Photo by Stringer/Getty Images
KHALANI MASO!
Nkhondo Imene Ikucitika ku Middle East—Kodi Baibo Ikambapo Ciani?
Anthu padzikoli ali ndi nkhawa cifukwa ca nkhondo imene ikucitika pakati pa maiko a America, Israel ndi Iran. Izi zacititsa kuti anthu ambili akhale ndi nkhawa yakuti mwina zimenezi zingabweletse nkhondo yaikulu imene ingakhuze maiko ambili. Kodi maboma angakwanitse kuthetsa nkhondo imeneyi ndi kubweletsa mtendele padzikoli?
Anthu amene anamvako za ulosi wa m’Baibo angayambe kuganiza kuti nkhondo imene ikucitika ku Middle East ndi ciyambi ca nkhondo ya Aramagedo yochulidwa m’buku la Chivumbulutso.
Kodi Baibo imakambapo ciani?
Kodi maboma adzakwanitsa kuthetsa nkhondo imene ikucitika ku Middle East?
Baibo imati: “Musamakhulupilile anthu olemekezeka kapena mwana wa munthu amene sangabweletse cipulumutso.”—Salimo 146:3.
Sitikudziwa ngati maboma angathe kukhazikitsa mtendele m’maiko amene akukhuzidwa ndi nkhondo ku Middle East. Komabe, Baibo imakamba momveka bwino kuti atsogoleli a ndale, maboma, kapena gulu lililonse la anthu sangathe kubweletsa mtendele padziko. Ndi Mulungu yekha ‘adzathetsa nkhondo padziko lonse lapansi.’—Salimo 46:9.
Kuti mudziwe zambili, welengani Nsanja ya Mlonda ya mutu wakuti “Kodi Nkhondo Zidzatha Bwanji?”
Kodi nkhondo imene ikucitika ku Middle East ikukwanilitsa ulosi?
Baibo imati: “Mudzamva phokoso la nkhondo ndi malipoti a nkhondo. . . . Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina.”—Mateyo 24:6, 7.
Nkhondo imene ikucitika ku Middle East ndi cizindikilo cina ca “mapeto a nthawi ino” komanso umboni wakuti tikukhaladi ‘m’masiku otsiliza.’ (Mateyo 24:3; 2 Timoteyo 3:1) Conco nkhondo zimene zikucitika masiku ano, zionetsa kuti posacedwapa Mulungu adzacitapo kanthu kuti athetse nkhondo komanso mabvuto ena amene tikukumana nao.
Kuti mudziwe zambili, welengani nkhani yakuti “Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti Nthawi “ya Mapeto” N’chiyani?”
kodi nkhondo ya Aramagedo idzayambila ku Middle East?
Baibo imati: “Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene mʼCiheberi amachulidwa kuti Aramagedo.”—Chivumbulutso 16:16.
Nkhondo ya Aramagedo si nkhondo ya pakati pa maboma a anthu imene idzayambila ku Middle East. Ndi nkhondo imene idzakhudza dziko lonse lapansi, ndipo idzacitika pakati pa maboma a anthu ndi Mulungu.
Kuti mudziwe zambili, welengani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo ya Aramagedo N’ciyani?”
N’ciani cingatithandize kukhala ndi mtendele wa mumtima pa nthawi zobvuta zimenezi?
Baibo imati: “Musamade nkhawa ndi cinthu ciliconse. Mʼmalomwake, nthawi zonse muzipemphela kwa Mulungu, muzimucondelela kuti azikutsogolelani pa ciliconse ndipo nthawi zonse muzimuthokoza.”—Afilipi 4:6.
Yehovaa Mulungu amafuna kuti tizipemphela kwa iye. Cifukwa cakuti Mulungu amatidela nkhawa, iye amamvetsela tikamapemphela ndipo amatithandiza kulimbana ndi nkhawa zimene timakhala nazo. (1 Petulo 5:7) Amacita zimenezi mwa kutithandiza kumvetsa cifukwa cake padzikoli pakucitika nkhondo, mmene adzazithetsela, komanso mmene adzathetsela mabvuto amene timakumana nao.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Kuti mudziwe mmene Mulungu amatithandizila, welengani nkhani yakuti “Kodi M’Baibulo Mungapezeke Mawu Omwe Angandilimbikitse?.”
a Yehova ndilo dzina leni-leni la Mulungu.—Salimo 83:18.