KHALANI MASO!
Dziko Lapansi Likuwonongedwa—Kodi Baibo Ikambapo Ciyani?
“Anthu akucita zinthu zambili zimene posacedwa zingapangitse ngozi zacilengedwe monga izi: Kusefukila kwa madzi m’mizinda ikulu-ikulu, nyengo zotentha kwambili, mphepo zoopsa zamkuntho, kusoŵa kwa madzi akumwa, komanso kuthelatu, kapena kuti kusoloka, kwa mitundu yosiyana-siyana ya zomela na zinyama. Imeneyi si nkhani yongopeka kapena kukokomeza ayi. N’zimene asayansi akuticenjeza monga zotsatilapo zake za mmene tikucitila na zinthu zacilengedwe.”—Mawu a António Guterres, kalembela wamkulu wa bungwe la United Nations, pa msonkhano wa maboma wokambilana za kusintha kwa nyengo, pa April 4, 2022.
“Asayansi akucenjezanso kuti m’zaka zaposacedwa kuwonongedwa kwa nyengo kudzakhudza malo osungilako zinyama zakuchile okwanila 423 [a m’dziko la United States], amene ali paciopsezo cifukwa ca kutentha kwa nyengo. Zinthu zoopsa zimenezi zikumveka ngati matsoka amene timaŵelenga m’Baibo. Ena mwa matsoka amenewo ni awa: Moto walupsa, kusefukila kwa madzi, kusungunuka kwa madzi oundana, mafunde oopsa apanyanja, komanso nyengo zotentha.”—Inatelo nyuzipepala ya The New York Times, ya June 15, 2022, m’nkhani yake yakuti “Kusefukila kwa Madzi Ambili Kudela la Yellowstone, Cizindikilo ca Matsoka Amene Akubwela.”
Kodi mavuto obwela cifukwa ca kuwonongedwa kwa cilengedwe adzathetsedwa? Ngati adzathetsedwa, ndani adzawathetsa? Onani zimene Baibo imakamba.
Baibo Inanenelatu Kuti Anthu Adzawononga Cilengedwe
Baibo imakamba kuti Mulungu ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Vesi iyi ya m’Baibo imatiphunzitsa mfundo zitatu izi:
1. Zocita za anthu zidzawononga dziko lapansi kwambili.
2. Anthu sadzapitiliza kuwononga dziko lapansi.
3. Mulungu ndiye adzakonza dziko limene likuwonongedwa, osati anthu ayi.
Dziko Lapansi Lidzakhalanso Bwino M’tsogolo
Baibo imanena kuti “dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.” (Mlaliki 1:4) Pazikhalabe anthu padziko lapansi.
“Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.
Dziko lapansi lidzakonzedwanso bwinobwino.
“Cipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dela lacipululu lidzakondwa ndipo lidzacita maluŵa n’kukhala lokongola ngati duŵa la safironi.”—Yesaya 35:1.