sinceLF/E+ via Getty Images
KHALANI MASO!
Kodi Ndani Adzapulumutsa Anthu?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Lipoti locokela ku bungwe la United Nations linati:
Kucoka pa October 7 kufika pa October 23, 2023, anthu 6,400 aphedwa pa nkhondo imene icitika ku Gaza, m’dziko la Israel. Ndipo anthu ena 15,200 avulazidwa. Ambili mwa anthuwa ni anthu wamba amene si asilikali. Kuwonjezela pa zimenezi, anthu masauzande ambili athaŵa na kusiya nyumba zawo.
Podzafika pa September 24, 2023, anthu 9,701 amene si asilikali anaphedwa pa nkhondo ya pakati pa Russia na Ukraine. Ndipo enanso okwana 17,748 anavulazidwa ku Ukraine.
Kodi Baibo imapeleka ciyembekezo cotani kwa anthu amene akuvutika cifukwa ca nkhondo?
Cifukwa cokhalila na ciyembekezo
Baibo imakamba kuti Mulungu adzathetsa “nkhondo padziko lonse lapansi.” (Salimo 46:9) Adzagwilitsa nchito boma la kumwamba, kapena kuti ufumu, umene udzaloŵa m’malo maboma onse a anthu. (Danieli 2:44) Ufumu wa Mulungu udzabweletsa mpumulo kwa anthu onse.
Onani zimene Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu Khristu, adzacita:
“Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, komanso wonyozeka ndi aliyense amene alibe womuthandiza. Adzamvela cisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzawapulumutsa kuti asawapondeleze komanso kuwacitila zaciwawa.”—Salimo 72:12-14.
Mulungu adzaseŵenzetsa Ufumu wake kucotsapo mavuto onse obwela cifukwa ca nkhondo na zaciwawa.
“Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kubuula kapena kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
Posacedwapa Ufumu wa Mulungu udzasintha zinthu padziko. Baibo inakambilatu za “nkhondo ndi malipoti a nkhondo” zimene zikucitika masiku ano. (Mateyu 24:6) Nkhondo komanso zocitika zina zambili zikuonetsa kuti tikukhala “m’masiku otsiliza” a ulamulilo wa anthu.—2 Timoteyo 3:1.