LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mrt nkhani 57
  • Pindulani na Nsembe ya Yesu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pindulani na Nsembe ya Yesu
  • Nkhani Zina
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Phunzilo la Baibo
  • Misonkhano ya Mboni za Yehova
  • Nkhani za pa intaneti komanso mavidiyo
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakupindulileni Motani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Kupezeka pa Misonkhano Kumaonetsa Kuti Ndife Anthu Otani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mavidiyo Pophunzitsa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Kodi Yesu Ndani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Nkhani Zina
mrt nkhani 57
Yesu wanyamula mtengo wozunzikilapo umene adzaphedwelapo.

Pindulani na Nsembe ya Yesu

Kamodzi pa caka, Mboni za Yehova komanso anthu mamiliyoni amene amaitanidwa, amasonkhana padziko lonse kuti acite Cikumbutso ca imfa ya Yesu monga mmene iye analamulila. (Luka 22:19) Cocitika cimeneci cimatithandiza kuyamikila zimene Yesu anaticitila popeleka moyo wake kaamba ka anthu. Cimationetsanso mmene nsembe yake ingatithandizile pali pano komanso m’tsogolo.—Yohane 3:16.

Kaya munapezekapo pa Cikumbutso ca caka cino kapena ayi, kodi mungapindule bwanji na nsembe ya imfa ya Yesu? Iye anaphunzitsa kuti tiyenela kucita zinthu ziŵili zofunika izi:

  1. 1. Phunzilani za Mulungu komanso Yesu. Popemphela kwa Atate wake wakumwamba, Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

  2. 2. Seŵenzetsani zimene mukuphunzila. Yesu anagogomeza kuti tiyenela kuseŵenzetsa zimene anaphunzitsa mu umoyo wathu. Mwacitsanzo, pomaliza Ulaliki wake wochuka wa pa Phili, Yesu anayamikila onse ‘omva mawu ake na kuwacita.’ (Luka 6:46-48) Mofananamo, pa cocitika cina, Yesu anati: “Ngati zimenezi mukuzidziŵa, ndinu odala mukamazicita.”—Yohane 13:17.

Kodi mungakonde kuphunzila zambili za Mulungu na Yesu? Kodi mukufuna malangizo okuthandizani mmene mungaseŵenzetsele zimene mukuphunzila? Nazi njila zina zimene zingakuthandizeni.

Phunzilo la Baibo

Pulogalamu yathu ya maphunzilo a Baibo okambilana yathandiza anthu ambili kuisanthula Baibo na kuiseŵenzetsa pa umoyo wawo.

  • Pitani pa tsamba lakuti Kuphunzila Baibo Mothandizidwa ndi Munthu Wina kuti mudziŵe zambili za pulogalamu imeneyi

  • Onelelani vidiyo yakuti Takulandilani ku Phunzilo Lanu la Baibo kuti muone mmene phunzilo la Baibo limacitikila na Mboni za Yehova.

Misonkhano ya Mboni za Yehova

Mboni za Yehova zimasonkhana kaŵili pa mlungu kumalo awo olambilila ochedwa Nyumba ya Ufumu. Pa misonkhanoyi timakambilana Baibo na mmene tingaseŵenzetsele zimene imaphunzitsa pa umoyo wathu.

Aliyense ni wolandilidwa pa misonkhanoyi; simuyenela kucita kukhala Mboni kuti mupezekepo. Malinga na mmene zinthu zilili kwanuko, mungasankhe kupezeka pa misonkhanoyi pamasom’pamaso kapena pa vidiyokonfalensi.

  • Tambani vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? kuti muone zimene mungayembekezele pa misonkhano imeneyi.

  • Pezani malo a misonkhano pafupi na kwanu mwa kupita pa tsamba lakuti Misonkhano ya Mpingo ya Mboni za Yehova.

Nkhani za pa intaneti komanso mavidiyo

Nkhani zambili na mavidiyo pa webusaiti ino zingakuthanzeni kuphunzila zimene Yesu anaphunzitsa na kufunika kwa nsembe yake.

Mwacitsanzo, kuti mudziŵe mmene imfa ya munthu mmodzi imapindulila anthu mamiliyoni, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?” komanso yakuti “N’cifukwa Ciani Yesu Anavutika Ndi Kufa?” kapena tambani vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Yesu Anafa?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani