Kodi Baibo Imatipo Ciyani pa Nkhani ya Nkhondo ya Nyukiliya?
Dzikoli lili pa ciopsezo cakuti pangacitike nkhondo ya nyukiliya, cifukwa maiko amphamvu padziko lonse akupitiliza kuwonjezela zida zawo zankhondo. Kuwonjezeka kwa zida za nkhondo kukupangitsa anthu kukhala ndi nkhawa yaikulu yakuti nkhondo ya nyukiliya ingathe kubuka. Anthu alinso ndi nkhawa yakuti kuphulitsidwa kwa bomba limodzi laling’ono la nyukiliya kungayambitse nkhondo yaikulu imene ingawononge dziko lonse. Monga mmene buku lakuti Bulletin of the Atomic Scientists linakambila, “tikukhala ndi ciopsezo cakuti nkhondo ya nyukiliya ikhoza kucitika nthawi ina iliyonse.”
Kodi n’zothekadi kuti pangacitike nkhondo ya nyukiliya? Ngati n’conco kodi dzikoli lidzapulumuka? Nanga tingatani ngati tili ndi nkhawa yakuti pangacitike nkhondo ya nyukiliya? Kodi Baibo ikutipo ciyani?
Zimene zili m’nkhani ino
Kodi Baibo inakambilatu kuti kudzacitika nkhondo ya nyukiliya?
Kodi mungatani kuti mucepetse mantha anu akuti kudzacitika nkhondo ya nyukiliya?
Kodi Baibo imakamba kuti Aramagedo ndi nkhondo ya nyukiliya?
Kodi buku la Chivumbulutso limafotokoza za nkhondo ya nyukiliya?
Kodi Baibo inakambilatu kuti kudzacitika nkhondo ya nyukiliya?
Baibo sikamba mwacindunji za nkhondo ya nyukiliya. Komabe inakambilatu za makhalidwe ndi zocitika zimene zingapangitse kuti pacitike nkhondo ya nyukiliya.
Yelekezelani zimene mavesi a m’Baibo awa akufotokoza ndi zimene zikucitika m’dzikoli masiku ano:
Mavesi a m’Baibo: Ophunzila a Yesu anamufunsa kuti: “Kodi cizindikilo ca kukhalapo kwanu ndi ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciyani?” Yesu anayankha kuti “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina.”—Mateyu 24:3, 7.
Zocitika za m’dzikoli: Maiko ambili, kuphatikizapo aja amene ali ndi zida za nyukiliya kapena aja amene angakwanitse kupanga zida zimenezi, nthawi zambili amamenyana pogwilitsa nchito zida za nkhondo.
“Masiku ano zaciwawa ndi mikangano zakhala zikuwonjezeka kwambili padziko lonse.”—Linatelo lipoti la The Armed Conflict Location & Event Data Project.
Mavesi a m’Baibo: “Mu nthawi yamapeto mfumu yakumwela idzayamba kukankhana ndi mfumu yakumpoto.”—Danieli 11:40.
Zocitika za m’dzikoli: Maiko ambili akulimbana ndipo amapikisana polimbilana ulamulilo monga mmene Baibo inakambila. Ngakhale kuti masiku ano maiko omwe ali ndi mabomba amphamvu a nyukiliya samenyana mwacindunji, iwo akupitilizabe kupanga mabomba amphamvu a nyukiliya kuti akhale amphamvu kwambili.
“M’zaka 10 zapitazi, taona kuwonjezeka kwa mikangano pakati pa maiko, kuphatikizapo maiko akuluakulu omwe amathandizila ma ulamulilo oukila.”—Linatelo lipoti la The Uppsala Conflict Data Program.
Mavesi a m’Baibo: “Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. Anthu . . . adzakhala osafuna kugwilizana ndi ena, onenela ena zoipa, osadziletsa, oopsa.”—2 Timoteyo 3:1-3.
Zocitika za m’dzikoli: Anthu ambili masiku ano amakonda kukangana. Nawonso atsogoleli a maiko nthawi zambili amakangana wina ndi mnzake. M’malo mothetsa mikangano yawo mwamtendele, iwo amayamba kuopsezana kapena kukakamizana kucita zimene wina sakufuna. Zinthu ngati zimenezi n’zimene zingapangitse kuti nkhondo ya nyukiliya iyambe.
“Ngati sitipeza njila yothandiza kuti anthu azicita zinthu mwa mtendele ndiye kuti mikangano yoopsa iziwonjezeleka”.—Anatelo S. Saran ndi J. Harman, a m’bungwe la World Economic Forum.
Kodi Mulungu angalole kuti kucitike nkhondo ya nyukiliya?
Baibo siikamba ciliconse pa nkhaniyi, koma imati masiku ano kudzacitika “zinthu zoopsa” ndi zocititsa mantha. (Luka 21:11) Citsanzo ca zimenezi n’zomwe zinacitika pa nkhondo yaciwili ya padziko lonse pamene anthu anaphulitsa mabomba m’mwamba. Baibo imafotokoza cifukwa cake Mulungu walola kuti nkhondo zizicitika. Kuti mudziwe zambili onelelani vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?
Kodi dziko lapansi lidzapulumuka?
Inde. Ngakhale anthu atagwilitsa nchito mabomba a nyukiliya, Mulungu sangalole kuti zinthu zifike poipa kwambili moti dziko lonse n’kuwonongedwa. Baibo imakamba zakuti dziko lapansi silidzawonongedwa ndiponso kutianthu adzakhala mmenemo kwamuyaya.
Athu ena amaganiza kuti m’tsogolo, padziko lapansi padzakhala anthu ocepa cabe ndipo anthuwo azidzavutika kwambili cifukwa dziko lapansi lidzakhala litawonongeka ndi nkhondo ya nyukiliya. Komabe, Baibo imaonetsa kuti zonse zimene zidzawonongeka padziko lapansi cifukwa ca nkhondo zidzakonzedwanso.
Mulungu amafuna kuti tikakhale ndi umoyo wacimwemwe m’dziko labwino
Mlengi wathu analenga dziko lapansi mocititsa cidwi kuti lizitha kudzikonza lokha. Tikudziwanso kuti Mulungu adzagwilitsa nchito mphamvu zake kukonzanso dziko lapansi. Inde dziko lapansi lidzakhalapo mpaka kalekale, ndipo anthu adzakhala mmenemo kwamuyaya.—Salimo 37:11, 29; Chivumbulutso 21:5.
Kodi mungatani kuti mucepetse mantha anu akuti kudzacitika nkhondo ya nyukiliya?
Anthu ena amakhala ndi mantha akuti kudzacitika nkhondo ya nyukiliya, imene ingabweletse mavuto aakulu. Malonjezo ndi malangizo a m’Baibo angathandize anthu amene ali ndi mantha amenewo kuti acepetse mantha awo. Motani?
Baibo imafotokoza kuti zinthu zidzakhala bwino kwa anthu amene adzakhala pa dziko lapansi. Ciyembekezo cimeneci cili “ngati nangula wa miyoyo yathu” ndipo cimatithandiza kucepetsako nkhawa. (Aheberi 6:19, mawu a m’munsi) Tingacepetsenso nkhawa mwa kupewa kumangoganizila zimene zidzacitike m’tsogolo. Yesu anati: “Mavuto a tsiku lililonse ndi okwanila pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.
Tonsefe tiyenela kusamalila thanzi lathu. Tingacite zimenezi mwa kupewa kuwelenga kapena kuonelela nkhani zimene zingatibweletsele nkhawa, kapena kupewa kumvetsela nkhani zofotokoza za kupangidwa kwa mabomba atsopano a nyukilila. Izi sizitanthauza kuti tizingokhala mu cimbulimbuli. M’malomwake, timayesetsa kupewa kuganizila zinthu zimene mwina sizingacitike n’komwe.
Musamangoganizila nkhani zoipa za panyuzi, koma muzipeza nthawi yoganizila zinthu zabwino zimene zikucitika pa umoyo wanu.
Baibo imapeleka ciyembekezo cotsimikizika ca tsogolo labwino
Kuphunzila zambili za malonjezo a Mulungu kungakupatseni ciyembekezo, cimwemwe komanso mtendele wa mumtima.
Kodi Baibo imakamba kuti Aramagedo ndi nkhondo ya nyukiliya?
Anthu ena amaganiza kuti Aramagedo idzakhala nkhondo ya padziko lonse ya nyukiliya. Mosakaikila, iwo amaganizila mmene nkhondo imeneyi idzawonongela zinthu padziko lapansi.
Koma Baibo ikamakamba za Aramagedo imakamba za nkhondo imene idzacitike pakati pa “mafumu apadziko lonse” lapansi kulikonse kumene kuli anthu, kapena kuti pakati pa maboma a anthu ndi Mulungu.a (Chivumbulutso 16:14, 16) Sikuti nkhondo ya Aramagedo idzapulula anthu onse ngati mmene bomba ya nyukiliya ingacitile, koma pa nkhondo imeneyi Mulungu adzawononga anthu okhawo amene ndi oipa. Ndipo izi zidzabweletsa mtendele weniweni ndi citetezo.—Salimo 37:9, 10; Yesaya 32:17, 18; Mateyu 6:10.
Kodi Baibo imati nkhondo zidzatha bwanji?
Yehovab Mulungu adzaonetsa kuti ndi wamphamvu kuposa maiko onse amene amacita nkhondo pothetsa mikangano yawo komanso kuwononga zida zawo za nkhondo. Iye adzacita zimenezi pogwilitsa nchito Ufumu wake umene ndi boma la kumwamba limene lidzalamulila dziko lonse lapansi.—Danieli 2:44.
Ufumu wa Mulungu udzaphunzitsa anthu mmene angakhalile mwamtendele komanso mogwilizana, popeza dziko lonse lizidzalamulidwa ndi boma limodzi. Mikangano yonse ya pakati pa maiko idzatha ndipo anthu sadzaphunzilanso nkhondo! (Mika 4:1-3) Padzakhala zotulukapo zotani? “Aliyense adzakhala mwamtendele pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa nkhuyu, palibe amene adzawacitisa mantha.”—Mika 4:4, Today’s English Version.
a Onani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo ya Aramagedo N’ciyani?”
b Yehova ndilo dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndani?”