ufulu, ndi cimwemwe cosatha.” Pambuyo pake, cikalataci cinamasulidwa m’zinenelo zingapo ndipo cinapulintidwa n’kumagwilitsidwa nchito mu utumiki. Ndipo makope pafupi-fupi 40 miliyoni anagawilidwa.

Koma sikuti Ophunzila Baibo anayamba kudziwika kuti Mboni za Yehova pa nthawiyi. Panatenga zaka zingapo kuti asinthe dzina lao. Koma apa anayamba kuzindikila kuti ali ndi udindo wocitila umboni Yehova.

KUBWELELAKO KWA ANTHU ACIDWI

Ophunzila Baibo ataonjezeka zungulile dziko lapansi, analimbikitsidwa kuti azibwelelako kwa anthu omwe anacita cidwi ndi uthenga wabwino. Kampeni yogawila kathilakiti kakuti Uthenga Wopatsa Ciyembezo itatha, Bulletina inapeleka malangizo akuti: “Bwelelan’koni kwa anthu omwe analandila kathilakiti kakuti Uthenga Wopatsa Ciyembekezo.”

Mu Bulletin ya January 1925 munali lipoti ili la Wophunzila Baibo wa mumzinda wa Plano, ku Texas: “N’zolimbikitsa kwambili kuti anthu m’magao amene talalikilamo kangapo, ali ndi cidwi kuposa m’magao amene tangoyamba kulalikilamo. M’gao lathu muli tauni ina yaing’ono imene yalalikidwa maulendo asanu pa zaka 10 zapitazi. . . . Caposacedwapa, Mlongo Hendrix ndi amai anabwelelako ku tauniyo ndipo anagawila mabuku ambili kuposa n’kale lonse.”

M’dziko la Panama, kopotala wina analemba kuti: “Anthu ambili omwe poyamba anakana kundimvetsela, amakhala atasintha pa ulendo waciwili kapena wacitatu. Caka cino, nthawi yanga yambili ya mu utumiki yathela pa kubwelelako kwa anthu acidwi. Ndipo ena mwa maulendowa akhala osangalatsa kwambili.”

KUYANG’ANA M’TSOGOLO

M’kalata yapacaka imene analembela akopotala onse, M’bale Rutherford anafotokoza mwacidule zocitika za m’caka ca 1925. Anawafotokozelanso nchito imene anafunika kugwila m’caka cotsatila. Anati: “Caka cino, munali ndi mwai wapadela wotonthoza anthu ambili acisoni. Nchitoyi yakupatsani cimwemwe . . . Caka catsopanoci cikupatseni mipata yocitila umboni Mulungu ndi Ufumu wake, komanso kuti ndani kwenikweni amene ali alambili ake. . . . Conco, tiyeni tonse pamodzi tigwilitse nchito mau athu potamanda Mulungu wathu ndi Mfumu yathu.”

Pomwe caka ca 1925 cinali kufika kumapeto, abale anayamba kuganiza zokuza Beteli ya ku Brooklyn. M’caka ca 1926 munali kudzagwilika nchito yomanga ya gulu imene inali isanacitikepo n’kale lonse.

Abale angoyamba kumene nchito yomanga zimango zatsopano.

Nchito yomanga pafupi ndi mseu wa Adams Street,ku Brooklyn, New York, mu 1926

a Masiku ano timati Umoyo ndi Utumiki Wathu Wacikhristu​—Kabuku ka Misonkhano.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani